Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es25 tsamba 17-26
  • February

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • February
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
  • Timitu
  • Loweruka, February 1
  • Lamlungu, February 2
  • Lolemba, February 3
  • Lachiwiri, February 4
  • Lachitatu, February 5
  • Lachinayi, February 6
  • Lachisanu, February 7
  • Loweruka, February 8
  • Lamlungu, February 9
  • Lolemba, February 10
  • Lachiwiri, February 11
  • Lachitatu, February 12
  • Lachinayi, February 13
  • Lachisanu, February 14
  • Loweruka, February 15
  • Lamlungu, February 16
  • Lolemba, February 17
  • Lachiwiri, February 18
  • Lachitatu, February 19
  • Lachinayi, February 20
  • Lachisanu, February 21
  • Loweruka, February 22
  • Lamlungu, February 23
  • Lolemba, February 24
  • Lachiwiri, February 25
  • Lachitatu, February 26
  • Lachinayi, February 27
  • Lachisanu, February 28
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
es25 tsamba 17-26

February

Loweruka, February 1

Ine ndidzakumvetserani.​—Yer. 29:12.

Mfumu Hezekiya atadwala kwambiri anapempha Yehova kuti amuchiritse ndipo Yehova anamuchiritsadi. (2 Maf. 20:1-6) Koma mtumwi Paulo atapempha Yehova kuti amuchotsere minga m’thupi, Yehova sanachotse vuto lakelo. (2 Akor. 12:7-9) Mtumwi Petulo ndi Yakobo,ankayembekezera kuphedwa ndi Mfumu Herode. Koma Yakobo anaphedwa pomwe Petulo anamasulidwa m’njira yodabwitsa. (Mac. 12:1-11) Ndiye tikhoza kumadabwa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova anapulumutsa Petulo koma Yakobo n’kumusiya kuti aphedwe?’ Baibulo silifotokoza chifukwa chake. Koma chomwe tikudziwa ndi chakuti nthawi zonse Yehova “sachita zinthu zopanda chilungamo.” (Deut. 32:4) Nthawi zina zinthu zimene sitimaziyembekezera ndi zimene zimachitika. Koma popeza timakhulupirira kuti nthawi zonse Yehova amayankha mapemphero athu mwachikondi komanso mwachilungamo, sitikayikira njira zimene amasankha poyankha mapemphero.—Yobu 33:13. w23.11 21 ¶6

Lamlungu, February 2

Nzeru yochokera kumwamba . . . ndi . . . yokonzeka kumvera.​—Yak. 3:17.

Yakobo anauziridwa kulemba kuti anthu anzeru amakhala ‘okonzeka kumvera.’ Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Tiyenera kukhala ofunitsitsa komanso okonzeka kumvera anthu amene Yehova wawapatsa udindo. Komabe, Yehova samayembekezera kuti tizimvera anthu amene akutipempha kuti tichite zinthu zosemphana ndi malamulo ake. (Mac. 4:18-20) Nthawi zina tingamaone kuti n’zosavuta kumvera Yehova kusiyana ndi kumvera munthu. Ndipotu Yehova nthawi zonse amatipatsa malangizo abwino. (Sal. 19:7) Zimenezitu n’zosiyana kwambiri ndi anthu omwe ali ndi udindo. Ngakhale zili choncho, Atate wathu wakumwamba anapereka udindo kwa makolo, akulu mumpingo komanso akuluakulu a boma. (Miy. 6:20; 1 Ates. 5:12; 1 Pet. 2:13, 14) Tikamamvera anthu amenewa timakhala tikumvera Yehova. w23.10 6 ¶2-3

Lolemba, February 3

Mawu amenewa ndi odalirika komanso oona.​—Chiv. 21:5.

Njira imodzi yomwe tingalimbitsire chikhulupiriro chathu ndi kuganizira mphamvu za Yehova. Iye ali ndi mphamvu zokwaniritsira chilichonse chomwe walonjeza. N’zoona kuti kwa anthu, lonjezo la moyo wosatha m’dziko latsopano lingaoneke losatheka. Koma nthawi zambiri Yehova amalonjeza zinthu zomwe anthu sangathe kuchita. Iyetu ndi Mulungu Wamphamvuyonse. (Yobu 42:2; Maliko 10:27; Aef. 3:20.) Iye anatsimikizira Abulahamu ndi Sara kuti adzakhala ndi mwana ngakhale kuti anali atakalamba. (Gen. 17:15-17) Anauzanso Abulahamu kuti ana ake adzapatsidwa dziko la Kanani. M’zaka zambiri zimene ana a Abulahamu, Aisiraeli, anali akapolo ku Iguputo, ziyenera kuti zinkaoneka ngati lonjezoli silidzakwaniritsidwa. Koma linakwaniritsidwa. Patapita zaka zambiri, Yehova analengeza kuti Elizabeti yemwe anali wokalamba adzakhala ndi mwana. Iye anauzanso Mariya yemwe anali namwali kuti adzabereka Mwana wake wamwamuna. Yehova anali atalonjeza za kubwera kwa Mwanayu zaka masauzande m’mbuyomo m’munda wa Edeni ndipo anakwaniritsa lonjezoli. (Gen. 3:15) Tikamaganizira zimene Yehova anachitapo m’mbuyomu polonjeza komanso kukwaniritsa malonjezowo, timakhulupirira kwambiri kuti ali ndi mphamvu zobweretsa dziko latsopano.—Yos. 23:14; Yes. 55:10, 11. w23.04 28 ¶10-12

Lachiwiri, February 4

Inu Yehova, imvani pemphero langa. Mvetserani kuchonderera kwanga kopempha thandizo.​—Sal. 143:1.

Yehova anayankha mapemphero a Davide oti amupulumutse. (1 Sam. 19:10, 18-20; 2 Sam. 5:17-25) Ifenso tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatithandiza. (Sal. 145:18) Iye sangayankhe mapemphero athu m’njira imene timayembekezera. Paulo anapempha Mulungu kuti amuchotsere “minga m’thupi.” Katatu konse anapempherera za vuto limeneli. Kodi Yehova anayankha mapemphero amenewo? Inde, koma osati m’njira imene Paulo ankayembekezera. M’malo mochotsa vutolo, Yehova anamupatsa mphamvu zomwe ankafunikira kuti apitirize kumutumikira mokhulupirika. (2 Akor. 12:7-10) Nthawi zina ifenso tingayankhidwe mapemphero athu m’njira imene sitimayembekezera. Koma tingakhale otsimikiza kuti Yehova amadziwa njira yabwino kwambiri yotithandizira. Iye “angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza.” (Aef. 3:20) Pa chifukwa chimenechi, iye angayankhe mapemphero athu pa nthawi komanso m’njira imene sitimayembekezera. w23.05 8-9 ¶4-6

Lachitatu, February 5

Nthawi ikubwera imene onse amene ali mʼmanda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka.​—Yoh. 5:​28, 29.

Tingachite bwino kuti nthawi ndi nthawi tiziganizira lonjezo la m’Baibulo lakuti akufa adzauka. Chifukwa chiyani? Chifukwa sitingadziwiretu nthawi imene tingadwale matenda aakulu kapena mwadzidzidzi munthu amene timamukonda angamwalire. (Mlal. 9:11; Yak. 4:13, 14) Kukhulupirira kuti akufa adzauka kungatithandize kuti tipirire mavuto ngati amenewa. (1 Ates. 4:13) Malemba amatitsimikizira kuti Atate wathu wakumwamba amatidziwa bwino ndipo amatikonda kwambiri. (Luka 12:7) Tangoganizani mmene Yehova Mulungu amatidziwira bwino kuti adzathe kutiukitsa ndi makhalidwe omwe tinali nawo komanso tikutha kukumbukira chilichonse. Ndipotu Yehova anasonyeza kuti amatikonda kwambiri potipatsa mwayi woti tidzakhale ndi moyo wosatha ngakhalenso kutiukitsa ngati titamwalira. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira lonjezo lakuti akufa adzauka? Tiyenera kukhala otsimikiza kuti amene akulonjezayo ndi wofunitsitsa komanso ali ndi mphamvu zochitira zimene akulonjezazo. w23.04 8-9 ¶2-4

Lachinayi, February 6

[Yosefe ndi Mariya,] chaka ndi chaka . . . ankakonda kupita ku Yerusalemu, kuchikondwerero cha Pasika.​—Luka 2:41.

Yosefe ndi Mariya ankachitira zinthu limodzi kuti ubwenzi wawo ndi Yehova ukhalebe wolimba. Iwo ankamvetsa kufunika kolambirira limodzi Yehova monga banja. (Luka 2:22-24, 41; 4:16) Ziyenera kuti zinali zovuta kuchita zimenezi makamaka pamene banja lawo linkakula, komabe anakwanitsa. Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa anthu okwatirana masiku ano. Ngati muli ndi ana ngati mmene Yosefe ndi Mariya analili, nthawi zina zingakhale zovuta kupezeka pamisonkhano kapena kupeza nthawi yochita Kulambira kwa Pabanja. Zingakhalenso zovuta kuti muzipeza nthawi yophunzira kapena kupemphera limodzi monga banja. Komabe muzikumbukira kuti mukamalambira limodzi Yehova, mumakhala naye pa ubwenzi wolimba komanso inuyo mumagwirizana kwambiri. Choncho kulambira kuzikhala pamalo oyamba m’banja mwanu. Ngati mukukumana ndi mavuto m’banja mwanu zingachititse kuti kuchita limodzi Kulambira kwa Pabanja kusamakhale kosangalatsa. Ngati ndi choncho, mungayambe ndi kukambirana kuti muchite zinazake zomwe ndi zosatenga nthawi yaitali, komanso zimene nonse mungasangalale nazo. Kuchita zimenezi kungathandize kuti muzikondana kwambiri ndiponso muzifunitsitsa kuchita limodzi zinthu zokhudza kulambira. w23.05 22 ¶7-8

Lachisanu, February 7

Obadiya anali munthu woopa Yehova kwambiri.​—1 Maf. 18:3.

Kodi mantha oyenera anathandiza bwanji Obadiya? Mwa zina, anamuthandiza kuti akhale woona mtima komanso wodalirika, zomwe zinachititsa kuti mfumu imuike kukhala woyang’anira nyumba yake. (Yerekezerani ndi Nehemiya 7:2.) Kuopa Mulungu kunathandizanso Obadiya kukhala wolimba mtima kwambiri, ndipo iye ankafunikadi kukhala ndi khalidweli. Iye anakhala ndi moyo pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Ahabu yemwe anali woipa. (1 Maf. 16:30) Komanso, Yezebeli mkazi wa Ahabu, yemwe ankalambira Baala, ankadana kwambiri ndi Yehova, moti anayesa kuthetseratu kulambira koona mu ufumu wa kumpoto. Iye anaphanso aneneri ambiri a Mulungu. (1 Maf. 18:4) Yezebeli atayamba kufunafuna aneneri a Mulungu kuti awaphe, Obadiya anabisa aneneri 100 ‘m’magulu awiri a aneneri 50 gulu lililonse ndipo ankawapatsa chakudya ndi madzi.’ (1 Maf. 18:13, 14) Ngati izi zikanadziwika, n’zosakayikitsa kuti munthu wolimba mtimayu akanaphedwa. N’zoona kuti Obadiya anali munthu ngati ife tomwe ndipo sankafuna kufa. Koma iye ankakonda kwambiri Yehova komanso atumiki ake kuposa mmene ankakondera moyo wake. w23.06 16 ¶9-10

Loweruka, February 8

Ine Yehova ndine . . . amene ndimakutsogolerani.​—Yes. 48:17.

Yehova akupitiriza kutsogolera anthu ake masiku ano. Iye amachita zimenezi pogwiritsa ntchito Mawu ake komanso Mwana wake, yemwe ndi mutu wa mpingo. Kodi pali umboni wosonyeza kuti m’masiku athu anonso, Yehova amagwiritsa ntchito anthu omuimira? Inde. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika m’zaka za m’ma 1800. Charles Taze Russell ndi anzake anayamba kuzindikira kuti chaka cha 1914 chidzakhala chofunika chifukwa ndi nthawi yomwe Ufumu wa Mulungu udzakhazikitsidwe. (Dan. 4:25, 26) Maulosi a m’Baibulo ndi omwe anawathandiza kudziwa zimenezi. Kodi Yehova ankawatsogolera pamene iwo ankafufuza m’Baibulo? Mosakayikira ankawathandiza. Zimene zinachitika mu 1914, zinatsimikizira kuti Ufumu wa Mulungu unali utayamba kulamulira. M’chakachi, nkhondo yoyamba ya padziko lonse inayambika, ndipo kunali miliri, zivomerezi komanso njala. (Luka 21:10, 11) Yehova ankagwiritsadi ntchito amuna a mitima yabwinowa kuti athandize anthu ake. w24.02 22 ¶11

Lamlungu, February 9

Mavuto a munthu wolungama ndi ambiri, koma Yehova amamupulumutsa ku mavuto onsewo.​—Sal. 34:19.

Monga anthu a Yehova, timadziwa kuti iye amatikonda ndipo amafuna kuti tizisangalala ndi moyo wabwino kwambiri panopa. (Aroma 8:35-39) Sitikayikiranso kuti nthawi zonse tikamatsatira mfundo za m’Baibulo, zinthu zimatiyendera bwino. (Yes. 48:17, 18) Koma bwanji ngati takumana ndi mavuto omwe sitimayembekezera? Mwachitsanzo, wachibale wathu angatikhumudwitse, tingadwale matenda aakulu omwe angachititse kuti tisamachite zambiri potumikira Yehova, kapenanso tingakumane ndi zotsatirapo za ngozi zam’chilengedwe. Tingathenso kuzunzidwa chifukwa cha zimene timakhulupirira. Tikakumana ndi mavuto ngati amenewa tingamadzifunse kuti: ‘N’chifukwa chiyani zimenezi zikundichitikira? Kodi ndalakwitsa chinachake? Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yehova sakundidalitsa?’ Kodi munayamba mwamvapo chonchi? Ngati ndi choncho musataye mtima. Atumiki ambiri okhulupirika a Yehova anamvaponso choncho.—Sal. 22:1, 2; Hab. 1:2, 3. w23.04 14 ¶1-2

Lolemba, February 10

Ndatsimikiza mtima kumvera malamulo anu nthawi zonse.​—Sal. 119:112.

Tikakumana ndi mayesero, nthawi yomweyo timapewa kuganizira kapena kuchita zinthu zimene zingawononge ubwenzi wathu ndi Mulungu. Yehova amayembekezera kuti ‘tizimumvera mochokera pansi pa mtima.’ (Aroma 6:17) Malangizo ake amathandiza ifeyo ndipo nthawi zonse timafunika kuwamvera. (Yes. 48:17, 18; 1 Akor. 6:9, 10) Mdyerekezi amatizunza pofuna kusokoneza cholinga chathu choti tikhale osasunthika. Cholinga chake ndi ‘kutimeza,’ kapena kuti kuwononga ubwenzi wathu ndi Yehova. (1 Pet. 5:8) Akhristu oyambirira ankaopsezedwa, kumenyedwa komanso kuphedwa chifukwa chakuti anali atatsimikiza mtima kukhalabe olimba. (Mac. 5:27, 28, 40; 7:54-60) Satana akupitirizabe kuchita zimenezi masiku ano. Timaona umboni wa zimenezi, tikaona mmene abale ndi alongo athu akuzunzidwira ku Russia ndi mayiko ena komanso kuukiridwa ndi anthu otsutsa. Kuwonjezera pa kuzunza mwachindunji atumiki a Yehova, Satana amagwiritsanso ntchito “zochita zachinyengo.”—Aef. 6:11. w23.07 15-16 ¶6-9

Lachiwiri, February 11

Tizisonyeza chikondi. Tikatero tidzakhala achikulire m’zinthu zonse.—Aef. 4:15.

Pamene mukuphunzira kwambiri Mawu a Mulungu, m’pamenenso mumayamba kumukonda kwambiri Yehova. Chikondicho chimakulimbikitsani kuti muzitsatira zimene mumaphunzira. Mumasankha zochita mwanzeru mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Mumasintha mmene mumaonera zinthu komanso khalidwe lanu chifukwa mumafuna kusangalatsa Mulungu. Mofanana ndi mwana amene amatsanzira kholo lake lachikondi, inunso mumatsanzira Atate wanu wakumwamba. (Aef. 5:1, 2) Mwina tingadzifunse kuti: ‘Kodi panopa ndimakonda kwambiri Yehova kuposa mmene ndinkamukondera nditangokhala kumene Mkhristu? Kungochokera pamene ndinabatizidwa, kodi ndimaganiza kapena kuchita zinthu ngati Yehova, makamaka posonyeza chikondi kwa abale ndi alongo?’ Ngati ‘chikondi chimene munali nacho poyamba’ chayamba kuchepa, musafooke. Zimenezi zinachitikiraponso Akhristu a mu nthawi ya atumwi. Yesu sanasiye kuwakonda, ndipo ifenso sangasiye kutikonda. (Chiv. 2:4, 7) Iye amadziwa kuti tingayambirenso kukhala ndi chikondi ngati chimene tinali nacho titangodziwa kumene choonadi. w23.07 8 ¶2-3

Lachitatu, February 12

Inu Yehova ndinu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.​—Sal. 86:5.

Mtumwi Petulo analakwitsa zinthu zingapo. Choyamba, iye anasonyeza kudzidalira ponena modzitama kuti adzakhalabe wokhulupirika ngakhale atumwi enawo atamusiya Yesu. (Maliko 14:27-29) Kenako analephera kukhala maso. (Maliko 14:32, 37-41) Pambuyo pake anathawa gulu la anthu litabwera kudzagwira Yesu. (Maliko 14:50) Pomaliza, Petulo anakana katatu kuti sakudziwa Yesu, mpaka anafika polumbirira bodzali. (Maliko 14:66-71) Kodi Petulo anatani atadziwa kuti walakwitsa kwambiri zinthu? Iye anasweka mtima ndipo analira kwambiri. (Maliko 14:72) M’malo mokalipira Petulo chifukwa cha zimene analakwitsa, Yesu anauza mnzakeyu kuti adzalandira maudindo akuluakulu. (Yoh 21:15-17) Petulo anadziwa kuti walakwitsa kwambiri koma sanataye mtima. N’chiyani chinamuthandiza? Iye ankadziwa kuti Mbuye wake Yesu sanasiye kumukonda. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Yehova amafuna tisamakayikire kuti amatikonda komanso kutikhululukira.—Aroma 8:38, 39. w24.03 18-19 ¶13-15

Lachinayi, February 13

Amene aphedwa ndi iyeyo ndi osawerengeka.—Miy. 7:26.

Khalidwe lachiwerewere lingachititse kuti munthu azichita manyazi, azidziona kuti ndi wachabechabe, atenge mimba yosayembekezera komanso lingasokoneze mabanja. Kunena zoona, ndi nzeru kukana kupita ‘kunyumba’ ya mkazi wopusa. Kuwonjezera pa kuwononga ubwenzi wawo ndi Yehova, ambiri amene amachita khalidwe lachiwerewere amatenga matenda, zomwe zimachititsa kuti afe msanga. (Miy. 7:23) Vesi 18 ya Miyambo chaputala 9, imamaliza ndi mawu akuti: “Alendo a mkaziyo ali m’dzenje la Manda.” Ndiye n’chifukwa chiyani anthu ambiri amavomera akaitanidwa ndi mkaziyu ngakhale kuti amakumana ndi mavuto? (Miy. 9:13-18) Msampha wofala kwambiri ndi kuonera zolaula. Ena amaona kuti kuonera zolaula kulibe vuto lililonse. Koma zoona n’zakuti kuonera zolaula n’koopsa, kumamuchotsera munthu ulemu komanso zimamuvuta kuti asiye. Zithunzi zolaula zimakhazikika m’maganizo ndipo zimakhala zovuta kuziiwala. Kuonera zolaula sikuthandiza munthu kuti athetse chilakolako cha kugonana, koma kumangochiwonjezera. (Akol. 3:5; Yak. 1:14, 15) Anthu ambiri amene amaonera zolaula amafika mpaka pochita zachiwerewere. w23.06 23 ¶10-11

Lachisanu, February 14

Koma udzaphwanya n’kuthetsa maufumu ena onsewa ndipo ndi ufumu wokhawu umene udzakhalepo mpaka kalekale.​—Dan. 2:44.

Ngakhale kuti nthawi zina mayiko ena angamalimbane ndi ulamuliro wa Britain ndi America, sadzaulowa m’malo. Tikudziwa zimenezi chifukwa “mwala” womwe ukuimira Ufumu wa Mulungu udzawononga mapazi a chifanizirochi, omwe akuimira ulamuliro wa Britain ndi America. (Dan. 2:34, 35, 44, 45) Kodi mumakhulupirira kuti ulosi wa Danieli wokhudza mapazi achitsulo chosakanizika ndi dongo ndi woona? Ngati ndi choncho, zimenezi zingakhudze mmene mumachitira zinthu pa moyo wanu. Simungamafunefune chuma m’dziko limene liwonongedwe posachedwapa. (Luka 12:16-21; 1 Yoh. 2:15-17) Kumvetsa ulosiwu kungakuthandizeninso kuti muziona kufunika kwa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. (Mat. 6:33; 28:18-20) Pambuyo pophunzira ulosiwu, mungachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene ndimasankha zimasonyeza kuti ndimakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu uthetsa maboma onse posachedwapa?’ w23.08 11 ¶13-14

Loweruka, February 15

Aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.​—Aroma 14:12.

Modzichepetsa, muzivomereza kuti simungathe kuchita zinthu zina panopa chifukwa cha msinkhu wanu, thanzi lanu komanso mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Mofanana ndi Barizilai, muzikhala wokonzeka kukana mautumiki ena ngati thanzi lanu silili bwino. (2 Sam. 19:35, 36) Mofanana ndi Mose, muzivomera kuthandizidwa komanso muzipatsa ena zochita ngati pakufunikira kutero. (Eks. 18:21, 22) Kudzichepetsa kumeneku kungakuthandizeni kuti musamakonze zochita zinthu zosatheka, zomwe zikhoza kungokutopetsani pampikisano wokalandira moyo. Sitiyeneranso kudziimba mlandu chifukwa chakuti ena sanasankhe bwino. Sitingasankhire ena zochita komanso si nthawi zonse pamene tingawateteze kuti asakumane ndi mavuto obwera chifukwa chosankha zinthu molakwika. Mwachitsanzo, mwana angasankhe kusiya kutumikira Yehova. Zimenezi zingachititse kuti makolo ake amve chisoni kwambiri. Komabe makolo akamadziimba mlandu chifukwa chakuti mwana wawo wasankha zinthu molakwika, amakhala akunyamula katundu wolemera. Ameneyu si katundu amene Yehova amafuna kuti iwo anyamule. w23.08 29 ¶11-12

Lamlungu, February 16

Samisoni anayamba kukonda mkazi wina . . . dzina lake Delila.​—Ower. 16:4.

Mofanana ndi ifeyo, nayenso Samisoni sanali wangwiro, choncho nthawi zina ankasankha zinthu molakwika. Pa nthawi ina, iye anasankha zinthu zomwe zinayambitsa mavuto aakulu. Atatumikira kwa kanthawi monga woweruza, Samisoni “anayamba kukonda mkazi wina wakuchigwa cha Soreki, dzina lake Delila.” M’mbuyomo iye ankafuna kukwatira mkazi wina wa Chifilisiti, koma Yehova ‘ndi amene anachititsa zimenezi,’ chifukwa “ankafunafuna mpata woti alange Afilisiti.” Kenako Samisoni anapita kukakhala kunyumba ya hule lina mumzinda wa Afilisiti wa Gaza. Pa nthawiyo, Yehova anapatsa mphamvu Samisoni kuti anyamule zitseko za geti la mzindawo, zomwe zinachititsa kuti ukhale wosavuta kuugonjetsa. (Ower. 14:1-4; 16:1-3) Koma nkhani ya Delila inali yosiyana chifukwa choti iye ayenera kuti anali Mwisiraeli. Delila analandira ndalama zambiri kuchokera kwa Afilisiti kuti apereke Samisoni. w23.09 5 ¶12-13

Lolemba, February 17

Kuzindikira kumachititsa kuti munthu abweze mkwiyo wake.​—Miy. 19:11.

Kuzindikira n’kothandiza kwambiri. Munthu wozindikira amadziletsa ena akamatsutsa zimene amakhulupirira. Mafunso ena tingawayerekezere ndi kholowa. Mbatata yeniyeniyo siioneka chifukwa imakhala munthaka. Mofanana ndi zimenezi, munthu angafunse funso kapena angafotokoze nkhawa inayake koma sitingazindikire cholinga chake. Choncho tisanayankhe tingachite bwino kuzindikira kuti nthawi zina sitingadziwe chimene chachititsa munthu kufunsa funsolo. (Miy. 16:23) Taganizirani mmene Gidiyoni anayankhira amuna a ku Efuraimu. Iwo anabwera kudzamufunsa mokwiya chifukwa chake sanawaitane kuti akawathandize pankhondo yolimbana ndi adani a Isiraeli. Kodi n’chifukwa chiyani iwo ankafuna kukangana naye? Kodi anachita zimenezi chifukwa chokwiya? Kaya iwo anachita zimenezi pa chifukwa chiti, Gidiyoni anachita zinthu mwanzeru, anamvetsa chifukwa chomwe chinawachititsa kuti akwiye ndiponso anawayankha mofatsa. Zotsatira zake n’zakuti iwo sanamenyane naye ndipo “mkwiyo wawo unaphwa.”—Ower. 8:1-3. w23.09 16 ¶8-9

Lachiwiri, February 18

Iye ankasangalala kwambiri ndi ine tsiku ndi tsiku.​—Miy. 8:30.

Yehova ndi Yesu amakondana kwambiri ngati mmene zimakhalira pakati pa bambo ndi mwana wake. Mosakayikira zinamupweteka kwambiri kuona Mwana wake akuchitiridwa nkhanza, kukanidwa komanso kuyesedwa. Kholo lililonse limene mwana wake anamwalira, limadziwa bwino chisoni chimene chimakhalapo chifukwa cha kuferedwako. Timakhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka, koma zimenezi sizithetsa ululu umene timamva munthu amene timamukonda akamwalira. Chitsanzochi chikutithandiza kumvetsa mmene Yehova anamvera poona Mwana wake akuvutika komanso kufa pa tsiku limenelo mu 33 C.E. (Mat. 3:17) Lisanafike tsiku la Chikumbutso, bwanji osakonza zoti muphunzire panokha kapena pa kulambira kwa pabanja nkhani zokhudza dipo? Komanso pa tsiku la Chikumbutso, musadzaiwale kuonera pulogalamu yapadera ya Kulambira Kwa M’mawa. Ngati titakonzekeretsa mtima wathu pa tsiku la Chikumbutso, tidzathandizanso ena kuti apindule ndi mwambowu.—Ezara 7:10. w24.01 11 ¶10-12

Lachitatu, February 19

Iye . . . adzakulimbitsani.​—1 Pet. 5:10.

Njira imodzi imene tingapezere mphamvu kuchokera kwa Yehova ndi kupemphera. Poyankha mapemphero athu, Yehova angatipatse “mphamvu yoposa yachibadwa.” (2 Akor. 4:7) Tingalimbikitsidwenso tikamawerenga Mawu ake komanso kuwaganizira. (Sal. 86:11) Paja Mawu a Yehova opezeka m’Baibulo ndi “amphamvu.” (Aheb. 4:12) Mukamapemphera kwa Yehova komanso kuwerenga Mawu ake, mudzapeza mphamvu zokuthandizani kupirira, kukhalabe osangalala komanso kukwanitsa kuchita utumiki wovuta. Taganizirani mmene Yehova anaperekera mphamvu kwa mneneri Yona. Yona anathawa utumiki wovuta umene Yehova anamupatsa. Chifukwa cha zimenezi, panyanja panachita mphepo yamkuntho ndipo iye komanso anthu omwe anakwera nawo chombo anatsala pang’ono kufa. Ataponyedwa m’nyanja, mosayembekezereka anapezeka ali m’mimba mwa chinsomba chachikulu, momwe munali mdima waukulu? Kodi Yona anatani kuti apeze mphamvu pamene anali yekhayekha m’mimba mwa chinsomba? Iye anapemphera.—Yona 2:1, 2, 7. w23.10 13 ¶4-6

Lachinayi, February 20

Mapeto a zinthu zonse ayandikira.​—1 Pet. 4:7.

Ngakhale kuti mtumwi Petulo ankalembera Akhristu a mu nthawi yake, Yehova anachititsa kuti makalatawo akhale mbali ya Baibulo. Choncho ifenso makalata amenewa angatithandize. (Aroma 15:4) Tikukhala pakati pa anthu omwe sakhulupirira maulosi a m’Baibulo. Otsutsa angamatinyoze chifukwa choti takhala tikuyembekezera mapeto kwa zaka zambiri. Anthu ena amanena kuti mapeto sadzafika. (2 Pet. 3:3, 4) Ngati titamva mwininyumba, mnzathu wakuntchito kapena wachibale akunena zimenezi, chikhulupiriro chathu chikhoza kufooka. Ndiyeno Petulo anafotokoza zimene zingatithandize pa nkhaniyi. Ena angamaone ngati Yehova akuchedwa kuwononga dziko loipali. Mawu a Petulo angatithandize kuti tikhale ndi maganizo oyenera ndipo amatikumbutsa kuti Yehova amaona nthawi mosiyana kwambiri ndi mmene anthufe timaionera. (2 Pet. 3:8, 9) Kwa Yehova, zaka 1, 000 zili ngati tsiku limodzi. Iye ndi woleza mtima ndipo sakufuna kuti wina aliyense adzawonongedwe. Komabe tsiku lake likadzafika, adzawononga dziko loipali. w23.09 26-27 ¶2-5

Lachisanu, February 21

Zinthu zimene tinamva tiyenera kuziganizira mozama kuposa nthawi zonse, kuti tisatengeke pang’onopang’ono n’kusiya chikhulupiriro.​—Aheb. 2:1.

N’chifukwa chiyani mtumwi Paulo analembera kalata Akhristu a Chiheberi omwe ankakhala ku Yudeya? N’kutheka kuti anachita zimenezi pa zifukwa ziwiri. Choyamba, kuti awalimbikitse. Ambiri mwa Akhristuwa anakulira m’chipembedzo cha Chiyuda, choncho atsogoleri a chipembedzo chawo chakale ayenera kuti ankawanyoza chifukwa chokhala Akhristu. N’chifukwa chiyani ankawanyoza? Chifukwa choti Akhristuwo analibe kachisi wochititsa chidwi woti azipitako kukalambira. Analibe guwa la nsembe looneka loti aziperekapo nsembe komanso analibe wansembe woti aziwatumikira. Zimenezi zikanatha kufooketsa ophunzira a Khristu ndiponso kuchititsa kuti chikhulupiriro chawo chiyambe kuchepa. (Aheb. 3:12, 14) Mwina ena akanatha kukopeka kuti abwererenso ku Chiyuda. Chachiwiri, Paulo ananena kuti Akhristu a Chiheberiwa sankachita khama kuti azimvetsa mfundo zatsopano kapena mfundo zozama za choonadi, zomwe ndi “chakudya chotafuna” chopezeka m’Mawu a Mulungu. (Aheb. 5:11-14) Zikuoneka kuti ena mwa Akhristuwo ankatsatirabe Chilamulo cha Mose. w23.10 24-25 ¶3-4

Loweruka, February 22

Akazi achitsikana uzilankhula nawo ngati achemwali ako, ndipo pochita zimenezi usakhale ndi maganizo alionse olakwika.—1 Tim. 5:2.

Alongo ena amasankha kuti asakwatiwe. (Mat. 19:10-12) Dziwani kuti Yehova ndi Yesu saona kuti Akhristu amene sali pabanja ndi osafunika. Alongo ambiri osakwatiwa amachita zambiri m’mipingo padziko lonse. Chikondi chawo, komanso mtima woganizira anthu ena umawalimbikitsa kuti akhale alongo kapena amayi auzimu a anthu ambiri. (Maliko 10:29, 30) Ena akuchita utumiki wa nthawi zonse. Akazi a Chikhristu amachita zambiri pa ntchito yolalikira padziko lonse. (Sal. 68:11) Kodi inuyo mungakonze zoti muyambe utumiki wa nthawi zonse? Mukhoza kuchita upainiya, kugwira nawo ntchito zomangamanga kapena kutumikira pa Beteli. Muzipempherera zolinga zimene muli nazo. Muzikambirana ndi anthu amene anakwaniritsa zolinga ngati zimenezo n’kuona zimene mungachite kuti nanunso muyenerere. Mukatero muzichita zinthu zimene zingakuthandizeni kukwaniritsa zolingazo. Mukayamba utumiki wa nthawi zonse, zidzakuthandizani kuti muchite zambiri potumikira Yehova. w23.12 22 ¶16-17

Lamlungu, February 23

Choyamba uthenga wabwino ukuyenera kulalikidwa.​—Maliko 13:10.

Pamene chisautso chachikulu chikuyandikira, n’zofunika kwambiri kuti tizimvera lamulo lakuti tizilalikira. Koma tikhoza kuvutika kuti tiziika maganizo athu onse pa ntchito yolalikira ngati anthu akutitsutsa kapena ngati tikukumana ndi mavuto a zachuma. Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba? Tisamakayikire kuti “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba” ali kumbali yathu. Iye adzatithandiza tikapitiriza kuika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba. Choncho palibe chifukwa choti tizichitira mantha. (Hag. 2:4) Yehova amafuna kuti tiziika maganizo athu onse pa ntchito yolalikira, yomwe ndi yopulumutsa moyo. Hagai analimbikitsa anthu a Mulungu kuti ayambirenso ntchito yomanga kachisi ngati kuti akuyala kumene maziko. Ndipo Yehova anawalonjeza kuti akatero ‘adzawadalitsa.’ (Hag. 2:18, 19) Ifenso Yehova adzatidalitsa tikamaika pamalo oyamba ntchito imene watipatsa. w23.11 16 ¶8; 17 ¶11

Lolemba, February 24

Onse ndi ochimwa.—Aroma 3:23.

M’kalata imene analembera Akhristu a ku Roma, mtumwi Paulo ananena kuti anthu onse ndi ochimwa. Ndiye kodi munthu angatani kuti Mulungu azisangalala naye n’kumamuona kuti ndi wolungama? Pofuna kuthandiza Akhristu kupeza yankho la funsoli, Paulo anafotokoza chitsanzo cha Abulahamu. Abulahamu ankakhala ku Kanani pamene Yehova anamutchula kuti anali wolungama. N’chifukwa chiyani iye ananena kuti Abulahamu anali wolungama? Kodi n’chifukwa chakuti iye ankatsatira malamulo omwe anali m’Chilamulo cha Mose? Ayi. (Aroma 4:13) Pajatu Yehova anapereka Chilamulo kwa Aisiraeli patatha zaka zoposa 400 kuchokera pamene ananena kuti Abulahamu anali wolungama. Ndiye kodi n’chiyani chinachititsa Yehova kuti azimuona monga wolungama? Chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu, Yehova ananena kuti Abulahamu anali wolungama chifukwa cha chikhulupiriro chake.—Aroma 4:2-4. w23.12 3 ¶4-5

Lachiwiri, February 25

Chitani chilichonse chimene mtima wanu ukufuna.—1 Mbiri 17:2.

“Usiku umenewo,” womwe mneneri Natani analankhula zomwe zili pamwambazi kwa Mfumu Davide, Yehova anauza mneneri Natani kuti Davide si amene adzamange kachisi. (1 Mbiri 17:3, 4, 11, 12) Kodi Davide anatani atamva uthengawu? Anayamba kusonkhanitsa chuma komanso zinthu zomwe mwana wake Solomo akanafunikira kuti amange kachisiyo. (1 Mbiri 29:1-5) Atangouza kumene Davide kuti si iye amene adzamange kachisi, Yehova anachita naye pangano. Iye analonjeza Davide kuti mmodzi mwa ana obadwira mumzere wake adzalamulira mpaka kalekale. (2 Sam. 7:16) Tangoganizani mmene Davide adzasangalalire m’dziko latsopano kudziwa kuti ali ndi moyo mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu, Mfumu yochokera m’banja lake. Nkhaniyi ikutithandiza kuona kuti ngakhale kuti sitingathe kuchita zonse zomwe tikufuna potumikira Yehova, Mulungu wathu angatisungire madalitso ena omwe sitimawayembekezera. w23.04 16 ¶8-10

Lachitatu, February 26

Yehova sadzataya anthu ake.​—Sal. 94:14.

Pali malemba ena m’Baibulo omwe amatilimbikitsa makamaka tikakhala ndi mantha. Mwachitsanzo, mukhoza kupeza mawu olimbikitsa m’mabuku a Yobu, Masalimo, Miyambo komanso m’mawu a Yesu opezeka m’chaputala 6 cha buku la Mateyu. Mukamapemphera kwa Yehova komanso kuwerenga Mawu ake, iye adzakutonthozani. Tisamakayikire kuti Yehova adzatithandiza pa nthawi imene takumana ndi mavuto aakulu. Sadzatisiya tokha. (Sal. 23:4) Yehova akulonjeza kuti adzatiteteza, kutithandiza kuti tisagwedezeke, kutilimbikitsa komanso kutitonthoza. Ponena za Yehova, lemba la Yesaya 26:3 limati: “Anthu amene amakudalirani ndi mtima wonse mudzawateteza. Mudzawapatsa mtendere wosatha, chifukwa amadalira inu.” Choncho muzidalira Yehova ndipo muzilola kuti akuthandizeni pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana. Mukatero mudzapeza mphamvu ngakhale pa nthawi imene mukukumana ndi mavuto aakulu. w24.01 25 ¶16-17

Lachinayi, February 27

Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana.—Yes. 54:17.

Ulosiwu ukukwaniritsidwa masiku ano. Mawu olimbikitsa otsatirawa, amafotokozanso za nthawi yathu ino: “Ana ako onse azidzaphunzitsidwa ndi Yehova, ndipo mtendere wa ana ako udzakhala wochuluka. Udzakhazikika molimba m’chilungamo. . . . Sudzaopa kanthu ndipo palibe chimene chidzakuchititse mantha, chifukwa palibe chilichonse choopsa chimene chidzakuyandikire.” (Yes. 54:13, 14) Ngakhale Satana, yemwe ndi “mulungu wa nthawi ino,” alibe mphamvu zoti n’kulepheretsa ntchito yophunzitsa ena, yomwe anthu a Yehova akugwira. (2 Akor. 4:4) Kulambira koona kunabwezeretsedwa ndipo sikudzasokonezedwanso, kudzakhalapo mpaka kalekale. Palibe chida chilichonse chomwe chidzapangidwe chimene chidzapambane. w24.02 4 ¶10

Lachisanu, February 28

Aliyense amene amakonda kwambiri bambo ake kapena mayi ake kuposa ine ndi wosayenera kuti akhale wophunzira wanga.​—Mat. 10:37.

Monga Akhristu, sitimaona mopepuka lonjezo lathu lodzipereka kwa Yehova. Zimenezi zingakhudze zosankha komanso zochita zathu pa nkhani zokhudza achibale. Timayesetsa kukwaniritsa mosamala udindo wathu wa m’Malemba wosamalira achibale athu, koma sitilola kuti zofuna za achibale athuwo zitilepheretse kuchita zimene Yehova amafuna. (Mat. 10:35, 36; 1 Tim. 5:8) Nthawi zina zimenezi zingachititse kuti tisankhe zinthu zomwe achibale athuwo sangasangalale nazo, koma zingasangalatse Yehova. Iye ndi amene anayambitsa banja ndipo amafuna kuti tizikhala ndi banja losangalala. (Aef. 3:14, 15) Ngati tikufuna kuti tizisangalaladi m’banja lathu tiyenera kumachita zimene Yehova amafuna. Musamakayikire kuti Yehova amasangalala ndi khama lomwe mumachita pomulambira komanso kusamalira anthu a m’banja lanu mwachikondi ndi mwaulemu.—Aroma 12:10. w24.02 18 ¶11, 13

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena