Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Onani Mphatso ya Moyo Wanu Kuti ndi Yamtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda—2004 | June 15
    • Onani Mphatso ya Moyo Wanu Kuti ndi Yamtengo Wapatali

      “Mwazi wa Kristu . . . udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo.”​—AHEBRI 9:14.

      1. Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti timaona moyo kuti ndi wamtengo wapatali?

      MUTAUZIDWA kuti mutchule mtengo wa moyo wanu, kodi mungati ndi wa ndalama zingati? Timaona kuti moyo ndi wamtengo wapatali, kaya ukhale wathu kapena wa anthu ena. Umboni wa zimenezi ndi wakuti, timapita ku chipatala kuti tikalandire chithandizo tikadwala kapena kuti tikapimidwe pofuna kudziŵa mmene thupi lathu lilili. Timafuna kukhala ndi moyo komanso thanzi labwino. Ngakhalenso ambiri amene tili okalamba kapena olemala sitifuna kufa; timafuna kukhala ndi moyo.

      2, 3. (a) Kodi lemba la Miyambo 23:22 limatisonyeza udindo wotani? (b) Kodi udindo wotchulidwa pa Miyambo 23:22 umam’khudza motani Mulungu?

      2 Ubwenzi wanu ndi anthu ena umakhudzidwa ndi mmene mumaonera moyo. Mwachitsanzo, Mawu a Mulungu amalangiza kuti: “Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amako atakalamba.” (Miyambo 23:22) ‘Kumvera’ sikutanthauza kungomva mawu chabe; mwambiwu umatanthauza kumva ndi kutsatira zomwe zanenedwazo. (Eksodo 15:26; Deuteronomo 7:12; 13:18; 15:5; Yoswa 22:2; Salmo 81:13) Kodi Mawu a Mulungu amapereka chifukwa chotani chomvera atate ndi amayi anu? Sikuti ndi chifukwa chokha chakuti iwo ndi aakulu kuposa inu kapenanso chifukwa chakuti aona zambiri m’moyo. Chifukwa chimene Mawu a Mulunguwo akupereka n’chakuti iwo ‘anakubalani.’ Mabaibulo ena, pa vesili amati: “Tamvera atate wako amene anakupatsa moyo.” M’pake kuti ngati mumaona moyo kukhala wamtengo wapatali, mumaona kuti muyenera kumuchitira zinazake amene anakupatsani moyowo.

      3 Zoonadi, ngati ndinu Mkristu woona, mumaona kuti Gwero lake lenileni la moyo wanu ndi Yehova. Chifukwa cha iyeyo inu ‘muli ndi moyo;’ mumatha “kuyendayenda,” kuchita zinthu monga wozindikira; ndipo mungathe “kupeza mkhalidwe,” kapena kuti kukhalapo ndi moyo ndi kuganizira kapena kukonza za tsogolo lanu, kuphatikizapo moyo wopanda malire. (Machitidwe 17:28; Salmo 36:9; Mlaliki 3:11) Mogwirizana ndi Miyambo 23:22, m’poyenera ‘kumvera’ Mulungu ndi kutsatira zomwe akunena. Muyenera kukhala wofunitsitsa kudziŵa mmene iye amaonera moyo ndi kutsatira maganizo akewo m’malo motsatira mmene anthu ena amauonera.

      Lemekezani Moyo

      4. Chakumayambiriro kwa mbiri ya anthu, kodi nkhani ya kulemekeza moyo inakhala yofunika motani ?

      4 Kale kwambiri m’mbiri ya anthu, Yehova anasonyeza momveka bwino kuti safuna kuti moyo anthu azingochita nawo chilichonse chomwe akufuna (chabwino kapena choipa). Chifukwa chokwiya ndiponso chifukwa cha nsanje, Kaini anadula moyo wa mbale wake wosalakwa, Abele. Kodi mukuganiza kuti Kaini anali ndi ufulu wochita nawo zimenezo moyo? Mulungu sanaganize choncho. Anauza Kaini kuti afotokoze chifukwa chomwe anachitira zimenezo. Mulungu anati: “Wachita chiyani? Mawu a mwazi wa mphwako andifuulira ine kunthaka.” (Genesis 4:10) Onani kuti mwazi wa Abele womwe unali kunthaka unaimira moyo wake, womwe anaudula mwankhanza, ndipo unali kufuulira Mulungu kuti abwezere.​—Ahebri 12:24.

      5. (a) Kodi Mulungu analetsa chiyani m’masiku a Nowa, ndipo lamulo lakelo linakhudza ndani? (b) Kodi lamulo limeneli linali lofunika kwambiri m’njira yotani?

      5 Chigumula chitapita, mtundu wa anthu unayambiranso ndi anthu asanu ndi atatu okha. M’mawu ake okhudza anthu onse, Mulungu anavumbula mfundo zinanso zosonyeza mmene iye amaonera moyo ndi magazi. Iye ananena kuti anthu angathe kudya nyama, koma anaika lamulo ili: “Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo. Koma nyama, mmene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye.” (Genesis 9:3, 4) Ayuda ena amati mawu ameneŵa amatanthauza kuti anthu sankayenera kudya nyama kapena magazi a nyama yomwe idakali ndi moyo. Koma pambuyo pake zinaoneka kuti Mulungu anali kuletsa kudya magazi ngati chakudya. Kuwonjezera pamenepo, lamulo limene Mulungu anapereka kudzera mwa Nowa linali lofunika kwambiri pokwaniritsa cholinga Chake chapamwamba chokhudza magazi. Cholinga chimenechi n’chimene chinadzathandiza anthu kupeza moyo wosatha.

      6. Kudzera mwa Nowa, kodi Mulungu anagogomezera motani kuti amaona moyo kukhala wamtengo wapatali?

      6 Mulungu anapitiriza kuti: “Mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; pa dzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi pa dzanja la munthu, pa dzanja la mbale wake wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu. Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m’chifanizo cha Mulungu Iye anam’panga munthu.” (Genesis 9:5, 6) Mungathe kuona pa lamulo limeneli, lomwe linaperekedwa kwa anthu onse, kuti Mulungu amaona kuti magazi a munthu amaimira moyo wa munthuyo. Mlengi amapatsa munthu moyo, ndipo aliyense sayenera kuchotsa moyo umenewo, womwe umaimiridwa ndi magazi. Ngati wina wapha munthu, monga mmene Kaini anachitira, Mlengi ali ndi ufulu ‘wofunanso’ moyo wa wopha mnzakeyo.

