Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mateyu 19:16-22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Tsopano munthu wina anabwera kwa iye nʼkumufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi ndi zinthu zabwino ziti zimene ndikuyenera kuchita kuti ndikapeze moyo wosatha?”+ 17 Iye anamuyankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukundifunsa zokhudza zinthu zabwino? Pali mmodzi yekha amene ndi wabwino.+ Choncho ngati ukufuna kukapeza moyo, uzisunga malamulo nthawi zonse.”+ 18 Iye anafunsa kuti: “Malamulo ake ati?” Yesu anayankha kuti: “Musaphe munthu,*+ musachite chigololo,+ musabe,+ musapereke umboni wabodza.+ 19 Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu,+ komanso lakuti, Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+ 20 Mnyamatayo anayankha Yesu kuti: “Ndakhala ndikutsatira zonsezi, nʼchiyaninso china chimene ndikuyenera kuchita?” 21 Yesu anamuuza kuti: “Ngati ukufuna kukhala wangwiro,* pita ukagulitse katundu wako yense ndipo ndalama zake ukapatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba,+ ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+ 22 Mnyamatayo atamva zimenezi anachoka ali ndi chisoni, chifukwa anali ndi katundu wambiri.+

  • Maliko 10:17-22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pamene ankachoka kumeneko, mwamuna wina anamuthamangira nʼkugwada pamaso pake. Kenako anamufunsa kuti: “Mphunzitsi Wabwino, ndichite chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?”+ 18 Yesu anamuyankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukunditchula kuti wabwino? Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.+ 19 Iwe umadziwa malamulo akuti: ‘Musaphe munthu,*+ musachite chigololo,+ musabe,+ musapereke umboni wabodza,+ musabere munthu mwachinyengo+ ndiponso lakuti muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu.’”+ 20 Munthuyo anamuyankha kuti: “Mphunzitsi, zonsezi ndakhala ndikuzitsatira kuyambira ndili wamngʼono.” 21 Yesu anamuyangʼana ndipo anamukonda. Kenako anamuuza kuti, “Chinthu chimodzi chikusowekabe mwa iwe: Pita ukagulitse zinthu zimene uli nazo ndipo ndalama zake ukapatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+ 22 Koma iye atamva mawu amenewo anakhumudwa ndipo anachoka ali ndi chisoni, chifukwa anali ndi katundu wambiri.+

  • Luka 10:25-28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Kenako munthu wina wodziwa Chilamulo anaimirira kuti amuyese ndipo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, ndizichita chiyani kuti ndidzapeze moyo wosatha?”+ 26 Yesu anamufunsa kuti: “Kodi mʼChilamulo analembamo chiyani? Umawerengamo zotani?” 27 Iye anayankha kuti: “‘Muzikonda Yehova* Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, mphamvu zanu zonse ndi maganizo anu onse.’+ Komanso ‘uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’”+ 28 Yesu anamuuza kuti: “Wayankha molondola. Uzichita zimenezo ndipo udzapeza moyo.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena