-
Mateyu 14:14-17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Yesu atatsika mʼngalawayo anaona gulu lalikulu la anthu ndipo anawamvera chisoni+ nʼkuwachiritsira anthu awo odwala.+ 15 Koma chakumadzulo ophunzira ake anabwera kwa iye nʼkunena kuti: “Kuno nʼkopanda anthu ndipo nthawi yatha, auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite mʼmidzimo kuti akagule chakudya choti adye.”+ 16 Koma Yesu anawayankha kuti: “Palibe chifukwa choti apitire. Inuyo muwapatse chakudya.” 17 Iwo anamuuza kuti: “Tilibe chilichonse pano, kupatulapo mitanda 5 ya mkate ndi nsomba ziwiri zokha basi.”
-
-
Maliko 6:35-38Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
35 Tsopano kunja kunayamba kuda ndipo ophunzira ake anabwera kwa iye nʼkunena kuti: “Kuno nʼkopanda anthu ndipo nthawi yatha.+ 36 Auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite mʼmidzi yapafupi ndi mʼmadera ozungulira kuti akagule chakudya choti adye.”+ 37 Koma iye anawayankha kuti: “Inuyo muwapatse chakudya.” Yesu atanena zimenezi iwo anamufunsa kuti: “Kodi tipite kukagula mitanda ya mkate ya ndalama zokwana madinari* 200 nʼkuipereka kwa anthuwa kuti adye?”+ 38 Iye anawafunsa kuti: “Muli ndi mitanda ingati ya mkate? Pitani mukaone!” Ataiona ananena kuti: “Ilipo 5 ndi nsomba ziwiri.”+
-
-
Luka 9:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Komano nthawi inali chakumadzulo. Choncho atumwi 12 aja anabwera kwa iye nʼkunena kuti: “Kuno nʼkopanda anthu ndipo nthawi yatha, auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite mʼmidzi ndi mʼmadera ozungulira kuti akapeze malo ogona komanso chakudya choti adye.”+ 13 Koma iye anawayankha kuti: “Inuyo muwapatse chakudya.”+ Iwo anati: “Tilibe chilichonse kupatulapo mitanda ya mkate isanu ndi nsomba ziwiri zokha basi. Kapenatu tipite kukagula chakudya chokwanira anthu onsewa.”
-