Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 1/15 tsamba 25-29
  • Chilungamo Chaumulungu—Chochititsa Kaamba ka Kusangalala!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chilungamo Chaumulungu—Chochititsa Kaamba ka Kusangalala!
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Achimwemwe Ali Awo Ochita Chilungamo”
  • “Landilani Mwambo Womwe Umapereka Chidziŵitso”
  • “Ziŵeruzo Zake Ziri Zowona Ndi Zolungama”
  • “Chilungamo​—Chilungamo Ndicho Mudzichitsata”
  • Mukuitanidwa ku Misonkhano ya Chigawo ya “Chilungamo Chaumulungu”
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Misonkhano Yosangalatsa Ichirikiza Chiphunzitso Chaumulungu
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Yehova—Gwero la Chilungamo Chenicheni
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Tsanzirani Yehova—Chitani Chilungamo
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 1/15 tsamba 25-29

Chilungamo Chaumulungu​—Chochititsa Kaamba ka Kusangalala!

“IDZANI imbani limodzi nafe . . . ‘Yehova akulamulira; lolani dziko lapansi lisangalale.’” Mawu amenewo anali mbali ya nyimbo yoimbidwa pakamwa pa nthumwi 9,000 za chiArabic, Chigriki, chiItaly, chiPortuguese, ndi chiSpanish ku Msonkhano Wachigawo wa “Chilungamo Chaumulungu” mu Montreal, Canada. Osonkhana anathamangira ku bwalo losonkhanira pa Olympic Stadium kaamba ka nthaŵi yotsirizira ya msonkhano wa masiku anayi umenewu kukagwirizana m’nyimbo ndi nthumwi 36,900 zokhala kale m’bwalomo.

Magulu ena a zinenero analipo kaamba ka programu ya msonkhano wofananawo m’malo osonkhanira apafupi ndi nyumba zosonkhaniramo. Tsopano iwo anagwirizana ndi opezekapo a chiFrench ndi Chingelezi m’kusonyezedwa kotsitsimula kwa ubale ndi chikhulupiriro​—chinachake chomwe chingakhoze kokha kuzindikiridwa pakati pa atumiki a Mulungu wa chilungamo chowona, Yehova. M’chiyang’aniro cha chisalungamo chofalikira m’dziko lamakono, mutu wa msonkhano​—“Chilungamo Chaumulungu”​—unali wa pa nthaŵi yake ndithudi. Wogwirizanitsidwa kupyola m’programu yonseyo, mutu umenewu unasindikiza chiyamikiro chathu kaamba ka mkhalidwe waukulu umenewu wa Yehova Mulungu.

“Achimwemwe Ali Awo Ochita Chilungamo”

Uyu unali mutu wa tsiku loyamba la msonkhano. (Salmo 106:3) Nkhani yaikulu yolonjera ya tcheyamani inachipanga icho kukhala chowonekera kuti chilungamo chaumulungu sichiri kokha kachitidwe wamba ka lamulo la kagwiridwe ka chiweruzo. M’malomwake, kuli kusungirira kwa chimene chiri cholondola m’njira yopanda tsankho ndi yabwino mogwirizana ndi miyezo ya Mulungu. Yehova amakhazikitsa miyezo yapamwamba ndipo ali wangwiro m’chilungamo chifukwa chakuti iye amamamatira ku izi. Ndiponso, chinganenedwe kuti “njira zake zonse ndi [chilungamo, NW].”​—Deuteronomo 32:4.

Ichi chinawunikiridwa mowonjezereka m’nkhani yaikulu, yokhala ndi mutu wakuti “Chilungamo Chimazindikiritsa Njira Zonse za Mulungu.” Yehova sanapatukepo kuchoka pa miyezo yake yolungama koma iye wagwiritsira ntchito njira zolungama zofananazo m’kuchita ndi anthu opanda ungwiro onse. (Malaki 3:6) Ngakhale kuti ena angapatse mlandu Mulungu monyenga wa kukhala wopanda chilungamo chifukwa chakuti iwo akuwona kusoweka kokulira kwa chilungamo m’chitaganya cha anthu, iye sali wa thayo kaamba ka kupatuka kwa mtundu wa anthu woipitsidwa.

Popeza kuti Yehova ali wokonda chilungamo, iye amatiyembekezera ife kuchita mkhalidwe umenewu mwa kuchita chimene chiri cholondola ndi chabwino. Tiyenera kuchita ichi kulinga kwa anthu anzathu ndi mabanja athu, mkati mwa mpingo, ndi m’mbali zonse za kulambira kwathu. Ichi chimabweretsa madalitso olemerera, monga momwe chingawonedwere kuchokera ku chomwe chinaperekedwa pa programu mkati mwa masiku otsala atatu a Msonkhano Wachigawo wa “Chilungamo Chaumulungu.”

“Landilani Mwambo Womwe Umapereka Chidziŵitso”

Tsiku lachiŵiri la msonkhano linali ndi mutu womwe watchulidwawo, wozikidwa pa Miyambo 1:3, (NW). Tinafulumizidwa “Kulandira Chilango ndi Kukhala Wanzeru,” umenewo pokhala mutu wa mbali yoyambirira pa programupo. Chilango chochokera kwa Yehova chimazindikiritsa njira ya moyo yomwe imaphatikizapo kuyengedwa kwa kapangidwe kathu ka kuzindikira kwa maganizo ndi makhalidwe abwino. Chirinso chisonyezero cha chikondi cha Mulungu kaamba ka ife. (Ahebri 12:4-11) Chilango choterocho chimatisunga ife kukhala ozindikira ku miyezo yokulira ya chilungamo​—chilungamo chaumulungu.

Kulongosola kwenikweni kumeneku kunatsatiridwa ndi nkhani yakuti “Khalani Oyera m’Maganizo ndi Thupi.” Inali yodzutsa maganizo chotani nanga! Iyo inasindikiza pa ife kufunika kwa kudzipereka ife eni kwa Mulungu monga anthu abwino, audongo, ndi oyera. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Yehova ali waudongo mokulira ndi woyera​—mkhalidwe womwe umamukhazikitsa iye mosiyana ndi milungu yoipa yonse ya mitundu. Kuwunikira pa nkhaniyi, mbale wachichepere wina analongosola kuti: “Chirichonse ponena za udongo wathu wa maganizo, makhalidwe abwino, kuthupi, ndi uzimu chinasanthulidwa. Kavalidwe kathu, kapesedwe, nyumba, galimoto, ndi umunthu zonsezo zinapatsidwa chisamaliro.” Mkulu wina anawona kuti: “Kuika uphungu wotero m’kugwira ntchito chidzapangitsa abale athu kuima mowonekera koposa ndi kale lonse kusiyana ndi anthu owazungulira ndipo kudzapereka mlingo wa umoyo wosadziŵika ndi dziko mwachisawawa.”

Chitsanzo chamakono cha “Kuikidwa Chizindikiro kaamba ka Kupulumuka” chinawonjezera lingaliro la kufulumira ku programuyo, popeza kuti chilungamo chaumulungu chiyenera kukhutiritsidwa mwamsanga. Kuwonetsera kodzutsa mtima kumeneku kunasonyeza mwakuya kuti chiri chofulumira kaamba ka onse kutsegula maso awo ku kufunika kwa nthaŵi yathu. Ndithudi, chipembedzo chonyenga chisanakanthidwe, tiyenera kuthamangira ku malo othaŵira ndi kuikidwa chizindikiro motsimikizirika kaamba ka kupulumuka.

Masana, nkhani yosiirana ya alankhuli inatsimikizira ku kufunika kaamba ka “Kulanga m’Chilungamo Mkati Mwa Banja.” Amuna ndi atate analangizidwa kukhala ndi programu yauzimu m’nyumba, kutenga chitsogozo m’pemphero, phunziro, ndi utumiki wopatulika. Mikhalidwe yaumuna ya atate ndi mmene angasamalire umutu wawo ziri ndi chiyambukiro chosindikiza pa kawonedwe ka mwana ka ulamuliro, ponse paŵiri waumulungu ndi wa anthu. Chotero, atate Achikristu ayenera kukhala olongosoka ndi okhazikika m’chilango chawo. Iwo ayenera kusonyeza chifundo ndi kutentha, mwakutero kusunga mbali zotseguka za kukambitsirana ndi ana awo.

Makolo analimbikitsidwa kugwirizanitsidwa malangizo awo kwa ana. Chiri chofunika kupereka chidziŵitso kwa ana mwa kulingalira mmene mungaphunzitsire ndi chimene mungaphunzitse ndi cholinga chofuna kufikira mitima yawo. Cholinga chiri kulola chowonadi kuyambukira banja lonse m’njira yophulapo kanthu.

