Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 1/15 tsamba 30
  • Chidziŵitso pa Nyuzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chidziŵitso pa Nyuzi
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Si Mwachiwonekedwe”
  • Kuganiza Kolakwika
  • Chosowa Chachikulu
  • Kodi Yesu Atafa Anakulungidwa mu Nsalu ya Maliro Yomwe Inasungidwa ku Turin?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Umodzi Wachikristu Ngwothekera?
    Galamukani!—1991
  • Carici Coona ndi Maziko Ace
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
Nsanja ya Olonda—1989
w89 1/15 tsamba 30

Chidziŵitso pa Nyuzi

“Si Mwachiwonekedwe”

Kufufuza kwa posachedwapa kwa sayansi kwatsimikizira kuti Shroud ya Turin chiri chinyengo cha m’zana la 14. Komabe, “Akatolika analimbikitsidwa kupitirizabe ndi kufunsira kwawo kwa shroud monga fano lochitira chithunzi Kristu, lokhozabe kuchita zozizwitsa,” yasimba tero The New York Times. Anastasio Ballestrero, bishopu wamkulu wa ku Turin, analongosola kuti: “Kuwonetsera kopatulidwa kwa mphamvu ya fano la Yesu Kristu kuyenera kusungiliridwa.”

Kodi chimenechi chikutanthauzanji? Chikutanthauza kuti ngakhale kuti tchalitchi chavomereza kuti fano loipitsidwalo la thupi la munthu pa shroud siliri lija la Yesu Kristu, Akatolika okhulupirika ngakhale ndi tero ayenera kupitirizabe kuwona ilo monga ngati kuti linali Kristu ndipo chotero monga chinachake choyera. Chifukwa ninji? Mogwirizana ndi Adam Otterbein, wansembe wa Roma Katolika wolamulira Shroud Guild Loyera, zifanizo zolambiridwa zonga ngati shroud zingathandize akhulupiriri kupereka ulemu kwa uyo amene fanolo likuimira.

Sichiri chodabwitsa kuti, mosasamala kanthu za kusowa kwake kutsimikizirika, shroud ikakhala chizindikiro champhamvu cha chikhulupiriro kaamba ka Tchalitchi cha Chikatolika. “Mafano, zopaka utoto ndi zithunzi zopatulikitsidwa . . . zikupatsidwa malo aulemu m’zochita za Chikatolika,” yadziŵitsa tero The New York Times.

Kodi Baibulo limachirikiza kugwiritsira ntchito kwa mafano oterowo m’kulambira? Ayi! Mawu a Mulungu amanena mowonekera bwino kuti: “Thawani kulambira mafano.” (1 Akorinto 10:14; yerekezani ndi Eksodo 20:4-6.) Akristu akulangizidwa kulambira Mulungu “mu mzimu ndi m’chowonadi,” osati ndi chithandizo cha mafano kapena zifanizo. (Yohane 4:24) Moyenerera, Paulo analemba kuti Akristu owona “akuyenda mwa chikhulupiriro, si mwa chiwonekedwe.”​—2 Akorinto 5:7.