      7. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chidwi ndi lamulo lomwe Mulungu anapereka kwa Nowa pankhani ya magazi?

      7 Mwa zimene ananenazi, Mulungu anali kulamula anthu kuti asamagwiritse ntchito magazi molakwa. Kodi munaganizapo kuti n’chifukwa chiyani? Inde, kodi n’chiyani chinachititsa Mulungu kuti aziona magazi motero? Kwenikweni, yankho lake likukhudza mfundo imodzi pa mfundo zofunika kwambiri zimene Baibulo limaphunzitsa. Mfundo imeneyi ndiyo maziko a uthenga wachikristu, ngakhale kuti matchalitchi ambiri amasankha kunyalanyaza mfundo imeneyi. Kodi mfundo imeneyo ndi yotani, ndipo kodi moyo, zoganiza, komanso zochita zanu zikukhudzidwa motani ndi mfundoyi?

      Kodi Magazi Anayenera Kugwiritsidwa Ntchito Motani?

      8. M’Chilamulo, kodi Yehova ananena kuti magazi azigwiritsidwa ntchito motani?

      8 Yehova anafotokoza mfundo zinanso pankhani ya moyo ndi magazi pamene anapatsa Aisrayeli mpambo wa Malamulo. Ndi zimenezi, iye anachitanso chinthu chofunika kwambiri pokwaniritsa cholinga chake. Mwinamwake inu mukudziŵa kuti Chilamulo chinafuna kuti anthu azipereka nsembe kwa Mulungu, monga ufa, mafuta, ndi vinyo. (Levitiko 2:1-4; 23:13; Numeri 15:1-5) Panalinso nsembe za nyama. Ponena za nsembe za nyamazi, Mulungu anati: “Moyo wa nyama ukhala m’mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake. Chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israyeli, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu.” Yehova ananenanso kuti ngati munthu, monga mlenje kapena mlimi, wapha nyama kuti adye, anayenera kukhetsa magazi ake ndi kuwafotsera ndi dothi. Dziko lapansi ndi choikapo mapazi a Mulungu, ndipo mwa kuthira magazi pansi, munthuyo anali kuvomereza kuti moyo uyenera kubwezeredwa kwa Wopatsa Moyo.​—Levitiko 17:11-13; Yesaya 66:1.

      9. Kodi Chilamulo chinasonyeza kuti ntchito imodzi yokha ya magazi inali yotani, ndipo cholinga chake chinali chiyani?

      9 Lamulo limeneli sikuti linali mwambo wachipembedzo chabe wopanda tanthauzo lililonse kwa ife. Kodi mwaona chifukwa chake Aisrayeli sanayenera kudya magazi? Mulungu anati: “Chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israyeli, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu.” Kodi chifukwa chake chinali chiyani? “Ndakupatsani [mwazi] pa guwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu.” Kodi mukuona kuti zimenezi zikutisonyeza chifukwa chake Mulungu anauza Nowa kuti anthu asamadye magazi? Mlengi anasankha kuti magazi aziwaona kuti n’chinthu chofunika kwambiri, anafuna kuti magazi agwire ntchito yapadera yotha kupulumutsa miyoyo yambiri. Magazi anadzagwira ntchito yofunika kwambiri pophimba machimo (chotetezera). Motero, m’Chilamulo, ntchito imodzi yokha ya magazi yomwe Mulungu anaivomereza inali ya pa guwa lansembe potetezera miyoyo ya Aisrayeli, omwe anali kufuna kuti Yehova awakhululukire.

      10. N’chifukwa chiyani magazi a nyama sakanathandiza anthu kuti akhululukidwe machimo onse, koma kodi nsembe zomwe zinkaperekedwa m’Chilamulo zinali kuwakumbutsa chiyani anthu?

      10 Mfundo imeneyi, yogwiritsa ntchito magazi monga chotetezera, ikugwiranso ntchito m’Chikristu. Pofotokoza mbali ya Chilamulo imeneyi, imene inakonzedwa ndi Mulungu, mtumwi wachikristu Paulo analemba kuti: “Monga mwa chilamulo zitsala zinthu pang’ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo wopanda kukhetsa mwazi kulibe kumasuka.” (Ahebri 9:22) Paulo anafotokoza momveka bwino kuti nsembe zomwe zinkafunikazo sizinachititse Aisrayeli kukhala angwiro, anthu opanda uchimo. Analemba kuti: “Mu [nsembezi] muli chikumbukiro cha machimo chaka ndi chaka. Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng’ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsera machimo.” (Ahebri 10:1-4) Komabe, nsembe zoterozo zinathandiza kwambiri. Zinali kukumbutsa Aisrayeliwo kuti anali ochimwa ndipo anafunikira chinthu chinanso chowonjezera kuti akhululukidwe machimo awo onse. Komano ngati sikukanatheka kuti mwazi umene unali kuimira miyoyo ya nyama uphimbe bwinobwino machimo onse a anthu, kodi mwazi wina uliwonse ukanatha kuchita zimenezo?

      Zomwe Wopatsa Moyo Anakonza

      11. Kodi timadziŵa bwanji kuti nsembe za mwazi wa nyama zinali kuimira chinthu china?

      11 Kwenikweni Chilamulo chinali kulozera anthu chinthu chodzakwaniritsa bwino kwambiri cholinga cha Mulungu. Paulo anafunsa kuti: “Nanga chilamulo tsono?” Anayankha funsoli kuti: “Chinawonjezeka chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbewu imene adailonjezera; ndipo chinakonzeka ndi angelo m’dzanja la nkhoswe [Mose].” (Agalatiya 3:19) Mogwirizana ndi mfundoyi, Paulo analemba kuti: “Chilamulo, [chili ndi] mthunzi wa zokoma zilinkudza, osati chifaniziro chenicheni cha zinthuzo.”​—Ahebri 10:1.

      12. Ponena za magazi, kodi tikuona motani cholinga cha Mulungu chikuvumbulidwa pang’onopang’ono?

      12 Mwachidule, m’nkhaniyi taona kuti m’masiku a Nowa, Mulungu analamula kuti anthu angadye nyama ngati chakudya, koma sanayenera kudya magazi. Panthaŵi ina, Mulungu anati “moyo wa nyama ukhala m’mwazi.” Zoonadi, iye anasankha kuona kuti magazi ndi chinthu choimira moyo ndipo anati: “Ndakupatsani [mwazi] pa guwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu.” Komabe, m’kupita kwa nthaŵi cholinga cha Mulungu chinadzafotokozedwa momveka bwino. Chilamulo chinali mthunzi wa zokoma zomwe zinali m’tsogolo. Kodi zinali zinthu zotani?

      13. N’chifukwa chiyani kufa kwa Yesu kunali kofunika?

      13 Zinthu zenizeni zimenezi zinagona pa imfa ya Yesu Kristu. Mukudziŵa inu kuti Yesu anazunzidwa ndi kupachikidwa. Anafa ngati chigaŵenga. Paulo analemba kuti: “Pamene tinali chikhalire ofooka, pa nyengo yake Kristu anawafera osapembedza. . . . Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife.” (Aroma 5:6, 8) Mwa kutifera, Kristu anapereka dipo lophimba machimo athu. Dipo limenelo ndiyo mfundo yaikulu ya uthenga wachikristu. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16; 1 Akorinto 15:3; 1 Timoteo 2:6) Kodi zimenezi zikukhudza motani mwazi ndi moyo, ndipo kodi moyo wanu ukukhudzidwa motani?

      14, 15. (a) Kodi mabaibulo ena amagogomezera motani imfa ya Yesu pa Aefeso 1:7? (b) Ndi mfundo yotani ya pa Aefeso 1:7 yomwe ingaphonyedwe?

      14 Matchalitchi ena amagogomezera kwambiri imfa ya Yesu, ndipo anthu a m’matchalitchi amenewo amanena mawu akuti “Yesu anandifera.” Taganizirani zimene mabaibulo ena amanena pa Aefeso 1:7: “Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulugu anatipulumutsa, ndipo anakhululukira zolakwa zathu.” (Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono) “Ndi imfa ya Kristu tinamasulidwa, ndipo machimo athu anakhululukidwa.” (Today’s English Version, 1966) “Tinamasulidwa kudzera mwa Kristu ndi nsembe ya moyo wake, kumasulidwa kumene kumatanthauza kukhululukidwa machimo.” (The New Testament, la William Barclay, 1969) “Kuli kudzera mu imfa ya Kristu kuti machimo athu amakhululukidwa ndipo timamasulidwa.” (The Translator’s New Testament, 1973) Mungathe kuona kuti mabaibulo ameneŵa amagogomezera kwambiri imfa ya Yesu. Ena anganene kuti, ‘Komatu imfa ya Yesu ndi yofunika kwambiri. Motero n’chiyani chikusoŵeka m’mabaibulo ameneŵa?’

      15 Kunena zoona, mutati muzingodalira mabaibulo otero, mukhoza kuphonya mfundo ina yofunika kwambiri, ndipo zimenezo zingakulepheretseni kumvetsa bwino uthenga wa m’Baibulo. Mabaibulo ameneŵa amabisa mfundo yakuti m’malemba oyambirira, lemba la Aefeso 1:7 lili ndi mawu achigiriki omwe amatanthauza kuti “mwazi.” Motero, zimene mabaibulo ambiri, monga Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu, amanena pa vesili zimagwirizana ndi zimene zili m’malemba oyambirirawo, zakuti: ‘Tili ndi mawomboledwe mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake.’

      16. Kodi mawu akuti “mwa mwazi wake” ayenera kutikumbutsa zotani?

      16 Mawu akuti “mwa mwazi wake” ali ndi tanthauzo lapadera ndipo ayenera kutikumbutsa zinthu zambiri. Imfa payokha, ngakhale imfa ya Yesu, yemwe anali munthu wangwiro, sinali yokwanira. Iye anakwaniritsa zimene Chilamulo chinali kuchitira mthunzi, makamaka pa Tsiku la Chitetezero. Patsiku lapadera limeneli, pankaperekedwa nsembe za nyama zimene Chilamulo chinkafuna. Kenako wansembe ankatenga magazi ena a nyamazo n’kupita nawo m’Malo Opatulikitsa m’chihema kapena m’kachisi. M’Malo Opatulikitsawo iye ankapereka magaziwo kwa Mulungu, ngati kuti waima pamaso pa Mulunguyo.​—Eksodo 25:22; Levitiko 16:2-19.

      17. Kodi Yesu anakwaniritsa motani zinthu zomwe zinkaimiridwa ndi Tsiku la Chitetezero?

      17 Malinga ndi mmene Paulo anafotokozera,Yesu anakwaniritsa zinthu zomwe zinkaimiridwa ndi zochitika za pa Tsiku la Chitetezero. Poyamba iye anatchula kuti mkulu wa ansembe ku Israyeli ankaloŵa kamodzi pachaka m’Malo Opatulikitsa atatenga mwazi umene ankapereka “chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu.” (Ahebri 9:6, 7) Mofanana ndi zochitika patsikuli, Yesu ataukitsidwa monga mzimu, anapita kumwamba. Poti anali mzimu motero sanali ndi thupi la nyama ndi mwazi, iye anatha kukaonekera “pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.” Kodi anapereka chiyani kwa Mulungu? Sanapereke chinthu chooneka ndi maso koma anapereka chinthu chofunika kwambiri. Paulo anapitiriza kufotokoza motere: “Atafika Kristu, Mkulu wa Ansembe . . . [osati ndi] mwazi wa mbuzi ndi ana a ng’ombe, koma mwa mwazi wa Iye yekha, analoŵa kamodzi ku malo opatulika, atalandirapo chiwombolo chosatha. Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi ng’ombe zamphongo . . . upatutsa kufikira chiyeretso cha thupi; koposa kotani nanga mwazi wa Kristu amene anadzipereka yekha wopanda chirema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?” Inde, Yesu anapereka kwa Mulungu mtengo wa mwazi wake.​—Ahebri 9:11-14, 24, 28; 10:11-14; 1 Petro 3:18.

      18. Kodi n’chifukwa chiyani mfundo za m’Baibulo zokhudza magazi ziyenera kukhala zofunika kwa Akristu masiku ano?

      18 Choonadi chochoka kwa Mulungu chimenechi chikutithandiza kumvetsa mfundo zochititsa chidwi zimene Baibulo limanena zokhudza magazi; mfundo monga chifukwa chimene Mulungu amaonera magazi motero, mmene ifeyo tiyenera kuwaonera, ndi chifukwa chake timafunika kumvera malamulo a Mulungu okhudza ntchito ya magazi. Mukamaŵerenga mabuku a Malemba Achigiriki Achikristu, mumaona malo ambiri otchula za mwazi wa Kristu. (Onani bokosi.) Malembaŵa amasonyezeratu kuti Mkristu aliyense ayenera kukhulupirira ‘mwazi [wa Yesu].’ (Aroma 3:25) N’zotheka kukhululukidwa machimo ndi kukhala pamtendere ndi Mulungu kokha ‘mwa mwazi’ umene Yesu anakhetsa. (Akolose 1:20) Umu ndi mmene zimakhaliradi kwa anthu amene Yesu anapangana nawo pangano lapadera lokalamulira naye kumwamba. (Luka 22:20, 28-30; 1 Akorinto 11:25; Ahebri 13:20) Zimakhalanso choncho kwa a “khamu lalikulu” masiku ano amene adzapulumuke ‘chisautso chachikulu’ ndi kukhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi pano. Mophiphiritsa, anthu ameneŵa ‘amatsuka zovala zawo m’mwazi wa Mwanawankhosa.’​—Chivumbulutso 7:9, 14.

      19, 20. (a) N’chifukwa chiyani Mulungu anasankha kuti anthu asagwiritse ntchito magazi mwachisawawa, ndipo tiyenera kumva motani ndi zimenezi? (b) Kodi tiyenera kukhala ofunitsitsa kudziŵa chiyani?

      19 N’zoonekeratu kuti magazi ali ndi tanthauzo lapadera kwa Mulungu. Amafunikanso kukhala otero kwa ife. Mlengi amene amaona kuti moyo ndi wofunika ali ndi ufulu woika malire a mmene anthu angagwiritsire ntchito magazi. Chifukwa choganizira kwambiri ngakhale moyo wathuwu, iye anakonza zopatula magazi kuti azigwiritsidwa ntchito m’njira imodzi yokha yofunika kwambiri, yomwe ikuchititsa kuti anthu adzathe kupeza moyo wosatha. Njira imeneyo inali yogwiritsira ntchito mwazi wamtengo wapatali wa Yesu. Tiyeneratu kukhala oyamikira kwambiri kuti Yehova Mulungu anachita zinthu zotipindulitsa mwa kugwiritsa ntchito mwazi, mwazi wa Yesu, m’njira yopulumutsa moyo! Ndipo tiyenera kumuyamikira kwambiri Yesu chifukwa chopereka mwazi wake monga nsembe yathu! Zoonadi, tingamvetse zimene mtumwi Yohane anafotokoza, kuti: “Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula ku machimo athu ndi mwazi wake; natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wake; kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthaŵi za nthaŵi. Amen.”​—Chivumbulutso 1:5, 6.

      20 Mulungu wathu wanzeru kwambiri ndiponso Wopatsa Moyo anayamba kale kwambiri kuganizira za ntchito yopulumutsa moyo imeneyi. Ndiye, tingafunse kuti, ‘Kodi zimenezi ziyenera kukhudza motani zimene timasankha ndiponso zimene timachita?’ Nkhani yotsatirayi iyankha funso limeneli.

      Kodi Mungayankhe Motani?

      • Kodi kuchokera pa nkhani ya Abele ndi ya Nowa tingaphunzire zinthu zotani zokhudza mmene Mulungu amaonera magazi?

      • M’Chilamulo, kodi Mulungu anati magazi azigwiritsidwa ntchito m’njira yotani, ndipo n’chifukwa chiyani?

      • Kodi Yesu anakwaniritsa motani zinthu zimene zinkaimiridwa ndi Tsiku la Chitetezero?

      • Kodi mwazi wa Yesu ungapulumutse moyo wathu motani?

  • Tsatirani Malangizo a Mulungu Wamoyo
    Nsanja ya Olonda—2004 | June 15
    • Tsatirani Malangizo a Mulungu Wamoyo

      ‘Tembenukirani kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo.’​—MACHITIDWE 14:15.

      1, 2. N’chifukwa chiyani kuli koyenera kuona Yehova kukhala “Mulungu wamoyo”?

      MTUMWI Paulo ndi Barnaba atachiritsa munthu, Paulo anatsimikizira anthu a ku Lustra omwe anali kuonerera zomwe zinachitazo kuti: “Ifenso tili anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo.”​—Machitidwe 14:15.

      2 N’zoona kuti Yehova si fano lopanda moyo, koma ndi “Mulungu wamoyo.” (Yeremiya 10:10; 1 Atesalonika 1:9, 10) Kuwonjezera pa mfundo imeneyi yakuti Yehova ndi wamoyo, iyeyonso ndi Gwero la moyo wathu. “Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:25) Iye amafuna kuti tizisangalala ndi moyo panopo ndiponso m’tsogolo. Paulo anawonjezera kuti Mulungu “sanadzisiyira iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.”​—Machitidwe 14:17.

      3. N’chifukwa chiyani tingadalire malangizo a Mulungu?

      3 Chidwi chomwe Mulungu ali nacho pa moyo wathu chimatipatsa chifukwa chodalirira malangizo ake. (Salmo 147:8; Mateyu 5:45) Ena sangaone choncho akapeza lamulo lina m’Baibulo limene sakulimvetsa kapena limene likuoneka kuti likuwamanitsa zinthu zina. Komatu ndi nzeru kudalira malangizo a Yehova. Tiyeni tiyerekezere motere: Ngakhale Mwisrayeli akanapanda kumvetsa kuti n’chifukwa chiyani pali lamulo loletsa kugwira mtembo, koma akanapindula nalo ndithu polimvera. Choyamba, kumvera kwake lamulo limenelo kukanam’thandiza kuti akhale paubwenzi wolimba ndi Mulungu wamoyo; ndipo chachiŵiri, kukanam’thandiza kupeŵa matenda.​—Levitiko 5:2; 11:24.

      4, 5. (a) Chikristu chisanayambe, kodi Yehova anapereka malangizo otani okhudza magazi? (b) Kodi tikudziŵa bwanji kuti lamulo la Mulungu pankhani ya magazi limakhudzanso Akristu?

      4 N’chimodzimodzinso ndi malangizo a Mulungu pankhani ya magazi. Mulungu anauza Nowa kuti anthu sayenera kudya magazi. Kenako m’Chilamulo, Mulungu anasonyeza kuti ntchito imodzi yokha yovomerezeka ya magazi ndiyo ya pa guwa la nsembe, pokhululukira machimo. Popereka malangizo ameneŵa, Mulungu anali kuyala maziko a ntchito yapamwamba kwambiri ya magazi, yopulumutsa miyoyo kudzera m’dipo la Yesu. (Ahebri 9:14) Inde Mulungu anapereka malangizo ake poganizira moyo wathu komanso kuti zinthu zitiyendere bwino. Pofotokoza lemba la Genesis 9:4, Adam Clarke, yemwe anali katswiri wa maphunziro a Baibulo wa m’zaka za m’ma 1800, analemba kuti: “Zipembedzo za Orthodox za m’mayiko a kum’maŵa zikutsatirabe kwambiri lamulo limeneli [lopita kwa Nowa] . . . Chilamulo chinaletsa kudya mwazi, chifukwa chakuti unali kuimira mwazi womwe unadzakhetsedwa patsogolo chifukwa cha machimo a dziko lonse; ndipo m’Mauthenga Abwino sunayenera kudyedwa, chifukwa nthaŵi zonse umafunika kuonedwa kuti ukuimira mwazi womwe unakhetsedwa kuti machimo akhululukidwe.”

      5 N’kutheka kuti katswiri ameneyu anali kunena za uthenga wabwino wofunika kwambiri wokhudza Yesu. Uthengawu umaphatikizapo zomwe Mulungu anachita potumiza Mwana wake kuti adzatifere ndiponso kuti adzakhetse mwazi wake kuti ife tithe kupeza moyo wosatha. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16; Aroma 5:8, 9) Zimene katswiriyu ananena zimakhudzanso lamulo lomwe linadzaperekedwa pambuyo pake lakuti otsatira Kristu ayenera kusala mwazi.

      6. Kodi Akristu anapatsidwa malangizo otani pankhani ya magazi, ndipo n’chifukwa chiyani?

      6 Mukudziŵa inu kuti Mulungu anapatsa Aisrayeli malamulo ambirimbiri. Yesu atafa, ophunzira ake sanafunikire kutsatira malamulo onsewo. (Aroma 7:4, 6; Akolose 2:13, 14, 17; Ahebri 8:6, 13) Koma patapita nthaŵi, panabuka funso lokhudza lamulo lina lofunika kwambiri, lamulo la mdulidwe wa amuna. Kodi anthu omwe sanali Ayuda koma omwe nawo ankafuna kupindula ndi mwazi wa Kristu anafunikira kudulidwa posonyeza kuti anali kutsatirabe Chilamulo? M’chaka cha 49 Kristu Atabwera, bungwe lolamulira lachikristu linakambirana nkhani imeneyo. (Machitidwe, chaputala 5) Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, atumwi ndi amuna akulu anaona kuti lamulo loti mwamuna aliyense azidulidwa linatha pamene Chilamulo chinatha. Komabe, Akristu anafunika kupitiriza kutsatira zinthu zina zomwe Mulungu anali kufuna m’Chilamulocho. M’kalata yomwe inapita kumipingo, bungwe lolamuliralo linalemba kuti: “Chinakomera Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi; kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu.”​—Machitidwe 15:28, 29.

      7. Kodi ‘kusala mwazi’ n’kofunika motani kwa Akristu?

      7 N’zoonekeratu kuti bungwe lolamulira linaona kuti ‘kusala mwazi’ ndi kofunika kwambiri mofanana ndi kukhala ndi makhalidwe abwino monga kupeŵa chiwerewere kapena kupeŵa kulambira mafano. Izi zikusonyeza kuti lamulo loletsa magazi siliyenera kuonedwa mopepuka. Akristu amene amalambira mafano kapena kuchita chiwerewere koma osalapa “sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu”; “cholandira chawo chidzakhala . . . imfa yachiŵiri.” (1 Akorinto 6:9, 10; Chivumbulutso 21:8; 22:15) Ndiye onani kuti ngati munthu samvera malangizo a Mulungu okhudza kupatulika kwa magazi mapeto ake ndi imfa yamuyaya, komano akamalemekeza nsembe ya Yesu angapeze moyo wamuyaya.

