Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 4/8 tsamba 26-29
  • Pamene Agogo Amakhala Makolo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Agogo Amakhala Makolo
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupsinjika Maganizo ndi Zovuta Zake
  • Ana Aukali
  • Kupirira Mavutowo
  • Kukhala Pamodzi Mwachikondi
    Galamukani!—1995
  • Kukhala Gogo—Kusangalatsa Kwake Ndiponso Mavuto Ake
    Galamukani!—1999
  • Kodi Ena a Mavutowo ndi Otani?
    Galamukani!—1995
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kudziŵana ndi Agogo Anga?
    Galamukani!—2001
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 4/8 tsamba 26-29

Pamene Agogo Amakhala Makolo

“Ndinali nditangochokera kumene kumsonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Ndinamva kugogoda kwambiri pachitseko, ndipo kunjako kunali apolisi aŵiri ndi ana aŵiri osasamba amene tsitsi lawo losapesa linkaoneka ngati atha miyezi asanasambitsidwe. Simukanazindikira msanga kuti anali ana! Iwo anali adzukulu anga, ndipo amayi awo—amene ankamwa mankhwala osokoneza bongo—anali atawalekerera. Mwamuna wanga anali atamwalira, ndipo ndinali ndi ana asanu ndi m’modzi anga a ine mwini. Komabe zinali zosatheka kuti ndikane.”—Sally.a

“Mwana wanga wamkazi anandipempha kuti nditenga ana ake kufikira iye atasintha makhalidwe. Sindinkadziŵa kuti ankamwa mankhwala osokoneza bongo. Zotsatira zake n’zakuti ndinayamba kulera ana ake aŵiri. Zaka zina pambuyo pake mwana wangayo anakhala ndi mwana wina. Sindinafune kum’tenga ameneyu, kufikira pomwe mdzukulu wanga wina anandipempha kuti, ‘Agogo, kodi sitingatengenso wina m’modzi yekha?’” Willie Mae.

KALE kukhala gogo kunkatchedwa kuti “chisangalalo popanda udindo.” Koma tsopano sizilinso choncho. Ena amayerekeza kuti mu United States mokha, ana okwana mamiliyoni atatu amakhala ndi agogo awo. Ndipo chiŵerengerocho chikukulabe.

Kodi chimapangitsa vuto limeneli n’chiyani? Ana amene mabanja a makolo awo amatha mapeto ake amakakhala ndi agogo awo. Zilinso choncho ndi ana amene makolo awo amangowalekerera kapena kuwachitira zoipa. Magazini yakuti Child Welfare inati, mankhwala osokoneza ubongo otchedwa ‘crack cocaine akusokoneza maganizo a anthu, chifukwa amalepheretsa makolo kuchita udindo wawo.’ Palinso ana mamiliyoni ambiri amene “alibe makolo” chifukwa chakuti anangowasiya, kapena anafa, kapena akudwala matenda osokoneza nzeru. Ana amene amayi awo amamwalira ndi AIDS nawonso zotsatira zake amakaleredwa ndi agogo awo.

Ndi chinthu chovuta kwambiri kutenga udindo wolera ana uli wachikulire kapena ‘m’masiku oipa’ amene umakhala utakalamba. (Mlaliki 12:1-7) Anthu ambiri sakhala ndi mphamvu zoti n’kumayang’ana zochita za mwana wamng’ono nthaŵi zonse. Agogo enanso amakhala ali pantchito yosamaliranso makolo awo okalambanso. Koma ena amakhala kuti amuna awo anamwalira kapena banja lawo linatha ndipo amachita zimenezo popanda mnzawo wothandizana naye. Ndipo ena amapeza kuti sanakonzekere, alibe ndalama zokwanira zoti n’kuchitira ntchito imeneyo. Pakufufuza kwina, agogo 4 mwa 10 amene amalera ana anapezeka kuti amalandira ndalama zochepa kwambiri mosasiyana kwenikweni ndi anthu osauka. Sally anati, “Anawo anali odwala. Ndinakakamizika kuwagulira mankhwala ndipo ndinalipira ndalama zambiri. Boma linkandithandiza ndi ndalama pang’ono kwambiri.” Mayi wina wachikulire akukumbukira kuti: “Ndinkagwiritsa ntchito ndalama zomwe ndinalandira nditapuma pantchito kusamalira adzukulu anga.”

Kupsinjika Maganizo ndi Zovuta Zake

Choncho n’zosadabwitsa kuti pakufufuza kwina kunapezeka kuti “kulera ana kunapangitsa agogo kukhala odandaula kwambiri, ndipo mwa agogo 60 amene anafufuzidwawo, 86 peresenti ndiwo amene anati ‘amakhala odandaula kapena ankhawa nthaŵi zambiri.’” Ndithudi ambiri amakhala ndi mavuto a zathanzi. Elizabeth, mayi amene amasamalira mdzukulu wake wachitsikana anati, “Zimanditopetsa, kundisokoneza maganizo, ndiponso kundisokoneza mwauzimu.” Willie Mae, wodwala nthenda ya mtima ndiponso nthenda ya magazi anati: “Dokotala wanga amakhulupirira kuti n’chifukwa chakuti ndimapanikizika kulera ana.”

Ena sanakonzekere za kusintha kakhalidwe kumene kulera adzukulu kumapangitsa.” Gogo wina anati, “Nthaŵi zina ndimalephera kupita kwina kulikonse. Ndimadzimva ngati kuti ndalakwa . . . ngati ndiwasiya ndi munthu wina, motero m’malo mwakuti ndipite kwina kapena kuchita chinachake, sindipita kapena sindichita chinthucho.” Wina anati nthaŵi yoti achite zofuna yekha “sikhalapo.” N’zofalanso kuwaona akumadzipatula ndi kukhala okha. Gogo wina wachikazi anati: “M’gulu lathu anzathu ambiri alibe ana [ang’onoang’ono] ndiye chifukwa cha chimenecho nthaŵi zambiri sitivomera akatiitana chifukwa ana athu [adzukulu] saitanidwa nawo.”

Chinthu chinanso chowawa ndicho madandaulo. Nkhani ina ya mu U.S.News & World Report inati: “Ambiri mwa iwo [agogo] amakhala ndi manyazi ndiponso kudzimva olakwa chifukwa chakuti ana awo alephera ntchito yawo monga makolo—ndipo ena amadziimba mlandu okha, akumadabwa kuti n’chiyani chimene iwowo analakwitsa polera ana awo monga makolo. Kuti asamalire bwino adzukulu awo, ena amayamba kunyalanyaza ana awo omwe amakhala atalowerera kumwa mankhwala osokoneza bongo.”

Pa kufufuza kwina panaperekedwa lipoti lotere: “Mwa agogo anayi . . . mmodzi analeka kusangalala ndi mwamuna wake kapena ndi mkazi wake chifukwa chakuti amakhala akusamalira ana.” Makamaka amuna ndiwo amaona kuti akunyalanyazidwa chifukwa akazi awo ndiwo amagwira ntchito yaikulu yosamalira ana. Amuna ena amapeza kuti sangakwanitse kulimbana ndi vutoli. Mayi wina wapabanja anati: “Anangotisiya. . . . Ndiganiza kuti ankaona kuti vutolo silidzatha.”

Ana Aukali

U.S.News & World Report inati: “Kupsinjika maganizoko kumakula chifukwa ana amene [agogo] amatengawo amakhala ovutika ofuna chithandizo mwachikondi, amene anasokonezedwa maganizo kwambiri ndipo aukali kwambiri m’dzikomu.”

Talingalirani za mdzukulu wamkazi wa Elizabeth. Tate wa mwanayo anangomuleka pamsewu pamene Elizabeth ankagwira ntchito yothandiza ana kuoloka msewu. Elizabeth anati, “Iye ndi mwana waukali kwambiri. Anakhumudwa kwambiri.” Adzukulu a Sally nawo ali ndi vuto lofananalo. “Mdzukulu wanga wamwamuna ndi waukali kwambiri. Amaona ngati kuti palibe aliyense amene amam’konda.” Kukhala ndi bambo ndi mayi achikondi ndiwo ufulu wobadwa nawo wa mwana. Lingalirani mmene mwana amaonera ngati iwo amusiya, amulekerera, kapena amukana! Kumvetsetsa zimenezi kungakhale kothandiza kwambiri kuti muzichita nawo modekha ana amene amayamba kukhala ndi vuto lamakhalidwe. Miyambo 19:11 imati: “Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo.”

Mwana amene anangom’leka angakane zoyesayesa zanu zakuti mum’samalire. Ngati mumvetsetsa mantha ndi nkhawa zimene mwanayo ali nazo kukhoza kukuthandizani kuti muchite naye mwachikondi. Mwinamwake kusonyeza kuti mukuzindikira chifukwa chake ali ndi mantha ndi kum’tsimikizira kuti mudzachita chilichonse chomwe mungathe kum’samalira kudzathandiza kuthetsa mantha akewo.

Kupirira Mavutowo

Wina amene ankasunga mwana anati, ‘Nthaŵi zonse ndakhala ndikudzimva wokhumudwa ndi wachisoni. Ichi sichinthu chofunika kuti chizitichitikira.’ Ngati zinthu zilinso choncho kwa inu, ndiye kuti mumamvanso chimodzimodzi. Koma si ndiye kuti vutolo silingathe. Vuto limodzi n’lakuti simukhala ndi mphamvu, koma kukula n’kwaphindu tikafika pankhani ya kukhala a nzeru, kuleza mtima, ndiponso maluso. Choncho n’zosadabwitsa pamene kufufuza kunasonyeza kuti “ana amene analeredwa ndi agogo awo okha zinthu zinkawayendera bwinoko kusiyana ndi ana okulira m’banja mokhala kholo lawo lenileni limodzi lokha.”

Baibulo limatilimbikitsa ‘kutaya pa Yehova nkhaŵa yathu yonse pakuti iye asamalira ife.’ (1 Petro 5:7) Choncho nthaŵi zonse pempherani kwa iye kuti akuthandizeni ndi kukutsogozani, monga mmene anachitira wamasalmo. (Yerekezerani ndi Salmo 71:18.) Muyenera kukhala tcheru kwambiri pa zinthu zauzimu. (Mateyu 5:3) Mayi wina wachikristu anati, “Misonkhano yachikristu ndi kulalikira kwa ena ndiko kunandithandiza ine kuti ndizikwanitse.” Ngati n’kotheka, yesani kuphunzitsa adzukulu anu njira ya Mulungu. (Deuteronomo 4:9) Mosakayikira Mulungu adzalimbikitsa zoyesayesa zanu zakulera adzukulu anu “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”—Aefeso 6:4.b

Simuyenera kuopa kufunafuna chithandizo. Nthaŵi zambiri mabwenzi angathe kukhala othandiza, makamaka mumpingo wachikristu. Sally akukumbukira kuti, “Abale ndi alongo mumpingo anandithandiza kwambiri. Zinkati zikandivuta kwambiri iwo ankandilimbikitsa. Ena ankandithandiza ngakhale mwakundipatsa ndalama.”

Simuyenera kunyalanyaza chithandizo chimene boma lingapereke. (Aroma 13:6) Komabe, malinga ndi kafukufuku wina wonena za agogo, “ambiri sadziŵa kuti kulinji kapena kuti ndi kuti kumene angapeze chithandizo.” (Child Welfare) Ogwira ntchito zaumoyo ndiponso mabungwe ena a kwanuko amene amathandiza okalamba akhoza kukutsogolerani kwakuti mupeze chithandizo.

Nthaŵi zambiri agogo amene amasunga ana amaonadi kuti zino ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1-5) Koma chokondweretsa n’chakuti, nthaŵi zovuta zino ndi chizindikiro chakuti Mulungu posachedwapa adzaloŵererapo ndi kulenga “dziko latsopano” mmene mavuto ngati amene amakhudza mabanja ambiri leroŵa adzakhala chabe zinthu zakale. (2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4) Padakali pano, agogo amene amalera ana ayenera kuchita zomwe angathe kuti agwire bwino ntchito yawoyo. Ambiri akuikwanitsa bwino ntchitoyo! Nthaŵi zonse muyenera kukumbukira kuti m’malo mokhumudwa, pakhoza kukhala chimwemwe. Mukhoza kusangalala kuona adzukulu anu akukhala okonda Mulungu moona mtima. Kodi ili silingakhale phindu labwino pa ntchito yomwe munaigwira mwakhama?

[Mawu a M’munsi]

a Maina ena asinthidwa.

b Buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja (lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.) lili ndi mfundo zambiri za m’Baibulo zimene agogo amene amasunga ana angagwiritsire ntchito polera adzukulu.

[Bokosi patsamba 29]

Za Malamulo

Zakuti kaya pafunika kupeza chilolezo mwalamulo chakuti mutenge adzukulu n’kuwalera ndi nkhani yofunika kuiona mwanzeru chifukwa ndi yovuta. Mary Fron yemwe ndi katswiri pankhani zimenezi analongosola kuti: “Mumakhala ndi udindo wochepa mwalamulo ngati simuloledwa kutenga ana. Nthaŵi zambiri, makolo awo enieni amabwera panthaŵi iliyonse ndi kutenga mwanayo kapena anawo. Koma, agogo ambiri amalephera kutengeratu ana, chifukwa zimenezi zimafuna kuti akaime m’khothi kunena kuti mwana wawo sakwanitsa udindo wokhala kholo.”—magazini ya Good Housekeeping.

Agogo amavutika kutumiza ana kusukulu ndiponso kuwapezera mankhwala ngati satenga ana kukhala awo mwalamulo. Komabe kuwatenga anawo mwalamulo ndi ntchito yofuna ndalama zambiri, nthaŵi, ndiponso yosokoneza maganizo. Ndipo ngakhale ngati zitatheka, boma limaleka kuwathandiza agogowo. Magazini yakuti Child Welfare inalangiza agogo “kupeza malangizo okhuza zamalamulo kwa loya wozoloŵera malamulo a m’dzikolo okhudza za mabanja, milandu ya kutenga ana, ndi zoyenera ana.”

[Bokosi patsamba 29]

Kuŵerengera Mtengo

Kuona mwana akusauka—makamaka ngati ali thupi ndi magazi ako—n’koŵaŵitsa mtima kwambiri. Ndiponso Baibulo limalamulira Akristu kuti azisamalira ‘mbumba ya iwo okha.’ (1 Timoteo 5:8) Komabe, nthaŵi zambiri agogo angachite mwanzeru ngati alingalirapo kaye bwino asanatenge udindo umenewu. (Miyambo 14:15; 21:5) Pafunikira kuŵerengera kaye mtengo.—Yerekezerani ndi Luka 14:28.

Lingalirani izi mwapemphero: Kodi mudzakwanitsa zofuna za mwanayo malinga ndi mphamvu zanu, malingaliro anu, zauzimu, ndi zachuma? Kodi nanga amuna anu kapena akazi anu amaiona motani nkhaniyo? Kodi pali njira yolimbikitsira kapena kuthandizira makolo a mwanayo kuti azim’samala okha? N’zachisoni kuti makolo ena osasamala amangopitiriza kumakhala moyo wachiwerewere. Gogo wina akukumbukira moŵawidwa mtima kuti: “Zinapangitsa kuti nditenge ana ake angapo. Koma mwana wanga wamkaziyo anapitirizabe kumamwa mankhwala osokoneza bongo ndi kumabalabe ana ena. Ndinafika pokana kuti sindikufunanso!”

Komanso, ngati sukusamala adzukulu ako, kodi chidzachitika n’chiyani kwa iwo? Kodi mudzatha kuugwira mtima pamene mulingalira zakuti akuwasamalira ndi anthu ena, mwinamwake anthu osawadziŵa? Nanga bwanji zimene anawo akufunikira mwauzimu? Kodi anthu enawo adzakwanitsa kuwalera mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna? Ena amati ngakhale kuti pali zovuta zomwe zimaloŵetsedwapo, palibe njira ina yomwe angatsate kusiyapo kungosenza udindowo.

Iyi ndi nkhani yovuta, ndipo aliyense payekha ayenera kusankha yekha zoyenera kuchita.

[Chithunzi patsamba 27]

Agogo ambiri amalephera kukwanitsa kuchita zofunika polera ana ang’ono

[Chithunzi patsamba 28]

Agogo oopa Mulungu angathe kukhala ndi chikhulupiriro chakuti akachita khama Yehova adzawathandiza

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena