Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/05 tsamba 3-5
  • Kumvera Lamulo la Mulungu Losala Magazi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kumvera Lamulo la Mulungu Losala Magazi
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 12/05 tsamba 3-5

Kumvera Lamulo la Mulungu Losala Magazi

1 M’zaka zochepa zapitazi, anthu ambiri aona kuti m’pofunika kukhala ndi chikalata cholemberatu mtundu wa chithandizo ndiponso mankhwala amene iwowo angavomere kulandira kuchipatala. Makhoti ambiri azindikira kuti odwala ali ndi ufulu wovomerezeka mwalamulo, wosankha chithandizo cha mankhwala chimene iwowo angakonde, ngakhale ngati atachita zimenezi mosutsana ndi azachipatala ndiponso akuluakulu azamalamulo.

2 Ofesi ya nthambi yatulutsa chikalata chatsopano chogwirizana ndi malamulo a dziko la Malawi. Dzina lake ndi Chikalata Chosasinthika Chopatsa Munthu Mphamvu Yondisankhira Thandizo la Mankhwala (DPA). Chikalata chatsopanochi chaphatikiza mfundo zake ndi mfundo zofunika za m’khadi la Chidziwitso kwa Madokotala/Chowamasulira ku Mlandu (AMD) n’kupanga chikalata chovomerezeka ndi malamulo. N’chifukwa chake chikalata cha DPA chidzalowa m’malo mwa khadi la AMD, limene tisiya kuligwiritsa ntchito. Khadi lakale la AMD linkafotokoza za zolinga zathu pokana kuikidwa magazi koma silinkanena zambiri zokhudza mtundu wina wa chithandizo cha mankhwala chimene tingalole kulandira. Chikalata chatsopanochi chikukupatsani mwayi wolola kapena kukana mitundu ina ya chithandizo ndi njira zinanso zokuthandizirani nazo ndiponso chikukupatsani mwayi wopereka malangizo a momwe angakusamalireni mutadwala polemba zilembo zoimira mayina anu. Chikalata cha DPA achipanga kuti chisamathe mphamvu m’kupita kwa nthawi ndipo ndi choti chidzikuimirani pa zofuna zanu ngati mutapita kumayiko ena. Sikofunikira kumalemba chikalata china chaka ndi chaka.

3 Mlembi wa mpingo akufunikira kumapereka chikalata cha DPA kwa ofalitsa onse amene abatizidwa m’kati mwa chaka. Oyang’anira maphunziro a buku angathe kuthandiza ofalitsa a m’gulu lawo kulemba bwino chikalata cha DPA, ngati angafunikire kuthandizidwa.

4 Tsopano tikambirana zigawo za m’chikalata chatsopano cha DPA. Chonde tengani chikalata chanu.

5 Pa mfundo 1, lembani bwinobwino dzina lanu lonse pamzere wosalemba kanthuwo.

6 Mfundo 2, m’pofuna kutsimikizira kuti, monga wa Mboni za Yehova, mwalamula kuti (1) zivute zitani, asakuikeni magazi athunthu kapena zigawo zake zikuluzikulu (zomwe ndi maselo ofiira, maselo oyera, maselo othandiza magazi kuundana ndi madzi a m’magazi) ndipo (2) mwakananso kuperekeratu magazi anu kuti asungidwe kaye n’cholinga choti adzakupatseninso magazi omwewo kapena adzawapereke kwa munthu wina (madokotala amatcha zimenezi PAD, kutanthauza Predeposited Autologous Donation). Mfundo zimenezi zalembedwa ndi cholinga chofuna kuthandiza azachipatala kumvetsetsa kuti simukukana kuthiridwa magazi pachifukwa chakuti magaziwo angakubweretsereni matenda m’thupi mwanu kapena kuti chithandizo chimenechi n’choipa ayi, koma kuti mukukana kwenikweni pachifukwa cha chipembedzo. Choncho, pokambirana ndi ogwira ntchito kuchipatala, n’kofunika kutsindika kuti mwasankha choncho chifukwa chakuti mwatsimikiza mtima kumvera lamulo la Yehova lakuti ‘musale mwazi.’—Mac. 15:29.

7 Mfundo 3 ikufotokoza zogwiritsa ntchito tizigawo ting’onoting’ono ta magazi pokupatsani thandizo. Posankha zochita, werengani kaye mfundo za m’Baibulo zofotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2004, masamba 22 mpaka 24 ndi 29 mpaka 31, ndipo mupemphere kaye musanasankhe zimenezi. (Ngati mulibe magazini imeneyi, kapena magazini alionse amene atchulidwa m’nkhani ino, mungachite bwino kukabwereka magazini amenewa kwa wina aliyense mu mpingo wanu kapena kwa munthu woyandikana naye amene amasunga magazini akale.) Nkhani yolola kapena kukana kulandira kachigawo kena kakang’ono ka magazi, ndi nkhani yosankha nokha malinga ndi chikumbumtima chanu. Komabe, ioneni kuti ndi nkhani yaikulu kwambiri chifukwa chakuti ikukhudza ubwenzi wanu ndi Yehova. [Werengani Aroma 14:12 ndi Agalatiya 6:5.] Malemba amenewa akusonyeza kuti munthu aliyense adzazengedwa mlandu ndi Yehova pa zimene angachite motsogozedwa ndi chikumbumtima chophunzitsidwa Baibulo. Choncho, m’pofunika kukhala ndi chikumbumtima chophunzitsidwa bwino kuti chizititsogolera ndipo tisamangotengera zomwe ena asankha.

8 Pambuyo poganizira za nkhani ya tizigawo ting’onoting’ono ta magazi imeneyi n’kupemphera kwa Yehova, lembani pachikalata chanu cha DPA zilembo zoimira mayina anu. (Mwachitsanzo, ngati dzina lanu lili Jemusi Alikis Banda, mulembe JAB; ngati ndinu Foloresi Yakobo Mwale, mulembe FYM.) Lembani zilembo zoyambirira za mayina anuzo mu mizere yaing’ono patsogolo pa mawu amene mwasankha pa mfundo zotsatirazi za pa chikalata chanu cha DPA:

(a) Ndikukana zonse. Zimenezi zikutanthauza kuti mukukana tizigawo tonse ting’onoting’ono ta magazi.

(b) Ndikukana zonse kupatulapo: . . . Ngati mwasankha mbali imeneyi, lembani bwinobwino tizigawo ting’onoting’ono ta magazi timene mungalandire.—Onani Nsanja ya Olonda ya June 15, 2004, tsamba 30, ndime 2 ndi 3.

(c) Mwina ndingalole kulandira tizigawo tina ting’onoting’ono ta magazi, koma m’pofunika kukambirana ndi ineyo mfundo zake zonse ngati sindinakomoke kapena ndi wondiimira pa za thandizo la mankhwala ngati sindikutha kulankhula. Ngati simukufuna kupatsa wokuimirani pa za thandizo la mankhwala mphamvu yosamalira udindo umenewu kapena ngati wokuimirani pa za thandizo la mankhwala sakufuna kukusankhirani zimenezi, khwatchani mawu akuti “kapena ndi wondiimira pa za thandizo la mankhwala ngati sindikutha kulankhula,” kenako lembani zilembo zoimira mayina anu pafupi ndi mawu okhwatchidwawo.

CHIDZIWITSO: Ngati zimene zili pamfundo 3 si zimene mukufuna kusankha, gwiritsani ntchito mfundo 6 (mizere yosalemba kanthu) kufotokoza zimene mukufuna, mwachitsanzo kunena kuti: “Ndikuvomereza tizigawo ting’onoting’ono tonse ta magazi” kapena “Ndikuvomereza tizigawo ting’onoting’ono tonse ta magazi kupatulapo:,” kenako lembani tizigawo ta magazi tokhato timene mukukana. Kumapeto kwa chiganizo chili pamfundo 3 chakuti “Za tizigawo ting’onoting’ono ta magazi: [lembani zilembo zoimira mayina anu pa zimene mukufuna],” mungalembe kuti “Onani mfundo 6 m’munsimu.”

9 Mfundo 4 ikufotokoza za thandizo la mankhwala lofuna kuti magazi anu amene angachotsedwe m’thupi mwanu kwa kanthawi agwiritsidwe ntchito. Posankha zochita, werengani kaye mfundo za m’Baibulo zofotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2000, masamba 30 ndi 31, ndipo mupemphere kaye musanasankhe zimenezi. Ndiye motsogozedwa ndi chikumbumtima chanu chophunzitsidwa Baibulo, lembani pa chikalata chanu cha DPA zilembo zoimira mayina anu pa iliyonse ya mbali zotsatirazi imene mukufuna:

(a) Ndikukana Zonse. Zimenezi zikutanthauza kuti mwakana njira zonse zogwiritsa ntchito magazi anu, kusiyapo kukutengani magazi ochepa chabe kuti akawapime.

(b) Ndikukana zonse kupatulapo: . . . Ngati mwasankha mbali imeneyi, lembani bwinobwino thandizo la mankhwala limene mudzalola lofuna kuti magazi anu amene angachotsedwe m’thupi mwanu kwa kanthawi agwiritsidwe ntchito.—Onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 2000, tsamba 31, ndime 1 mpaka 3.

(c) Mwina ndingalole kulandira zithandizo zina zofuna magazi anga omwe, koma m’pofunika kukambirana ndi ineyo mfundo zake zonse ngati sindinakomoke kapena ndi wondiimira pa za thandizo la mankhwala ngati sindikutha kulankhula. Ngati simukufuna kupatsa wokuimirani pa za thandizo la mankhwala mphamvu yosamalira udindo umenewu kapena ngati wokuimirani pa za thandizo la mankhwala sakufuna kukusankhirani zimenezi, khwatchani mawu akuti “kapena ndi wondiimira pa za thandizo la mankhwala ngati sindikutha kulankhula,” kenako lembani zilembo zoimira mayina anu pafupi ndi mawu okhwatchidwawo.

CHIDZIWITSO: Ngati zimene zili pamfundo 4 si zimene mukufuna kusankha, gwiritsani ntchito mfundo 6 (mizere yosalemba kanthu) kufotokoza zimene mukufuna, mwachitsanzo kunena kuti: “Pondipanga opaleshoni, ndikulola kundipatsa thandizo lonse la mankhwala lofuna kuti magazi anga omwe agwiritsidwe ntchito” kapena “Pondipanga opaleshoni, ndikulola kundipatsa thandizo lonse la mankhwala lofuna kuti magazi anga omwe agwiritsidwe ntchito kupatulapo:,” kenako lembani thandizo la mankhwala lokhalo limene mukukana. Kumapeto kwa chiganizo chili pamfundo 4 chakuti: “Za zithandizo za mankhwala zofuna kuti magazi anga omwe agwiritsidwe ntchito, zosaphatikizapo zotenga magazi okayeza pofuna kudziwa matenda: [lembani zilembo zoimira mayina anu pa zimene mukufuna],” mungalembe kuti “Onani mfundo 6 m’munsimu.”

Mfundo 3(c) ndi 4(c): Zosankha zanu n’zofunika kwambiri, chifukwa zimene wokuimirani anganene motsindika kwa achipatala ndi ena ngati simukutha kulankhula ndi zosankha zanu zilizonse ndiponso zofuna zanu zokhazo zimene munamuuza pasadakhale pokambirana nkhani zimenezi.

