-
Deuteronomo 21:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Ngati munthu wachita tchimo loyenera chiweruzo choti aphedwe,+ ndiyeno munthuyo waphedwa, ndipo mwamupachika pamtengo,+ 23 mtembo wake usamakhale pamtengopo usiku wonse.+ Mʼmalomwake, muzionetsetsa kuti mwamuika mʼmanda tsiku lomwelo, chifukwa munthu aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa ndi Mulungu.+ Musamaipitse dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale cholowa chanu.”+
-
-
Luka 23:50-52Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
50 Ndiyeno panali mwamuna wina dzina lake Yosefe, amene anali wa mʼKhoti Lalikulu la Ayuda. Munthu ameneyu anali wabwino komanso wolungama.+ 51 (Iye sanavomereze chiwembu chawo komanso zimene anachita.) Yosefe anali wochokera ku Arimateya, mzinda wa Ayudeya ndipo ankayembekezera Ufumu wa Mulungu. 52 Iye anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu.
-