Misonkhano ya Utumiki ya March
Mlungu Woyambira March 1
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph. 17: “Chikumbutso cha Imfa ya Kristu Chapadziko Lonse.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo mfundo za mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 1997, masamba 11-12, ndime 10-14. Gogomezerani mmene chikondi chachikulu cha Yehova chinam’sonkhezerera kutipatsa dipo.
Mph. 20: Zifukwa Zabwino Zochitira Upainiya Wothandiza m’April ndi m’May. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera yokambidwa ndi woyang’anira utumiki, akumalimbikitsa onse kuganiza mofatsa zochita upainiya wothandiza. Pendani kusintha kwa maola a apainiya okhazikika ndi othandiza, monga mmene zilili mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 1999, patsamba 7. Kusintha kumeneku kuyenera kupangitsa anthu ambiri kukhala ndi mwayi wochita utumiki wa nthaŵi zonse. Fotokozani mmene kuyamikira kwathu nsembe ya Kristu kuyenera kutisonkhezera kuchita changu m’kulalikira anthu ena. (2 Akor. 5:14, 15) Chaka chino Chikumbutso chidzachitika tsiku loyamba la mwezi wa April. N’chisonkhezero chabwinodi kwa ofalitsa za Ufumu onse kupatula mwezi wonse kuti achite utumiki wowonjezereka! Pendani mfundo zosankhidwa mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 1997 ndi March 1998 zokhudza utumiki waupainiya wothandiza. Lingalirani njira zomwe mungatsatirire ndandanda zomwe zinaperekedwa monga chitsanzo. Fotokozani makonzedwe a pampingopo a utumiki, omwe amapereka nthaŵi yochuluka yochita utumiki ndi anthu ena. Limbikitsani ofalitsa kutenga mafomu a upainiya wothandiza pamapeto a msonkhano.
Nyimbo Na. 44 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 8
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 20: “Aitaneni Kuti Afike.” Mafunso ndi mayankho. Gogomezerani kufunika koitanira anthu okondwerera chatsopano ku misonkhano ya mpingo nthaŵi zonse. Sonyezani chitsanzo cha kukambirana ndi munthu wokondwerera, gwiritsani ntchito nkhani ya m’buku la Chidziŵitso, patsamba 159, ndime 20, ndi masamba 162-3, ndime 5-8. Limbikitsani aliyense kuyesetsa kwambiri kuthandiza ophunzira Baibulo ndi okondwerera ena kufika ku Chikumbutso pa April 1. Onse ayenera kuyamba mlungu uno kuitanira anthu okondwerera ku Chikumbutso.
Mph. 15: “Mmene Banja Limachitira Zinthu Pamodzi Kuti Onse Azitengamo Mbali Mokwanira—Pa Misonkhano ya Mpingo.” Kukambirana kwa banja. Pamene akukamba mfundo zazikulu za m’nkhaniyi, akambirane mmene angakonzekerere misonkhano monga banja. Akambirane njira zimene angathandizirane wina ndi mnzake kutengamo mbali ndiponso zimene ayenera kuchita kuti banja lidzifika pamisonkhano nthaŵi yabwino.
Nyimbo Na. 62 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 15
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Pendani nkhani yakuti “Kodi Mudzapezekapo?”
Mph. 15: “Atumiki Otumikira Amachita Ntchito Yofunika.” Nkhani yokambidwa ndi mtumiki wotumikira waluso. Pendani mfundo zazikulu zofotokozedwa m’buku la Olinganizidwa, masamba 57-9. Fotokozani mmene atumiki otumikira amathandizira mpingowo.
Mph. 20: “Pologalamu Yatsopano Yomanga Nyumba za Ufumu.” Pendani ndime 1 mpaka 12 kuchokera m’mphatika mwa mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 68 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 22
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lengezani mayina a anthu amene adzachite upainiya wothandiza m’April. Fotokozani kuti sikuchedwa kupereka fomu yofunsira upainiya pakali pano. Longosolani ndandanda yonse ya misonkhano yomwe yakonzedwa yokonzekera utumiki wakumunda m’April. Limbikitsani onse kutsatira ndandanda ya kuŵerenga Baibulo ya Chikumbutso ya March 27–April 1, monga alembera m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—1999 ndi pa Kalenda ya 1999.
Mph. 15: Konzekerani Chikumbutso. Nkhani. Onse ayenera kupanga makonzedwe kuti athandize ophunzira Baibulo ndi anthu ena okondwerera kudzafika pa Chikumbutso. Achatsopano angakhale asakudziŵa amene ali oyenera kudya zizindikiro kapena tanthauzo la chochitikachi. Pendani zomwe zinalembedwa mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 1996, masamba 6-8, ndipo sonyezani mmene tingathandizire wokondwerera chatsopano kuzindikira tanthauzo ndi cholinga cha phwando limeneli. Malizani ndi kupenda “Zokumbutsa za Chikumbutso” ndipo fotokozani makonzedwe a mpingowo a Chikumbutso.
Mph. 20: “Pologalamu Yatsopano Yomanga Nyumba za Ufumu.” Pendani ndime 13 mpaka 24 kuchokera m’mphatika mwa mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 92 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 29
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Akumbutseni onse kupereka malipoti autumiki wakumunda a March. Mwezi wa April tidzagaŵira masabusikiripishoni a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kapena makope a magaziniwo. Sonyezani magazini atsopano, tchulani nkhani zimene angaonetse anthu pamene akugaŵira, ndipo tchulaninso mfundo zina zokambirana. Onse ayenera kuyenda ndi bolosha la Mulungu Amafunanji ndi kuligwiritsa ntchito kuyambitsira maphunziro a Baibulo ndi anthu okondwerera.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 18: Kodi ndi Motani Mmene Tiyenera Kuchitira ndi Uphungu? Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Tonse tingapatsidwe uphungu wonena za maganizo anthu, makhalidwe, mayanjano, kapena kutenga mbali mu zochitika za mumpingo. Nthaŵi zina timakana uphungu kapena timakhumudwa. Kufunitsitsa kulabadira uphungu ndi kuugwiritsa ntchito n’kofunika pamoyo wathu wauzimu. Pendani mfundo zofunika kwambiri zogogomezera chifukwa chake tiyenera kulabadira ndi kuyamikira uphungu.—Onani Nsanja ya Olonda ya April 1, 1987, masamba 27-30.
Nyimbo Na. 118 ndi pemphero lomaliza.