      8. N’chiyani chikusonyeza kuti Akristu oyambirira sananyalanyaze malangizo a Mulungu pankhani ya magazi?

      8 Kodi Akristu oyambirira anawamva motani malangizo a Mulungu okhudza magazi ndipo anawatsatira motani? Kumbukirani zimene Clarke ananena zakuti: “M’Mauthenga Abwino [mwazi] sunayenera kudyedwa, chifukwa nthaŵi zonse umafunika kuonedwa kuti ukuimira mwazi womwe unakhetsedwa kuti machimo akhululukidwe.” Zochitika zakale zimatsimikizira kuti Akristu oyambirira nkhaniyi ankaiona kuti n’njofunika kwambiri. Tertullian analemba kuti: “Talingalirani za anthu osusuka chifukwa cha ludzu, amene pachionetsero m’bwalo lamaseŵero, amatcherezera magazi a munthu wamlandu . . . kuti akachizire matenda awo a khunyu.” Mosiyana ndi akunja omwe ankadya magazi, Tertullian ananena kuti Akristu ‘ngakhale pakati pa zakudya [zawo] panalibe magazi a nyama . . . Pa ziyeso za Akristu mumawapatsa masoseji a magazi. Koma mumakhala mukudziŵiratu kuti kwa iwo [kuteroko] n’kuswa lamulo.’ Inde ngakhale kuti ankawaopseza kuti awapha, Akristu sankadya magazi. Kwa iwo, malangizo a Mulungu anali ofunika kwambiri.

      9. Kodi kusala magazi kunaphatikizapo chiyani kuwonjezera pa kusadya magazi enieniwo?

      9 Ena angaganize kuti bungwe lolamulira linali kungotanthauza kuti Akristu sanayenera kudya kapena kumwa magazi enieniwo kapena kudya nyama yosakhetsa magazi kapena chakudya chomwe asakanizamo magazi. N’zoona kuti limenelo ndilo linali tanthauzo loyambirira la lamulo lomwe Mulungu anapatsa Nowa. Ndipo lamulo la atumwi linauza Akristu kuti ‘asale zopotola,’ kutanthauza nyama yomwe sinakhetsedwe magazi. (Genesis 9:3, 4; Machitidwe 21:25) Komabe Akristu oyambirira anadziŵa kuti sizinali zokhazo. Nthaŵi zina anthu ankadya magazi monga mankhwala. Tertullian anafotokoza kuti anthu ena akunja ankadya magazi aaŵisi pofuna kuchiza matenda awo a khunyu. Ndipo n’kutheka kuti ankagwiritsanso ntchito magazi m’njira zina pofuna kuchiza matenda ena kapena pofuna kukhala ndi thanzi labwinopo. Motero, kwa Akristu, kukana magazi kunaphatikizapo kusadya magazi pazifukwa za “mankhwala.” Sanasinthe maganizo awo pankhaniyi ngakhale panthaŵi yomwe kuchita zimenezo kunkaika moyo wawo pangozi.

      Kugwiritsa Ntchito Magazi Monga Mankhwala

      10. Kodi magazi akugwiritsidwa ntchito m’njira zotani monga mankhwala, zomwe zikuchititsa kuti pakhale mafunso otani?

      10 Masiku ano kugwiritsa ntchito magazi monga mankhwala n’kofala kwambiri. Kale anthu ankawaika magazi athunthu omwe awatenga m’thupi mwa wina, n’kuwasunga, kenaka n’kupatsa munthu wodwala, mwachitsanzo amene wavulala kunkhondo. M’kupita kwa nthaŵi, ofufuza anapeza njira zogaŵira magazi m’zigawo zake zikuluzikulu. Mwa kupatsa munthu chigawo chimodzi cha magazi, madokotala ankatha kupereka magazi womwewomwewo kwa odwala angapo. Ankatha kupereka madzi a m’magazi kwa munthu wina amene wavulala, ndipo maselo ofiira ankatha kuwapereka kwa munthu winanso. Popitiriza kuchita kafukufuku anapeza kuti angathenso kugaŵa chigawo chachikulu chilichonse cha magazi, monga madzi a m’magazi, n’kukhala tizigawo ting’onoting’ono tambiri, tomwe angapatsenso odwala ambirimbiri. Ntchito yoyesa kugaŵa magazi m’tizigawo ting’onoting’onoyi ikupitirira, ndipo akutulukiranso ntchito zina zatsopano za tizigawo ting’onoting’onoti. Kodi nkhani imeneyi Mkristu ayenera kuiona motani? Iye anatsimikiza mtima kuti sadzalola kuikidwa magazi, koma dokotala wake akum’kakamiza kuti alandire chigawo chachikulu chimodzi cha magazi, mwinamwake maselo ofiira okhaokha. Kapena mwina chithandizocho chingafune kuti apatsidwe kachigawo kakang’ono kamodzi kotengedwa m’chigawo chachikulu cha magazi. Kodi mtumiki wa Mulungu angasankhe motani zoti achite pankhanizi, pokumbukira kuti magazi ndi opatulika ndiponso kuti mwazi wa Kristu ndiwo wopulumutsadi moyo?

      11. Kodi ndi maganizo olondola ati okhudza kulandira magazi amene Mboni zakhala nawo kwa nthaŵi yaitali?

      11 Zaka zambiri zapitazo Mboni za Yehova zinamveketsa bwino maganizo awo. Mwachitsanzo, zinatumiza nkhani ku magazini ya The Journal of the American Medical Association (November 27, 1981; nkhani yomwe inasindikizidwanso mu kabuku kakuti Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu? masamba 27-9).a Nkhani imeneyo inagwira mawu m’mabuku a Genesis, Levitiko, ndi Machitidwe. Ndiyeno inati: “Pamene kuli kwakuti mavesiŵa sananenedwe m’mawu a zamankhwala, Mboni zimawalingalira kukhala oletsa kuthiridwa mwazi wathunthu, ma RBC [maselo ofiira okhaokha] ndi madzi a m’mwazi ndiponso WBC [maselo oyera a mwazi] ndi kupatsidwa zinthu za m’mwazi.” Buku la zachipatala lakuti Emergency Care la mu 2001, pamutu wakuti “Mmene Magazi Anapangidwira,” linati: “Magazi ali ndi zigawo zikuluzikulu zingapo: madzi, maselo ofiira ndi oyera, ndi maselo othandiza magazi kuundana.” Motero, mogwirizana ndi mfundo za achipatala, Mboni zimakana kuikidwa magazi athunthu kapena chigawo china chilichonse mwa zigawo zake zikuluzikulu zinayi.

      12. (a) Kodi maganizo athu ndi otani pankhani ya tizigawo ting’onoting’ono totengedwa m’zigawo zikuluzikulu za magazi? (b) Kodi mungapeze kuti mfundo zina zowonjezera zokhudza nkhaniyi?

      12 Nkhani yofotokoza za mankhwalayo inapitiriza motere: “Kuzindikira kwachipembedzo kwa Mboni sikumaletseratu kugwiritsiridwa ntchito kwa [tizigawo ting’onoting’ono ta magazi monga] albumin, immune globulins, ndi zosungunula mwazi; Mboni iliyonse iyenera kudzisankhira ngati ingavomereze zimenezi.” Kuchokera mu 1981, akatswiri apeza tizigawo ting’onoting’ono tambiri tomwe akutha kutigwiritsa ntchito kuchokera m’chigawo chilichonse cha zigawo zinayi zikuluzikulu zija. Motero, Nsanja ya Olonda ya June 15, 2000, inali ndi mfundo zabwino kwambiri zokhudza nkhaniyi m’nkhani ya “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga.” Pofuna kuthandiza anthu ambiri amene amaŵerenga magazini ano panopa, yankholo talisindikizanso pa masamba 29-31 a magazini ino. Likulongosola zinthu mwatsatanetsatane ndiponso lili ndi mfundo zofunika kuziganizira, komabe muona kuti mfundo zomwe zili m’nkhaniyi zikugwirizana ndi mfundo zikuluzikulu zomwe zinafotokozedwa mu 1981.

      Ntchito ya Chikumbumtima Chanu

      13, 14. (a) Kodi chikumbumtima n’chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani chimafunika kugwiritsidwa ntchito pankhani zokhudza magazi? (b) Kodi Mulungu anapereka kwa Israyeli malangizo otani pankhani yodya nyama, koma kodi n’kutheka kuti anthu ankakhala ndi mafunso otani?

      13 Mfundo zimenezi zimafunika kugwiritsa ntchito chikumbumtima. Chifukwa chiyani tikutero? Akristu amavomereza kuti m’pofunika kutsatira malangizo a Mulungu, komabe pankhani zina munthu amafunika kudzisankhira zochita, ndipo apa m’pamene pamafunika chikumbumtima. Chikumbumtima ndi chibadwa chimene chimachititsa munthu kuganizira zinthu mosamala makamaka zokhudza khalidwe labwino. (Aroma 2:14, 15) Komatu mukudziŵa inu kuti chikumbumtima cha anthu chimasiyanasiyana.b Baibulo limanena kuti ena ali ndi ‘chikumbumtima chofooka,’ kusonyeza kuti chikumbumtima cha ena n’cholimba. (1 Akorinto 8:12) Akristu amasiyanasiyana pa zimene akudziŵa zokhudza zimene Mulungu amanena, mmene Mulungu amaganizira, ndiponso mmene angagwiritsire ntchito zimenezi pa zochita zawo. Apa tingapereke chitsanzo cha Ayuda pankhani ya kudya nyama.

      14 Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti munthu womvera Mulungu sangadye nyama yosakhetsa magazi. Lamulo limeneli linali lamphamvu kwambiri moti ngakhale panthaŵi ina asilikali achiisrayeli zinthu zitawapanikiza n’kufika podya nyama yosakhetsa magazi, anachimwa kwambiri. (Deuteronomo 12:15, 16; 1 Samueli 14:31-35) Komabe, n’kutheka kuti anthu ankakhala ndi mafunso osiyanasiyana. Mwisrayeli akapha nkhosa, kodi anayenera kukhetsa magazi ake mwamsanga bwanji? Kodi ankafunika kuiboola nkhwiko kuti magaziwo atulukirepo? Kodi pankafunika kuikoloŵeka nkhosayo penapake ataimanga miyendo yam’mbuyo? Nanga akanatero kwanthaŵi yaitali motani? Kodi akanachita zotani ndi ng’ombe yaikulu kwambiri? Ngakhale pambuyo pokhetsa nyamayo, magazi ena angathe kutsalirabe m’minofu. Kodi iye akanadya nyama yoteroyo? Kodi ndani anafunika kusankha zochita pamenepo?

      15. Kodi Ayuda ena ankachita chiyani ndi nkhani ya kudya nyama, koma kodi Mulungu anawalangiza chiyani?

      15 Yerekezani kuti Myuda amene amatsatiradi chikhulupiriro chake akuganizira mafunso ngati ameneŵa. Mwina akanaona chinthu chanzeru kwambiri kusadya nyama yogulitsidwa pamsika, monganso momwe wina angakanire kudya nyama ngati akuiganizira kuti ingakhale itaperekedwa nsembe kwa mafano. N’kutheka kuti Ayuda ena ankadya nyama pokhapokha akatsatira mwambo wochotsera magazi m’thupi la nyama.c (Mateyu 23:23, 24) Kodi mukuganiza bwanji za kusiyanasiyana maganizo kumeneku? Komanso, popeza kuti Mulungu sanafune kuti anthu aganize moteromo, kodi kukanakhala koyenera kuti Ayuda atumize mafunso ambirimbiri ku bungwe la akuluakulu achipembedzo kuti ligamulepo pa nkhani iliyonse? Ngakhale kuti mwambo umenewu unayambika pakati pa Ayuda, n’zosangalatsa kudziŵa kuti Yehova sanalamule olambira oona kuti azichita zimenezo posankha zochita pankhani ya magazi. Mulungu anapereka mfundo zikuluzikulu zophera nyama zoyera ndi kukhetsa magazi ake, koma sanaperekenso malangizo ena kuwonjezera pa amenewo.​—Yohane 8:32.

      16. Kodi n’chifukwa chiyani Akristu angasiyane maganizo pankhani yolandira jekeseni wa kachigawo kakang’ono kochoka m’chigawo chachikulu chimodzi cha magazi?

      16 Monga momwe taonera m’ndime 11 ndi 12, Mboni za Yehova sizilola kuikidwa magazi athunthu kapena zigawo zake zikuluzikulu zinayi, zomwe ndi madzi a m’magazi, maselo ofiira, maselo oyera, ndi maselo othandiza magazi kuundana. Nanga bwanji za tizigawo ting’onoting’ono tochokera m’chigawo chachikulu chimodzi, monga tizigawo totengedwa m’madzi a m’magazi tokhala ndi chitetezo chothandiza thupi la munthu kulimbana ndi matenda kapena ululu wa njoka? (Onani tsamba 30, ndime 4.) Ena amaona kuti magazi akawagaŵa m’tizigawo ting’onoting’ono kwambiri toteroto, tizigawoto si magazi ayi motero sitikhudzidwa ndi lamulo ‘losala mwazi.’ (Machitidwe 15:29; 21:25; tsamba 31, ndime 1) Umenewo ndi udindo wawo. Chikumbumtima cha ena chimawaletsa kulandira chilichonse chotengedwa m’magazi (kaya a nyama kapena a munthu), ngakhale kachigawo kochepetsetsa ka chigawo chachikulu chimodzi chokha.d Ndiye pali ena amene amalola kulandira jekeseni wa mapuloteni a m’madzi a m’magazi kuti alimbane ndi matenda kapena ululu wa njoka m’thupi lawo, koma angakane tizigawo ting’onoting’ono tina tonse ta magazi. Komanso, tina mwa tizigawo ta m’magazi tingagwire ntchito mofanana kwambiri ndi chigawo chachikulu chonsecho n’kumuthandiza munthu kuti akhalebe ndi moyo moti Akristu ambiri angaone kuti tizigawo toteroto n’tosavomerezeka kwa iwowo.

      17. (a) Kodi chikumbumtima chathu chingatithandize motani pamene tili ndi mafunso okhudza tizigawo ting’onoting’ono ta magazi? (b) N’chifukwa chiyani si nkhani yopepuka kusankha zochita pankhaniyi?

      17 Zimene Baibulo limanena pankhani ya chikumbumtima ndi zothandiza pamene tikusankha zochita pambaliyi. Choyamba, m’pofunika kuphunzira zimene Mawu a Mulungu amanena ndi kuyesetsa kuzoloŵeretsa chikumbumtima chanu kuchita zinthu mogwirizana ndi zimenezo. Izi zidzakuthandizani kusankha zochita mogwirizana ndi malangizo a Mulungu m’malo mouza munthu wina kuti akusankhireni zochita. (Salmo 25:4, 5) Pankhani yolandira tizigawo ting’onoting’ono ta magazi, ena amaganiza kuti, ‘Iyi ndi nkhani ya chikumbumtima, motero ndi nkhani yochepa.’ Maganizo oterowo n’ngolakwika. Kunena kuti nkhani inayake ndi yoyendera chikumbumtima cha munthu sizikutanthauza kuti nkhaniyo ndi yochepa. Ingathe kukhala nkhani yaikulu kwambiri. Chifukwa chimodzi n’chakuti nkhaniyo ingathe kukhudza anthu ena amene chikumbumtima chawo chikusiyana ndi chathu. Timaona zimenezi m’malangizo a Paulo pankhani ya nyama yomwe ingakhale kuti inakaperekedwa nsembe kwa mafano ndipo kenako ikugulitsidwa pamsika. Mkristu afunika kudera nkhaŵa kuti ‘asalase chikumbumtima cha ofooka.’ Ngati akhumudwitsa ena, iye ‘angataye mbale wake amene Kristu anam’fera’ motero angachimwire Kristu. Chotero, ngakhale kuti nkhani zokhudza tizigawo ting’onoting’ono ta magazi zikudalira pa zimene munthu angasankhe payekha, zimenezo sizofunika kuziona mopepuka.​—1 Akorinto 8:8, 11-13; 10:25-31.

      18. Kodi Mkristu angapeŵe motani kupha chikumbumtima chake posankha zochita pankhani yokhudza magazi?

      18 Mbali inanso yofunika kuiganizira ikusonyeza kuti kusankha zochita pankhani ya magazi si nkhani yochepa. Iyi ndi mbali ya mmene zimene mungasankhezo zingakukhudzireni. Ngati mungavutike ndi chikumbumtima chanu chophunzitsidwa ndi Baibulo chifukwa cholandira kachigawo kakang’ono ka magazi, musachinyalanyaze chikumbumtimacho. Komanso simuyenera kupondereza chikumbumtima chanucho chabe chifukwa chakuti munthu wina wakuuzani kuti, “Palibe vuto kulandira kachigawo aka; anthu ambiri alandirapo.” Kumbukirani kuti anthu ambiri masiku ano amanyalanyaza zomwe chikumbumtima chawo chikuwauza, ndipo chimafa, n’kuwalola kuti azinama kapena kuchita zinthu zina zoipa thima lili zii. Akristu amafunika kupeŵeratu mtima wotero.​—2 Samueli 24:10; 1 Timoteo 4:1, 2.

      19. Posankha zochita pankhani zachipatala zokhudza magazi, kodi chinthu chachikulu chomwe tiyenera kuchiganizira chiyenera kukhala chiyani?

      19 Yankho lomwe talisindikizanso pamasamba 29-31, chakumapeto kwake likuti: “Kodi popeza kuti malingaliro ndiponso zosankha zachikumbumtima zimatha kusiyana ndiye kuti si nkhani yodetsa nkhaŵa? Iyayi. Ndi nkhanitu yaikulu.” Ndi nkhani yaikulu makamaka chifukwa chakuti ikukhudza ubwenzi wanu ndi “Mulungu wamoyo.” Ndi ubwenzi wokhawu womwe ungapezetse munthu moyo wosatha, chifukwa cha mphamvu yopulumutsa ya mwazi wokhetsedwa wa Yesu. Magazi muziwaona kuti n’ngolemekezeka kwambiri chifukwa cha mmene Mulungu akuwagwiritsira ntchito, kupulumutsa miyoyo. Paulo ananena zoona kuti: ‘Munali . . . opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m’dziko lapansi. Koma tsopano mwa Yesu Kristu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m’mwazi wa Kristu.’​—Aefeso 2:12, 13.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena