-
Luka 6:12-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Mʼmasiku amenewo, Yesu anapita kuphiri kukapemphera+ ndipo anachezera usiku wonse kupemphera kwa Mulungu.+ 13 Kutacha, anaitana ophunzira ake nʼkusankhapo 12, amenenso anawapatsa dzina lakuti atumwi.+ 14 Iye anasankha Simoni, amene ankatchulidwa kuti Petulo, ndi Andireya mchimwene wake. Anasankhanso Yakobo, Yohane, Filipo,+ Batolomeyo, 15 Mateyu, Tomasi,+ Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni wotchedwa “wakhama.” 16 Komanso anasankha Yudasi mwana wa Yakobo ndi Yudasi Isikariyoti, amene pambuyo pake anamupereka.
-