Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide.
109 Inu Mulungu amene ndimakutamandani,+ musakhale chete.
2 Chifukwa anthu oipa ndiponso achinyengo akundinenera zinthu zoipa
Iwo akulankhula zinthu zabodza zokhudza ine.+
3 Andizungulira ndipo akulankhula mawu osonyeza kuti amadana nane,
Komanso akundiukira popanda chifukwa.+
10 Ana ake* aziyendayenda ndipo akhale opemphapempha.
Azichoka mʼmabwinja mmene akukhala, nʼkukafunafuna chakudya.
12 Pasapezeke womuchitira chifundo,*
Ndipo pasapezeke aliyense wosonyeza kukoma mtima kwa ana ake amasiyewo.
15 Nthawi zonse Yehova azikumbukira zimene achita.
Ndipo achititse kuti asadzakumbukiridwenso padziko lapansi.+
16 Chifukwa chakuti sanakumbukire kusonyeza chifundo,*+
Koma anapitiriza kuthamangitsa munthu woponderezedwa,+ wosauka komanso wosweka mtima,
Kuti amuphe.+
17 Iye ankakonda kutemberera, choncho matemberero anabwera pa iye.
Analibe mtima wofuna kudalitsa, choncho sanalandire madalitso.
18 Iye anavekedwa matemberero ngati chovala.
Ndipo anathiridwa mʼthupi mwake ngati madzi,
Ndiponso mʼmafupa ake ngati mafuta.
19 Matemberero ake akhale ngati nsalu imene amadziphimba nayo,+
Komanso ngati lamba amene amavala nthawi zonse.
20 Amenewa ndi malipiro amene Yehova amapereka kwa amene amalimbana nane+
Komanso kwa amene amalankhula zinthu zoipa zokhudza ine.
Ndipulumutseni chifukwa chikondi chanu chokhulupirika nʼchabwino.+
23 Ine ndikutha ngati chithunzithunzi chimene chimazimiririka.
Ndili ngati dzombe lomwe lakutumulidwa pa chovala.
Akandiona akumapukusa mitu yawo.+
26 Ndithandizeni, inu Yehova Mulungu wanga.
Ndipulumutseni ndi chikondi chanu chokhulupirika.
27 Iwo adziwe kuti zimenezi zachitika chifukwa cha dzanja lanu.
Adziwe kuti inu Yehova mwachita zimenezi.
28 Alekeni anditemberere, koma inu mundipatse madalitso.
Iwo akaimirira kuti andiukire, inu muwachititse manyazi,
Koma lolani ine mtumiki wanu kuti ndisangalale.
31 Chifukwa adzaima kudzanja lamanja la munthu wosauka,
Kuti amupulumutse kwa amene akumuweruza mopanda chilungamo.