Misonkhano Yautumiki ya May
Mlungu Woyambira May 4
Mph. 8: Zilengezo zapampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Mbiri Yateokrase.
Mph. 15: “Mzimu wa Yehova Uli Nafe.” Mafunso ndi mayankho. Pokambitsirana ndime 3, phatikizanipo mfundo zoyenerera zogwidwa mawu mu 1998 Yearbook.
Mph. 22: “Sankhani Nkhani Zokopa Chidwi cha Anthu.” Pendani mfundo zazikulu zankhaniyo. Fotokozani kuti ngakhale makope akale omwe akali mumkhalidwe wabwino angagaŵiridwe mwa njira imeneyi. Pemphani ofalitsa kuti asimbe nkhani zimene anagwiritsira ntchito nkupeza zotsatirapo zabwino. Chitirani chitsanzo ulaliki uli m’ndime 7.
Nyimbo Na. 212 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 11
Mph. 8: Zilengezo zapampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 12: “Kodi Mukulinganiza Kudzatani m’Chilimwe?” Mkulu akambitsirane ndi ofalitsa aŵiri kapena atatu zimene akulinganiza kudzachita m’chilimwe chikudzachi. Namasimbirana njira zimene akonza zokapezeka pamsonkhano, kuonjezera ntchito yawo mu utumiki wakumunda, kupita kuholide, kukachezera mabwenzi ndi achibale. Onsewo akuvomera kuti sadzanyalanyaza phunziro laumwini, misonkhano, utumiki wakumunda, ndipo akufotokoza mmene alinganizira kudzamatsatira ndandanda yateokrase.
Mph. 25: “Maphunziro a Baibulo Enanso Akufunika.” Kambani nkhani yonseyo. Nkhani yokambitsirana ndi omvetsera yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Pendani ntchito ya maphunziro a Baibulo ya kwanuko. Yamikirani mpingo pambali imene ukuchita bwino. Tchulani zina zimene angachite pofuna kuyambitsa maphunziro a Baibulo ndi kuwachititsa, kuphatikizapo maphunziro abanja. Chitirani chitsanzo ndime 5 mwa kufunsa kholo lina limene limachita bwino pakuchititsa phunziro labanja. Ŵerengani ndime 8, ndi kugogomezera mfundo zisanu ndi ziŵiri zomwe zili m’menemo. Fotokozani ndime 13 mwa kupempha wofalitsa wina yemwe ngwaluso pakuchititsa maphunziro kuti asimbe mmene kulili kotheka kuphunzitsa popanda kuchedwa mosafunikira. Phatikizanipo chokumana nacho china chosonyeza mmene ena anaonera zotulukapo zabwino kwanuko.
Nyimbo Na. 48 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 18
Mph. 8: Zilengezo zapampingo. Lengezani makonzedwe a utumiki wakumunda a pawikendi.
Mph. 15: “Kodi Muli ndi ‘Munga m’Thupi’?” Mafunso ndi mayankho. Kambanipo mawu ena pa “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1987, tsamba 29.
Mph. 22: “Kuthandiza Ofalitsa Osakhazikika ndi Ofooka.” Kambani nkhani yonseyo. Mlembi akambitsirane ndi mkulu mmodzi kapena aŵiri omwe amachititsa Phunziro la Buku la Mpingo. Phatikizanipo malingaliro ena othandiza omwe angalimbikitse ofalitsa a kwanuko amene ali odumphadumpha.
Nyimbo Na. 139 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 25
Mph. 10: Zilengezo zapampingo.
Mph. 15: Zosoŵa zapampingo.
Mph. 20: Chifukwa Chimene Ndimakondera Misonkhano Yampingo. Mkulu akukambitsirana ndi kagulu ka ofika pamisonkhano nthaŵi zonse koimira osiyanasiyana mumpingomo, mwina kuphatikizapo mwamuna ndi mkazi wake, munthu wina wachikulire, ndi wachinyamata. Akufotokoza chifukwa chimene amapezekerapo nthaŵi zonse: mayanjano abwino, malangizo a Mulungu, ndi uphungu wabwino, zimene zimawathandiza kupirira mavuto a tsiku ndi tsiku ndi kukhalabe olimba mwauzimu. Mawu awo agogomezere mmene tonsefe timadalitsidwira tikamapezeka pamisonkhano nthaŵi zonse.
Nyimbo Na. 222 ndi pemphero lomaliza.