Kwa Akolose
1 Ine Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu,+ pamene ndili limodzi ndi Timoteyo+ m’bale wathu, 2 ndikulembera oyera ndi abale okhulupirika amene ali ogwirizana+ ndi Khristu ku Kolose, kuti:
Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu zikhale nanu.+
3 Nthawi zonse tikamakupemphererani,+ timayamika+ Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu. 4 Timatero chifukwa tinamva za chikhulupiriro chanu mwa Khristu Yesu, ndi chikondi chanu pa oyera onse,+ 5 chimene muli nacho chifukwa cha chiyembekezo+ chodzalandira zimene akusungirani kumwamba.+ Munamva za chiyembekezo chimenechi pamene choonadi cha uthenga wabwino chinalengezedwa kwa inu.+ 6 Uthenga wabwinowu unafika kwa inu popeza ukubala zipatso+ ndipo ukuwonjezeka+ m’dziko lonse.+ Ukuteronso pakati panu, kuyambira tsiku limene munamva ndi kudziwa molondola za kukoma mtima kwakukulu+ kwa Mulungu monga mmene kulilidi.+ 7 Zimenezi mwaziphunzira kwa Epafura,+ kapolo mnzathu wokondedwa, amene ndi mtumiki wokhulupirika wa Khristu m’malo mwa ife. 8 Iye ndi amenenso anatidziwitsa za chikondi chanu+ chimene munachikulitsa mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu.
9 N’chifukwa chake ifenso, kuyambira tsiku limene tinamva zimenezo, sitinaleke kukupemphererani.+ Takhala tikupemphanso kuti mukhale odziwa molondola+ chifuniro chake, ndiponso kuti mukhale ndi nzeru+ zonse komanso muzimvetsetsa zinthu zauzimu.+ 10 Tikupemphereranso kuti muziyenda mogwirizana ndi zimene Yehova+ amafuna,+ kuti muzimukondweretsa pa chilichonse,+ pamene mukupitiriza kubala zipatso m’ntchito iliyonse yabwino, ndi kuwonjezera kumudziwa Mulungu molondola.+ 11 Tikupemphereranso kuti mulandire mphamvu zazikulu chifukwa cha mphamvu zake zaulemerero,+ kuti muthe kupirira+ zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso achimwemwe, 12 komanso muziyamika Atate, amene anakuyeneretsani kuti mupatsidweko gawo pa cholowa+ cha oyerawo,+ amene ali m’kuwala.+
13 Iye anatilanditsa ku ulamuliro+ wa mdima, n’kutisamutsira+ mu ufumu+ wa Mwana wake wokondedwa.+ 14 Mwa Mwana wakeyo, tinamasulidwa ndi dipo,* kutanthauza kuti machimo athu anakhululukidwa.+ 15 Iye ndiye chifaniziro+ cha Mulungu wosaonekayo,+ woyamba kubadwa+ wa chilengedwe chonse, 16 chifukwa kudzera mwa iye+ zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi. Inde, zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka, kaya ndi mipando yachifumu, kapena ambuye, kapena maboma, kapena maulamuliro.+ Zinthu zina zonse zinalengedwa kudzera mwa iye,+ ndiponso chifukwa cha iye. 17 Ndiponso, iye ali patsogolo pa zinthu zina zonse,+ ndipo zinthu zina zonse zinakhalapo kudzera mwa iye.+ 18 Iye ndiyenso mutu wa thupilo, lomwe ndi mpingo.+ Iye ndiye chiyambi, woyamba kubadwa kuchokera kwa akufa,+ kuti adzakhale woyamba+ pa zinthu zonse. 19 Zili motero chifukwa kunamukomera Mulungu kuti zinthu zonse+ zikhale mwa mwana wakeyo ndipo zidzazemo bwino. 20 Kuti kudzera mwa mwana wakeyo iye agwirizanitsenso+ zinthu zina zonse ndi iyeyo,+ pokhazikitsa mtendere+ mwa magazi+ amene iye anakhetsa pamtengo wozunzikirapo,*+ kaya zikhale zinthu zapadziko lapansi kapena zinthu zakumwamba.
21 Ndithudi, inu amene kale munali otalikirana+ naye ndiponso adani ake chifukwa maganizo anu anali pa ntchito zoipa,+ 22 tsopano wagwirizana+ nanunso pogwiritsa ntchito thupi lanyama la mwanayo kudzera mu imfa yake.+ Wachita izi kuti akuperekeni pamaso pa iyeyo, muli opatulika ndi opanda chilema,+ ndiponso opanda chifukwa chokunenezerani.+ 23 Adzaterodi, malinga ngati mupitirizabe m’chikhulupiriro,+ muli okhazikika pamaziko+ ndiponso olimba, osasunthika+ pa chiyembekezo cha uthenga wabwino umene munamva,+ umenenso unalalikidwa+ m’chilengedwe chonse+ cha pansi pa thambo. Uthenga wabwino umenewu ndi umene ineyo Paulo ndinakhala mtumiki wake.+
24 Ndikusangalala tsopano ndi masautso amene ndikukumana nawo chifukwa cha inu.+ Ndipo inenso kumbali yanga, ndikuona kuti sindinazunzikebe mokwanira+ monga chiwalo cha thupi la Khristu, limene ndi mpingo.+ 25 Ndinakhala mtumiki+ wa mpingo umenewu mogwirizana ndi udindo+ umene Mulungu anandipatsa, woti ndilalikire mawu a Mulungu mokwanira, kuti inuyo mupindule. 26 Mawuwo ndi chinsinsi chopatulika+ chimene chinabisidwa nthawi* zakale,+ ndiponso kwa mibadwo yakale. Koma tsopano chaululidwa+ kwa oyera ake. 27 Mulungu anaululira anthu a mitundu ina chinsinsi chopatulikachi,+ chimene chili chodzaza ndi ulemerero ndi chuma chauzimu.+ Chinsinsicho n’chakuti Khristu+ ndi wogwirizana ndi inuyo, zimene zikutanthauza kuti muli ndi chiyembekezo chodzalandira ulemerero pamodzi naye.+ 28 Tikulengeza,+ kuchenjeza, ndi kuphunzitsa munthu aliyense za ameneyu mu nzeru zonse,+ kuti tipereke munthu aliyense kwa Mulungu ali wokhwima mwauzimu+ mogwirizana ndi Khristu. 29 Ineyo ndikugwira ntchito mwakhama kuti ndichite zimenezi, poyesetsa kwambiri+ mogwirizana ndi mphamvu+ yake imenenso ikugwira ntchito mwa ine.+
2 Ndikufuna kuti mudziwe nkhondo+ yaikulu imene ndikumenya chifukwa cha inuyo ndi anthu a ku Laodikaya,+ ndi onse amene sanandionepo maso ndi maso. 2 Ndikufuna kuti mtima wa aliyense ulimbikitsidwe,+ ndiponso kuti onse akhale ogwirizana m’chikondi.+ Achite zimenezi kuti onse alandire chuma chimene chimabwera chifukwa chomvetsa bwino zinthu,+ popanda kukayikira chilichonse, ndiponso chifukwa chodziwa molondola chinsinsi chopatulika cha Mulungu, chomwe ndi Khristu.+ 3 Chuma chonse chokhudzana ndi nzeru ndiponso kudziwa zinthu+ chinabisidwa mosamala mwa iye. 4 Ndikunena zimenezi kuti munthu aliyense asakunyengeni ndi mfundo zokopa.+ 5 Popeza ngakhale kuti sindili kumeneko, ndili nanu ndithu mumzimu.+ Ndine wosangalala poona kuti mumachita zinthu mwadongosolo,+ komanso kuti muli ndi chikhulupiriro+ cholimba mwa Khristu.
6 Tsopano popeza mwalandira Khristu Yesu Ambuye wathu, yendanibe mogwirizana+ naye. 7 Khalanibe ozikika mozama+ mwa iye, ndipo monga mmene munaphunzitsidwira, pitirizani kukula+ pamene mukumuona iye monga maziko anu, ndi kukhazikika m’chikhulupiriro.+ Sefukiranibe ndi chikhulupiriro popereka mapemphero oyamikira.+
8 Samalani: mwina wina angakugwireni+ ngati nyama, mwa nzeru za anthu+ ndi chinyengo chopanda pake,+ malinga ndi miyambo ya anthu, malinganso ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli,+ osati malinga ndi Khristu, 9 chifukwa iye ndi wodzaza bwino kwambiri+ ndi makhalidwe+ a Mulungu.+ 10 Kudzera mwa iyeyo, inu simukusowa kalikonse. Iye ndiye mwini ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse.+ 11 Popeza muli naye pa ubwenzi,+ mwadulidwa,+ osati ndi manja a anthu koma mwa kuvula thupi lauchimo,+ chifukwa mdulidwe wa atumiki a Khristu umakhala wotero. 12 Zinatero popeza munakwiriridwa naye limodzi mwa kubatizidwa ubatizo wofanana ndi wake,+ ndipo chifukwa choti muli naye pa ubwenzi, munaukitsidwa+ naye limodzi kudzera m’chikhulupiriro chimene muli nacho+ mu zinthu zimene zinachitika chifukwa cha mphamvu+ ya Mulungu, amene anamuukitsa kwa akufa.+
13 Ndiponso, ngakhale kuti munali akufa m’machimo anu ndipo munali osadulidwa, Mulungu anakupatsani moyo kuti mukhale ogwirizana ndi Khristu,+ ndipo anatikhululukira machimo athu onse motikomera mtima.+ 14 Anafafanizanso+ chikalata cholembedwa ndi manja,+ chokhala ndi malamulo+ operekedwa monga malangizo, chimene chinali kutitsutsa.+ Ndipo Iye wachichotsa mwa kuchikhomera+ pamtengo wozunzikirapo.*+ 15 Pogwiritsa ntchito mtengo wozunzikirapowo, iye anavula maboma ndi olamulira n’kuwasiya osavala,+ ndipo anawaonetsa poyera pamaso pa anthu onse kuti aliyense aone kuti wawagonjetsa,+ n’kumayenda nawo ngati akaidi.+
16 Choncho munthu asakuweruzeni+ pa nkhani ya kudya ndi kumwa+ kapena chikondwerero chinachake,+ kapenanso kusunga tsiku lokhala mwezi,+ ngakhalenso kusunga sabata,+ 17 pakuti zinthu zimenezo ndi mthunzi+ wa zimene zinali kubwera, koma zenizeni+ zake zili mwa Khristu.+ 18 Musalole kuti munthu aliyense amene amasangalala ndi kudzichepetsa kwachinyengo komanso ndi kulambira angelo akumanitseni+ mphotoyo.+ Anthu oterowo amaumirira zinthu zimene aona ndipo maganizo awo ochimwa amawachititsa kudzitukumula popanda chifukwa chomveka. 19 Amatero koma osagwira mwamphamvu amene ali mutu,+ amene kuchokera kwa iye, thupi lonselo, limene limapeza zonse zimene limafunikira ndipo ndi lolumikizika bwino+ mwa mfundo zake ndi minyewa, limakulabe mothandizidwa ndi Mulungu.+
20 Ngati munafa+ limodzi ndi Khristu pa mfundo zimene ndi maziko+ a moyo wa m’dzikoli,+ n’chifukwa chiyani mukupitiriza kukhala ngati kuti mudakali mbali ya dzikoli, pogonjeranso malamulo+ akuti: 21 “Usatenge ichi, kapena usalawe ichi,+ kapena usakhudze ichi?”+ 22 Zinthu zimenezi zidzawonongedwa mwa kuzigwiritsa ntchito ndipo malamulo amenewa ndi ziphunzitso za anthu basi.+ 23 Ndithudi, zinthu zimenezo zimaonekera pa kulambira kochita kudzipangira, podzichepetsa mwachinyengo komanso pozunza thupi,+ ndipo zimaonekadi ngati zanzeru, koma n’zosathandiza kwa munthu polimbana ndi zilakolako za thupi.+
3 Komabe, ngati munaukitsidwa+ limodzi ndi Khristu, pitirizani kufuna zinthu zakumwamba,+ kumene Khristu wakhala kudzanja lamanja la Mulungu.+ 2 Ikani maganizo anu pa zinthu zakumwamba,+ osati pa zinthu zapadziko.+ 3 Pakuti munafa,+ ndipo moyo+ wanu wabisidwa mwa Khristu mogwirizana+ ndi Mulungu. 4 Khristuyo, amene ndiye moyo wathu,+ akadzaonetsedwa,+ inunso mudzaonetsedwa limodzi naye mu ulemerero.+
5 Choncho chititsani ziwalo za thupi+ lanu padziko lapansi kukhala zakufa+ ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana,+ chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje,+ kumene ndiko kulambira mafano. 6 Chifukwa cha zinthu zimenezi, mkwiyo wa Mulungu ukubwera.+ 7 Inunso munayendapo m’zinthu zimenezi, pamene munali kukhalira kuchita zomwezo.+ 8 Koma tsopano zonsezo muzitaye kutali ndi inu.+ Mutaye mkwiyo, kupsa mtima, kuipa, ndi mawu achipongwe,+ ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana.+ 9 Musamanamizane.+ Vulani umunthu+ wakale pamodzi ndi ntchito zake, 10 ndipo muvale umunthu watsopano+ umene Mulungu amapereka, kutanthauza kuti mwa kudziwa zinthu molondola, muchititse umunthu wanu kukhala watsopano mogwirizana ndi chifaniziro+ cha Mulungu. 11 Mukatero, sipadzakhala Mgiriki kapena Myuda, kudulidwa kapena kusadulidwa, mlendo, Msukuti, kapolo, kapena mfulu,+ koma Khristu ndiye zinthu zonse ndipo ali mwa onse.+
12 Chotero monga ochita kusankhidwa ndi Mulungu,+ oyera ndi okondedwa, valani chifundo+ chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa,+ kufatsa,+ ndi kuleza mtima.+ 13 Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse,+ ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira+ za mnzake. Monga Yehova* anakukhululukirani+ ndi mtima wonse, inunso teroni. 14 Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi,+ pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu+ kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.
15 Komanso, mtendere+ wa Khristu ulamulire m’mitima+ yanu, popeza munaitanidwa ku mtenderewo monga ziwalo za thupi limodzi.+ Ndiponso, sonyezani kuti ndinu oyamikira. 16 Mawu a Khristu akhazikike mwa inu ndipo akupatseni nzeru zonse.+ Pitirizani kuphunzitsana+ ndi kulangizana mwa masalimo,+ nyimbo zotamanda Mulungu, ndi nyimbo zauzimu+ zogwira mtima. Pitirizani kuimbira Yehova+ m’mitima yanu. 17 Ndipo chilichonse chimene mukuchita m’mawu kapena mu ntchito,+ muzichita zonse m’dzina la Ambuye Yesu,+ ndipo muziyamika+ Mulungu Atate kudzera mwa iye.
18 Inu akazi, muzigonjera+ amuna anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera kwa anthu otsatira Ambuye. 19 Inu amuna, musaleke kukonda akazi+ anu ndipo musamawapsere mtima kwambiri.+ 20 Ananu, muzimvera+ makolo anu pa zinthu zonse, pakuti kuchita zimenezi kumakondweretsa Ambuye. 21 Inu abambo, musamakwiyitse ana+ anu, kuti angakhale okhumudwa. 22 Inu akapolo, muzimvera ambuye anu a padziko lapansi+ pa zinthu zonse, osati mwachiphamaso ngati ofuna kukondweretsa+ anthu, koma moona mtima ndiponso moopa Yehova.+ 23 Chilichonse chimene mukuchita, muzichichita ndi moyo wanu wonse+ ngati kuti mukuchitira Yehova,+ osati anthu, 24 chifukwa mukudziwa kuti mudzalandira cholowa+ kuchokera kwa Yehova+ monga mphoto yanu. Tumikirani Ambuye wanu, Khristu, monga akapolo.+ 25 Ndithudi, amene akuchita zolakwa adzalandiranso+ zolakwa zake zimene akuchitazo, chifukwa Mulungu sakondera.+
4 Inu anthu amene muli ambuye, pitirizani kuchitira akapolo+ anu zinthu zachilungamo ndi zoyenera, podziwa kuti inunso muli ndi Ambuye kumwamba.+
2 Muzilimbikira kupemphera.+ Mukhale maso pa nkhani ya kupemphera ndipo mukhale oyamikira.+ 3 Muzitipemphereranso ifeyo,+ kuti Mulungu atitsegulire khomo+ kuti tithe kulalikira mawu ndi kulankhula za chinsinsi chopatulika+ chonena za Khristu, chimene ndinamangidwira n’kukhala m’ndende muno,+ 4 kuti ndidzalalikire ndi kulankhula za chinsinsicho ngati mmene ndiyenera kulankhulira.+
5 Pitirizani kuyenda mwanzeru pochita zinthu ndi anthu akunja,*+ ndipo muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.*+ 6 Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo,+ okoma ngati kuti mwawathira mchere,+ kuti mudziwe mmene mungayankhire+ wina aliyense.
7 Tukiko,+ m’bale wanga wokondedwa komanso mtumiki wokhulupirika, ndi kapolo mnzanga mwa Ambuye, adzakudziwitsani zonse za ine. 8 Ndikumutumiza ndi cholinga chimenechi, kuti inuyo mudziwe za ife, ndi kutinso alimbikitse mitima yanu.+ 9 Ndamutumiza limodzi ndi Onesimo,+ m’bale wanga wokhulupirika ndi wokondedwa, amene anachokera pakati panu. Amenewa adzakusimbirani zonse zakuno.
10 Arisitako+ mkaidi mnzanga akuti moni nonse. Komanso Maliko+ msuweni* wa Baranaba, (amene ndinakulangizani kuti mumulandire+ nthawi iliyonse akadzafika kwa inu,) 11 ndi Yesu, wotchedwanso Yusito, akuti moni. Amenewa ali m’gulu la anthu odulidwa. Okhawa ndiwo antchito anzanga pa zinthu zokhudzana ndi ufumu wa Mulungu, ndipo amenewa andithandiza ndi kundilimbikitsa. 12 Epafura,+ amene anachokera pakati panu, kapolo wa Khristu Yesu, akuti moni. Iye amakupemphererani mwakhama nthawi zonse, kuti pomalizira pake mukhale okhwima mwauzimu+ ndi osakayika ngakhale pang’ono za chifuniro chonse cha Mulungu. 13 Ndikumuchitiradi umboni kuti amadzipereka kwambiri chifukwa cha inu ndi abale a ku Laodikaya+ ndi ku Herapoli.
14 Luka,+ dokotala wokondedwa, akuti moni nonse. Dema+ nayenso akuti moni. 15 Mundiperekere moni kwa abale a ku Laodikaya ndi kwa Numfa ndi mpingo umene umasonkhana panyumba pake.+ 16 Ndipo kalatayi mukaiwerenga kwanuko, konzani zoti ikawerengedwenso+ ku mpingo wa Alaodikaya, ndiponso mukawerenge yochokera ku Laodikaya. 17 Komanso Arikipo+ mumuuze kuti: “Uonetsetse kuti utumiki umene unaulandira mwa Ambuye ukuukwaniritsa.”
18 Tsopano landirani moni wanga wolemba ndekha ndi dzanja langa,+ ineyo Paulo. Pitirizani kukumbukira maunyolo+ amene andimanga nawo kundende kuno. Kukoma mtima kwakukulu kukhale nanu.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto 9.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto 9.
Onani Zakumapeto 2.
Amenewa ndi anthu amene sali mumpingo wachikhristu.
Mawu ake enieni, “muzigula nthawi yoikidwa.”
Kapena kuti, “mwana wa amalume a Baranaba.”