Ndandanda ya Mlungu wa August 11
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 11
Nyimbo Na. 99 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 14 ndime 20-25 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Numeri 7-9 (Mph. 10)
Na. 1: Numeri 9:9-23 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Munthu Akapulumutsidwa Sizitanthauza Kuti Wapulumutsidwa Nthawi Yonse—rs tsa. 96 ndime 3-6 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tiziopa Anthu Akufa?—bh tsa. 58 ndime 5-6 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: “1914-2014: Patha Zaka 100 Ufumu wa Mulungu Ukulamulira!” Nkhani yokambirana. Werengani ndime imene ili pamwamba pa tsamba lino. Nkhani za mu Msonkhano wa Utumiki za mwezi uno zikunena zokhudza Ufumu. Fotokozani dongosolo limene mpingo wanu uzitsatira polowa mu utumiki m’mwezi uno.
Mph. 10: “Mmene Tingagwiritsire Ntchito Kapepala Kodziwitsa Anthu za Webusaiti Yathu.” Kambiranani zimene zili m’kapepelaka ndipo chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akugawira kapepalaka. Kenako wofalitsayo asonyeze munthuyo mmene angalowere pa webusaiti yathu ya jw.org/ny, pogwiritsa ntchito foni kapena chipangizo china chokhala ndi Intaneti.
Mph. 15: “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tiziuza Anthu Zokhudza Ufumu Molimba Mtima.” Nkhani yokambirana. Pemphani ofalitsa awiri kuti achite chitsanzo ichi: Wofalitsa ali pamzere m’sitolo, kudikira kuti alipire zinthu zimene wagula. Munthu amene ali kumbuyo kwake akuwerenga nyuzipepala ndipo akunena kuti: “Koma ndiye zinthu zaipatu. Ngakhale kuti anthu ambiri akunena kuti akhoza kukonza zinthu, palibe amene akukwanitsa kuchita zimenezi ndipo zinthu zikungoipiraipirabe.” Wofalitsayo akudzilankhulira yekha ndipo akunena kuti: ‘Ndikufunika ndimuuze zimene Ufumu udzachite.’ Kenako akuuza munthuyo kuti: “N’zoona kuti zinthu zikungoipiraipira. Koma ndili ndi kapepala aka. Kodi mungakonde kuti ndikupatseni? Kapepalaka kakunena za webusaiti imene yathandiza anthu ambiri kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri.” Wofalitsayo afotokoze mfundo imodzi ya m’kapepalako, ndipo munthuyo asonyeze kuti wachita chidwi.
Nyimbo Na. 92 ndi Pemphero