Kukhupuka ndi Kugwa kwa Dongosolo Lamalonda
Gawo 1b: Kodi Nkusanthuliranji Dongosolo Lamalonda?
DZIKO lopanda udani wandale, kukangana kwa zipembedzo, ndi nkhaŵa zachuma nlovuta kuliyerekezera m’maganizo. Masiku onse ndale zadziko, chipembedzo, ndi zamalonda zimatiyambukira m’njira zambiri. Mutachotsa mizati itatuyi ya chitaganya cha anthu, pakhoza kukhala chipwirikiti.
Paliponse pamene magulu a anthu akhala pamodzi, dongosolo lakutilakuti la zachuma—losamalira banja—nlofunika kuwapezera zinthu ndi mautumiki amene iwo afunikira. (Onani bokosi pansipa.) Chotero banja lirilonse limakalimira kukhala ndi mkhalidwe wabwino wazachuma. Mofananamo, mkhalidwe wazachuma wa boma lirilonse umaphatikizapo zinthu zinayi zazikulu izi: (1) kudziŵa zinthu ndi mautumiki amene ayenera kutulutsidwa, (2) kusankha njira imene zinthuzo ndi mautumiki ziyenera kutulutsidwira, (3) kupeza njira yoperekera zimene zitulutsidwa, ndiyeno (4) kulinganiza zinthu kotero kuti mkhalidwe wazachuma upite patsogolo pamlingo woyenera ndi kupereka ntchito kwa onse.
Madongosolo a zachuma oyambitsidwa ndi anthu mosakanika apangitsa moyo kukhala wabwino, akumatipatsa zinthu ndi mautumiki amene sitikakhoza kudzipezera. Kaŵirikaŵiri madongosolo ameneŵa apititsa patsogolo kwambiri njira ya moyo. Njira zolankhulana zopita patsogolo zimatilola kukambitsirana ndi anthu kumbali iriyonse ya dziko mwakugwiritsira ntchito telefoni m’timphindi tochepa, kuwatumizira mauthenga pa fax m’mphindi zochepa, ndipo ngakhale kupanga ulendo m’maola ochepa kukalankhula nawo mwachindunji.
Komabe, sitinganyalanyaze mfundo yakuti dongosolo lamalonda limasonkhezera anthu mwa njira yaikulu koposadi. Pamodzi ndi chipembedzo ndi ndale zadziko, lingayambukire mtsogolo mwathu mwenimwenimo.a Chotero nkoyenerera tsopano kupenda mbali yaikulu yachitatu ya chitaganya cha anthu, dongosolo lamalonda. Kodi linakhala motani lamphamvu chotero? Kodi likupita kuti? Kodi ilo limatikhudza motani monga munthu payekha?
[Mawu a M’munsi]
a Galamukani! yafalitsa mipambo iŵiri ya nkhani zimene zinasonyeza mowonekera bwino mmene zimenezi ziliri tero ponena za chipembedzo ndi madongosolo andale zadziko. “Mtsogolo mwa Chipembedzo Poyerekezera ndi Nthaŵi Yake Yapita,” January 8, 1989 mpaka January 8, 1990; “Ulamuliro wa Anthu Uyesedwa Pamiyeso,” August 8, 1990 mpaka January 8, 1991.
[Bokosi patsamba 5]
Kumasulira Dongosolo Lamalondalo
Inu mwina mungakupeze kukhala kovuta kumasulira mawu onga ngati “zamalonda,” “malonda,” “indasitale,” “bizinesi,” ndi “zachuma.” Collins Cobuild English Language Dictionary imamasulira “zamalonda” mokhweka kukhala “machitachita ndi njira zoloŵetsedwa m’kugula ndi kugulitsa zinthu.” Kwakukulukulu zimenezi zimaloŵetsamo “malonda,” amene ali “ntchito ya kugula, kugulitsa, kapena kusinthana zinthu kapena mautumiki pakati pa anthu, makampani, kapena maiko.” Ndithudi, zinthu ziyenera kupangidwa kapena kukonzedwa zisanagulitsidwe, kachitidwe kamene kamatchedwa “indasitale.” Ndipo ntchito yokhudza zamalonda ndi malonda imatchedwa “bizinesi.”
“Zachuma,” ndizo “kupenda kupezedwa kwa chuma ndi kugwiritsiridwa ntchito kwa zinthu ndi mautumiki m’chitaganya, ndi kulinganizidwa kwa ndalama zake, maindasitale, ndi malonda.” Chenicheni chakuti liwulo linatengedwa ku Chigiriki chofotokoza kusamaliridwa kwa banja kapena katundu chimatipatsa chidziŵitso chowonjezereka chonena za tanthauzo lake.