Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira April 14
Mph. 7: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Nkhani yokambidwa ndi mkulu.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 18: “Oonekera Monga Mauniko.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Malizani ndi nkhani ya mphindi zisanu yochokera mu Nsanja ya Olonda ya June 1, 1997, masamba 14-15 ndime 8-13. Gogomezerani chifukwa chake sitibisira anthu ena uthenga wa Ufumu.
Nyimbo Na. 134 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 21
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: “Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa Chaka cha 2003 Wakuti ‘Patsani Mulungu Ulemerero.’” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi mlembi wa mpingo. Yamikirani onse kuchokera pansi pa mtima chifukwa chokonzekera msonkhano mofulumira.
Mph. 20: “Ilandireni.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo kufunsa wofalitsa mmodzi kapena aŵiri amene akugwiritsira ntchito bwino mphatso yosakwatira kapena yosakwatiwa kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu. Afunseni chimene chimawathandiza kuti akhale osangalala mu utumiki wawo.
Nyimbo Na. 35 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 28
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wakumunda a April. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zili patsamba 8, sonyezani zitsanzo ziŵiri za maulaliki a Nsanja ya Olonda ya April 15 ndi Galamukani! ya April 8. Paulaliki uliwonse, magazini onse aŵiri ayenera kugaŵiridwa ngakhale kuti ndi imodzi yokha imene mwachitira chitsanzo.
Mph. 15: “Kodi Mumalemekeza Malo Anu Olambirira?” Ikambidwe ndi mkulu. Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
Mph. 20: “Maulendo Obwereza Amathandiza Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi mkulu ndipo agwiritsire ntchito mafunso omwe aperekedwa. Pemphani omvera kufotokoza zokumana nazo zachidule za utumiki wakumunda zimene zikuchirikiza mfundo zomwe zikukambidwa. Pokambirana ndime 5, chitani chitsanzo cha zimene zinachitikadi m’gawo pamene phunziro la Baibulo linayambika.
Nyimbo Na. 89 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 5
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mwa kugwiritsira ntchito mfundo zili patsamba 8, sonyezani zitsanzo ziŵiri za maulaliki ogaŵira Nsanja ya Olonda ya May 1 ndi Galamukani! ya April 8.
Mph. 20:“Mmene Choonadi Chimatimasulira.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga zimene zili m’bokosi pa tsamba 6 mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1998. Pemphani omvetsera kuti anenepo mmene choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu chawapatsira ufulu.
Mph. 15: Lipoti Labwino Limasangalatsa. (Miy. 15:30) Nkhani yokambirana ndi omvera yosonyeza zimene mpingo unachita chifukwa cha kuyesetsa mwapadera komwe anachita mu March ndi April. Pemphani mpingo kusimba zokumana nazo zolimbikitsa zimene anali nazo m’mbali zotsatirazi: (1) kuthandiza munthu wachidwi kupezeka pa Chikumbutso, (2) kutumikira monga mpainiya wothandiza, (3) kulimbikitsa wofalitsa wofooka kuyambanso kugwira ntchito ndi mpingo, (4) kuthandiza watsopano kuyamba kufalitsa, ndi (5) kukulitsa chidwi cha omwe anafika pa Chikumbutso. Uzani anthu ena kukonzekera zina mwa ndemangazi nthaŵi ikadalipo. Yamikirani ndipo limbikitsani onse kupitirizabe kuyesetsa pambali zimenezi m’tsogolo.
Nyimbo Na. 126 ndi pemphero lomaliza.