Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 4/8 tsamba 3
  • Kodi Kuli Aliyense Kunja Kumeneko?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kuli Aliyense Kunja Kumeneko?
  • Galamukani!—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Zamoyo Zakuthambo—Kupeza Yankho
    Galamukani!—1990
  • Zamoyo Zakuthambo—Kodi Ziri Kuti?
    Galamukani!—1990
  • Ma UFO—Kodi Ali Amithenga Ochokera kwa Mulungu?
    Galamukani!—1996
  • Zamoyo Zakuthambo—Loto Lakalekale
    Galamukani!—1990
Galamukani!—1990
g90 4/8 tsamba 3

Kodi Kuli Aliyense Kunja Kumeneko?

KULI munthu ku Massachusetts, U.S.A., amene monga mbali ya ntchito yake ya tsiku ndi tsiku amafufuza kuwona ngati kwabwera mauthenga alionse. Tsiku ndi tsiku, sipakhala alionse. Kwa zaka zambiri tsopano, sikunabwere uliwonse. Koma iye amafufuzabe mokhazikika, ndipo amakhumudwitsidwa mokhazikika. Kodi iye ngwopenga? Kodi makina ake oyankhira ngowonongeka?

Ayi. Iye amafufuza makina, koma siolumikizidwa ku laini ya lamya. Ndi kompyuta yolumikizidwa ku khutu lalikulu lamagetsi limene limaloza m’mwamba, kutali ndi dziko lathu, mkati mwenimweni mwa thambo: radio telescope. Munthuyu akuthandiza gulu la asayansi kusanthula nyenyezi kaamba ka uthenga wochokera kwa zamoyo zakuthambo zaluntha, zamoyo zokhala kunja kwa dziko lathu.

Ena, monga iye, akhalanso akumvetsera kwa zaka 30 tsopano. Mu 1960 katswiri wa zakuthambo Frank Drake anakhala munthu woyamba kumvetsera ndi radio telescope kaamba ka zizindikiro za zamoyo zakuthambo zaluntha. Chiyambire pamenepo, munthu, m’chenicheni, waika makutu ake kuthambo. Kufufuza kwina kosiyanasiyana kofutukulidwa 50 kwa thambo kwapangidwa kale.

Maradio telescope pa dziko lonse agwirizana m’kufufuzako—mu France, Federal Republic ya Germany, Netherlands, Australia, Soviet Union, Argentina, United States, ndi Canada. Monga mmene munthu wina ananenera kuti: “SETI [chidule cha chinenero Chachingelezi cha Search for Extraterrestrial Intelligence (Kufufuza Zamoyo Zaluntha Zakuthambo) kwa munthu] ikukhala ya mitundu yonse monga thambo lenilenilo.” Nkhani yosiirana ina pa nkhaniyo inakoka asayansi 150 kuchokera ku maiko 18 ochokera ku makontinenti onse asanu.

Komabe, ntchito yonyadirika kwambiri ya SETI idzayambika mu 1992. NASA, National Aeronautics and Space Administration ya ku United States, ikukonzekera kugwiritsira ntchito chipangizo chatsopano champhamvu kwambiri chimene chidzatheketsa kufufuza mamiliyoni a mphamvu ya wailesi pa nthaŵi imodzi. Kufufuzako kwalingaliridwa kuti kudzatenga zaka khumi pa mtengo wa $90 miliyoni. Idzakhala yodula kuŵirikiza nthaŵi mamiliyoni zikwi khumi kuposa kufufuza kwapapita konse kutaikidwa pamodzi.

Koma pamene munthu akufunsa za chilengedwe chonse chachikuluchi kuti, “Kodi kuli aliyense kunja kumeneko?” iye adzafunikira ziwiya zoposa za luso lazopangapanga lapamwamba kuti apeze yankho. M’njira zambiri liri funso lauzimu. M’kufunafuna yankho, munthu amavumbula zina za ziyembekezo zake zokondeka kwambiri: kutha kwa nkhondo, kutha kwa matenda, mwinamwake ngakhale kufikira kusafa kwenikweniko. Chotero ngozizo n’zapamwamba. Koma pambuyo pa zaka mazana a kuzizwa ndi zaka makumi a kufufuza, kodi munthu wayandikira motani ku yankho?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena