-
1 Samueli 1:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Hana anali wokhumudwa kwambiri ndipo anayamba kupemphera kwa Yehova+ uku akulira kwambiri. 11 Iye analonjeza kuti: “Inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, mukaona kuvutika kwa ine kapolo wanu nʼkundikumbukira ndiponso mukapanda kundiiwala ine kapolo wanu nʼkundipatsa mwana wamwamuna,+ ndidzamʼpereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake ndipo lezala silidzadutsa mʼmutu mwake.”+
-