Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb25 November tsamba 12-13
  • December 15-21

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • December 15-21
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2025
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2025
mwb25 November tsamba 12-13

DECEMBER 15-21

YESAYA 9-10

Nyimbo Na. 77 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Analosera za “Kuwala Kwakukulu”

(10 min.)

“Kuwala kwakukulu” kunali koti kudzaonekera ku Galileya (Yes 9:​1, 2; Mt 4:​12-16; ip-1 125-126 ¶16-17)

Mtundu umene udzalandire kuwalako udzakula kwambiri komanso anthu ake adzakhala osangalala (Yes 9:3; ip-1 126-128 ¶18-19)

Zotsatira za kuwala kwakukulu kumeneko zidzakhalapo mpaka kalekale (Yes 9:​4, 5; ip-1 128-129 ¶20-21)

Yesu ndi wophunzira wake akulalikira bambo wina ndi mwana panyumba yawo. Mayi yemwe wanyamula mtsuko waukulu paphewa, akumvetsera zimene akukambirana pamene akudutsa chapafupi.

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Yes 9:6—Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali “Mlangizi Wodabwitsa”? (ip-1 130 ¶23-24)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Yes 10:1-14 (th phunziro 11)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Lalikirani munthu amene si Mkhristu. (lmd phunziro 1 mfundo 4)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pitirizani kukambirana pogwiritsa ntchito kapepala kamene munamusiyira pa ulendo wapita. (lmd phunziro 9 mfundo 3)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

(5 min.) Chitsanzo. Ijwfq nkhani Na. 35—Mutu: Kodi a Mboni za Yehova Anasintha Zina N’zina M’Baibulo Kuti Zigwirizane ndi Zimene Amakhulupirira? (th phunziro 12)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 95

7. Kuwala Kukuwonjezerekabe

(5 min.) Nkhani yokambirana.

Dzuwa likuwala pamwamba pa nkhalango yomwe yakutidwa ndi nkhungu.

Gulu la Yehova likupitiriza kupita patsogolo. Kodi mukuyenda nalo limodzi? Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zosonyeza mmene gulu la Yehova lakhala likuyendera komanso mmene zimenezo zatithandizira.

  • Lembani chitsanzo chosonyeza kusintha kwa mmene tinkamvera mfundo inayake yachoonadi cha m’Baibulo komanso mmene kusinthako kwatithandizira.—Miy 4:18

  • Lembani chitsanzo chosonyeza kusintha pa nkhani ya mmene timagwirira ntchito yolalikira komanso mmene kusinthako kwatithandizira kukwaniritsa ntchito imene Yesu anatipatsa.—Mt 28:​19, 20

  • Lembani chitsanzo chosonyeza kusintha komwe kwachitika pa nkhani ya mmene zinthu zimayendera m’gululi komanso mmene kusinthako kwatithandizira.—Yes 60:17

8. Vidiyo ya Zimene Gulu Lathu Lachita ya December

(10 min.)

Onerani VIDIYOYI.

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) lfb mawu oyamba gawo 8 komanso mutu 44-45

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 92 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena