Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es25 tsamba 26-36
  • March

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • March
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
  • Timitu
  • Loweruka, March 1
  • Lamlungu, March 2
  • Lolemba, March 3
  • Lachiwiri, March 4
  • Lachitatu, March 5
  • Lachinayi, March 6
  • Lachisanu, March 7
  • Loweruka, March 8
  • Lamlungu, March 9
  • Lolemba, March 10
  • Lachiwiri, March 11
  • Lachitatu, March 12
  • Lachinayi, March 13
  • Lachisanu, March 14
  • Loweruka, March 15
  • Lamlungu, March 16
  • Lolemba, March 17
  • Lachiwiri, March 18
  • Lachitatu, March 19
  • Lachinayi, March 20
  • Lachisanu, March 21
  • Loweruka, March 22
  • Lamlungu, March 23
  • Lolemba, March 24
  • Lachiwiri, March 25
  • Lachitatu, March 26
  • Lachinayi, March 27
  • Lachisanu, March 28
  • Loweruka, March 29
  • Lamlungu, March 30
  • Lolemba, March 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
es25 tsamba 26-36

March

Loweruka, March 1

Chiyembekezocho sichitikhumudwitsa.​—Aroma 5:5.

Dziko latsopano silinafike. Komabe taganizirani zinthu zomwe mumaziona monga nyenyezi, mitengo, nyama komanso anthu anzanu. Palibe angakayikire kuti zinthuzi ndi zenizeni ngakhale kuti pa nthawi ina kunalibe. Zinthuzi zilipo chifukwa choti Yehova anazilenga. (Gen. 1:1, 26, 27) Mulungu wathu akufunanso kubweretsa dziko latsopano. Iye adzakwaniritsa cholinga chakechi. M’dziko latsopano anthu adzasangalala ndi moyo wosatha ali ndi thanzi labwino. Pa nthawi yake, Mulungu adzatipatsa dziko latsopano, ndipo mofanana ndi chilengedwe timaonachi, dzikolo lidzakhala lenileni. (Yes. 65:17; Chiv. 21:3, 4) Panopa muzichita chilichonse chomwe mungathe kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu. Muziyamikira kwambiri dipo. Muziganizira mphamvu za Yehova. Muzitanganidwa ndi zinthu zokhudza kulambira. Mukamachita zimenezo, mungakhale m’gulu la anthu amene “mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima, akulandira zinthu zimene Mulungu analonjeza monga cholowa chawo.”—Aheb. 6:11, 12. w23.04 31 ¶18-19

Lamlungu, March 2

Kodi sindinakuuze kuti ngati ungakhulupirire udzaona ulemerero wa Mulungu?​—Yoh. 11:40.

Yesu akuyang’ana kumwamba n’kupemphera anthu onse akuona. Iye akufuna kupereka ulemerero wonse kwa Yehova pa zonse zomwe zichitike. Kenako Yesu akufuula kuti: “Lazaro, tuluka!” (Yoh. 11:43) Ndipo Lazaro akutuluka m’mandamo. Apatu Yesu wachita zinthu zimene anthu ena amaona ngati n’zosatheka. Nkhaniyi, imatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka. N’chifukwa chiyani tikutero? Kumbukirani zimene Yesu anauza Marita kuti: “Mlongo wako adzauka.” (Yoh. 11:23) Mofanana ndi Atate wake, Yesu amafunitsitsa kuukitsa akufa ndipo ali ndi mphamvu zokwaniritsira lonjezo limeneli. Zimene anachita pogwetsa misozi zimasonyeza kuti iye amafunitsitsa kudzathetsa imfa komanso chisoni chimene imfa imabweretsa. Lazaro atatuluka m’mandamo, Yesu anasonyeza kuti ali ndi mphamvu zotha kuukitsa akufa. Takumbukiraninso zimene Yesu anakumbutsa Marita, zomwe zili mu lemba lalero. Tili ndi zifukwa zomveka zokhulupirira kuti lonjezo la Mulungu lakuti akufa adzauka lidzakwaniritsidwa. w23.04 11-12 ¶15-16

Lolemba, March 3

Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuitana, onse amene amamuitana m’choonadi.​—Sal. 145:18.

Pamene tikumvetsa bwino cholinga cha Mulungu, nthawi zina tingafunike kusintha zomwe tikupempherera. Tizikumbukira kuti Yehova ali ndi cholinga, ndipo adzachikwaniritsa pa nthawi yake. Cholinga chakechi chikuphatikizapo kuchotseratu mavuto onse omwe anthu amakumana nawo monga ngozi zam’chilengedwe, matenda komanso imfa. Yehova adzachita zimenezi pogwiritsa ntchito Ufumu wake. (Dan. 2:44; Chiv. 21:3, 4) Komabe panopa walola kuti Satana azilamulira dzikoli. (Yoh. 12:31; Chiv. 12:9) Ngati Yehova atati azithetsa mavuto a anthu panopa, mwa njira inayake zingaoneke ngati Satana akulamulira bwino. Komabe pamene tikuyembekezera kuti Yehova akwaniritse malonjezo ake, sizikutanthauza kuti tikakumana ndi mavuto satithandiza. Yehova amatithandiza. w23.05 8 ¶4; 9-10 ¶7-8

Lachiwiri, March 4

Mudziwe mmene mungayankhire munthu aliyense.​—Akol. 4:6.

Kodi tingathandize bwanji ena kuti adzapindule ndi mwambo wa Chikumbutso? Chinthu choyamba ndi kuwaitanira kumwambowu. Kuwonjezera pa anthu omwe timawalalikira nthawi zonse, tingalembenso mayina a anthu amene tikufuna kuwaitana. Anthuwa angaphatikizepo achibale athu, anzathu a kuntchito, a kusukulu ndi ena. Ngakhale zitakhala kuti tilibe timapepala tokwanira toitanira anthu ku Chikumbutso, tingathe kuwatumizira linki ya timapepala tapazipangizo zamakono. Mukhoza kudabwa ndi kuchuluka kwa anthu omwe angabwere. (Mlal. 11:6) Muzikumbukira kuti anthu amene mungawaitanire ku Chikumbutso angakhale ndi mafunso makamaka ngati n’koyamba kupezeka pamisonkhano yathu. Tingachite bwino kudziwiratu mafunso omwe angatifunse n’kukonzekera mmene tingawayankhire. Ngakhale pambuyo pa Chikumbutso, anthu achidwi omwe anabwera angakhale ndi mafunso ena. Tikufuna kuchita zomwe tingathe kuti tithandize anthu a “maganizo abwino” kupindula ndi mwambowu Chikumbutso chisanachitike, chikamadzachitika komanso pambuyo pake.—Mac. 13:48. w24.01 12 ¶13, 15; 13 ¶16

Lachitatu, March 5

Muli ngati nkhungu imene imangooneka kwa kanthawi kochepa kenako nʼkuzimiririka.​—Yak. 4:14.

Baibulo limatchula nkhani za anthu 8 omwe anaukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo padzikoli. Bwanji osaphunzira mosamala nkhani zimenezi? Mukamawerenga, muziona zimene mukuphunzirapo. Muziganizira mmene nkhani iliyonse ikusonyezera kuti Mulungu ndi wofunitsitsa komanso ali ndi mphamvu zoukitsa anthu. Koposa zonse muziganizira za kuukitsidwa kwa Yesu komwe ndi kofunika kwambiri. Kumbukirani kuti anthu ambiri anaona ndi maso Yesu ataukitsidwa ndipo zimenezi zimalimbitsa chikhulupiriro chathu. (1 Akor. 15:3-6, 20-22) Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa cha lonjezo lake lakuti akufa adzaukitsidwa. Sitingakayikire kuti lonjezoli lidzakwaniritsidwa chifukwa Yehova ndi wofunitsitsa ndiponso ali ndi mphamvu zochitira zimenezi. Tiyeni tikhale otsimikiza kuti tipitiriza kukhulupirira kwambiri chiyembekezo chamtengo wapatalichi. Tikamachita zimenezi tidzakhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu yemwe tingati akulonjeza wina aliyense wa ife kuti: ‘Okondedwa anu adzauka.’—Yoh. 11:23. w23.04 8 ¶2; 12 ¶17; 13 ¶20

Lachinayi, March 6

Uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.​—Mika 6:8.

Kudziwa malire athu n’kogwirizana ndi kudzichepetsa. Timasonyeza kuti tikuzindikira malire athu podziona moyenera n’kumadziwa kuti pali zina zomwe sitingakwanitse. Timasonyeza kuti ndife odzichepetsa tikamalemekeza ena komanso kuwaona kukhala otiposa. (Afil. 2:3) Kawirikawiri, munthu amene amazindikira zomwe sangakwanitse amakhalanso wodzichepetsa. Gidiyoni ankazindikira malire ake ochitira zinthu komanso anali wodzichepetsa. Pamene mngelo wa Yehova anauza Gidiyoni kuti iye ndi amene wasankhidwa kuti akalanditse Aisiraeli m’manja mwa Amidiyani, omwe anali amphamvu, munthu wodzichepetsayu anayankha kuti: “Banja lathu ndi laling’ono kwambiri m’fuko lonse la Manase, ndipo m’nyumba ya bambo anga, wamng’ono kwambiri ndine.” (Ower. 6:15) Iye ankaona kuti sangakwanitse ntchito yomwe anapatsidwayi, koma Yehova ankaona kuti angakwanitse. Mothandizidwa ndi Yehova, Gidiyoni anakwanitsa utumiki womwe anapatsidwa. Akulu amayesetsa kuti azizindikira malire awo komanso kukhala odzichepetsa pa zinthu zonse. (Mac. 20:18, 19) Iwo samadzitamandira chifukwa cha zimene akwanitsa kuchita, komanso samadziona kuti ndi achabechabe chifukwa cha zimene amalakwitsa. w23.06 3 ¶4-5

Lachisanu, March 7

Mbadwa ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako.​—Gen. 3:15.

Kuphwanya mutu wa Satana, kudzachitika zaka zoposa 1,000 kutsogoloku. (Chiv. 20:7-10) Koma zimenezi zisanachitike, Baibulo linaneneratu zinthu zapadera zotsatirazi. Choyamba, mayiko adzalengeza za “bata ndi mtendere.” (1 Ates. 5:2, 3) “Nthawi yomweyo” chisautso chachikulu chidzayamba pomwe mayiko adzaukire zipembedzo zonse zabodza. (Chiv. 17:16) Pambuyo pake, Yesu adzaweruza anthu onse ndipo adzalekanitsa nkhosa ndi mbuzi. (Mat. 25:31-33, 46) Koma sikuti Satana adzangokhala. Chifukwa chokwiya, iye adzalimbikitsa mgwirizano wa mayiko, womwe Baibulo limautchula kuti Gogi wa kudziko la Magogi, kuti aukire anthu a Yehova. (Ezek. 38:2, 10, 11) Pa nthawi ina chisautso chachikulu chitayamba, odzozedwa omwe adzakhale ali padzikoli adzatengedwa kuti akakhale limodzi ndi Khristu ndi gulu lankhondo la kumwamba kuti adzamenye nkhondo ya Aramagedo, ndipo chimenechi chidzakhala chimake cha chisautso chachikulu. (Mat. 24:31; Chiv. 16:14, 16) Kenako Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu udzayamba kulamulira dzikoli.—Chiv. 20:6. w23.10 20-21 ¶9-10

Loweruka, March 8

Mtumiki wanu ndakhala ndikuopa Yehova kuyambira ndili mwana.—1 Maf. 18:12.

Masiku ano atumiki ambiri a Yehova akukhala m’mayiko amene ntchito yathu ndi yoletsedwa. Iwo amapereka ulemu woyenerera kwa akuluakulu a boma, koma mofanana ndi Obadiya, amapereka ulemu waukulu kwambiri kwa Yehova ndipo sasiya kumulambira. (Mat. 22:21) Iwo amasonyeza kuti amaopa Mulungu pomumvera m’malo moopa anthu. (Mac. 5:29) Amachita zimenezi popitirizabe kulalikira uthenga wabwino komanso kuchita misonkhano mobisa. (Mat. 10:16, 28) Iwo amaonetsetsa kuti abale ndi alongo awo akupeza chakudya chauzimu chomwe akufunikira. Taganizirani chitsanzo cha Henri, yemwe amakhala ku Africa m’dziko lina lomwe ntchito yathu inali yoletsedwa kwa kanthawi. Pa nthawiyo, iye anadzipereka kuti azikapereka chakudya chauzimu kwa a Mboni anzake. Henri analemba kuti: “Mwachibadwa ndine wamanyazi. . . . Yehova anandithandiza kuti ndikhale wolimba mtima.” Inunso mungakhale wolimba mtima ngati Henri. Zimenezi zingatheke ngati mumaopa Mulungu moyenera. w23.06 16 ¶9, 11

Lamlungu, March 9

Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi.​—Aroma 5:12.

Adamu ndi Hava atachimwa zinkaoneka ngati Satana walepheretsa cholinga cha Mulungu choti padzikoli pakhale anthu angwiro komanso omvera. Satana ayenera kuti ankaganiza kuti Yehova sangakwaniritsenso cholinga chake. Mwina ankaona kuti Mulungu apha Adamu ndi Hava n’kulenganso banja lina kuti akwaniritse cholinga chake chokhudza anthu. Koma ngati Mulungu akanachita zimenezi, ndiye kuti Mdyerekezi akananena kuti Mulunguyo ndi wabodza. Chifukwa chiyani? Chifukwa mogwirizana ndi Genesis 1:28, Yehova anali atauza Adamu ndi Hava kuti ana awo adzadzaza dziko lapansi. Mwina Satana ankaganiza kuti Yehova adzalola kuti Adamu ndi Hava akhale ndi ana omwe sizidzatheka kuti akhale angwiro. (Mlal. 7:20; Aroma 3:23) Apa ndiye kuti Mdyerekezi akananena kuti Yehova ndi wolephera. Chifukwa chiyani? Chifukwa njira imeneyi sikanakwaniritsa cholinga cha Mulungu choti padzikoli pakhale ana a Adamu ndi Hava angwiro komanso omvera. w23.11 6 ¶15-16

Lolemba, March 10

Musapitirire zinthu zolembedwa.—1 Akor. 4:6.

Yehova amatipatsa malangizo omveka bwino kudzera m’Mawu ake komanso m’gulu lake. Tilibe zifukwa zomveka zowonjezerera mfundo zathu pa malangizo amene amatipatsa. (Miy. 3:5-7) Choncho sitimapitirira zimene zinalembedwa m’Baibulo kapenanso kuikira malamulo Akhristu anzathu pa nkhani zimene aliyense ayenera kusankha yekha. Satana amagwiritsa ntchito “chinyengo chopanda pake” ndi “mfundo zimene anthu am’dzikoli amayendera” pofuna kusocheretsa ndi kugawanitsa anthu. (Akol. 2:8) M’nthawi ya atumwi, zimenezi zinkaphatikizapo nzeru za anthu, miyambo ya Chiyuda yosemphana ndi Malemba komanso chiphunzitso chakuti Akhristu azitsatira Chilamulo cha Mose. Izi zinali zachinyengo chifukwa zinkachititsa kuti anthu asamaganizire za Mwiniwake wa nzeru yemwe ndi Yehova. Masiku ano, Satana amagwiritsa ntchito mawailesi, TV kapenanso malo ochezera a pa intaneti pofuna kufalitsa nkhani zabodza zomwe atsogoleri andale amalimbikitsa. w23.07 16 ¶11-12

Lachiwiri, March 11

Ntchito zanu ndi zazikulu kwambiri inu Yehova. Maganizo anu ndi ozama kwambiri.​—Sal. 92:5.

Yehova anathetsa nkhani imene inayambitsidwa ndi Satana komanso anthu oyambirirawa m’njira yoti Satanayo analibenso mawu. Polola Adamu ndi Hava kuti akhale ndi ana, Yehova anasonyeza kuti amanena zoona osati zabodza. Anasonyezanso kuti akanena kuti achita chinachake, palibe chimene chingamulepheretse. Yehova anaonetsetsa kuti cholinga chake chikwaniritsidwe popereka “mbadwa” yoti ipulumutse ana omvera a Adamu ndi Hava. (Gen. 3:15; 22:18) Satana ayenera kuti anagoma ndi zimene Yehova anakonza zokhudza dipo. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa zinasonyeza kuti Yehova ali ndi chikondi chopanda dyera. (Mat. 20:28; Yoh. 3:16) Satana alibe khalidwe limeneli chifukwa iye ndi wadyera. Ndiye kodi ndi zinthu ziti zimene zidzachitike chifukwa cha dipo? Kumapeto kwa Ulamuliro wa Khristu wa Zaka 1,000, ana angwiro komanso omvera a Adamu ndi Hava adzakhala m’Paradaiso padziko lapansi mogwirizana ndi cholinga cha Yehova choyambirira. w23.11 6 ¶17

Lachitatu, March 12

Mulungu adzaweruza.​—Aheb. 13:4.