Kuganiza Kolakwika

M’kusungilira ndi chikhoterero chowonekera kulinga ku kusatenga mosamalitsa miyezo ya Baibulo pakati pa akatswiri a chipembedzo, “chiwerengero chomakulakula cha akatswiri a zaumulungu a ku U.S. chikutsutsa kuti matchalitchi Achikristu afunikira kukhala ndi masinthidwe a kugonana,” yasimba tero Star Tribune. Nyuzipepala ya ku Minnesota imeneyi ikugwira mawu mawonedwe ogogomezeredwa ndi anthu otchuka oterowo onga ngati John Spong, bishopu wa ku Newark kaamba ka Episcopal Church ya ku America, ndi James Nelson, katswiri wa chiyambi cha kugonana pa United Theological Seminary mu New Brighton. Pepalayo yadzinenera kuti akatswira a zaumulungu amenewa ndi ena amadzimva kuti matchalitchi ayenera “kudalitsa ogonana ofanana ziwalo m’mapwando a tchalitchi, akumavomereza ntchito yawo kwa wina ndi mnzake mu unansi wokondeka, ndi wa makhalidwe abwino; . . . kupatsa achichepere otomerana madalitso a tchalitchi ngati iwo akhalirira mu unansi wa chikondi, wodzipereka, ngakhale kuti sali okwatirana”; ndi “kuvomereza pamane achikulire ali odzutsidwa mwa kugonana m’njira zokhala ndi thayo, ngakhale kuti ali osakwatirana kwa wina ndi mnzake.” Nchifukwa ninji akatswira a zaumulungu amenewa amakhulupirira kuti masinthidwe amenewa ali ofunika? Spong akudzinenera kuti “timapereka kuvomereza kwathu ku kakhalidwe kosakhala ka lamulo” ngati kugwirizana koteroko sikunadalitsidwe.

Chimene Spong ndi ena akulephera kuwona, ngakhale ndi tero, chiri chakuti kuli kudalitsidwa komweko kwa kugwirizanako komwe kumakhazikitsa kugwizana kwa tchalitchiko ku “kukhala ndi moyo kosakhala kwa lamulo” koteroko. Mawu a Mulungu ali omvekera. “Adama, . . . kapena achigololo, . . . kapena [amuna ogonana ndi amuna, NW] . . . sadzalowa ufumu wa Mulungu.” Atsatiri a Kristu sakulamulidwa kokha “kusayanjana” ndi oterowo komanso akuuzidwa “kuchotsa woipayo” pakati pawo.​—1 Akorinto 6:9-11; 5:11, 13.

Chosowa Chachikulu

Chaka chino, ripoti la kuŵerengera la Free Church Federal Council ya ku Britain yavumbula kutsika kowonjezereka kwa mitundu ya magulu ake achipembedzo ogwirizana nalo 15. Kwa nthaŵi yoyamba, ziwalo zabwerera m’mbuyo osafika pa mlingo wa miliyoni imodzi, yasimba tero Church Times, nyuzipepala ya Church of England. Chifukwa chake? Ngakhale kuti matchalitchi amanena kuti iwo ali odzipereka ku “unyinji wokulira . . . womwe chosowa chawo chachikulu chiri kaamba ka kuwomboledwa,” nkhaniyo yadziŵitsa kuti “a Free Church apitiriza kupereka nthaŵi yokulira ndi mphamvu ku . . . mayanjano.” Mogwirizana ndi Church Times, “ngati Matchalitchi akubwerera m’mbuyo, sichiri chifukwa chakuti zogulitsa zawo za chaka ndi chaka zatsika kapena zotulutsidwa zokulira za chitaganya chawo sizikuchirikizidwa: chiri chifukwa chakuti sanatenge utumiki wawo wa chiwombolo mosamalitsa mokwanira.”

Atsogoleri a chipembedzo a m’tsiku la Yesu sanatenge utumiki wawo mosamalitsa nkomwe. Yesu anasuliza iwo molondola kaamba ka kukhala atapanga “mawu a Mulungu kukhala opanda pake” ndi miyambo yawo. Iye ananena kuti iwo anali onyenga, omwe ‘analemekeza Mulungu ndi milomo yawo ngakhale kuti mitima yawo inali kutali ndi iye.’​—Marko 7:6, 7, 13.

Atumiki owona a Yehova Mulungu, ngakhale ndi tero, ali odzipereka “ku utumiki wa mawu.” Iwo amatenga lamulo la Yesu mosamalitsa la “kupanga ophunzira,” ndipo amatsatira chitsanzo cha atumwi, omwe “sanaleke kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu.” Kwa Akristu owona, ntchito imeneyi iri ya chifuno chokulira.​—Machitidwe 6:4; Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 5:42.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena