DECEMBER 22-28
YESAYA 11-13
Nyimbo Na. 14 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Kodi Baibulo Linaneneratu Zotani Zokhudza Mesiya?
(10 min.)
Adzakhala mbadwa ya Jese kudzera mwa mwana wake Davide (Yes 11:1; ip-1 159 ¶4-5)
Adzakhala ndi mzimu wa Mulungu ndipo azidzaopa Yehova (Yes 11:2, 3a; ip-1 159 ¶6; 160 ¶8)
Adzakhala woweruza wachilungamo komanso wachifundo (Yes 11:3b-5; ip-1 160 ¶9; 161 ¶11)
FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA: Kodi n’chiyani chimachititsa Yesu kukhala wolamulira wabwino kwambiri kuposa anthu?
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Yes 11:10—Kodi ulosiwu unakwaniritsidwa bwanji? (ip-1 165-166 ¶16-18)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Yes 11:1-12 (th phunziro 11)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunziro 2 mfundo 5)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Gwiritsani ntchito webusaiti ya jw.org poyankha funso limene munthuyo wafunsa. (lmd phunziro 8 mfundo 3)
6. Kuphunzitsa Anthu
(5 min.) Thandizani wophunzira wanu kuti akonzekere kudzalalikira nanu kunyumba ndi nyumba. (lmd phunziro 11 mfundo 4)
Nyimbo Na. 57
7. Kodi ‘Mumaweruza ndi Chiweruzo Cholungama’?
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Tsiku lililonse timaweruza anthu ena, koma nthawi zina sitidziwa n’komwe kuti tikuwaweruza. Nthawi zambiri timakonda kuweruza ena potengera zomwe taona. Komabe, Yesu yemwe ndi chitsanzo chathu, amaweruza mosiyana ndi anthufe. (Yes 11:3, 4) Yesu amakwanitsa kuona mumtima n’kuzindikira zimene munthu akuganiza, chifukwa chake akuganiza zimenezo komanso zolinga zake. Ifeyo tilibe luso limeneli. Komabe, tikhoza kuchita zonse zomwe tingathe kuti titsanzire Yesu. Iye anati: “Siyani kuweruza potengera maonekedwe akunja, koma muziweruza ndi chiweruzo cholungama.”—Yoh 7:24.
Khama lathu komanso mmene timachitira utumiki wathu, zikhoza kusokonezeka ngati timaweruza ena potengera zomwe taona. Mwachitsanzo, kodi timazengereza kulalikira anthu a m’dera linalake lomwe muli anthu a mtundu winawake kapena chipembedzo chinachake? Nanga bwanji za madera amene kuli anthu olemera kapena osauka? Kodi timaganiza kuti munthu sangakhale ndi chidwi potengera mmene akuonekera? Cholinga cha Mulungu ndi choti “anthu osiyanasiyana apulumuke n’kukhala odziwa choonadi molondola.”—1Ti 2:4.
Onerani VIDIYO yakuti Zimene Ndinaphunzira mu Nsanja ya Olonda—Musamaweruze Ena Potengera M’mene Akuonekera. Kenako funsani mafunso awa:
Kodi ndi zinthu ziti zatsankho zimene zatchulidwa muvidiyoyi?
Ngati tingalole kuti mumpingo mulowe tsankho, kodi zimenezi zingakhudze bwanji mpingowo?
Kodi n’chiyani chinathandiza abale ndi alongo a muvidiyoyi kuti asamaweruze potengera maonekedwe akunja?
Kodi inuyo mwaphunzira chiyani munkhani ya mu Nsanja ya Olonda imeneyi?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 46-47