Misonkhano Yautumiki ya November
Mlungu Woyambira November 3
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. “Uthenga Wabwino pa Internet.” Fotokozani lipoti la utumiki wakumunda la July, la m’dziko ndi la mpingo wanu.
Mph. 15: “Khomo Lalikulu Loloŵera Kuntchito Nlotseguka.” Nkhani yokambidwa ndi mkulu, yophatikizapo kukambitsirana ndi omvetsera. Limbikitsani onse amene angathe, kuti akalimire kuchita mbali yaikulu pantchito yolalikira. Phatikizanipo uphungu umene unaperekedwa mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 1988, tsamba 22.
Mph. 20: “Bwererani kwa Amene Anachita Chidwi ndi Uthenga wa Ufumu.” Mafunso ndi mayankho. Chitirani chitsanzo maulaliki ali m’ndime 6. Paulaliki wina, sonyezani kuyambika kwa phunziro la Baibulo.
Nyimbo Na. 144 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 10
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti. Dziŵitsani mpingo za gawo limene latsala loti lifoledwe ndi Uthenga wa Ufumu Na. 35. Limbikitsani onse kutengamo mbali mokwanira pamlungu wotsirizira uno wa mkupiti wapadera.
Mph. 15: Zosoŵa zapamalopo.
Mph. 20: “Afikireni a Muukwati Amene si Mboni.” Kukambitsirana kwa akulu aŵiri omwe akufuna kudziŵa bwino za amuna kapena akazi osakhulupirira mwa kukawachezera. Akambitsirananso malingaliro a mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 1989, masamba 17-18, ndime 6-9. Phatikizanipo zokumana nazo za mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1995, masamba 10-11, ndime 11-12.
Nyimbo Na. 148 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 17
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Longosolani makonzedwe a utumiki wakumunda a kumapeto kwa mlungu ukudzawo. Kambitsiranani zimene munakumana nazo kwanuko pa mkupiti wa Uthenga wa Ufumu Na. 35.
Mph. 20: Gwiritsirani Ntchito Mwaŵi Umenewu! Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1996, masamba 21-3.
Mph. 15: “Kodi Ndikati Chiyani?” Kukambitsirana ndi omvetsera. Ŵerengani ndime yoyamba patsamba 8 m’buku la Kukambitsirana, longosolani mmene bukulo lakonzedwera kutithandiza kuchitira umboni mogwira mtima pamitu yosiyanasiyana ya Baibulo. Chitirani chitsanzo mwa ulaliki umodzi kapena maulaliki aŵiri okonzedwa bwino.
Nyimbo Na. 151 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 24
Mph. 8: Zilengezo zapamalopo.
Mph. 15: Khalidwe Labwino pa Phunziro la Buku la Mpingo. Timayamikira mzimu wakuchereza wa mabanja amene amatilola kuchitira phunziro la buku m’nyumba zawo. Zimenezo zingafune kukonzekera ndithu ndiponso zimawavutitsa. Pamene tili paphunzirolo, tizikhala a khalidwe labwino ndi aulemu, ndi kusamalanso zinthu zonga zotsatirazi: (1) Tizipukuta mapazi athu mosamala tisanaloŵe, kuti tisaipitse m’nyumbamo. (2) Makolo ayenera kumawayang’anira ana awo, kuti atsimikize kuti sakuchita mphulupulu ndi kutinso akhaladi m’chipinda chimene chinaperekedwa kuchitiramo phunzirolo. (3) Ngakhale kuti kaguluko kangakhale kakang’ono, ndipo ngakhale kuti mkhalidwe paphunziropo umakhala womasukirapo, umenewu uli msonkhano wampingo ndithu, ndipo tiyenera kuvala monga mmene timavalira popita ku Nyumba ya Ufumu. (4) Kucheza pambuyo pamsonkhano kuzikhala kwachidule, kuti banjalo lizitsala ndi nthaŵi yawoyawo. (5) Ngakhale kuti mwini nyumba imene phunzirolo limachitikiramo nthaŵi zina angamaphikire anthu tiyi, onse ayenera kudziŵa kuti sitimayembekezera zimenezo, ndipo sizofunika.
Mph. 22: Pangani Ophunzira, Mukumawaphunzitsa. Mkulu akukambitsirana ndi ofalitsa atatu kapena anayi, namayankha mafunso ochokera m’buku la Uminisitala Wathu, masamba 88-92: (1) Kodi nchifukwa ninji kupanga maulendo obwereza kuli kofunika kuti utumiki ukhale wogwira mtima? Kodi munthu angakwanitse bwanji maulendo obwereza? (2) Kodi nchifukwa ninji timalimbikira kuyesayesa kuyambitsa maphunziro a Baibulo? Kodi tingakhale bwanji aluso pochititsa maphunziro? (3) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kutsogolera ophunzira ku gulu? Nanga tingachite bwanji zimenezo? Kaguluko kafotokozenso mmene mphatika za Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996 ndi March ndi April 1997 zawathandizira pa mfundo imeneyi.
Nyimbo Na. 160 ndi pemphero lomaliza.