DECEMBER 8-14
YESAYA 6-8
Nyimbo Na. 75 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. “Ine Ndilipo! Nditumizeni”
(10 min.)
Popanda kuzengereza, Yesaya anadzipereka kuti akhale mneneri wa Mulungu (Yes 6:8; ip-1 93-94 ¶13-14)
Utumiki wa Yesaya unali woti udzakhala wovuta (Yes 6:9, 10; ip-1 95 ¶15-16)
Utumiki wa Yesaya unkasonyeza ntchito imene Yesu adzagwire (Mt 13:13-15; ip-1 99 ¶23)
FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA: Kodi ndingasinthe zinthu ziti kuti ndizichita zambiri potumikira Yehova?
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Yes 7:3, 4—N’chifukwa chiyani Yehova anapulumutsa Ahazi, yemwe anali mfumu yoipa? (w06 12/1 9 ¶4)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Yes 8:1-13 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambiranani mfundo imodzi ya choonadi yopezeka mu zakumapeto A, m’kabuku kakuti Muzikonda Anthu. (lmd phunziro 4 mfundo 5)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 9 mfundo 3)
6. Ulendo Wobwereza
(5 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Musonyezeni mmene phunziro la Baibulo limachitikira. (lmd phunziro 9 mfundo 5)
Nyimbo Na. 83
7. Timadziwika ndi Ntchito Yolalikira Kunyumba ndi Nyumba
(15 min.) Nkhani yokambirana.
A Mboni za Yehova amadziwika ndi ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba, yomwe amaigwira potsanzira Yesu Khristu komanso Akhristu a m’nthawi ya atumwi.—Lu 10:5; Mac 5:42.
N’zoona kuti ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba inaimitsidwa kaye pa nthawi ya mliri wa COVID-19. Choncho tinkauza ena uthenga wabwino polalikira mwamwayi, polemba makalata komanso poimba mafoni. Timasangalala kwambiri kuti tinali ndi mwayi wodziwa bwino njira zolalikirira zimenezi. Komabe, kulalikira kunyumba ndi nyumba idakali njira yaikulu yolalikirira uthenga wabwino. Kodi mumakwanitsa kugwira nawo ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba nthawi zonse?
Kodi kulalikira kunyumba ndi nyumba kumatithandiza bwanji kuchita zinthu zotsatirazi?
Kulalikira gawo lathu lonse
Kukulitsa luso lathu lophunzitsa komanso kukulitsa makhalidwe abwino monga kulimba mtima, kupanda tsankho komanso kudzipereka
Kuyambitsa maphunziro a Baibulo
Onerani VIDIYO yakuti Timalalikira M’nyengo Iliyonse. Kenako funsani funso ili:
Kodi mwaphunzira chiyani pa kudzipereka kwa abale ndi alongo amene ankalalikira kuzilumba za Faroe?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 42-43