Mlankhuli wotsirizira wa nkhani yosiiranayi anapanga kufikira kotentha kwa ana kuchita chimene Yehova amawayembekezera iwo mkati mwa makonzedwe a banja. Achichepere anafulumizidwa kupewa mzimu wowukira wa chitaganya chololera cha makono ndi kusangalala m’chilango chomwe chimapereka chidziŵitso.

M’mawu ozikidwa pa Miyambo 2:1-9, osonkhana analimbikitsidwa “Kupitiriza Kufunafuna monga Chuma Chobisika.” Chinachitiridwa chitsanzo kuti zinthu za mtengo wapatali zauzimu zingapezedwe kupyolera m’phunziro la khama ndi kufufuza. Polankhula pa nkhani yakuti “Yang’anani Kwa Yehova kaamba ka Chidziŵitso,” mlankhuli wotsatira analongosola kuti chidziŵitso chiri kuthekera kwa kuwona mu mkhalidwe, kuyang’ana kupyola pa zenizeni ndi kupeza lingaliro la chinachake. (Mateyu 13:13-15; Aroma 3:11; Aefeso 5:17) Tsiku losangalatsa limeneli kenaka linadza kumapeto pamene Olympic Stadium inalumikizidwa ndi lamya ndi mizinda ina yambiri mu Canada ndi United States. Nkhani zosiirana za mbali ziŵiri zinawunikiridwa mwa kutulutsidwa kwa chofalitsidwa cha mavolyumu aŵiri cha Insight on the Scriptures, chokhala ndi masamba oposa 2,500 a nkhani zodziŵitsa ndi zitsanzo zomwe zidzazamitsa chiyamikiro chathu cha zinthu zauzimu.

“Ziŵeruzo Zake Ziri Zowona Ndi Zolungama”

Pa tsiku lachitatu, lomwe linali ndi mutu umenewu wozikidwa pa Chibvumbulutso 19:2, panali zambiri zotipangitsa kusangalala. Nkhani yakuti “Udongo wa Makhalidwe Abwino Uli Kukongola Kwa Uchichepere” inapanga kusindikiza kwamphamvu kwa achichepere. Iwo anafulumizidwa kuwona kukhala kwa mtengo wapatali kukongola kogwirizana ndi kusungilira miyezo ya Mulungu ya kuyera kwa kuthupi, kwa makhalidwe, ndi kwauzimu. Nyimbo zolongosola kugonana, maprogramu a chisembwere a wailesi ya kanema, akanema owonetsa umaliseke ndi mabukhu, ndi kudidikiza kwa mabwenzi kwakantha mokhazikika achichepere Achikristu. Mogwirizana ndi magwero amodzi, ali kokha munthu wachichepere wosakhudzidwa wa apa ndi apo yemwe sanakhalepo ndi kugonana kosakhala kwa mu ukwati podzafika pa msinkhu wa zaka 19 zakubadwa. Koma osonkhanawo anawomba m’manja motenthedwa pamene mlankhuli anayamikira zikwi za achichepere omwe ali Mboni amene amadzisonyeza iwo eni kukhala osiyanako mwa kusungirira miyezo yapamwamba ya chilungamo. Maukwati ofulumira ali odzala ndi mavuto, ndipo chinasonyezedwa kuti mawu a Paulo onena za kukwatira chifukwa cha “kutentha mtima” amanenedwa osati kwa a zaka za pakati pa 13 ndi 19 koma kwa awo omwe “apitirira pa unamwali wawo.”​—1 Akorinto 7:9, 36.

“Musamangidwe m’Goli Ndi Osakhulupirira” unali mutu wotsatira. Kulabadira malamulo a Mulungu a kukwatira “kokha mwa Ambuye” kumatipulumutsa ife ku zisonkhezero zowawa. (1 Akorinto 7:39) Kuwonjezerapo, kulibe china chirichonse chomwe chiri cholimbikitsa ku ukwati kuposa kudzipereka kogawana kwa Yehova ndi kumamatira ku miyezo yake yolungama. Chotsatira tinathandizidwanso kuwona mmene tiyenera “Kuchita Ndi Ulemu ndi Mantha a Umulungu.”

Kenaka kunadza kuwunikira kosangalatsa​—nkhani yakuti “Ubatizo Womwe Umatsogolera ku Chiweruzo Chabwino,” yotsatiridwa ndi kumizidwa kwa anthu odzipereka chatsopano. Chinagogomezeredwa kuti zambiri zinayembekezeredwa kwa iwo kuposa kokha kuleka makhalidwe oipa a kuthupi. Kulapa, kutembenuka, ndi utumiki wa moyo wonse wopatulika uyenera kugwirizana ndi kudzipereka kwawo ndi ubatizo ngati iwo ati asangalale ndi chiweruzo choyanja chochokera kwa Yehova.

Programu ya masana inali yokumbukirika ndithudi. Kachiŵirinso ndi kulumikizidwa kwa lamya, ziwalo za Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova zinadzutsa opezekapowo modutsa North America ndi kaperekedwe kochititsa nthumanzi ka nkhani yosiirana yakuti “Nthaŵi Zoikidwiratu Ziri Pafupi.” Kwa zaka makumi angapo, mboni zodzozedwa za Yehova zalengeza mauthenga a chiweruzo chaumulungu motsutsana ndi Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Pa msonkhano uwu, ngakhale kuli tero, mauthenga amenewa anatenga kumvekera kwa mphamvu. Babulo Wamkulu wakhala wa liwongo la kuswa malamulo olungama a Yehova. Iye ali woyenerera chiwonongeko, popeza kuti “machimo ake aunjikana kufika kumwamba, ndipo Mulungu wakumbukira chisalungamo chake ku mtima.” Chotero, monga momwe mngelo wa Yehova akulengezera, “m’tsiku limodzi, imfa ndi maliro ndi njala, ndipo udzapsyerezedwa ndi moto, chifukwa [Yehova, NW] Mulungu, wouweruza, ndiye wolimba.”​—Chibvumbulutso 18:5, 8.

Kulankhula pa nkhani yakuti “‘Mkazi Wachigololo’ Wa Mbiri Yoipa​—Kugwa Kwake ndi Chiwonongeko,” mlankhuli wotsirizira wa nkhani yosiirana imeneyi anakoka chisamaliro ku kaindeinde wokulira wa Chibvumbulutso. Kaindeinde ameneyu amafikiridwa ndi ukwati wa Mwanawankhosa, yemwe amagwirizana ndi mkwatibwi wake, mzinda woyera, m’kudalitsa mtundu wa anthu ndi moyo wosatha. Dzina la Yehova likwezedwa! Nkhani yosiiranayo inamaliza ndi ndemanga yodzutsa maganizo yakuti nthaŵi yoikidwiratu iri pafupi kwenikweni kuposa ndi mmene tingalingalire! Ndithudi, kaindeinde wokulira wa Chibvumbulutso ali pakhomo!

Pamene opezekapo ankawombabe m’manja, panadza kutulutsidwa kwa bukhu latsopano la masamba 320 la Revelation​—Its Grand Climax At Hand! Chinali chochititsa kusangalala chotani nanga! Chofalitsidwa chimenechi chidzakhala chochititsa chokhutiritsa motsimikizirika cha kulengeza kuti Babulo Wamkulu waukiridwa, kuti mitundu tsopano ikuyang’anizana ndi Armagedo, ndi kuti Yehova ali pafupi kupereka chiweruzo. Lolani oyamikira onse ayankhe chiitano cha “mzimu ndi mkwatibwi” cha “idzani” ku madzi a moyo. (Chibvumbulutso 21:2, 9; 22:17) Chofalitsidwa chosindikizidwa chosangalatsa chimenechi chinatsatiridwa ndi china chochititsa kusangalala. Ndi kukhutiritsidwa kwa chimwemwe, opezekapo pa msonkhano anatenga chigamulo mogwirizana chomvekera bwino ndi chowona chonena za kuda kwathu Babulo Wamkulu.

“Chilungamo​—Chilungamo Ndicho Mudzichitsata”

Wozikidwa pa Deuteronomo 16:20, uyu unali mutu wa tsiku lomalizira. Alankhuli a m’mawa anagogomezera chenicheni chakuti ponena za kuti tipindule kuchokera ku chilungamo chaumulungu, tiyenera kukhala osiyana ndi dziko. Lingalirani nkhani yakuti “Kusungirira Thanzi Lauzimu m’Dziko Lodwala.” Iyo inasonyeza mmene tingapewere kuipitsidwa ku dziko lopanda umoyo wauzimu mwa kudzisunga motsutsana ndi kufoka kwa kuthupi, zisonkhezero za kudziko, ndi “machenjera a Mdyerekezi.” (Aefeso 6:11, 12; Aroma 7:21-25; 1 Yohane 2:15-17) Nkhani yakuti “Kodi Chikhulupiriro Chanu Chimatsutsa Dziko?” inasonyeza kuti ngati tiri ndi chikhulupiriro chofanana ndi chija cha Nowa, tidzakhala osiyana ndi dziko. M’tsiku la Nowa, panali kusiyana kowonekera pakati pa opulumuka Chigumula ndi aja omwe anawonongeka. Chofananacho chiri chowona lerolino.

Nsonga yofunika imeneyi inawunikiridwa m’chitsanzo cha Baibulo chakuti “Ziweruzo Za Yehova Motsutsana Ndi Anthu Onyalanyaza Lamulo.” Iyo inasonyeza mwakuya anthu onyalanyaza lamulo m’tsiku la Nowa ndi Loti ndi aja okhala m’nthaŵi yathu. Nowa ndi Loti anakhala osiyana nawo kwenikweni, ndipo chikhulupiriro chawo chinatsutsa anzawowo. Kodi timaima mwaumwini mosiyana kuchokera ku anthu lerolino omwe ali otanganitsidwa ndi zinthu za kuthupi ndipo ali okonda chomwe chiri choipa?

Nkhani ya Baibulo, “Chilungamo kaamba ka Onse Ndi Woweruza Woikidwa ndi Mulungu,” inali kusanthula komwereketsa kwa mawu a mtumwi Paulo ku anthu a ku Atene pa Aleopagasi, kapena Phiri la Mars. Ozunguliridwa monga momwe tiriri ndi kupanda chilungamo kokulira ndi chipembedzo chonyenga, mawu a mtumwiyo ali ndi tanthauzo lokulira kaamba ka ife. Makamaka tingakhale ndi chifukwa cha kusangalarira chifukwa chakuti tikukhala pa nthaŵi yoipitsitsa ya chiweruzo pamene tingatenge kachitidwe ka kukhala ndi kuvomerezedwa kwa Mulungu. Inde, monga momwe Paulo ananenera kuti, Yehova walinganiza “kuweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu [Yesu Kristu] amene anamuikiratu, napatsa anthu onse chitsimikizo pamene anamuukitsa iye kwa akufa.”​—Machitidwe 17:31.

Pamene programu inafika kumapeto, tinasonkhezeredwa “Kupitiriza Kutsatira Chilungamo Pamene Mapeto Akuyandikira.” Msonkhano wabwino kwambiriwu wa masiku anayi unatidzadza ife ndi chitsimikiziro cha kuchita tero. Programuyo inasindikizanso pa ife ndi kapenyedwe ka ubale wathu wa mitundu yonse. Mwachitsanzo, ndi chisangalalo chotani nanga chomwe icho chinali kumvetsera ku amishonale ochezera omwe akhala akutumikira mokhulupirika mu magawo awo kwa zaka!

Tinachoka pa msonkhano ndi chigamulo chopangidwanso chatsopano cha kukhala osiyana ndi dziko iri ndi kudzisunga oyera mwauzimu, mwa makhalidwe, mwa maganizo, ndi kuthupi. Pamene tinagwirizana mwadongosolo m’nyimbo yotsekera, tinali osangalala kuimba zitamando za Yehova, okondwera kuti chilungamo chaumulungu chimatipatsa ife chochititsa chokulira kaamba ka kusangalala.

Pa misonkhano yoposa 125 mu United States ndi Canada mokha, anthu 1,440,932 analipo ndipo 19,878 anabatizidwa

[Zithunzi patsamba 26]

1, 2. Zofalitsidwa za Insight on the Scriptures ndi Revelation​—Its Grand Climax At Hand! zikutulutsidwa pa Yankee Stadium, Mzinda wa New York, ndi ziwalo za Bungwe Lolamulira J. E. Barr ndi W. L. Barry

3, 4. Zochitika kuchokera ku chitsanzo cha Baibulo cha “Ziweruzo za Yehova Motsutsana ndi Anthu Onyalanyaza Lamulo”

5. Zikwi zingapo anabatizidwa m’chizindikiro cha kudzipereka kwawo kwa Yehova Mulungu

6. Chochitika kuchokera ku chitsanzo chamakono cha “Kuikidwa Chizindikiro kaamba ka Kupulumuka”

7. Amishonale ochezera, onga ngati John Cutforth wa ku Papua New Guinea, anagawana zokumana nazo zawo ndi osonkhana

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena