-
Mateyu 20:17-19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Ali panjira yopita ku Yerusalemu, Yesu anatengera pambali ophunzira ake 12 aja nʼkuwauza kuti:+ 18 “Tsopano tikupita ku Yerusalemu ndipo Mwana wa munthu akaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi. Iwo akamuweruza kuti aphedwe+ 19 ndipo akamupereka kwa anthu a mitundu ina kuti amuchitire chipongwe, kumukwapula ndi kumupachika pamtengo+ ndipo pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+
-
-
Luka 18:31-33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Kenako anatengera pambali ophunzira 12 aja nʼkuwauza kuti: “Tamverani! Tsopano tikupita ku Yerusalemu ndipo zonse zimene zinalembedwa ndi aneneri zokhudza Mwana wa munthu zikakwaniritsidwa.+ 32 Mwachitsanzo, akamupereka kwa anthu a mitundu ina+ ndipo akamuchitira chipongwe,+ kumunyoza komanso kumulavulira.+ 33 Akakamaliza kumukwapula akamupha,+ koma pa tsiku lachitatu iye adzauka.”+
-