Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 2 Thessalonians 1:1-3:18
  • 2 Atesalonika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 2 Atesalonika
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
2 Atesalonika

Kalata Yachiwiri kwa Atesalonika

1 Ine Paulo, pamene ndili limodzi ndi Silivano ndi Timoteyo,+ ndikulembera mpingo wa Atesalonika wogwirizana ndi Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu, kuti:

2 Kukoma mtima kwakukulu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu,+ zikhale nanu.

3 Tiyeneradi kumayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu+ abale. N’koyenera kutero chifukwa chikhulupiriro chanu chikukula+ kwambiri, ndipo chikondi cha aliyense wa inu kwa mnzake chikuwirikiza.+ 4 Choncho ifeyo timakunyadirani+ ku mipingo ya Mulungu chifukwa cha kupirira kwanu ndi chikhulupiriro chanu pokumana ndi mazunzo ndi masautso onse amene mukulimbana nawo.+ 5 Umenewu ndi umboni wakuti Mulungu amaweruza molungama,+ ndipo chifukwa cha zimenezi mwaonedwa kuti ndinu oyenerera ufumu wa Mulungu,+ umene mukuuvutikira.+

6 Chiweruzo cha Mulunguchi n’cholungama chifukwa akubwezera masautso kwa amene amakusautsani.+ 7 Pa nthawi imene Ambuye Yesu adzaonekere*+ kuchokera kumwamba limodzi ndi angelo ake amphamvu+ m’moto walawilawi, inuyo amene panopo mukuvutika mudzapeza mpumulo pamodzi nafe. 8 Pa nthawi imeneyo adzabwezera chilango+ kwa anthu osadziwa Mulungu+ ndi kwa anthu osamvera uthenga wabwino+ wonena za Ambuye wathu Yesu.+ 9 Amenewa adzawaweruza kuti alandire chilango+ cha chiwonongeko chamuyaya,+ kuwachotsa pamaso pa Ambuye ndi ku ulemerero wa mphamvu zake.+ 10 Adzatero pa nthawi imene adzabwere kudzalandira ulemerero mogwirizana ndi oyera ake.+ Pa tsiku limenelo, onse amene anakhulupirira mwa iye, adzamusirira ndi kumuyang’anitsitsa, chifukwa pakati panu, munakhulupirira umboni umene tinapereka.

11 Pa chifukwa chimenechi, ndithu timakupemphererani nthawi zonse. Timatero kuti Mulungu wathu akuoneni kuti ndinu oyenereradi kuitanidwa ndi iye.+ Mulunguyo achite mokwanira zinthu zonse zabwino zimene akufuna kuchita ndi mphamvu zake, ndipo achititse kuti ntchito zanu zachikhulupiriro zikhale zopindulitsa, 12 kuti dzina la Ambuye wathu Yesu lilemekezeke mwa inu,+ ndi inu mwa iye,+ mogwirizana ndi kukoma mtima kwakukulu+ kwa Mulungu wathu, ndi kwa Ambuye Yesu Khristu.

2 Komabe abale, za kukhalapo*+ kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi kusonkhanitsidwa kwathu kwa iye,+ tikukupemphani 2 kuti musafulumire kugwedezeka pa maganizo anu, kapena kutengekatengeka ndi mawu ouziridwa+ onena kuti tsiku la Yehova lafika.+ Musatero ayi, ngakhale utakhala uthenga wapakamwa,+ kapena kalata+ yooneka ngati yachokera kwa ife.

3 Wina asakunyengeni pa nkhani imeneyi m’njira iliyonse. Pakuti tsikulo silidzayamba kufika mpatuko+ usanachitike, ndiponso asanaonekere+ munthu wosamvera malamulo,+ amene ndiye mwana wa chiwonongeko.+ 4 Iye ndi wotsutsa+ amene amadzikweza pamwamba pa aliyense wotchedwa “mulungu” kapena chilichonse chopembedzedwa, moti amakhala pansi m’kachisi wa Mulungu, n’kumadzionetsera ngati mulungu.+ 5 Kodi simukukumbukira kuti pamene ndinali nanu ndinali kukuuzani+ zimenezi?

6 Ndipo inu mukudziwa chimene+ chikuchititsa kuti panopa asaonekere,+ kuti adzaonekere mu nthawi yake yoyenera.+ 7 Zoona, chinsinsi cha kusamvera malamulo kumeneku chilipo kale,+ koma chingokhalapo kufikira atachoka amene panopa ali choletsa.+ 8 Pamenepo, wosamvera malamuloyo adzaonekera ndithu, amene Ambuye Yesu adzamuthetsa ndi mzimu wa m’kamwa mwake,+ pomuwonongeratu pa nthawi imene kukhalapo kwa Yesuyo kudzaonekere.+ 9 Koma kukhalapo kwa wosamvera malamuloyo kukutheka mwa mphamvu+ za Satana. Adzachita ntchito iliyonse yamphamvu ndi zizindikiro zabodza ndi zodabwitsa,+ 10 ndi kusalungama ndi chinyengo chilichonse.+ Zonsezi adzazichita kwa amene akupita kukawonongedwa.+ Izi zidzakhala chilango kwa iwo chifukwa sanasonyeze kuti akulakalaka+ choonadi, kuti apulumuke.+ 11 Ichi n’chifukwa chake Mulungu walola kuti iwo anyengedwe ndipo azikhulupirira bodza,+ 12 kuti onsewo adzaweruzidwe chifukwa sanakhulupirire choonadi,+ koma anakonda zosalungama.+

13 Komabe, tiyeneradi kumayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu abale okondedwa ndi Yehova. Tiyenera kutero chifukwa Mulungu anakusankhani+ kuchokera pachiyambi kuti mudzapulumuke mwa kukuyeretsani+ ndi mzimu,+ ndiponso mwa chikhulupiriro chanu m’choonadi.+ 14 Anakuitanani ku chipulumutso chimenechi kudzera mu uthenga wabwino umene tikulengeza,+ kuti mudzapeze ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 15 Choncho abale, khalani olimba+ ndipo gwirani mwamphamvu miyambo+ imene munaphunzitsidwa, kaya mwa uthenga wapakamwa kapena mwa kalata yochokera kwa ife. 16 Komanso, Ambuye wathu Yesu Khristu mwiniyo, ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda+ ndipo amatilimbikitsa m’njira yosalephera ndiponso anatipatsa chiyembekezo chabwino,+ mwa kukoma mtima kwakukulu, 17 alimbikitse mitima yanu ndi kukulimbikitsani muntchito yabwino iliyonse ndiponso m’mawu.+

3 Pomalizira abale, pitirizani kutipempherera+ kuti mawu a Yehova*+ apitirize kufalikira mofulumira+ ndi kulemekezedwa ngati mmene akuchitira pakati panu. 2 Muzitero kutinso tilanditsidwe kwa anthu opweteka anzawo ndi oipa,+ pakuti chikhulupiriro sichikhala ndi anthu onse.+ 3 Koma Ambuye ndi wokhulupirika ndipo adzakulimbitsani ndi kukutetezani kwa woipitsitsayo.+ 4 Komanso ifeyo monga otsatira a Ambuye, tili ndi chikhulupiriro+ mwa inu kuti mukuchita zimene tinalamula ndipo mudzapitiriza kutero.+ 5 Ambuye apitirize kutsogolera mitima yanu kuti muzikonda+ Mulungu ndi kuti muzipirira+ chifukwa cha Khristu.

6 Tsopano tikukulangizani+ abale m’dzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti mupewe+ m’bale aliyense woyenda mosalongosoka+ komanso mosagwirizana ndi mwambo umene tinakupatsani.+ 7 Pakuti inuyo mukudziwa mmene muyenera kutitsanzirira.+ Sitinakhale mosalongosoka pakati panu,+ 8 kapena kudya chakudya cha wina aliyense kwaulere.+ M’malomwake, mwa ntchito yathu imene tinagwira mwakhama ndi thukuta lathu,+ tinagwira ntchito usiku ndi usana kuti aliyense wa inu asatilipirire kanthu kalikonse pofuna kutithandiza.+ 9 Sikuti tinatero chifukwa chopanda ulamuliro,+ koma kuti tikhale chitsanzo kwa inu, kuti inu mutitsanzire.+ 10 Ndiponso, pamene tinali ndi inu, tinali kukupatsani lamulo ili:+ “Ngati wina sakufuna kugwira ntchito, asadye.”+ 11 Pakuti tikumva kuti ena akuyenda mosalongosoka+ pakati panu, sakugwira ntchito n’komwe, koma akulowerera nkhani zimene sizikuwakhudza.+ 12 Anthu otero tikuwalamula ndi kuwadandaulira mwa Ambuye Yesu Khristu kuti, mwa kugwira ntchito mwakhama popanda kulowerera nkhani za anthu ena, adye chakudya chimene iwowo achigwirira ntchito.+

13 Koma inu abale, musaleke kuchita zabwino.+ 14 Koma ngati wina sakumvera mawu athu+ a m’kalatayi, muikeni chizindikiro+ ndipo lekani kuchitira naye zinthu limodzi,+ kuti achite manyazi.+ 15 Komabe musamuone monga mdani, koma pitirizani kumulangiza+ monga m’bale.

16 Tsopano Ambuye wamtendere mwiniyo, akupatseni mtendere nthawi zonse m’njira iliyonse.+ Ambuye akhale nanu nonsenu.

17 Landirani moni wanga, ineyo Paulo, wolemba ndekha m’kalembedwe kanga,+ komwe ndi chizindikiro m’kalata yanga iliyonse. Aka ndiko kalembedwe kanga.

18 Kukoma mtima kwakukulu+ kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale nanu nonsenu.

Kapena kuti “adzaululike.”

Onani Zakumapeto 8.

Onani Zakumapeto 2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena