Kuda Nkhaŵa Chifukwa cha Magazi Amatenda
PAMENE Demetrio Pessoa, katswiri wa maphunziro a biochemistry wa ku Bolivia anachitidwa opaleshoni, anadwalanso atangotuluka m’chipatala ndipo mwamsanga anam’tengeranso kuchipatala. Kumeneko anamuika magazi, ndipo anayamba kupezako bwino. Komabe, mosakhalitsa, katswiri wa biochemistry ameneyu anayamba kumva ngati akudwala malungo. Atamuyeza, madokotala anamuuza uthenga womvetsa chisoni: Bamboyu yemwe dzina lake ndi Pessoa anali atalandira magazi amene anali ndi kachilombo kotchedwa Trypanosoma cruzi. Ndiye kuti anatenga matenda otchedwa Chagas.”
Bambo Pessoa si munthu yekhayo amene anakumana ndi zoterezi ku Bolivia, likutero bungwe lofalitsa nkhani la ku London lotchedwa Panos. Kafukufuku wa zachipatala amene anachitidwa kwa nthaŵi yaitali m’mayiko 12 a ku Latin America akusonyeza kuti kumeneko, matenda oyamba chifukwa cha magazi amatenda ndi ofala. M’dziko lina la ku Latin America, mwa odwala 10,000 alionse amene analandira magazi, odwala 220 anatenga matenda opatsirana. Kusonyeza kuti munthu mmodzi mwa anthu 45 alionse anagwidwa ndi matendawo!
Komabe, si matenda a Chagas okhawo amene angatengedwe. Kafukufuku yemweyu akusonyeza kuti mayiko angapo a ku Latin America sankayeza magazi operekedwa ndi anthu kuti aone ngati ali ndi matenda a Hepatitis C ndiponso kuti m’mayiko ena magazi ankayesedwa ngati ali ndi matenda a chindoko mwa kamodzikamodzi basi. Kuphatikizanso apo, mayiko angapo analibe zida zokwanira kuti aziyeza magazi ngati ali ndi HIV. Ponenapo za magazi amatenda, Tonchi Marinkovic, amene ali nduna ya za Umoyo ku Bolivia, ananena kuti: “Mulungu mutiteteze kuti tisathe ndi matenda a chindoko, kutupa chiŵindi, Chagas kapena AIDS kuti asabukenso.”
Ngakhale kuti mwina sichinali cholinga chake, koma munthu woimira boma ameneyu anasonyezadi njira yolondola yothetsera matenda oopsa ameneŵa. Zaka zambiri m’mbuyomu, magazini yotchedwa Notícias Bolivianas inalemba m’nkhani yake ina yonena za kuopsa koika munthu magazi kuti: “Kusala magazi ndiko kovomerezeka mogwirizana ndi lamulo la Baibulo.” Lamulo la Baibulo limene magazini ya ku Bolivia imeneyi ikunena limapezeka pa Machitidwe 15:29. Ndipo limati: “Musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino.”—Onaninso Genesis 9:4; Levitiko 3:17.