58 Koma Petulo anapitiriza kumutsatira ali chapatali ndithu, mpaka anafika mʼbwalo lapanyumba ya mkulu wa ansembeyo. Atalowa mkati, anakhala pansi limodzi ndi antchito amʼnyumbamo kuti aone zotsatira zake.+
15 Ndiyeno Simoni Petulo komanso wophunzira wina ankatsatira Yesu.+ Wophunzira winayo ankadziwana ndi mkulu wa ansembe, choncho analowa limodzi ndi Yesu mʼbwalo lapanyumba ya mkulu wa ansembe.