Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/99 tsamba 2
  • Misonkhano ya Utumiki ya May

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano ya Utumiki ya May
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira May 3
  • Mlungu Woyambira May 10
  • Mlungu Woyambira May 17
  • Mlungu Woyambira May 24
  • Mlungu Woyambira May 31
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 5/99 tsamba 2

Misonkhano ya Utumiki ya May

Mlungu Woyambira May 3

Nyimbo Na. 7

Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Mbiri Yateokalase.

Mph. 17: “Phunzitsani Ena Kuti Apindule.” Nenani mawu oyamba m’mphindi yosapitirira imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mogwiritsa ntchito mutu 13 wa m’buku la Chidziŵitso, sonyezani mmene anthu athandizidwira chifukwa chophunzira, kumvetsetsa, ndi kugwiritsa ntchito mapulinsipulo a Baibulo.

Mph. 20 : “Njira Zofutukulira Utumiki Wanu.” Akulu aŵiri akambirane nkhaniyi poyankha mafunso ofunsidwa ndi anthu osiyanasiyana mwa omvetsera. Wofalitsa wachinyamata, banja, ndi mbale amene anapuma pantchito akufunsa za njira zimene angafutukulire utumiki wawo. Iwo akupereka malingaliro othandiza kuchokera m’nkhaniyi ndiponso m’chaputala 9 m’buku la Uminisitala Wathu, pamutu wonena kuti “Kodi Zonulirapo Zanu Zauzimu Zamtsogolo Nzotani?” pamasamba 116-18. Ofalitsa akuyamikira nkhani zothandiza zimene Sosaite imapereka zosonyeza mmene tingafutukulire ntchito ya utumiki patsogolopa.

Nyimbo Na. 11 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira May 10

Nyimbo Na. 15

Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 12: Kodi Mukulingalira Kudzachita Chiyani m’Chilimwe? Banja lipende makonzedwe awo okapezeka pamsonkhano wachigawo, kuchita upainiya wothandiza, kupita kutchuthi, ndi kokasanguluka. (Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 1998, patsamba 7.) Akukambirana mmene angakonzere ndi mmene angachitire umboni wamwamwayi, ndipo achite chitsanzo chosonyeza mmene angayambire makambitsirano. Gogomezerani kufunika kochita phunziro laumwini ndi phunziro la Baibulo la banja, kupita kumisonkhano ya mpingo pamene mwapita kwina kulikonse, komanso kutumiza malipoti antchito ya utumiki wakumunda kumpingo wa kwanu. Banja lisimbe zokumana nazo zabwino zimene linakumana nazo pamene linachezera mipingo ina komanso chimwemwe chomwe linapeza. Apende njira za mmene angakhalire ochereza alendo kwa aliyense amene angabwere mumpingo.

Mph. 25: “Msonkhano Wachigawo wa 1999 wa ‘Mawu Aulosi a Mulungu.’” (Ndime 1-8) Mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndime zonse. Gogomezerani chifukwa chake kuli kofunika kupezeka pa msonkhano wonse, kuyambira tsiku Lachisanu.

Nyimbo Na. 19 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira May 17

Nyimbo Na. 27

Mph. 10: Zilengezo za pampingo.

Mph. 15: “Konzekereranitu!” Nkhani yopenda zochitika zonse zateokalase zomwe zakonzedwa kumaloko m’miyezi ingapo ikudzayi. Limbikitsani onse kuika chizindikiro pa madeti ameneŵa pamakalendala awo ndipo asalole zinthu zina kudodometsa.

Mph. 20: “Msonkhano Wachigawo wa 1999 wa ‘Mawu Aulosi a Mulungu.’” (Ndime 9-16) Mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndime zonse 18-21. Gogomezerani kufunika kotsatira malangizo a Sosaite obweretsa chakudya chathu chamasana tsiku lililonse la msonkhano. Gwiritsani ntchito malemba ogwidwa mawu ndi osonyezedwawo pogogomezera chifukwa chake kavalidwe, kapesedwe, ndi khalidwe zili nkhani zofunika kuzisamalira kwambiri.

Nyimbo Na. 29 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira May 24

Nyimbo Na. 41

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Lengezani makonzedwe apadera a utumiki wakumunda pa May 31. Pendani kalata ya ku Sosaite ya October 15, 1998, yonena za fomu Yobwerera kwa Amene Anasonyeza Chidwi ya (S-43). Fotokozani mmene zimenezi zingatithandizire kubwerera kwa amene asonyeza chidwi pamene tilalikira mwamwayi komanso pamene tikumana ndi anthu amene amalankhula chilankhulo china. Limbikitsani ofalitsa kugwiritsa ntchito bwino mafomu ameneŵa.

Mph. 12: Bokosi la Mafunso. Nkhani yokambidwa ndi mkulu.

Mph. 18: Kodi Tikugwira Nawo Ntchito Yolekanitsa? Nkhani yolimbikitsa yokambidwa ndi woyang’anira utumiki, yochokera mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1997, masamba 30-1.

Nyimbo Na. 32 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira May 31

Nyimbo Na. 43

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani onse kupereka malipoti autumiki wakumunda a May. Pendani mabuku ogaŵira mu June. Pamene mukugaŵira buku la Chidziŵitso, mungaphatikizepo buku lililonse la masamba 192 amene mpingo uli nawo ambiri m’sitoko. Sonyezani chitsanzo cha ulaliki.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 15: Cholakwika n’Chiyani ndi Chipembedzo Changa? Kukambirana kwa atumiki otumikira aŵiri. Timakumana ndi anthu ambiri amene angamvetsere choonadi ndipo amasirira Mboni za Yehova. Komabe, mgwirizano umene uli pa iwo ndi tchalitchi chawo umawalepheretsa. Zimawavuta kukhulupirira kuti ndife tokha amene tili ndi chipembedzo choona ndi kuti mapembedzedwe awo ndi onyenga. Ichi ndicho kwenikweni chimene chimawalepheretsa kupita patsogolo mwauzimu. Abale akupenda mfundo zisanu ndi imodzi zotchulidwa patsamba 275 za m’buku la Kukambitsirana, zimene zimasonyeza bwino kuti zipembedzo zina sizitsatira Baibulo. Limbikitsani omvetsera kugwiritsa ntchito mfundo zimenezi mwaluso pothandiza anthu oona mtima kuti apende zikhulupiriro za zipembedzo zawo.

Nyimbo Na. 50 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena