Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki
Kupenda kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa September 4 kufikira December 18, 1995. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.
[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]
Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:
1. Malinga ngati Mkristu alingalira kuti chimene akuchita nchoyenera, zosankha zake nzabwino. (Miy. 14:12) [uw-CN tsa. 8 ndime 8(2)]
2. Chiphunzitso cha Utatu chinayamba ndi Dziko Lachikristu. [uw-CN tsa. 15 ndime 8]
3. Pamene Yesu anatchula “chuma chosalungama” pa Luka 16:9, anali kulankhula za chuma chopezedwa mwa njira yosaona mtima. [gt-CN mutu 87]
4. Mwa kuyerekezera Aroma 8:16 ndi Aroma 1:7, tingaone kuti Paulo anali kunena za anthu onse kukhala “ana a Mulungu.” [uw-CN tsa. 26 ndime 12(3)]
5. ‘Kutengedwa’ kotchulidwa pa Luka 17:34 kumatanthauza chiwonongeko. [gt-CN mutu 93]
6. Kudzipereka kwaumulungu kumasonyeza kumamatira mwachikondi kwa Yehova chifukwa cha kuyamikira iye ndi njira zake. [uw-CN tsa. 19 ndime 15]
7. Pamene Yesu ananena kuti otsatira ake ayenera ‘kuda’ achibale awo, anatanthauza kuti ayenera kuwada m’lingaliro lowakonda mocheperapo poyerekezera ndi mmene amakondera iye. (Luka 14:26) [gt-CN mutu 84]
8. Mzimu wodzigangira unayambitsidwa ndi Hava. [uw-CN tsa. 10 ndime 10]
9. Nkhani ya m’Baibulo pa Luka 16:19-31 yonena za munthu wachuma ndi Lazaro ili chochitika chenicheni. [gt-CN mutu 88]
10. Afarisi ndi alembi anagwiritsira ntchito liwu lachihebri lakuti ‛am ha·’aʹrets, “anthu adziko [dziko lapansi],” kutchula anthu wamba, amene anawaona monga litsiro. [gt-CN mutu 85]
Yankhani mafunso otsatirawa:
11. Popeza kuti chikondi chachikulu cha Yehova chinamsonkhezera kutumiza Mwana wake kudzapereka moyo wake kaamba ka ife, kodi chikondi chathu kwa Mulungu chiyenera kutisonkhezera kuchitanji? (2 Akor. 5:14, 15) [uw-CN tsa. 14 ndime 6]
12. Kodi kuyenda m’dzina la Yehova kumatanthauzanji? [uw-CN tsa. 18 ndime 14]
13. Kodi mawu a Yesu a pa Yohane 11:26 adzakwaniritsidwa liti m’lingaliro lenileni ndipo kwa yani? [gt-CN mutu 90]
14. Kodi nchifukwa ninji kuukitsidwa kwa Lazaro kwa akufa kunali nkhonya yamphamvu makamaka kwa Asaduki? [gt-CN mutu 91]
15. Ngati munthu anena kuti akhulupirira Utatu, kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru kumpempha kuti alankhule zimene adziŵa pankhaniyo musanatsutse Utatu? [uw-CN tsa. 16 ndime 10]
16. Kodi ndi zinthu zinayi zazikulu ziti zimene zimathandizira chigwirizano chimene anthu a Yehova akusangalala nacho lerolino? [uw-CN mas. 8-9 ndime 8, 9]
17. Malinga ndi kunena kwa Salmo 9:10, kodi kudziŵa dzina la Mulungu kumatanthauzanji? [ uw-CN mas. 18 ndime 14]
18. Kuwonjezera pa mikhalidwe yapadera ya Yehova ya chikondi, chilungamo, nzeru, ndi mphamvu, kodi tingaphunzirenji ponena za umunthu wake wabwino pa Eksodo 34:6 Salmo 86:5, ndi Machitidwe 10:34, 35? [uw-CN tsa. 13 ndime 3]
19. Titayerekezera Yohane 14:9, 10 ndi Luka 5:12, 13, kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Yehova ali wachifundo kwa anthu ovutika? [uw-CN tsa. 25 ndime 12(1)]
20. Kodi tiyenera kulimva motani yankho la Yesu kwa Afarisi pamene anati: “Ufumu wa Mulungu uli mkati mwa inu”? (Luka 17:21) [gt-CN mutu 93]
Perekani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:
21. Ebedimeleki anaphiphiritsira ․․․․․․․․, amene adzapulumutsidwa pa ․․․․․․․․ chifukwa chakuti anapalana ubwenzi ndi ․․․․․․․․ a abale a Kristu ndi kuwathandiza. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w82-CN 10/1 tsa. 27 ndime 11.]
22. Ngakhale kuti Yesu akutchedwa “Mulungu,” pa Yohane 17:3 iye anatcha Yehova kuti “Mulungu woona ․․․․․․․․,” ndipo pa Yohane 20:17 anatcha Yehova kuti “Mulungu ․․․․․․․․, ndi Mulungu ․․․․․․․․.” [uw-CN tsa. 18 ndime 12]
23. Zochitika zosimbidwa pa Yeremiya 52:5-11 zinachitika mu ․․․․․․․․ B.C.E. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 4/1 tsa. 14 ndime 18.]
24. Ngakhale kuti “alembi” aumunthu okwanira ․․․․․․․․ anagwiritsiridwa ntchito kulemba Baibulo, Mwini wake weniweni ali ․․․․․․․․. [uw-CN tsa. 20 ndime 2]
25. Ophunzira a Yesu ali mchere wa dziko lapansi m’lingaliro lakuti ․․․․․․․․. [gt-CN mutu 84]
Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:
26. Baibulo lili Mawu a Mulungu chifukwa chakuti (otembenuza ake analitcha motero; linalembedwa ndi anthu odzipereka pachipembedzo; Mulungu anatsogolera kulembedwa kwake). [uw-CN tsa. 20 ndime 2]
27. Ngati muŵerenga masamba (limodzi; aŵiri; anayi) okha a Baibulo tsiku lililonse, mukhoza kulimaliza pafupifupi (m’miyezi 6; m’miyezi 9; m’chaka chimodzi). [uw-CN tsa. 24 ndime 9]
28. Pa Genesis 1:1 ndi 1:26, liwu lachihebri lotembenuzidwa “Mulungu” ndilo (‘Adho·nai’; ‘El·o·him’; ‘Shad·dai’) [uw-CN tsa. 17 ndime 11(4)]
29. Yehova “anapusitsa” Yeremiya m’njira yakuti Iye (anamnyenga kuti alalikire uthenga wa chiwonongeko; anamgwiritsira ntchito kuchita chimene sakanatha ndi nyonga ya iye yekha; sanabweretse chiwonongeko chimene Yeremiya analosera). (Yer. 20:7, NW) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 5/1 tsa. 31.]
30. Lemba la Yohane 1:1 limanena za anthu (mmodzi; aŵiri; atatu) [uw-CN tsa. 17 ndime 11(3)]
Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:
Miy. 3:5, 6; Yer. 23:33; 32:9, 10; Maliro 3:44; Chiv. 15:3, 4
31. Maziko a chigwirizano chenicheni cha kulambira ndiwo kudziŵa Yehova ndi kukhala ndi moyo mogwirizana ndi njira zake zolungama. [uw-CN tsa. 5 ndime 1]
32. Njira yathu yonse ya moyo—zilibe kanthu ndi kumene tili, zilibe kanthu ndi zimene tikuchita—iyenera kupereka umboni wakuti malingaliro athu ndi zolinga zathu zili zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. [uw-CN tsa. 10 ndime 11]
33. Yehova samamvetsera mapemphero a anthu oipa. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 7/15 tsa. 15.]
34. Uthenga wamphamvu waulosi wochokera m’Mawu a Mulungu ukusonyeza tsoka lalikulu, ukumalengeza chiwonongeko choyandikira cha Dziko Lachikristu. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w94-CN 3/1 tsa. 12 ndime 18, 20.]
35. Poloŵa m’zochita za bizinesi ndi alambiri a Yehova anzathu, kukhala ndi chivomerezano cholembedwa kungapeŵetse kumvana molakwa kumene kungabukepo nthaŵi ina pambuyo pake. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 5/1 tsa. 30.]
S-97-CN Mal, Moz & Zam #288b 4/96