Kodi Mumakambirana za Chipembedzo?
“Chonde, tiyeni tisiye nkhaniyi. Pali zinthu ziŵiri zimene sindikambako—zachipembedzo ndi zandale!”
“Zachipembedzo ndimalekera mkazi wanga ndi ana.”
“Sindifuna kukamba za chipembedzo tsopano. Ndangofika kumene panyumba kuchokera ku tchalitchi.”
KODI mawu amenewa mwawamvapo kambiri? Ena amasankha kusakambirana ndi anzawo za chipembedzo chifukwa amaona kuti ndi nkhani yongokhudza iwo eni ndi Mulungu basi. Yesu mwiniyo anati: “Koma iwe popemphera, loŵa m’chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali mtseri, ndipo Atate wako wakuona mtseri adzakubwezera iwe.”—Mateyu 6:6.
Komabe Yesu ndi ophunzira ake sanapange nkhani iliyonse yachipembedzo kukhala yodziŵa anthu pang’ono. Iwo ankakamba nkhani zauzimu momasuka ndiponso poyera, ndipo zimenezi zinapangitsa kuti chiphunzitso chawo chifalikire padziko lonse. (Machitidwe 1:8; Akolose 1:23) Koma si onse omwe ankafuna kumalankhula nawo, ndipo ena mwa amene ankamvetsera ankakayika.
Zilinso choncho lerolino. Anthu osiyanasiyana ndiponso azikhalidwe zosiyanasiyana amaona kukambirana za chipembedzo mosiyananso. Mwachitsanzo, m’mayiko a Kumadzulo, anthu amadera nkhaŵa kwambiri zakuthupi—maphunziro, ntchito, maseŵera, makompyuta, TV, ndi zina. M’mayiko ena, anthu amakhala ofunitsitsa kulankhula za zikhulupiriro zawo. Komabe mosasamala kanthu zakuti anthuwo moyo wawo wakale unali wotani, zina zimachitika m’moyo wawo ndipo ena omwe sankafuna kumvetsera amayamba kulingalira zauzimu.
Kusalolerana Zipembedzo Kumafooketsa Ambiri
Amene amakana kukambirana za chipembedzo mwina amakhala kuti anaonapo kapena iwo anakwiyitsanapo ndi ena pankhaniyi. Katswiri wolankhula pagulu wina anati, “Kusiyana zipembedzo kumabutsa mikangano kwambiri kuposa kusiyana pa zandale.” Komanso Richard M. Johnson, amene kale anali wachiŵiri kwa pulezidenti wa dziko la America, anati: “Kukondetsetsa chipembedzo kumapangitsa tsankho lalikulu m’malingaliro mwa anthu; ndiponso, ngati osalingalira bwino, kukhoza kusokoneza dziko tikumakhala ndi malingaliro olakwika akuti tikuchita utumiki wa Mulungu.”
Kodi zikukudabwitsani kuti chiphunzitso cha Baibulo chomwe chiyenera kutipatsa nzeru ndi kutipangitsa kukhala olemekezeka chikugwiritsidwa ntchito molakwa n’kupangitsa anthu kusalolera zipembedzo za ena, n’kukhala anthu osamva za anzawo, ndiponso kupangitsa anthu kudana? Kwenikweni, si chiphunzitso cha Baibulo chimene chimapangitsa chipembedzo kukhala choipa kwa ambiri. Koma n’chifukwa chosokoneza chiphunzitsocho. Mwachitsanzo, lingalirani za Chikristu.
Mwa mawu ake ndiponso mwakusonyeza chitsanzo, Woyambitsa Chikristu, Yesu Kristu, ankalimbikitsa kukonda Mulungu ndi anansi athu, osati kusalolerana ndi kuumirira mwambo mosalingalira bwino. Zida zimene Kristu ndi omutsatira ankagwiritsa ntchito mu utumiki wawo zinali kulongosola ndi kulimbikitsa kuganiza. (Mateyu 22:41-46; Machitidwe 17:2; 19:8) Ndipo ankapempherera adani awo ndiponso amene ankawazunza.—Mateyu 5:44; Machitidwe 7:59, 60.
Chipembedzo choona chimapangitsa munthu kukhala ndi mtima ndi malingaliro abwino ndipo chimagwirizanitsa anthu. Choncho kwa onse amene amafuna choonadi moona mtima, kukambirana za chipembedzo moyenera kungakhale kothandiza, monga mmene tionere.
[Bokosi patsamba 3]
Zimene Atsogoleri Otchuka Anenapo
“Ngati Yesu ndiye njira yopita kwa Mulungu, n’koyenera kuti omwe amam’tsatira aziuzako anthu ena.”—Ben Johnson, polofesa wa zaulaliki pa Columbia Theological Seminary.
“Yesu anauza ophunzira ake kuti auzeko anthu ena uthenga wabwino. Posonyeza kumvera Lamulo Lalikululi tifunikira kuyenda padziko lonse. Ambuye analamulira omutsatira kuti apite m’misewu ikuluikulu ndi m’tinjira ting’onoting’ono tomwe.”—Kenneth S. Hemphill, mkulu wa Southern Baptist Center for Church Growth.
“Sitingakhale Akristu enieni pokhapokha titakhala Mboni. . . . Mkristu aliyense anaitanidwa kuti adzakhale m’mishonale ndi mboni.—Papa Yohane Paulo II.
“Alaliki ambiri . . . ali ndi chidwi n’kukulitsa mipingo ndi kumanga matchalitchi ndi kuganiza za ntchito imene adzapatsidwa kuposa kulalikira uthenga womwe susintha ndipo umene umawakhumudwitsa wopezeka mu Uthenga Wabwino.”—Cal Thomas, mlembi.
“Tiyenera kumafika ndi kugogoda pa zitseko . . . Monga a Mboni (za Yehova) ndi ena mwa magulu enawo, tiyenera kupita kukalengeza Uthenga Wabwino wa Yesu Kristu.”—Thomas V. Daily, bishopu wa Katolika.