Mbiri Yateokalase
◼ Mboni za Yehova zinalembetsedwa mwalamulo ku Bulgaria pa October 7, 1998. Pamodzi ndi ofalitsa 946 amene ali kumeneko, tikuthokoza Yehova chifukwa cha nkhaniyi.
◼ Pa October 12, 1998, boma la Latvia linaloleza kuti mipingo yoyambirira iŵiri mwa mipingo 21 imene ili m’dzikolo ilembetse.
◼ Abale ku France akupirira pa ntchito yawo yolalikira Ufumu mosasamala kanthu za chitsutso. Mu November ndi December, ndawala yoyesa kuchititsa anthu a dzikolo kulingalira za Baibulo inalinganizidwa pa kugaŵira mwapadera bolosha la Buku la Anthu Onse. Pafupifupi anthu a pabeteli 50 a ku France asamukira ku Britain kuti akathandize ntchito yosindikiza ndi kutumiza mabuku pa nthambiyo, pamene anthu otsala 250 a banja la Beteli ya ku France ndi abale amene ali m’dzikolo akupitiriza kutumikira mwachimwemwe m’mikhalidwe yanthaŵi zonse.