Timamvera lamulo la Yehova lokhudza kupatulika kwa moyo ndi magazi. Chifukwa chiyani? Yehova amanena kuti magazi amaimira moyo, umene ndi mphatso yamtengo wapatali imene anatipatsa. (Lev. 17:14) Pa nthawi yoyamba imene Yehova analola kuti anthu azidya nyama, anawalamula kuti asamadye magazi. (Gen. 9:4) Iye anabwerezanso lamuloli pamene anapereka Chilamulo cha Mose kwa Aisiraeli. (Lev. 17:10) Ndipo anatsogoleranso bungwe lolamulira la m’nthawi ya atumwi kuti lipereke lamulo lakuti Akhristu onse ‘apitirize kupewa . . . magazi.’ (Mac. 15:28, 29) Timakhala osasunthika pomvera lamulo limeneli tikamasankha thandizo lamankhwala loti tilandire. Timatsatiranso ndi mtima wonse mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. Pogwiritsa ntchito mawu a fanizo, mtumwi Paulo anatilangiza kuti ‘tichititse ziwalo za thupi lathu kukhala zakufa,’ kumene ndi kuchita zonse zomwe tingathe kuti tisamalakelake zinthu zoipa. Timapewa kuyang’ana kapena kuchita zinthu zomwe zingachititse kuti tichite chiwerewere.​—Akol. 3:5; Yobu 31:1. w23.07 15 ¶5-6

Lachinayi, March 13

Pamapeto pake, Samisoni anamuululira zonse.​—Ower. 16:17.

Kodi Samisoni ankamukhulupirira kwambiri Delila chifukwa choti ankamukonda, moti sankadziwa zomwe ankafuna kuchita? Kaya zinthu zinali bwanji, mobwerezabwereza Delila anakakamiza Samisoni kuti amuululire kumene kunkachokera mphamvu zake, ndipo pamapeto pake Samisoni anamuuza. N’zomvetsa chisoni kuti zimene Samisoni anachita zinapangitsa kuti mphamvu zake zithe komanso Yehova asiye kumukonda kwa kanthawi. (Ower. 16:16-20) Samisoni anakumana ndi mavuto aakulu chifukwa chokhulupirira Delila m’malo modalira Yehova. Afilisiti anamugwira ndipo anamuboola maso. Iye anaikidwa m’ndende ku Gaza ndipo anakhala kapolo wopera tirigu. Kenako Afilisiti anamuchititsa manyazi pamene anasonkhana kuti achite phwando. Iwo anapereka nsembe kwa mulungu wawo Dagoni, ngati kuti iye ndi amene anapereka Samisoni m’manja mwawo. Afilisitiwo anatulutsa Samisoni m’ndende n’kubwera naye paphwandolo kuti ‘adzawasangalatse.’—Ower. 16:21-25. w23.09 5-6 ¶13-14

Lachisanu, March 14

Muziganizira zimene anthu onse amaziona kuti ndi zabwino.​—Aroma 12:17.

Mwina mnzathu wakuntchito kapena kusukulu angatifunse chifukwa chake timatsatira mfundo za m’Baibulo pa nkhani inayake. Tingachite bwino kumufotokozera zimene timakhulupirira koma m’njira yosonyeza kuti tikulemekeza maganizo ake. (1 Pet. 3:15) M’malo moganiza kuti watifunsa n’cholinga choti akangane nafe kapena kutitsutsa, tiziona kuti funso lakelo litithandiza kudziwa zimene zikumudetsa nkhawa. Kaya munthu wafunsa funso pa zifukwa ziti, tiyenera kumuyankha mofatsa komanso mokoma mtima. Yankho lathu likhoza kumuthandiza kuti asinthe maganizo ake. Ngati mnzathu wakuntchito watifunsa chifukwa chake sitikondwerera tsiku lobadwa, tingadzifunse kuti: Kodi n’kutheka kuti iye akufuna kudziwa ngati timaloledwa kukhala ndi nthawi yosangalala? Kapena akuona kuti tichititsa kuti anthu asamagwirizane pakampanipo? Tingayambe ndi kumuyamikira chifukwa choganizira anzake ogwira nawo ntchito ndipo kenako tingamutsimikizire kuti ifenso tikakhala kuntchito timafuna kuti tizisangalala. Izi zingachititse kuti mukambirane bwino zimene Baibulo limanena pa nkhani yokondwerera tsiku lobadwa. w23.09 17 ¶10-11

Loweruka, March 15

Chenjerani kuti anthu ophwanya malamulowo asakusocheretseni ndi zochita zawo zoipa nʼkuchititsa kuti mugwe chifukwa cholephera kukhala olimba.​—2 Pet. 3:17.

Tilitu ndi mwayi wogwiritsa ntchito nthawi yotsalayi kuchitira umboni kwa anthu a mitundu yonse. Mtumwi Petulo anatilimbikitsa kuti ‘tizikumbukira nthawi zonse’ tsiku la Yehova. (2 Pet. 3:11, 12) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Ngati n’zotheka, tsiku lililonse tiziganizira madalitso omwe tidzapeze m’dziko latsopano. Muziyerekezera mukupuma kampweya kabwino, mukudya zakudya zopatsa thanzi, mukulandira okondedwa anu omwe aukitsidwa komanso mukuphunzitsa anthu akale mmene maulosi a m’Baibulo anakwaniritsidwira. Kuganizira zimenezi kungakuthandizeni kuti muziyembekezera tsiku la Yehova komanso musamakayikire zoti tikukhala m’nthawi ya mapeto. ‘Kudziwiratu’ zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo, kungatithandizenso kuti ‘tisasocheretsedwe’ ndi aphunzitsi abodza. w23.09 27 ¶5-6

Lamlungu, March 16

Muzimvera makolo anu mogwirizana ndi zimene Ambuye amafuna, chifukwa kuchita zimenezi n’koyenera.—Aef. 6:1.

Nthawi zambiri achinyamata amakhala ndi anzawo omwe ndi “osamvera makolo.” (2 Tim. 3:1, 2) N’chifukwa chiyani achinyamata ambiri samamvera? Ena amaona kuti makolo awo ndi achinyengo. Anawo amauzidwa kuti azichita zimene makolowo sachita. Ena amaona kuti malangizo a makolo awo ndi achikale, osathandiza kapena opanikiza. Ngati ndinu wachinyamata, kodi inunso mumaona choncho? Ambiri amavutika kutsatira lamulo la Yehova lomwe likupeza mulemba laleroli. Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muzimvera? Mungathe kuphunzira kumvera kuchokera kwa Yesu, yemwe ndi chitsanzo chabwino. (1 Pet. 2:21-24) Iye anali wangwiro, koma makolo ake sanali angwiro. Yesu ankalemekeza makolo ake ngakhale kuti nthawi zina iwo ankalakwitsa zinthu komanso sankamumvetsa.—Eks. 20:12. w23.10 7 ¶4-5

Lolemba, March 17

Malamulo oyambawo akuchotsedwa chifukwa ndi operewera komanso osathandiza.​—Aheb. 7:18.

Mtumwi Paulo anafotokoza kuti nsembe zomwe zinkaperekedwa mogwirizana ndi Chilamulo sizikanachotseratu machimo. Chifukwa cha zimenezi, Chilamulo ‘chinachotsedwa.’ Choncho Paulo anayamba kuwaphunzitsa mfundo zozama za choonadi. Iye anakumbutsa Akhristu anzakewo za “chiyembekezo cha zinthu zabwino” kudzera mu nsembe ya Yesu, chomwe chikanawathandiza “kuyandikira Mulungu.” (Aheb. 7:19) Paulo anafotokozera abale ake a Chiheberi kuti njira imene Akhristu ankaitsatira polambira inali yapamwamba kwambiri kusiyana ndi yomwe ankatsatira m’mbuyomo. Zimene Ayuda ankachita polambira zinali chabe “mthunzi wa zimene zinali kubwera, koma zenizeni zake zinakwaniritsidwa ndi Khristu.” (Akol. 2:17) Mthunzi wa chinthu umangosonyeza mmene chinthu chenicheni chimaonekera. Choncho zimene Ayuda akale ankachita polambira zinali mthunzi wa zinthu zenizeni zimene zinkabwera. Tiyenera kumvetsa njira imene Yehova wapereka yotithandiza kuti machimo athu akhululukidwe kuti tizimulambira m’njira yovomerezeka. w23.10 25 ¶4-5

Lachiwiri, March 18

Mu nthawi yamapeto mfumu yakum’mwera idzayamba kukankhana ndi mfumu yakumpoto ndipo mfumu yakumpotoyo idzabwera mwamphamvu kudzamenyana nayo.​—Dan. 11:40.

Chaputala 11 cha buku la Danieli chimafotokoza za mafumu awiri kapena kuti maulamuliro, omwe amalimbana kuti azilamulira dziko lonse. Tikayerekezera ulosi umenewu ndi maulosi ena otchulidwa m’Baibulo, timazindikira kuti “mfumu yakumpoto” ndi dziko la Russia ndi mayiko omwe amagwirizana nalo komanso “mfumu yakum’mwera” ndi ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America. Anthu a Mulungu omwe amakhala m’madera olamuliridwa ndi “mfumu yakumpoto” akuzunzidwa ndi mfumuyi. A Mboni ena akhala akumenyedwa komanso kuikidwa m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo. M’malo moti zochita za “mfumu yakumpoto” zizifooketsa abale athu, zimangolimbitsa chikhulupiriro chawo. Tikutero chifukwa chakuti abale athu amadziwa kuti kuzunzidwa kwa anthu a Mulungu kukukwaniritsa ulosi wa Danieli. (Dan. 11:41) Kudziwa zimenezi kumatithandiza kuti tikhale ndi chiyembekezo ndiponso tipitirizebe kukhala okhulupirika. w23.08 11 ¶15-16

Lachitatu, March 19

Amene akukukhudzani, akukhudza mwana wa diso langa.​—Zek. 2:8.

Popeza kuti Yehova amatikonda amamvetsa mmene timamvera ndipo amakhala wokonzeka kutiteteza. Tikamamva kupweteka nayenso amamva kupweteka. Choncho mpake kuti tingapemphere kwa iye kuti: “Nditetezeni ngati mwana wa diso lanu.” (Salimo 17:8) Diso ndi lamtengo wapatali komanso chimodzi mwa ziwalo zofunika kutetezedwa kwambiri. Choncho Yehova akamatiyerekezera ndi mwana wa diso lake, zimakhala ngati akunena kuti, ‘Aliyense wofuna kukuvulazani akuvulaza chinthu chamtengo wapatali kwa ine.’ Yehova amafuna tizidziwa kuti amakonda munthu aliyense payekha. Koma amadziwa kuti chifukwa cha zimene zinatichitikirapo m’mbuyomu, mwina tingamakayikire ngati amatikonda. Mwinanso tikukumana ndi mavuto amene angatichititse kukayikira kuti Yehova amatikonda. Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisamakayikire zimenezi? Chimene chingatithandize ndi kuphunzira mmene amasonyezera chikondi kwa Yesu, odzozedwa komanso kwa tonsefe. w24.01 27 ¶6-7

Lachinayi, March 20

Dzanja la Mulungu wathu linkatithandiza pa ulendowu moti anatipulumutsa kwa adani.​—Ezara 8:31.

Ezara anali ataona Yehova akuthandiza anthu ake pa nthawi yamavuto. Mu 484 B.C.E., iye ayenera kuti ankakhala ku Babulo pamene Mfumu Ahasiwero inalamula kuti Ayuda onse mu ufumu wa Perisiya aphedwe. (Esitere 3:7, 13-15) Pa nthawiyo moyo wa Ezara unali pangozi. Zitatero, Ayuda “m’zigawo zonse” anayamba kulira komanso kusala kudya popempha Yehova kuti awatsogolere. (Esitere 4:3) Kodi mukuganiza kuti Ezara ndi Ayuda anzake anamva bwanji zinthu zitasintha n’kuwaipira anthu omwe anakonza chiwembucho? (Esitere 9:1, 2) Zimene Iye anaona pa nthawiyo zinamuthandiza kukonzekera mavuto omwe anakumana nawo m’tsogolo, ndipo ziyenera kuti zinamuthandiza kukhulupirira kwambiri kuti Yehova amateteza anthu ake. w23.11 17 ¶12-13

Lachisanu, March 21

Mulungu amamuona kuti ndi wolungama ngakhale kuti zimene wachita sizikugwirizana kwenikweni ndi Chilamulo.​—Aroma 4:6.

Mtumwi Paulo ankanena za zimene anthu ankachita potsatira Chilamulo cha Mose, chomwe Mulungu anapatsa Aisiraeli paphiri la Sinai. (Aroma 3:21, 28) Zikuoneka kuti m’nthawi ya Paulo, Akhristu ena a Chiyuda zinkawavuta kuvomereza kuti Chilamulo cha Mose komanso zimene anthu ankafunika kuchita pochitsatira zinali zitasiya kugwira ntchito. Choncho Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo cha Abulahamu pofuna kusonyeza kuti kukhala olungama sikunkadalira zimene munthu angachite potsatira Chilamulo, koma chofunika chinali chikhulupiriro. Zimenezitu ndi zolimbikitsa, chifukwa zikutithandiza kuona kuti n’zotheka kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu n’kumachita zomusangalatsa. Zikutanthauzanso kuti n’zotheka kumakhulupirira Mulungu ndi Khristu, zomwe zingachititse kuti azisangalala nafe. Koma ntchito zimene Yakobo anatchula muchaputala 2, si zimene munthu amachita potsatira Chilamulo zomwe Paulo anafotokoza. Yakobo ankanena za ntchito zimene Akhristu amachita tsiku lililonse. (Yak. 2:24) Ntchito zimenezo ndi zimene zimasonyeza kuti Mkhristu ali ndi chikhulupiriro chenicheni kapena ayi. w23.12 3 ¶8; 4-5 ¶10-11

Loweruka, March 22

Mwamuna ndi mutu wa mkazi wake.—Aef. 5:23.

Alongo amene akufuna kukhala pabanja ayenera kukhala osamala kwambiri posankha munthu amene akufuna kukwatirana naye. Kumbukirani kuti mwamuna amene mudzakwatiwe naye ndi amene adzakhale mutu wanu. (Aroma 7:2; Aef. 5:33) Choncho muzidzifunsa kuti: ‘Kodi iye ndi Mkhristu wolimba mwauzimu? Kodi amaika zinthu zauzimu pamalo oyamba? Kodi amasankha zochita mwanzeru? Kodi amavomereza akalakwitsa zinazake? Kodi amalemekeza akazi? Kodi angandithandize kulimbitsa ubwenzi wanga ndi Mulungu, kundipezera zofunika pa moyo komanso kukhala mnzanga wapamtima? Komabe dziwani kuti ngati mukufuna kupeza mwamuna wabwino inuyonso muyenera kukhala mkazi wabwino. Mkazi wabwino amakhala “womuthandiza” mwamuna wake ndiponso “mnzake womuyenerera.” (Gen. 2:18) Komanso popeza amakonda Yehova amayesetsa kuti mbiri ya mwamuna wake ikhale yabwino. (Miy. 31:11, 12; 1 Tim. 3:11) Kuti mukonzekere udindo wanu wam’tsogolowu, muyenera kukonda kwambiri Yehova komanso kumathandiza anthu ena kunyumba kwanu ndiponso mumpingo. w23.12 22-23 ¶18-19

Lamlungu, March 23

Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu.​—Yak. 1:5.

Yehova amalonjeza kuti azitipatsa nzeru zomwe timafunikira kuti tizisankha bwino pa nkhani zosiyanasiyana. Timafunika nzeru za Mulungu makamaka tikamasankha zochita pa nkhani zomwe zidzatikhudze kwa moyo wathu wonse. Iye amatipatsanso mphamvu kuti tipirire. Monga mmene anachitira ndi Paulo, Yehova angatipatsenso mphamvu kuti tipirire mayesero amene tikukumana nawo. (Afil. 4:13) Njira imodzi yomwe amagwiritsa ntchito ndi kudzera mwa abale ndi alongo athu. Pa usiku wake womaliza asanapereke moyo wake monga nsembe, Yesu anapemphera mochokera pansi pa mtima. Iye anachonderera Yehova kuti asalole kuti anthu ena azimuona ngati wonyoza Mulungu. Koma m’malo mochita zomwe anapemphazo, Yehova anathandiza Yesu pomutumizira mmodzi mwa angelo ake kuti akamulimbikitse. (Luka 22:42, 43) Ifenso Yehova angatithandize kudzera mwa m’bale kapena mlongo yemwe watiimbira foni kapena kutiyendera kuti atilimbikitse. Tonsefe tikhoza kupeza mipata yoti tizilankhula “mawu abwino” kwa Akhristu anzathu.—Miy. 12:25. w23.05 10-11 ¶9-11

Lolemba, March 24

Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana.​—1 Ates. 5:11.

N’kutheka kuti anthu amene anasiya kusonkhana, omwe apezeka pa Chikumbutso ankaopa kuti mwina sadzalandiridwa bwino. Choncho muzipewa kuwafunsa mafunso omwe angawachititse manyazi kapena kulankhula zinthu zomwe zingawapweteke. Abale ndi alongowa ndi Akhristu anzathu ndipo tikusangalala kuti tayambiranso kusonkhana nawo. (Sal. 119:176; Mac. 20:35) Timayamikira kuti Yesu anakonza zoti chaka ndi chaka tizichita mwambo wokumbukira imfa yake. Mwambowu umatithandiza ifeyo komanso anthu ena m’njira zambiri. (Yes. 48:17, 18) Timayamba kukonda kwambiri Yehova ndi Yesu. Timasonyeza kuti timayamikira kwambiri zimene atichitira. Timayamba kugwirizana kwambiri ndi Akhristu anzathu. Komanso tingathandize ena kudziwa kuti angathe kudzasangalala ndi madalitso amene amatheka chifukwa cha dipo. Tiyeni tichite zonse zomwe tingathe kuti tikonzekere kudzapezeka pa tsiku la Chikumbutso, lomwe ndi lofunika kwambiri pa chaka. w24.01 14 ¶18-19

Lachiwiri, March 25

Ine Yehova ndine . . . amene ndimakutsogolerani.​—Yes. 48:17.

Kodi Yehova amatitsogolera bwanji? Njira yaikulu ndi kudzera m’Mawu ake, Baibulo. Komanso iye amagwiritsa ntchito anthu. Mwachitsanzo, amagwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” potipatsa chakudya chauzimu chomwe chimatithandiza kuti tizisankha zochita mwanzeru. (Mat. 24:45) Yehova amagwiritsanso ntchito amuna ena oyenerera kuti azititsogolera. Oyang’anira madera komanso akulu, amatilimbikitsa ndiponso kutipatsa malangizo omwe amatithandiza kupirira m’nthawi yovutayi. Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa chotipatsa malangizo odalirika m’masiku otsiriza ano. Malangizowa amatithandiza kuti tizichita zimene iye amasangalala nazo komanso tipitirize kuyenda panjira ya kumoyo. Komabe, nthawi zina zingamativute kutsatira malangizo a Yehova, makamaka akamaperekedwa ndi anthu omwe si angwiro. Pa nthawi ngati imeneyi, tingafunike kukhulupirira kwambiri kuti Yehova ndi amene akutsogolera anthu ake ndiponso kuti kutsatira malangizowo kungachititse kuti tipeze madalitso. w24.02 20 ¶2-3

Lachitatu, March 26

Tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tizisonyezana chikondi chenicheni m’zochita zathu.​—1 Yoh. 3:18.

Chinthu china chomwe chingatithandize kuti tipitirize kukonda kwambiri Mulungu ndi kuphunzira Mawu ake mwakhama. Mukamawerenga Baibulo, muziyesa kuona mmene zomwe mwawerengazo zikukuthandizirani kudziwa zokhudza Yehova. Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi nkhaniyi ikusonyeza bwanji kuti Yehova amandikonda? Kodi ikundithandiza kudziwa zifukwa ziti zondichititsa kukonda Yehova?’ Kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima nthawi zonse kungatithandizenso kuti tizimukonda kwambiri. (Sal. 25:4, 5) Tikamatero, iye amayankha mapemphero athu. (1 Yoh. 3:21, 22) Tiyenera kumakondanso anthu ena. Patapita zaka zingapo kuchokera pamene anakhala Mkhristu, mtumwi Paulo anakumana ndi wachinyamata wina dzina lake Timoteyo. Wachinyamatayu ankakonda Yehova komanso anthu. Paulo anauza Akhristu a ku Filipi kuti: “Ndilibe wina amene ali ndi mtima ngati [Timoteyo], amene angasamaliredi moona mtima zosowa zanu.” (Afil. 2:20) N’zoonekeratu kuti iye ankachita chidwi ndi mmene Timoteyo ankakondera abale ndi alongo. Mosakayikira, abale ndi alongo ankayembekezera mwachidwi maulendo a Timoteyo okachezera mipingo yawo.—1 Akor. 4:17. w23.07 9 ¶7-10

Lachinayi, March 27

Sindidzakusiyani kapena kukutayani.—Aheb. 13:5.

Mose anamwalira Aisiraeli asanalowe m’Dziko Lolonjezedwa. Ndiye kodi Yehova anasiya kuthandiza anthu ake munthu wokhulupirikayu atamwalira? Ayi. Yehova ankawasamalira akapitiriza kukhala okhulupirika. Mose asanamwalire, Yehova anamuuza kuti asankhe Yoswa kuti adzatsogolere anthu ake. Mose anakhala akuphunzitsa Yoswa kwa zaka zambiri. (Eks. 33:11; Deut. 34:9) Kuwonjezera pamenepo, panali amuna ambiri omwe anali atsogoleri a anthu 1000, 100, 50 komanso ngakhale 10. (Deut. 1:15) Anthu a Mulungu anapitiriza kusamalidwa bwino. Ndi zomwenso zinachitika m’nthawi ya Eliya. Kwa zaka zambiri iye ankatsogolera kulambira koona ku Isiraeli. Koma nthawi ina Yehova anamusamutsira chakummwera ku Yuda kuti akachite utumiki wake kumeneko. (2 Maf. 2:1; 2 Mbiri 21:12) Kodi anthu okhulupirika a mu ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10 anali atasiyidwa? Ayi. Eliya anali ataphunzitsa Elisa kwa zaka zambiri. Yehova anapitiriza kukwaniritsa cholinga chake ndipo ankasamalira atumiki ake okhulupirika. w24.02 5 ¶12

Lachisanu, March 28

Pitirizani kuyenda ngati ana a kuwala.—Aef. 5:8.

Akhristu a ku Efeso anali ataona kuwala kwa choonadi cha m’Malemba. (Sal. 119:105) Anali atasiya miyambo ya chipembedzo chabodza komanso makhalidwe oipa. Iwo anayamba kutsanzira Mulungu ndipo ankachita zonse zimene angathe kuti azimulambira komanso kumusangalatsa. (Aef. 5:1) Ifenso tisanaphunzire choonadi tinali mumdima pa nkhani ya kulambira komanso makhalidwe. Ena ankachita maholide a chipembedzo chabodza pomwe ena anali achiwerewere. Koma titaphunzira mfundo za Yehova pa nkhani ya zoyenera ndi zolakwika, tinasintha. Tinayamba kusintha moyo wathu kuti ugwirizane ndi mfundo zake zolungama ndipo tsopano tikupeza madalitso ambiri. (Yes. 48:17) Komabe panopa pali mavuto amene tikukumana nawo. Tiyenera kutalikirana ndi mdima womwe tinausiya n’kupitiriza “kuyenda ngati ana a kuwala.” w24.03 21 ¶6-7

Loweruka, March 29

Mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo pochita zomwe tikuchitazo.—Afil. 3:16.

Mwina mungamaone kuti simunakonzeke kuti mudzipereke komanso kubatizidwa. N’kuthekanso kuti mukufunika kusintha zinthu zina kuti muzitsatira mfundo za Yehova. Kapenanso mukufunika nthawi yambiri kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu. (Akol. 2:6, 7) Sikuti ophunzira onse amapita patsogolo mofanana ndiponso ana samakhala okonzeka kudzipereka komanso kubatizidwa pa msinkhu wofanana. Muziyesa kuona mmene mukupitira patsogolo mogwirizana ndi zomwe mungakwanitse ndipo musamadziyerekezere ndi munthu wina. (Agal. 6:4, 5) Ngakhale mutaona kuti simunakonzeke kudzipereka kwa Yehova, muzipitirizabe kukhala ndi cholinga chimenechi. Muzimupempha kuti akuthandizeni kukonza zomwe mukufunika kusintha. (Afil. 2:13) Dziwani kuti iye adzamva pemphero lanu ndipo adzakuthandizani.—1 Yoh. 5:14. w24.03 5 ¶9-10

Lamlungu, March 30

Amuna, pitirizani kukhala ndi akazi anu mowadziwa bwino.​—1 Pet. 3:7.

Pa nthawi ina, Sara anakhumudwa kwambiri mpaka ankaimba mlandu Abulahamu kuti ndi amene anachititsa vuto limene anakumana nalo. Abulahamu ankadziwa kuti Sara anali mkazi wogonjera komanso ankamuthandiza kwambiri. Iye anamumvetsera ndipo anayesetsa kuthetsa vutolo. (Gen. 16:5, 6) Ndiye kodi tikuphunzirapo chiyani? Amuna, muli ndi udindo wosankha zochita pa nkhani zokhudza banja lanu. (1 Akor. 11:3) Komabe, mungasonyeze chikondi ngati mutamvetsera maganizo a mkazi wanu musanasankhe zochita, makamaka pa nkhani zimene zingamukhudze. (1 Akor. 13:4, 5) Pa nthawi ina, Abulahamu ankafuna kuchereza alendo omwe anafika kunyumba kwawo mwadzidzidzi. Iye anapempha Sara kuti asiye kaye zomwe ankachita, n’kukonza makeke ambiri. (Gen. 18:6) Sara anachitapo kanthu mwamsanga pochita zimene Abulahamu anamupempha. Akazi, mungatsanzire Sara pogwirizana ndi zimene amuna anu asankha. Mukamachita zimenezi, mumalimbitsa banja lanu.—1 Pet. 3:5, 6. w23.05 24-25 ¶16-17

Lolemba, March 31

Nzeru yochokera kumwamba ndi . . . yokonzeka kumvera.—Yak. 3:17.

Gidiyoni ataikidwa kukhala woweruza ankafunika kukhala womvera komanso wolimba mtima. Iye anapatsidwa ntchito yovuta yoti akagwetse guwa lansembe la bambo ake, lomwe ankalambirirapo Baala. (Ower. 6:25, 26) Kenako atasonkhanitsa asilikali, kawiri konse iye anauzidwa kuti achepetse chiwerengero chawo. (Ower. 7:2-7) Pamapeto pake, anauzidwa kuti akaukire adani awo pakati pa usiku. (Ower. 7:9-11) Akulu ayenera kukhala ‘okonzeka kumvera.’ Mkulu womvera amakhala wofunitsitsa kugonjera zimene Malemba amanena komanso kutsatira malangizo ochokera ku gulu la Mulungu. Akatero amapereka chitsanzo chabwino kwa ena. Koma ngakhale zili choncho, nthawi zina zingamuvute kuti amvere. Mwachitsanzo, mwina zingamuvute kutsatira malangizo amene aperekedwa. Pa zochitika zina, iye angamakayikire ngati malangizo enaake alidi anzeru kapena othandiza. Kapena mwina angapemphedwe kuti agwire ntchito inayake yomwe ingachititse kuti amangidwe. Kodi akulu angatsanzire bwanji Gidiyoni pa zochitika ngati zimenezi? Iwo ayenera kumvetsera malangizo mosamala komanso kuwagwiritsa ntchito. w23.06 4-5 ¶9-11

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena