Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 7/8 tsamba 8-11
  • Mmene Mungakhalire ndi Maganizo Abwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungakhalire ndi Maganizo Abwino
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Poizoni pa Ubongo
  • Sankhani Zosangalatsa Mwanzeru
  • Pemphani Mulungu Akutsogozeni
  • Kodi Mungasankhe Bwanji Zosangalatsa Zabwino?
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Mukhoza Kupeza Zosangulutsa Zabwino
    Galamukani!—1997
  • Kodi Tingasankhe Bwanji Zosangalatsa?
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Kodi Wailesi Yakanema Yakusinthani?
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 7/8 tsamba 8-11

Mmene Mungakhalire ndi Maganizo Abwino

THANZI lathu limakhala labwino makamaka chifukwa cha zimene timadya. Munthu akamangokhalira kudya chakudya chosamanga thupi , sakhala ndi thanzi labwino. Zili chimodzimodzi ndi maganizo.

Mwachitsanzo, mungayerekezere kuti zinthu zimene timaloŵetsa m’maganizo mwathu zili ngati chakudya cha maganizo. Zingakhale chakudya cha maganizo? Inde, mawu amene timaŵerenga m’mabuku, m’magazini, kuwamva pa wailesi yakanema, m’mafilimu, m’maseŵera avidiyo, pa internet, ndi mawu a nyimbo zimene timamvetsera zingasinthe maganizo athu ndi umunthu wathu monga mmenedi chakudya chenicheni chimasinthira thupi lathu. Mwa njira yanji?

Jerry Mander, yemwe kale anali katswiri pa zotsatsa malonda, ponena za mmene wailesi yakanema imakhudzira moyo wathu, analemba kuti: “Wailesi yakanema imajambula zithunzi pa ubongo wathu kuposa mmene chimachitira chinthu china chilichonse.” Komabe, zithunzi za m’maganizo zimenezo, sizimangotisangalatsa kokha. Magazini yotchedwa The Family Therapy Networker inati: “Chinenero, zithunzithunzi, nyimbo kapena mawu enaake, malingaliro, zinthu zimene zimaonedwa ngati zofunika kwambiri, zinthu zimene zimaonedwa ndi anthu ambiri ngati zokongola, zakhala nkhani zosachoka m’maganizo.”

Inde, kaya timazindikira kapena sitizindikira, maganizo athu amatengeka ndi zimene timaona pa wailesi yakanema, kutengekanso ndi mitundu ina ya maseŵera. Ndipo pamenepo mpamene pali ngozi. Monga mmene Mander ananenera, “anthufe timasintha pang’onopang’ono mpaka n’kukhala ngati zithunzi zimene tili nazo m’maganizo mwathu.”

Poizoni pa Ubongo

Anthu ambiri amene amasankha kwambiri zakudya zawo zathupi, sasankha chikakhala chakudya chamaganizo, amangoloŵetsa m’maganizo chilichonse chimene amva kapena kuŵerenga m’nyuzipepala. Mwachitsanzo, kodi munamvapo wina akunena kuti: “Palibe chilichonse chosangalatsa kuonera pa TV!” Ena anangomwerekera, saleka kufunafuna masiteshoni ena kuti mwina angatulukire kanthu kena kabwino. Saganiza zoti angotseka TV’yo iyayi!

Mapologalamu ambiri a pa TV, kusiyapo kuti amawononga nthaŵi kwambiri, amakhalanso ndi nkhani zimene Akristu ayenera kuzipeŵa. Gary Koltookian, wolemba nkhani za pa TV, anati: “Kusiyapo nkhani zonyansa, nkhani zina zobutsa mikangano ndi zakugonana lero zimaonekaoneka kwambiri pa TV kuposa kale.” Pa kafukufuku waposachedwapa ku United States, panapezeka kuti zithunzi zakugonana zimaoneka nthaŵi 27 paola, makamaka panthaŵi imene anthu ambiri amakhala akuonerera TV.

Zimenezi zingapangitse munthu kuganiza za mmene zoterezi zikukhudzira maganizo a anthu. Ku Japan, seŵero lina la pa wailesi yakanema linakopa anthu ambiri kwambiri moti nyuzipepala ina ya kumeneko inanena kuti seŵerolo linapangitsa “anthu ochita chigololo kuchuluka.” Ndiponso, omwe analemba buku lotchedwa Watching America anati: “Lero njira zambiri zakugonana . . . zikungoonedwa ngati chinthu chimene munthu aliyense angadzisankhire monga moyo wake.”

Komabe, mapologalamu a pa TV, amene amatamanda kugonana angokhala mbali ina yavutolo. Chiwawa chosonyezedwa mwatsatanetsatane chafalanso. China chodetsa nkhaŵa kwambiri n’chakuti mapologalamu a pa TV ndi mafilimu amaipitsa maganizo a ana, poti iwo sachedwa kutengeka maganizo ndizinthu. Mkulu wina wankhondo yemwenso ali katswiri wodziŵa zimene zimalimbitsa anthu mtima popha anzawo, David Grossman, anati: “Ana akaona wina akuwomberedwa, akulasidwa ndi mpeni, akugwiriridwa, kuchitidwa nkhanza, kunyozedwa, kapena kuphedwa pa TV, kwa iwowo zimakhala ngati zikuchitikadi.” Magazini yotchedwa The Journal of the American Medical Association pothirira ndemanga pavuto lomweli, inati: “ana ambiri azaka zitatu ndi zinayi sadziŵa kusiyanitsa zochitika zenizeni ndi zongoyerekezera, ndipo sazindikirabe ngakhale achikulire awafotokozere.” Mwa mawu ena, ngakhale kholo limuuze mwana kuti, ‘Anthu amene ajatu sanafe ayi, akungonamizira kuti afa,’ maganizo a mwana sasiyanitsabe ngakhale pang’ono. Kwa mwana wamng’ono, chiwawa cha pa TV n’chenicheni ndithu.

Magazini ya Time, pofotokoza mwachidule zimene “chiwawa cha pa TV” chimachita, inati: “Kwatsala ofufuza oŵerengeka chabe tsopano amene amadzivutabe n’kumatsutsa kuti ana akamaonerera kuphana pa TV ndi pa kanema, zimawakhudza kwambiri.” Kodi zimawakhudza bwanji anawo? Wothirira ndemanga pa zamafilimu, Michael Medved, anati: “Chifukwa chakuti anthu akhala akuonerera zosangalatsa zachiwawa kwa zaka makumi ambiri, maganizo awo azoloŵera, sazionanso ngati zoopsa.” Iye anatinso: “Anthu akaleka kuchita mantha ndi chiwawa, ndiye kuti zinthu zalakwika.” N’chifukwa chake mlembi wina ananena kuti kupita ndi mwana wazaka zinayi kufilimu yachiwawa “kuli ngati kutsanulira poizoni muubongo [wake].”

Panopa sitikuti mapologalamu onse a wailesi yakanema n’ngoipa iyayi. Chimodzimodzinso ndi mabuku ena, magazini, mafilimu, maseŵera a pakompyuta, ndi mitundu inanso ya zosangalatsa. Komabe, n’zachionekere kuti zambiri zimene zimatchedwa zosangalatsa n’zosayenera kwa anthu amene akufuna kukhala ndi maganizo abwino.

Sankhani Zosangalatsa Mwanzeru

Zithunzi zimene timaona zimaloŵa m’maganizo n’kukhazikika momwemo ndipo zimatisonkhezera kumangoganiza za izo ndi kuchita zomwezo. Mwachitsanzo, titamangoganiza za zosangalatsa zonena za kugonana, tingalephere kumvera lamulo la Baibulo lakuti “thaŵani dama.” (1 Akorinto 6:18) Chimodzimodzinso ngati timakonda kuonerera maseŵera osonyeza “anthu akuchita zopanda pake,” tingalephere ‘kukhala ndi mtendere ndi anthu onse.’ (Salmo 141:4; Aroma 12:18) Kuti tipeŵe zimenezi, tiyenera ‘kusaika chinthu choipa pamaso pathu.’—Salmo 101:3; Miyambo 4:25, 27.

N’zoona kuti chifukwa chakuti tinabadwa opanda ungwiro, tonsefe timafunikira kulimbikira kuchita zabwino. Mtumwi Paulo anavomereza mosabisa mawu, kuti: “Ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiona lamulo lina m’ziwalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziwalo zanga.” (Aroma 7:22, 23) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Paulo anali kungodzilekerera chifukwa thupi lake linali lofooka? Kutalitali! Anati: “Ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti. . .ndingakhale wotayika ndekha.”—1 Akorinto 9:27.

Ifenso sitiyenera kudzikhululukira chifukwa cha kupanda ungwiro kwathu. Wolemba Baibulo, Yuda, anati: “Okondedwa, . . . ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu [“mumenyere zolimba,” NW] chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima.” (Yuda 3, 4) Inde, tifunikira ‘kumenyera zolimba chifukwa cha chikhulupiriro’ ndi kupeŵa zosangalatsa zimene zimatisonkhezera kuchita zoipa.a

Pemphani Mulungu Akutsogozeni

Kuyesayesa kukhala ndi maganizo abwino n’kovuta nthaŵi zambiri m’dongosolo lino la zinthu. Komabe, Baibulo limatilonjeza kuti n’kotheka kukhala ndi maganizo oyera ndi makhalidwenso oyera. N’kotheka bwanji? Pa Salmo 119:11, timaŵerenga kuti: “Ndinawabisa mawu anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.”

Kusunga mawu a Mulungu kumatanthauza kuwaona monga chinthu cha mtengo wapatali kapena kuwalemekeza kwambiri. Sitingathe kulilemekeza Baibulo ngati sitikudziwa zimene limanena. Tikamaphunzira chidziŵitso cholongosoka m’Mawu a Mulungu, timakhala ndi maganizo a Mulungu. (Yesaya 55:8, 9; Yohane 17:3) Ndiye timatakata mwauzimu, ndipo timaganiza mwapamwamba kwambiri.

Kodi pali njira ina yodalirika yodziŵira chimene chili chabwino pamkhalidwe wathu wauzimu ndi pamaganizo athu? Inde! Mtumwi Paulo analangiza kuti: “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.”—Afilipi 4:8.

Koma kuti tipinduledi, tifunikira zambiri, osati kungodziŵa za Mulungu basi. Mneneri Yesaya anauziridwa kulemba kuti: ‘Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.’ (Yesaya 48:17) Inde, sitingofunikira kupempha Mulungu kutitsogoza komanso tifunikira kuchita malingana ndi chidziŵitso chimenecho.

Njira ina yopindulira mwauzimu ndi mwamakhalidwe ndiyo kulankhula ndi Yehova, “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2; 66:19) Tikamafikira Mlengi wathu moona mtima ndi modzichepetsa, adzamva madandaulo athu. Ndipo ‘tikam’funa Iye, tidzam’peza.’—2 Mbiri 15:2.

Choncho, kodi n’kotheka kukhala ndi maganizo abwino m’dziko lachiwawa ndi lachisembwereli? N’kotheka ndithu! Mwa kusalola maganizo athu kufooketsedwa ndi zosangalatsa za dzikoli, mwa kukulitsa luso lathu lakuganiza pophunzira Mawu a Mulungu, ndi mwa kupempha Mulungu kutitsogoza, tingakhale ndi maganizo abwino!

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mudziŵe zambiri pankhani yakusankha zosangalatsa zabwino, onani Galamukani! ya June 8, 1997, masamba 22-24.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

“Ana ambiri sadziŵa kusiyanitsa zochitika zenizeni ndi zongoyerekezera za pa wailesi yakanema”

[Mawu Otsindika patsamba 11]

“Chifukwa chakuti anthu akhala akuonerera zosangalatsa zachiwawa kwa zaka makumi ambiri, maganizo awo azoloŵera, sazionanso ngati zoopsa”

[Bokosi patsamba 11]

Kupeŵa Tsoka Logwidwa ndi Nthenda ya Mtima

Magazini ya Nutrition Action Healthletter inatchula njira zotsatirazi zopeŵera nthenda ya mtima.

• Lekani kusuta fodya. Mutalekeratu lero mungapeŵe nthenda ya mtima m’chaka chimodzi, ngakhale mutakhala kuti mwanenepa.

• Chepetsani thupi. Ngati muli wonenepa, mutachepetsa thupi ndi makilogalamu aŵiri kapena anayi zingakhale bwino.

• Chitani maseŵera olimbitsa thupi. Kuchita maseŵera olimbitsa thupi nthaŵi zonse (mwina katatu pamlungu) kumathandiza kuchepetsa mankhwala opezeka m’thupi otchedwa cholesterol (LDL), amene ali oipa, kumathandizanso magazi kusathamanga kwambiri, ndipo simunganenepe kwambiri.

• Idyani zakudya zopanda mafuta ambiri. Ngati LDL yanu yakwera, yambani kudya nyama yopandiratu mafuta ndiyeno yesani kumwa mkaka (wokhala ndi 1 peresenti ya mafuta) kapena mkaka wa ufa (wopandiratu mafuta) m’malo mwa mkaka wokhala ndi 2 peresenti ya mafuta.

• Chepetsani kumwa moŵa. Pali umboni wakuti amene amamwako pang’ono vinyo wofiira amapeŵa nthenda ya mtima.

• Idyani zipatso zambiri, zamasamba zambiri, ndi zakudya zina zopukusika msanga.

[Chithunzi patsamba 8]

Chiwawa cha pa TV chili ngati poizoni chikaloŵa muubongo wa mwana

[Chithunzi patsamba 9]

Nthaŵi zina ana amatsanzira chiwawa chimene amaona pa TV

[Chithunzi patsamba 10]

Makolo angathandize ana mwa kuwapatsa mabuku oŵerenga abwino osiyanasiyana

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena