Khalani ndi Khalidwe Labwino Limene Limalemekeza Mulungu
1 Kulikonse kumene tili, khalidwe lathu, kavalidwe kathu, ndi kapesedwe kathu kamachitira umboni za ife ndi Mulungu amene timalambira. Zimenezi zimaoneka kwambiri pamisonkhano ikuluikulu ya anthu a Mulungu, pamene anthu ambiri amationa. Tikakhala achitsanzo chabwino, dzina la Yehova limalemekezeka. (1 Pet. 2:12) Komabe, khalidwe loipa kapena zochita zosayenera zochitidwa ndi anthu ochepa zingatonzetse dzina la Mulungu ndiponso anthu ake. (Mlal. 9:18b) Kumbukirani kuti anthu akunja amaweruza gulu lathu ndiponso Mulungu amene timalambira mwa makhalidwe athu. Izi ziyenera kutipangitsa kukhala osamala mwa ‘kuchita zonse ku ulemerero wa Mulungu.’—1 Akor. 10:31.
2 Malo Ogona: Nthaŵi zambiri abale amakonza kukakhala ndi achibale kapena mabwenzi awo m’mizinda yomwe mumachitikira msonkhano. Kumidzi, abale amamanga misasa kapena amagona m’misasa yogonamo anthu ambiri yomwe antchito odzifunira amamanga. Pamisonkhano ingapo, osonkhana amagona m’nyumba zogona za ana asukulu. Ngati mukugona kwa abale kapena achibale, si bwino kupezerapo mwayi pa kuchereza kwa abale athu n’kumangokhalabe komweko masiku ambiri kuti muthere konko tchuthi msonkhanowo utatha. Zipinda zimenezo ndi zanthaŵi ya msonkhano yokha. Choncho amene apatsidwa malo ayenera kuona kuti iwowo pamodzi ndi ana awo akuchita mwaulemu panyumbapo ndi kuti sakuwononga chilichonse kapena kugwiragwira zinthu kapena kuloŵa malo osayenera iwo kuloŵamo. Ngati eninyumba akuona kuti zina ndi zina zikuwavuta pankhani imeneyi, ayenera kukauza Dipatimenti ya Zipinda pamsonkhanopo, ndipo abale kumeneko adzawathandiza.
3 Kupeŵa Moto ndi Ngozi Zina: Mosakayikira, chimene makamaka chimabutsa moto pamisonkhano sindicho kuphika chakudya pafupi ndi misasa, koma ana osayang’aniridwa amene amaseŵera ndi moto kapena kuuyang’anira. Chotero, kaamba kodziteteza nokha komanso abale anu, musalole ana anu kuyendayenda okha; musauze ana aang’ono kuti ayang’anire madzi oŵira, kapena kuti ayang’anire moto wophikira. Iwo angathe kuchita bwino lomwe zinthu zimenezi kunyumba, koma malo a msonkhano ndi malo ena ndipo pafunika kusamala kwambiri kuti pasachitike ngozi. Anthu ambiri amakhalirana pafupi, ndipo ana amakonda kuseŵera pamene ali ndi ana anzawo. Sachedwa kudodometsedwa ndipo saganizako za ngozi, choncho sitiyenera kuwapatsa makandulo, macheso kapena nyali. Vuto lina limabuka pamene makolo apita kukamvetsera mapulogalamu ndi kusiya ana aang’ono kumsasa popanda owayang’anira. Ana ayenera kukhala pamodzi ndi makolo awo panthaŵi ya mapulogalamu. Pamene akalinde aona ana akuyendayenda okha pamalo a msonkhano, ayenera kuwapititsa kwa makolo awo. Makolo, chonde gwirizanani ndi antchito a msonkhano ndipo mwakutero sonyezani ‘kukonda abale.’—1 Pet. 2:17.
4 Gulu la Yehova mwachikondi limapereka zikumbutso zapanthaŵi yake zokhudza misonkhano. N’zachisoni kuti pamisonkhano ingapo m’zaka zapitazi, ena opezeka pamisonkhano zinthu zawo zinawonongeka chifukwa cha moto umene ukanapeŵedwa. Abale amene ali ndi udindo pamisonkhano, makamaka makolo, akupemphedwa kusamalira kwambiri mfundo zofunika zimenezi kuti misonkhano yathu idzakhale ya mayanjano omangirira ndi okondweretsa, isadzakhale ya kulira ndi chisoni chifukwa cha kusasamala komwe kungachititse ngozi.
5 Kuvala Bwino pa Msonkhano: Malo alionse amene tikuchitirapo msonkhano tiyenera kuwaona monga Nyumba ya Ufumu yaikulu, mosasamala kanthu kuti malowo ndi otani. Payenera kuoneka mavalidwe ndi mapesedwe abwino monga mmene timachitira popita ku misonkhano ya kumpingo kwathu. Pamapulogalamu ndiponso mapulogalamu akatha, abale ndi alongo ayenera kupeŵa kuvala zovala zosapereka ulemu kapena za mafashoni, zimene zimasonyeza mzimu wadziko zomwe zingatipangitse kukhala kovuta kuoneka kuti ndife osiyana kwambiri ndi ena. Alongo ayenera kuonetsetsa kuti masitayelo ndi kutalika kwa masiketi ndi madiresi awo n’zopatsa ulemu. (1 Tim. 2:9, 10) Kaya tapita kumsonkhano, kukhala m’nyumba yalendi, kudya mu resitilanti, kapena kugula zinthu m’sitolo, nthaŵi zonse tiyenera kusonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu, osakhumudwitsa m’chinthu chilichonse.—2 Akor. 6:3.
6 Pamsonkhano ubatizo udzachitika Loŵeruka m’maŵa. Tsamba 30 la Nsanja ya Olonda ya April 1, 1995, limafotokoza mkhalidwe umene tiyenera kusonyeza pamwambo umenewu. Limanena kuti “tiyenera kupatsa ubatizo ulemu woyenera. Si nthaŵi ya kukuwa motengeka maganizo, kapena yochita phwando, ndiponso phokoso lachikondwerero. Komanso si kuti ndi nthaŵi yachisoni kapena yoopsa.” Kukakhala kosayenera kwambiri kwa amuna kapena akazi opita kuubatizo kuvala zovala zosambira zifupizifupi kwambiri kapena zoonetsa m’kati. Choncho, onse ayenera kusonyeza ulemu ndi chimwemwe cha ubatizo wachikristu.
7 Petro akutikumbutsa kuti ‘tiyenera ife kukhala anthu otani nanga m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo.’ (2 Pet. 3:11) Mawu athu ndi zochita zathu pamsonkhano wakuti “Akuchita Mawu a Mulungu” zithandizetu otiona kudziŵa ndi kulambira Mulungu wathu wamkulu, amene ali woyenera ulemu ndi ulemerero wonse.—1 Akor. 14:24, 25.