10 Mfundo 5 ikufotokoza za nkhani yothetsa moyo wa munthu. Posankha zochita, werengani kaye Galamukani! ya November 8, 1991, masamba 24 mpaka 30, ndipo mupemphere kaye musanasankhe zimenezi. Ndiye motsogozedwa ndi chikumbumtima chanu chophunzitsidwa Baibulo, lembani pa chikalata chanu cha DPA zilembo zoimira mayina anu pa imodzi ya mbali zotsatirazi imene mwasankha. Ngati m’pofunikira kutero, mungafotokoze zosankha zanu pamfundo 6.

(a) Sindikufuna kuti moyo wanga autalikitse ngati, malinga n’kuona kwawo achipatala, akutsimikiza kuti palibe chiyembekezo choti ndichira.

(b) Ndikufuna kuti moyo wanga autalikitse mmene angathere malinga ndi zimene malamulo a chipatala amalola, ngakhale kuti zimenezi zingafune kuti ndikhale kumakina ondithandiza kukhala wamoyo zaka zambiri.

11 Pa mfundo 6, lembani bwinobwino malangizo ena okhudza thandizo la mankhwala, monga mankhwala amene mukulandira panopa, mankhwala osagwirizana ndi thupi lanu, ndi matenda anu.

12 M’madanga ake amene aperekedwa, lembani bwinobwino mayina, maadiresi, ndi manambala a foni a munthu woyamba wokuimirani pa za thandizo la mankhwala ndi wokuimirani wachiwiri pa za thandizo la mankhwala. Amenewa akhale anthu amene mumawakhulupirira ndiponso amene akumvetsa zikhulupiriro zanu ndi mfundo zimene mumayendera.

13 Chikalata cha DPA chiyenera kulembedwa bwinobwino muli kunyumba. Koma payenera kukhala mboni ziwiri posaina chikalatacho. Mboni zimenezi asakhale okuimirani pa za thandizo la mankhwala.

14 Kudzera mwa gulu la “mdindo wokhulupirika,” Yehova akutipatsa zonse zomwe timafunikira kuti timvere lamulo lake loletsa chithandizo chosalemekeza Mulungu choika munthu magazi. Tingachite bwino kwambiri ngati titaiganizira mofatsa nkhani imeneyi n’kupemphera pasadakhale ndiponso kugwiritsa ntchito zinthu zonse zimene gulu latipatsa mwachikondi chake.—Luka 12:42; Miy. 22:3; Yes. 48:17; Mac. 15:28, 29.

[Bokosi patsamba 5]

Nkhani Zofunsidwa Kawirikawiri

1. Kodi ntchito ya anthu oimira munthu wina pa za thandizo la mankhwala ndi yotani?

◼ Yankho: Amaonetsetsa kuti malangizo amene munthu angapereke onena za chithandizo cha chipatala akutsatiridwa. Kudziwa bwino chikhulupiriro ndi mfundo zimene mumayendera kudzathandiza munthu wokuimirani kutsatira bwino malangizo omwe mwalemba. Choncho, udindo woimira wina pa za thandizo la mankhwala ndi waukulu zedi.

2. Kodi muyenera kuganizira kaye za chiyani musanasankhe anthu okuimirani pa za thandizo la mankhwala?

◼ Yankho: Muyenera kuganizira kaye ngati anthu amene mwasankha akhoza kukwanitsa kugwira ntchito imeneyi ndipo angathe kudziwa zochita mogwirizana ndi chikhulupiriro ndiponso mfundo zimene mumayendera ngati a zachipatala ndi akhoti akutsutsana nazo.

3. Kodi ndi ndani amene mungasankhe kuti akhale okuimirani pa za thandizo la mankhwala?

◼ Yankho: Anthu amene mumawakhulupirira ndiponso amene amamvetsa chikhulupiriro chanu ndi mfundo zimene mumayendera, monga mkazi kapena mwamuna wanu, achibale anu, kapena anzanu apamtima. Werengani chidziwitso pa DPA chonena za amene muyenera kusankha ndi amene simuyenera kusankha kuti akhale wokuimirani pa za thandizo la mankhwala.

4. Kodi ndi nkhani zotani zimene mufunikira kukambirana ndi anthu amene mwawasankha kukhala okuimirani?

◼ Yankho: Maganizo anu pa nkhani ya tizigawo ting’onoting’ono ta magazi, njira zachipatala zokhudza kugwiritsa ntchito magazi anu omwe, nkhani za kutalikitsa moyo wanu, ndi nkhani zosiyanasiyana za thandizo la mankhwala. Tsimikizirani kuti anthu okuimiraniwo amvetsetsa malangizo amene mwalemba ndiponso amvetsa chifukwa chake mumakhulupirira zinthu zimenezo. Anthu amene mukufuna kuti akhale okuimiraniwo muyenera kukambirana nawo nkhani ngati zimenezi mukamawasankha.

5. Kodi anthu ondiimira angazengedwe mlandu chifukwa cha zinthu zimene angandisankhire?

◼ Yankho: Ayi. Ngati anthu okuimirani pa za thandizo la mankhwala achita zonse moona mtima, sangazengedwe mlandu chifukwa cha zinthu zimene akusankhirani ndiponso sangalipitsidwe ndalama chifukwa cha thandizo la mankhwala limene inuyo mwapatsidwa.

6. Kodi nditani nacho chikalata changa cha DPA ndikamaliza kuchilemba?

◼ Yankho: Musanapinde chikalatachi, pangani mafotokope ooneka bwino okapatsa wokuimirani wanu, wokuimirani wanu wachiwiri. Fotokope ina musunge inuyo. Mukhozanso kupereka fotokope imodziimodzi kwa mlembi wa mpingo wanu, achibale anu, kapena anzanu apamtima. Kenako mungapinde DPA yanu yoyamba ija kutsatira mizera yodukizadukiza kotero kuti mbali yakuti “MUSANDIIKE MAGAZI” ikhale pamwamba. Ndiyeno sungani chikalata chanu pamodzi ndi laisensi yanu ya galimoto kapena kuchiika m’chikwama chanu limodzi ndi zikalata zina zofunikira.

7. Kodi m’pofunika kukambirana ndi dokotala wanga za ondiimira pa za thandizo la mankhwala ndiponso malangizo amene ndalemba pa chikalata changa?

◼ Yankho: Inde, ngati muli ndi dokotala kapena madokotala, amene mumapitako kukalandira thandizo. Dziwitsani dokotala wanu pasadakhale ponena za wokuimirani pa za thandizo lamankhwala, ndipo kambiranani naye za malangizo amene mwalemba pa chikalata chanu amene mwakambirana ndi okuimirani. Mungagwiritse ntchito nkhani ya mu Galamukani! ya January 8, 2000, masamba 3 mpaka 11, ndi ya December 8, 1991, tsamba 28. Ngati madokotala adziwa bwino zosankha zanu, palibe dokotala amene angavute pokusamalirani. Mungapatsenso dokotola wanu fotokope ya chikalata chanu cha DPA.

8. Kodi kungakhale kofunikira kulembanso chikalata china chatsopano cha DPA pambuyo polemba choyambachi?

◼ Yankho: Ngati mukufuna kusintha chinthu china chilichonse pa chikalata chanu, monga kusintha zofuna zanu, okuimirani, adiresi, nambala ya foni, ndi zina zotero, kapena ngati chikalata chanu chasowa kapena ngati chawonongeka, kungakhale kofunika kulembanso chikalata china cha DPA. Ngakhale zina zimene mukufuna kusintha zitakhala zinthu zazing’ono, muyenerabe kulembanso chikalata china chatsopano ndi kupanga mafotokope atsopano olowa m’malo mwa mafotokope onse a chikalata choyamba chija.

9. Kodi achibale ali ndi mphamvu mwalamulo zosintha malangizo amene ali pa chikalata changa cha DPA?

◼ Yankho: Ayi. Ngati wachibale sakugwirizana ndi malangizo anu okhudza thandizo la mankhwala, alibe mphamvu mwalamulo zosintha chilichonse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena