Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 1 Thessalonians 1:1-5:28
  • 1 Atesalonika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 1 Atesalonika
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
1 Atesalonika

Kalata Yoyamba kwa Atesalonika

1 Ine Paulo, pamene ndili limodzi ndi Silivano+ ndi Timoteyo,+ ndikulembera mpingo wa Atesalonika wogwirizana+ ndi Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu, kuti:

Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere+ zikhale nanu.

2 Nthawi zonse timayamika Mulungu tikamatchula za inu nonse m’mapemphero athu.+ 3 Timatero pakuti timakumbukira nthawi zonse ntchito zanu zachikhulupiriro,+ ndi ntchito zanu zachikondi. Timateronso pokumbukira mmene munapiririra chifukwa cha chiyembekezo+ chanu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate. 4 Pakuti tikudziwa, inu abale okondedwa ndi Mulungu, kuti Mulunguyo ndiye anakusankhani.+ 5 Chifukwa pamene tinali kulalikira uthenga wabwino kwa inu, sitinali kungolankhula basi, koma uthengawo unakukhudzani kwambiri, komanso unabwera limodzi ndi mphamvu+ ya mzimu woyera, ndipo unachititsa kuti mukhale otsimikiza+ mtima kwambiri. Ndipo inuyo mukudziwa zimene tinakuchitirani pofuna kukuthandizani.+ 6 Choncho munatsanzira+ ifeyo komanso munatsanzira Ambuye,+ pakuti munalandira mawuwo ndi chimwemwe cha mzimu woyera+ ngakhale kuti munali m’masautso+ ambiri, 7 moti munakhala chitsanzo kwa okhulupirira onse ku Makedoniya ndi ku Akaya.

8 Ndipotu, si kuti mawu a Yehova+ ochokera kwa inu amveka ku Makedoniya ndi ku Akaya kokha ayi, koma kwina kulikonse chikhulupiriro+ chanu mwa Mulungu chafalikira,+ moti ife sitikufunika kunenapo kanthu. 9 Pakuti iwo amanena mmene ife tinafikira pakati panu koyamba. Amanenanso mmene inu munatembenukira kwa Mulungu, kusiya mafano+ anu kuti mutumikire Mulungu wamoyo+ ndi woona,+ 10 ndi kuyembekezera+ Mwana wake kuchokera kumwamba,+ amene anamuukitsa kwa akufa.+ Mwanayo ndi Yesu, amene akutipulumutsa ku mkwiyo ukubwerawo.+

2 Kunena zoona, inuyo mukudziwa abale, kuti ulendo+ wathu kwa inu sunali wopanda phindu.+ 2 Koma mukudziwa kuti choyamba titavutika+ ndi kuchitidwa zachipongwe+ ku Filipi,+ tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu ndipo tinalankhula+ kwa inu uthenga wabwino wa Mulungu movutikira kwambiri. 3 Pakuti sitikukudandaulirani chifukwa cha maganizo olakwika kapena odetsedwa,+ kapenanso mwachinyengo ayi. 4 Koma popeza Mulungu wationa kuti ndife oyenera kupatsidwa+ ntchito yolalikira uthenga wabwino, tikulankhula monga anthu okondweretsa+ Mulungu, yemwe amavomereza mitima+ yathu, osati monga okondweretsa anthu.

5 Ndipotu, sitinayambe talankhulapo mawu okuyamikirani mwachinyengo,+ (monga mukudziwira), kapena kuchita zachiphamaso+ chifukwa cha kusirira kwa nsanje.+ Mulungu ndiye mboni yathu. 6 Sitinali kungodzifunira ulemerero kwa anthu+ ayi, kaya kwa inu kapena kwa anthu ena. Sitinatero, ngakhale kuti monga atumwi a Khristu, tikanatha kupempha kuti mutilipirire+ zinthu zina kuti mutithandize. 7 M’malomwake, tinakhala odekha pakati panu monga mmene mayi woyamwitsa amasamalirira+ ana ake. 8 Choncho popeza timakukondani kwambiri,+ tinali okonzeka kukupatsani uthenga wabwino wa Mulungu. Ndipotu osati uthenga wokha ayi, komanso miyoyo+ yathu yeniyeniyo, chifukwa tinakukondani kwambiri.+

9 Ndithudi abale, mukukumbukira ntchito+ yathu imene tinagwira mwakhama ndi thukuta lathu. Mwa kugwira ntchito usiku ndi usana kuti aliyense wa inu asatilipirire kanthu kalikonse pofuna kutithandiza,+ tinalalikira uthenga wabwino wa Mulungu kwa inu. 10 Inu ndinu mboni, Mulungunso ndi mboni, za mmene tinakhalira okhulupirika, olungama, ndi opanda chifukwa chotinenezera,+ kwa inu okhulupirira. 11 Mogwirizana ndi zimenezi, inu mukudziwa bwino mmene tinali kudandaulira kwa aliyense wa inu, monga mmene bambo+ amachitira ndi ana ake, kukulimbikitsani+ ndi kukuchondererani, 12 n’cholinga choti mupitirize kuyenda+ m’njira imene Mulungu, amene akukuitanani+ ku ufumu+ wake ndi ulemerero, amafuna.

13 Ndithudi, n’chifukwa chake ifenso timayamikadi+ Mulungu mosalekeza. Pakuti pamene munalandira mawu a Mulungu+ amene munamva kwa ife, simunawalandire monga mawu a anthu+ ayi, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu. Mawu amenewa akugwiranso ntchito mwa inu okhulupirira.+ 14 Pakuti inu abale munatsanzira mipingo ya Mulungu yogwirizana ndi Khristu Yesu imene ili ku Yudeya. Munatero chifukwa inunso munayamba kuvutitsidwa+ ndi anthu akwanu, ngati mmene iwonso akuvutitsidwira ndi Ayuda, 15 amene anapha ngakhale Ambuye Yesu+ ndi aneneri+ ndi kuzunzanso ifeyo.+ Ndipo iwo sakukondweretsa Mulungu, koma akutsekereza zinthu zopindulitsa anthu onse. 16 Akutero pamene akuyesa kutiletsa+ kulankhula kwa anthu a mitundu ina kuti angapulumutsidwe.+ Chotsatira chake n’chakuti, pochita zimenezi nthawi zonse akudzazitsa+ machimo awo. Koma tsopano mkwiyo wake wawafikira.+

17 Koma ifeyo abale, pamene tinakakamizika kusiyana nanu kwa nthawi yochepa, tinapitiriza kukukumbukirani ngakhale kuti sitinali kukuonani, ndipo tinayesetsa kwambiri kuti tikwaniritse chilakolako+ chachikulu chimene tinali nacho chofuna kuona nkhope zanu. 18 Pa chifukwa chimenechi, tinafuna kubwera kwa inu. Ineyo Paulo ndinafuna kubwera kawiri konse, koma Satana anatchinga njira yathu. 19 Kodi chiyembekezo chathu, kapena chimwemwe chathu n’chiyani? Inde, mphoto*+ yathu yoinyadira pamaso pa Ambuye wathu Yesu, pa nthawi ya kukhalapo*+ kwake n’chiyani? Si inu amene kodi? 20 Ndithudi, inu ndinudi ulemerero wathu ndi chimwemwe chathu.

3 Choncho pamene sitinathenso kupirira, tinaona kuti ndi bwino tingotsala tokha ku Atene.+ 2 Chotero tinatumiza Timoteyo+ m’bale wathu ndi mtumiki wa Mulungu pa uthenga wabwino+ wonena za Khristu, kuti adzakulimbitseni ndi kukutonthozani pa chikhulupiriro chanu, 3 kuti pasapezeke wina wopatutsidwa ndi masautso+ amenewa. Pakuti inu nomwenso mukudziwa kuti tinayeneradi kukumana ndi zimenezi.+ 4 Ndiponso pamene tinali nanu limodzi, tinali kukuuziranitu+ kuti tiyenera kudzakumana ndi masautso,+ ndipo mmene zachitikiramu ndi mmenenso inu mukudziwira.+ 5 Ndiye chifukwa chake pamene sindinathenso kupirira, ndinamutuma kuti ndidziwe za kukhulupirika+ kwanu, kuti mwina mwa njira ina, Woyesayo+ angakhale atakuyesani, ndipo ntchito imene tinagwira mwakhama ingakhale itapita pachabe.+

6 Koma Timoteyo wangofika kumene kwa ife kuchokera kwa inu+ ndipo watiuza nkhani yabwino ya kukhulupirika kwanu ndi chikondi+ chanu. Akuti mukupitiriza kutikumbukira nthawi zonse, ndiponso mukulakalaka kutiona, monganso mmene ife tikulakalakiradi kukuonani.+ 7 Ndiye chifukwa chake abale, mwa kukhulupirika kumene mukusonyeza,+ mwatilimbikitsa+ m’kusowa kwathu konse ndi m’masautso athu onse. 8 Ndipo ife tsopano tilidi ndi moyo chifukwa inu mukukhala olimba mwa Ambuye.+ 9 Kodi Mulungu tingamuyamike bwanji pa nkhani ya inuyo, kuti timubwezere chifukwa cha chimwemwe+ chonse chimene tili nacho chifukwa cha inuyo pamaso pa Mulungu wathu? 10 Komanso usiku ndi usana timapereka mapembedzero amphamvu+ kuti tidzaone nkhope zanu ndi kukwaniritsa zimene zikusowa pa chikhulupiriro chanu.+

11 Tsopano Mulungu wathu ndi Atate mwiniyo, ndi Ambuye wathu Yesu,+ atitsogolere pa ulendo wathu wobwera kwa inu kuti zonse ziyende bwino. 12 Komanso, Ambuye akuthandizeni kuti muwonjezereke,+ ndiponso kuti chikondi+ chanu kwa okhulupirira anzanu ndi kwa ena onse chikule. 13 Achite zimenezi mpaka atalimbitsa mitima yanu ndi kukupangitsani kukhala opanda cholakwa+ ndi oyera pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate, pa nthawi ya kukhalapo*+ kwa Ambuye wathu Yesu, limodzi ndi oyera ake onse.+

4 Pomalizira abale, tinakulangizani za mmene muyenera kuyendera+ ndi mmene muyenera kukondweretsera Mulungu, ndipo mukuchitadi zimenezo. Tsopano tikufuna kukudandaulirani ndi kukupemphani m’dzina la Ambuye Yesu kuti mupitirize kuchita zimenezi mowonjezereka.+ 2 Pakuti mukudziwa malamulo+ amene tinakupatsani mwa ulamuliro wa Ambuye Yesu.

3 Mulungu akufuna kuti mukhale oyera+ mwa kupewa dama.*+ 4 Akufunanso kuti aliyense wa inu akhale woyera mwa kudziwa kulamulira thupi lake+ m’njira yoyera+ kuti mukhale olemekezeka pamaso pa Mulungu, 5 osati mwa chilakolako chosalamulirika cha kugonana,+ ngati chimene anthu a mitundu ina+ osadziwa Mulungu+ ali nacho. 6 Koma akufuna kuti pasapezeke wina wopweteka m’bale wake kapena womuphwanyira ufulu wake pa nkhani imeneyi,+ chifukwa Yehova adzalanga anthu onse ochita zimenezi,+ monga mmene tinakuuzirani kale ndi kukufotokozerani momveka bwino.+ 7 Pakuti Mulungu sanatiitane mwa kulekerera zodetsa, koma kuti tikhale oyera.+ 8 Choncho munthu wonyalanyaza+ chiphunzitso chimenechi sakunyalanyaza munthu, koma Mulungu+ amene amaika mzimu wake woyera+ mwa inu.

9 Koma za kukonda abale,+ n’zosafunika kuti tizichita kukulemberani pakuti inu nomwe, Mulungu amakuphunzitsani+ kukondana.+ 10 Ndipo inu mukuchitadi zimenezi kwa abale onse ku Makedoniya konse. Koma tikukudandaulirani abale kuti mupitirize kutero mowonjezereka. 11 Ndiponso muyesetse kukhala mwamtendere,+ kusalowerera mu nkhani za eni,+ ndi kugwira ntchito ndi manja anu+ monga mmene tinakulamulirani. 12 Mutero kuti muziyenda moyenerera+ pamaso pa anthu akunja*+ ndiponso kuti mukhale osasowa kanthu.+

13 Komanso abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa za amene akugona+ mu imfa, kuti musachite chisoni mofanana ndi mmene onse opanda chiyembekezo+ amachitira. 14 Pakuti ngati timakhulupirira kuti Yesu anafa ndi kuukanso,+ ndiye kuti amenenso agona mu imfa kudzera mwa Yesu, Mulungu adzawasonkhanitsa kuti akhale naye limodzi.+ 15 Pakuti tikukuuzani izi mogwirizana ndi mawu a Yehova+ kuti, ife amoyofe amene tidzakhalapo pa nthawi ya kukhalapo* kwa Ambuye,+ sitidzakhala patsogolo pa amene agona mu imfa. 16 Chifukwa Ambuye mwini adzatsika kumwamba,+ ndi mfuu yolamula ya mawu a mkulu wa angelo,+ ndi lipenga+ la Mulungu. Ndipo amene anafa mwa Khristu adzauka choyamba.+ 17 Pambuyo pake ife amoyo otsalafe, limodzi ndi iwowo,+ tidzatengedwa+ m’mitambo+ kukakumana+ ndi Ambuye m’mlengalenga, ndipo tizikakhala ndi Ambuye nthawi zonse.+ 18 Choncho, muzilimbikitsana ndi mawu amenewa.

5 Koma tsopano za nthawi ndi nyengo+ abale, simukufunika kukulemberani kanthu. 2 Pakuti inu eni mukudziwa bwino kuti tsiku la Yehova*+ lidzabwera ndendende ngati mbala usiku.+ 3 Pamene azidzati:+ “Bata ndi mtendere!”+ chiwonongeko+ chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo monga zowawa za pobereka za mkazi wapakati,+ ndipo sadzapulumuka.+ 4 Koma inu abale simuli mu mdima ayi,+ kuti tsiku limenelo lidzakudzidzimutseni ngati mmene lingachitire kwa mbala.+ 5 Pakuti inu nonse ndinu ana a kuwala+ ndiponso ana a usana.+ Si ife a usiku kapena a mdima ayi.+

6 Chotero tisapitirize kugona+ ngati mmene enawo akuchitira,+ koma tikhalebe maso+ ndipo tikhalebe oganiza bwino.+ 7 Pakuti ogona+ amagona usiku,+ ndipo amene amaledzera amakonda kuledzera usiku. 8 Koma ife amene tili a usana, tikhalebe oganiza bwino ndipo tivale chodzitetezera pachifuwa+ chachikhulupiriro+ ndi chikondi. Tivalenso chiyembekezo chachipulumutso+ monga chisoti,+ 9 chifukwa Mulungu sanatisankhe kuti tidzaone mkwiyo.+ Anatisankha kuti tipeze chipulumutso+ kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 10 Iye anatifera,+ kuti kaya tikhala maso kapena tigona, tikhale ndi moyo limodzi ndi iye.+ 11 Choncho pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana+ monga mmene mukuchitira.+

12 Tsopano tikukupemphani abale, kuti muzilemekeza anthu amene akugwira ntchito mwakhama pakati panu, amenenso amakutsogolerani+ mwa Ambuye ndi kukulangizani. 13 Muwapatse ulemu waukulu mwachikondi chifukwa cha ntchito yawo.+ Khalani mwamtendere pakati panu.+ 14 Komanso tikukudandaulirani abale kuti, langizani ochita zosalongosoka,+ lankhulani molimbikitsa kwa amtima wachisoni,+ thandizani ofooka, khalani oleza+ mtima kwa onse. 15 Onetsetsani kuti wina asabwezere choipa pa choipa kwa wina aliyense,+ koma nthawi zonse yesetsani kuchita zabwino kwa okhulupirira anzanu ndi kwa ena onse.+

16 Muzikhala okondwera nthawi zonse.+ 17 Muzipemphera mosalekeza.+ 18 Muziyamika+ pa chilichonse, pakuti chimenechi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu. 19 Musazimitse moto wa mzimu.+ 20 Musanyoze mawu aulosi.+ 21 Tsimikizirani zinthu zonse.+ Gwirani mwamphamvu chimene chili chabwino.+ 22 Pewani zoipa zamtundu uliwonse.+

23 Mulungu wamtendere+ mwiniyo akupatuleni+ kuti muchite utumiki wake. Ndipo m’mbali zonse abale, mzimu wanu, moyo wanu, ndi thupi lanu, zisungidwe zopanda chilema ndi zopanda cholakwa chilichonse, pa nthawi ya kukhalapo* kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 24 Amene akukuitanani ndi wokhulupirika, ndipo adzachitadi zimenezi.

25 Abale, pitirizani kutipempherera.+

26 Perekani moni kwa abale onse ndi kupsompsonana kwaubale.+

27 Ndikukulamulani mwa Ambuye kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse.+

28 Kukoma mtima kwakukulu+ kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale nanu.

Mawu ake enieni, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”

Onani Zakumapeto 8.

Onani Zakumapeto 8.

Onani Zakumapeto 7.

Amenewa ndi anthu amene sali mumpingo wachikhristu.

Onani Zakumapeto 8.

Onani Zakumapeto 2.

Onani Zakumapeto 8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena