132 Inu Yehova, kumbukirani Davide
Komanso mavuto onse amene anakumana nawo.+
2 Kumbukirani kuti analumbira kwa inu Yehova,
Analonjeza kwa Wamphamvu wa Yakobo kuti:+
3 “Sindidzalowa mutenti yanga, mʼnyumba yanga.+
Sindidzagona pabedi langa.
4 Sindidzalola kuti ndigone
Kapena kutseka maso anga,
5 Mpaka nditamupezera Yehova malo okhala,
Malo abwino oti Wamphamvu wa Yakobo azikhalamo.”+