Malo Kuchokera ku Dziko Lolonjezedwa
Yordano Amene Simungamdziŵe
KUTCHULIDWA kwenikweniko kwa Mtsinje wa Yordano kungakukumbutseni zochitika zozoloŵereka: Kuwoloka kwa Aisrayeli pansi pa Yoswa pamalo ouma pafupi ndi Yeriko; kusamba kwa Namani nthaŵi zisanu ndi ziŵiri m’madzi ake kuti achiritsidwe khate lake; kudzabatizika kwa Ayuda ambiri, ndipo pambuyo pake kubatizidwa kwa Yesu, kochitidwa ndi Yohane.—Yoswa 3:5-17; 2 Mafumu 5:10-14; Mateyu 3:3-5, 13.
Mwachiwonekere, zochitika zotchuka zonsezi zinachitikira mmalo aatali ndipo odziŵika kwambiri a Yordano, chigawo cha kum’mwera kwa Nyanja ya Galileya ndi kunsi kwa Nyanja Yakufa. Koma ophunzira akhama a Mawu a Mulungu angakhale akunyalanyaza kufutukuka kwina kwa Yordano—mbali ya kumpoto kwa mtsinjewo ndi malo ake ozungulira. Onani pamapu.a Chigawo cha kunsi pakatipo chiri mbali ya Great Rift Valley, mbali yosiidwa m’zithunzi zina yochokera ku Suriya kunka ku Afirika.
Magwero atatu aakulu a Mtsinje wa Yordano ndiwo mifuleni yomwe imachokera ku kusungunuka kwa chipale chofeŵa pa Phiri la Hermoni. Mfuleni wa kummawa kwenikweni (tsamba 17, pamwamba) umachokera pa njereza ya therezi pafupi ndi m’mphepete mwa phiri. Uku nkomwe kunali Kaisareya wa Filipi; kumbukirani kuti Yesu anapita kumeneko mwamsanga asanasandulike pa ‘phiri lalitali.’ (Mateyu 16:13–17:2) Mfuleni wina umachokera pachiundasi kumene mzinda wa Dani unamangidwira, pomwe Aisrayeli a ufumu wa kumpoto anadziimitsira mwana wang’ombe wagolidi. (Oweruza 18:27-31; 1 Mafumu 12:25-30) Mfuleni wachitatu unathira mwa iŵiriyi ndikupanga Mtsinje wa Yordano, womwe umathira mamita oposa mazana atatu m’makilomita pafupifupi khumi ndi limodzi.
Kenaka chigwacho chimakhala chathyathyathya ndikupanga Khwawa la Hula, kupangitsa madzi a Yordano kumwazikana, ndikupanga dambo lalikulu. M’nthaŵi zakale madzi ambiri ankathiridwa m’damu lakuya lotchedwa Nyanja ya Hula (kapena Huleh). Koma Nyanja ya Hula kulibeko chifukwa chakuti m’nthaŵi zamakono mtunda wa Yordano unasalalitsidwa, ngalande zinawonjezeredwa kuchotsa madzi adera la dambolo, ndipo kotulukira madzi a nyanjayo kunazamitsidwa. Chotero, mutapenya paderalo pa mapu ndikuwona kumpoto kwa Nyanja ya Galileya, nyanja ya (Hula), mudzazindikira kuti mapuyo ikusimba za dera la m’nthaŵi zakale, osati monga mmene mumaiwonera lerolino.
Komabe, mutaichezera, mudzapeza malo achilengedwe omwe angakupatseni lingaliro la mmene deralo linaliri m’nthaŵi ya Baibulo, pamene kunali mitundu yapadera ya zomera, monga ngati nkhalango yodzala ndi gumbwa ndi mabango.—Yobu 8:11.
Deralo linali mudzi wa mbalame zosiyanasiyana. Akakowa, zimeza, vuwo, njiwa, ndi mbalame zina zinali zambiri, mwapang’ono chifukwa chakuti matenjetenje ndi nyanjazo zinapanga malo opumira abwino kwambiri pamaulendo awo a pakati pa Ulaya ndi Afirika. (Deuteronomo 14:18; Salmo 102:6; Yeremiya 8:7) Zolengedwa zina zokhala m’deralo zingakhale zinali zosawonekawoneka, koma kukhalamo kwawo kunapangitsa kudutsa Khwawa la Hula kukhala kowopsya. Izi mwachidziŵikire zinaphatikizapo mkango, mvuu, mbulu, ndi nguluwe. (Yobu 40:15-24; Yeremiya 49:19; 50:44; Habakuku 1:8) M’nyengo zina malungo odzetsedwa ndi udzudzu amakhala ofala, mwachiwonekere awa ndi amodzi a malungo otchulidwa m’Baibulo.
Momvekera, ponse paŵiri munthu woyenda paulendo yekha ndi magulu apaulendo ankalambalala dera la matenjetenjeli. Chotero kodi nkuti kumene akawolokera Mtsinje wa Yordano kumpoto kwa chigwa cha Nyanja ya Galileya?
Pafupi ndi Nyanja ya Galileya panali matanthwe otundumuka; kutundumuka konga damuku ndiko kunachititsa madzi kubwerera ndi kupanga Nyanja ya Hula. Inu mungaiwone mbali ya kutundumukaku patsamba 16. Pamene Yordano athira mu iko chakum’mwera kwa Nyanja ya Galileya (yowonekera patali), madzi amayenda mwaliŵiro kwakuti amakhala oyera. Mwachiwonekere, apaulendo akale ayenera kukhala anachipeza kukhala chovuta kutsikira m’mpata wakuyawo ndi kuwoloka madzi aliŵiro a Yordano.
Pakati pa dera la matenjetenje la Khwawa la Hula ndi mpatawo panali kamfuleni kakafupi, kathyathyathya mmene madzi anayenda mwabata. Panopa apaulendo akalewo akadawoloka mtsinjewo mwachisungiko, ndipo kanakhala njira yaikulu kupyola Dziko Lolonjezedwa. Tsopano pali ulalo pamalowa, omwe adakali malo oyambirira owolokera Yordano.
Khwawa la Hula lerolino ndi dera lachonde lamalimidwe; uku kulinso madziŵe a nsomba. Zonsezi nzothekera chifukwa cha madzi ambirimbiri omwe amadzathirira m’dera limeneli la Mtsinje wa Yordano.
[Mawu a M’munsi]
a Yerekezani ndi mapu yaikulu ndi chithunzi cha mu 1990 Kalenda ya Mboni za Yehova.
[Mapu patsamba 17]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Hula
Sea of Galilee
[Mawu a Chithunzi]
Zozikidwa pa mapu yolembedwanso ndi Pictorial Archive (Near Eastern History) Est. ndi Survey of Israel
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 17]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
Zithunzi za nyama: Safari-Zoo of Ramat-Gan, Tel Aviv