Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • T-19 tsamba 2-6
  • Kodi Dzikoli Lidzapulumuka?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Dzikoli Lidzapulumuka?
  • Kodi Dzikoli Lidzapulumuka?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Dziko Litha—Lina Liriloŵa M’Malo
  • Mtsogolo mwa Dzikoli
  • “Chizindikiro”
  • Pamene Dziko Latsopano Lidzadza
    Galamukani!—1993
  • “Mapeto a Dziko” Ayandikira!
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Madzi Anawononga Dziko—Kodi Zidzachitikanso?
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Kodi Mapeto a Dziko Oloseredwa Ali Pafupi?
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Kodi Dzikoli Lidzapulumuka?
T-19 tsamba 2-6

Kodi Dzikoli Lidzapulumuka?

Palibe mbadwo wina umene wamva zochuluka ponena za mapeto adziko. Ambiri amawopa kuti dzikoli lidzathera m’chipiyoyo cha nyukliya. Ena amaganiza kuti kuipitsa kungawononge dziko. Enanso amadera nkhaŵa kuti mavuto achuma adzachititsa magulu a anthu kumenyana.

Kodi dzikoli lingathedi? Ngati likatero, kodi zikatanthauzanji? Kodi dziko linayambapo latha?

Dziko Litha—Lina Liriloŵa M’Malo

Inde, dziko linatha. Lingalirani za dziko limene linafikira kukhala loipa kwambiri m’masiku a Nowa. Baibulo limafotokoza kuti: “Dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidawonongeka.” Baibulo limanenanso kuti: “[Mulungu] sanalekerere dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wachilungamo, ndi anzake asanu ndi aŵiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula.”—2 Petro 2:5; 3:6.

Wonani chimene kutha kwa dziko limenelo kunatanthauza ndi chimene sikunatanthauze. Sikunatanthauze kutha kwa mtundu wa anthu. Nowa ndi banja lake anapulumuka Chigumula cha dziko chimenecho. Chimodzimodzinso pulanetili Dziko Lapansi ndi miyamba yokongola ya nyenyezi. Linali “dziko la osapembedza” limene linawonongeka, dongosolo loipa la zinthu.

Potsirizira pake, pamene mbadwa za Nowa zinali kuwonjezeka, dziko lina linayambika. Dziko lachiŵiri limeneli, kapena dongosolo la zinthu, lakhalako kufikira kutsiku lathu. Mbiri yake yakhala yodzazidwa ndi nkhondo, upandu, ndi chiwawa. Kodi nchiyani chimene chidzachitikira dzikoli? Kodi lidzapulumuka?

Mtsogolo mwa Dzikoli

Chitatha kunena kuti dziko la m’tsiku la Nowa linawonongeka, cholembedwa cha Baibulo chimapitirizabe kuti: “Miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mawu omwewo zaikika kumoto.” (2 Petro 3:7) Ndithudi, monga momwe wolemba Baibulo wina akufotokozera: “Dziko lapansi [limene liripo lerolino] lipita.”—1 Yohane 2:17.

Baibulo silikutanthauza kuti dziko lapansi lenilenili kapena miyamba ya nyenyezi zidzapita, monga momwedi zimenezi sizinapitire m’tsiku la Nowa. (Salmo 104:5) Mmalomwake, dzikoli, ndi “miyamba” yake, kapena olamulira a maboma otsogozedwa ndi Satana, ndi “dziko” lake, kapena chitaganya cha anthu, zidzawonongedwa monga ngati ndi moto. (Yohane 14:30; 2 Akorinto 4:4) Dziko lino, kapena dongosolo la zinthu, lidzawonongeka monga momwedi linachitira dziko lokhalako Chigumula chisanadze. Ngakhale Yesu Kristu ananena za mkhalidwe wa “masiku a Nowa” monga chitsanzo cha zimene zikachitika choyambirira kumapeto adzikoli.—Mateyu 24:37-39.

Kwakukulukulu, pamene Yesu ananena za masiku a Nowa, anali kuyankha funso la atumwi ake lakuti: “Kodi nchiyani chimene chidzakhala chizindikiro chakudza kwanu, ndi cha mapeto a dziko?” (Mateyu 24:3, King James Version) Otsatira a Yesu anadziŵa kuti dzikoli likatha. Kodi chiyembekezo chimenechi chinawawopsa?

Mosiyana, pamene Yesu anafotokoza zochitika zimene zikachitika mapeto adziko asanafike, iye anawalimbikitsa kukondwera ‘chifukwa chakuti chiwomboledwe chawo chinali kuyandikira.’ (Luka 21:28) Inde, kuwomboledwa kuchoka kwa Satana ndi dongosolo lake loipa la zinthu kuloŵa m’dziko latsopano la mtendere!—2 Petro 3:13.

Koma kodi dzikoli lidzatha liti? Kodi ‘nchizindikiro’ chotani chimene Yesu anapereka cha ‘kudza kwake, ndi chamapeto adziko’?

“Chizindikiro”

Liwu la Chigiriki lotembenuzidwa pano kuti ‘kudza’ ndilo pa·rou·siʹa, ndipo limatanthauza “kukhalapo,” ndiko kuti, kukhala ulipo kwenikweni. Chotero pamene “chizindikiro” chiwoneka, sikukatanthauza kuti Kristu anali kudza msanga koma kuti anali atadza kale ndipo analipo. Kukatanthauza kuti iye anali atayamba kulamulira mosawoneka monga mfumu yakumwamba ndi kuti mwamsanga adzawononga adani ake.—Chivumbulutso 12:7-12; Salmo 110:1, 2.

Yesu sanapereke chochitika chimodzi chokha monga “chizindikiro.” Anafotokoza zochitika zadziko zambiri ndi mikhalidwe. Zonsezi zikachitika mkati mwa nthaŵi imene olemba Baibulo anatcha “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1-5; 2 Petro 3:3, 4) Lingalirani zina za zinthu zimene Yesu ananeneratu kuti zikasonyeza “masiku otsiriza.”

“Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina ndi ufumu ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Nkhondo makono ano zakhala zazikulu kwambiri koposa ndi kale lonse. Wolemba mbiri wina anati: “Nkhondo Yadziko Yoyamba [yoyambika mu 1914] inali nkhondo ‘yotheratu yoyamba.’” Komabe, nkhondo yadziko yachiŵiri inali yowononga mowonjezereka kwambiri. Ndipo nkhondo zikupitirizabe kuwononga dziko lapansi. Inde, mawu a Yesu akwaniritsidwa mwapadera!

“Kudzakhala njala.” (Mateyu 24:7) Motsatira Nkhondo Yadziko I panadza mwinamwake njala yaikulu koposa m’mbiri yonse. Njala inanso yowopsa inatsatira Nkhondo Yadziko II. Mliri wakusadya mokwanira umayambukira kufikira pachigawo chimodzi mwazisanu za chiŵerengero cha dziko lapansi, ukumapha ana okwanira mamiliyoni 14 chaka chirichonse. Ndithudi, “kwakhala njala”!

“Kudzakhala zivomezi zazikulu.” (Luka 21:11) Pa avereji, anthu ambiri oŵirikiza nthaŵi khumi afa chaka chirichonse ndi zivomezi chiyambire 1914 m’zaka mazana zapitazo. Lingalirani chabe zina zoŵerengeka zazikulu: 1920, China, ophedwa 200,000; 1923, Japan, ophedwa kapena osowa pafupifupi 140,000; 1939, Turkey, ophedwa 32,700; 1970, Peru, ophedwa 66,800; ndi 1976, China, pafupifupi ophedwa 240,000 (kapena, malinga ndi magwero ena, 800,000). Ndithudi, “zivomezi zazikulu”!

“Miliri m’malo akutiakuti.” (Luka 21:11) Itangotha Nkhondo Yadziko I, anthu okwanira mamiliyoni 21 anafa ndi fuluwenza ya Spanya. Science Digest inasimba kuti: “M’mbiri yonse simunakhale kufikiridwa ndi imfa, kwamphamvu ndi kofulumira chotero.” Chiyambire pamenepo, nthenda ya mtima, kansa, AIDS, ndi miliri ina yambiri yapha mamiliyoni mazana ambiri.

“Kuchuluka kwa kusayeruzika.” (Mateyu 24:12) Chiyambire 1914 dziko lathu lakhala lodziŵika ndi upandu ndi chiwawa. M’malo ambiri palibe aliyense amamva kukhala wotetezereka m’makwalala ngakhale nthaŵi ya masana. Usiku anthu amakhala m’nyumba zawo za makomo okhomedwa ndi loko ndi ochinga, amantha kutuluka kunja.

Zinthu zina zambiri zinanenedweratu kuti zikachitika mkati mwa masiku otsiriza, ndipo zonsezi nazonso zikukwaniritsidwa. Zimenezi zikutanthauza kuti mapeto adziko ali pafupi. Koma, mwachimwemwe, padzakhala opulumuka. Litatha kunena kuti “dziko lapansi lipita,” Baibulo limalonjeza kuti: “Iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala nthaŵi zonse.”—1 Yohane 2:17.

Chotero tifunikira kuphunzira chifuniro cha Mulungu ndi kuchichita. Pamenepo tingathe kupulumuka mapeto adzikoli ndi kusangalala kosatha ndi madalitso a dziko latsopano la Mulungu. Baibulo limalonjeza kuti panthaŵiyo: “Mulungu . . . adzawapukutira [anthu] misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Kusiyapo ngati kutasonyezedwa mwanjira ina, mawu onse a Baibulo ogwidwa muno ngochokera mu Revised Union Nyanja Version.

[Mawu a Chithunzi patsamba 6]

Magwero a Zithunzithunzi: Ndege: Chithunzithunzi cha USAF. Mwana: WHO chithunzithunzi cha W. Cutting. Chivomezi: Y. Ishiyama, Hokkaido University, Japan.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena