Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira August 14
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Thirirani ndemanga pa lipoti la utumiki wakumunda wa May la dziko lino ndi la mpingo wanuwo. Kwatsala mapeto a mlungu aŵiri okha kuti mwezi wa August uthe, chotero limbikitsani aliyense kuchita nawo utumiki mweziwu usanathe. Pendani ndandanda ya misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda kumapeto a mlungu.
Mph. 15: “Menyani Nkhondo Yabwino ya Chikhulupiriro.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Wonjezeranipo ndemanga za m’buku la Uminisitala Wathu masamba 44-5, za mmene ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo amalinganizira ntchito ya utumiki wakumunda ya magulu awo ndiponso mmene amathandizira aliyense amene akufuna kuthandizidwa kuti azichita nawo utumiki ndi kupereka lipoti la utumiki wawo mokhazikika.
Mph. 18: Mmene Kupita ku Sukulu Kungakuthandizireni. Bambo akulankhula ndi ana ake kuwathandiza kuzindikira chifukwa chake maphunziro akudziko ali ofunika. (Onani buku la Achichepere, masamba 133-9.) Achinyamata ambiri amaganiza kuti kupita kusukulu n’chinthu chovuta kwambiri m’nthaŵi ya anthu opanda khalidweyi. Sakhalanso achidwi, amati zimene akaphunzire sizothandiza kwenikweni. Bambo apende mfundo za m’Malemba ndiponso zifukwa zikuluzikulu zosonyeza kufunika kophunzira mokwanira maphunziro akudziko. Alimbikitse ana ake kuphunzira ndi kumvetsera m’kalasi.
Nyimbo Na. 127 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 21
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Onetsani chitsanzo cha utumiki wakumunda chokonzekeredwa bwino chosonyeza mmene tingayankhire funso lakuti: “Kodi n’chifukwa ninji Mulungu wa chikondi walola kuvutika kupitirizabe kwa nthaŵi yaitali?” (Buku la Kukambitsirana, masamba 224-225) Limbikitsani aliyense kuchita nawo utumiki mapeto a mlungu uno.
Mph. 8: “Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera.” Nkhani. Lengezani tsiku la msonkhano wapadera ukudzawo ngati mukulidziŵa, ndipo limbikitsani onse kudzakhalapo tsiku lonse. Limbikitsani ofalitsa kuitanira anthu amene asonyeza chidwi posachedwapa ndiponso ophunzira Baibulo.
Mph. 25: “Kodi Mukupindula?” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 152 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 28
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani onse kupereka malipoti autumiki wakumunda a August. Ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo aonetsetse kuti aliyense wa m’gulu lawo wapereka malipoti kuti onse akhale atasonkhanitsidwa pofika pa September 6.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20: “Misonkhano Imapindulitsa Achinyamata.” Kukambirana mwa mafunso ndi mayankho kochitidwa ndi mkulu. Pokambirana ndime 8, pendani zina zimene zingathandize kuti munthu azimvetsera ndi kukhala watcheru pamisonkhano. (Onani Galamukani! ya October 8, 1998, masamba 23-24.) Limbikitsani makolo kutsimikiza mtima kuti ana awo azipezeka pamisonkhano yonse mokhazikika.—Onani chokumana nacho cha mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 1997, patsamba 25.
Nyimbo Na. 176 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 4
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Pemphani ofalitsa anene zokumana nazo zimene anapeza mwa kuchitira umboni wa mwamwayi popita kumsonkhano, ali pamsonkhano, kapena akuchokera kumsonkhano wachigawo.
Mph. 10: Nthaŵi Yathu N’njapadera. Nkhani yokambidwa ndi mkulu, kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1996, masamba 22-3.
Mph. 20: “Kodi Mukupirira?” Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Limbikitsani onse kulingalira za mmene apambanira mwa kusonyeza chipiriro mu utumiki wachikristu. Ngati pali kufooka, ndiye kuti m’pofunika kudzilimbitsa mwauzimu. Phatikizanipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1999, masamba 20-1, ndime 17-21. Pemphani ofalitsa aŵiri kapena atatu amene apirira mokhulupirika kwa zaka zambiri kusimba zimene iwo akuchita kuti athe kupitirizabe kupirira.
Nyimbo Na. 206 ndi pemphero lomaliza.