Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/03 tsamba 1
  • Misonkhano Yachigawo Yatilimbikitsa Kupatsa Mulungu Ulemerero!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yachigawo Yatilimbikitsa Kupatsa Mulungu Ulemerero!
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Nkhani Yofanana
  • Patsani Mulungu Ulemerero Osati Anthu
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Mukuonetsa Ulemerero wa Yehova?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Musalole Chilichonse Kukulepheretsani Kupeza Ulemerero
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kodi Mudzawalitsa Ulemerero wa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 10/03 tsamba 1

Misonkhano Yachigawo Yatilimbikitsa Kupatsa Mulungu Ulemerero!

Misonkhano Yachigawo yakuti “Patsani Mulungu Ulemerero” imene yakhala ikuchitika mpaka pano yapereka umboni wamphamvu kwambiri. Misonkhano yauzimu yapadera imeneyi yalemekeza dzina la Yehova ndipo yatithandiza kudziŵa bwino zimene tingachite kuti ‘tim’patse Yehova ulemerero wa dzina lake.’ (Sal. 96:8) Indedi, Yehova ndi wofunika kumulemekeza chifukwa cha zinthu zodabwitsa zimene analenga, zimene zimasonyeza makhalidwe ake ochititsa chidwi.—Yobu 37:14; Chiv. 4:11.

Mwakugwiritsa ntchito mafunso amene ali m’munsiŵa komanso notsi zimene munalemba, konzekerani kuti mudzayankhe nawo pa kubwereramo kwa pulogalamu ya msonkhano wachigawo kumene kudzachitike mlungu woyambira October 20.

1. Kodi zinthu zopanda moyo zimene Mulungu analenga zimalengeza bwanji ulemerero wa Mulungu, ndipo kodi zimenezi zimasiyana bwanji ndi mmene anthu amamulemekezera? (Sal. 19:1-3; nkhani yakuti “Chilengedwe Chimalengeza Ulemerero wa Mulungu”)

2. Kodi kusandulika kwa Yesu kwakwaniritsidwa motani panopa, ndipo kodi Akristu masiku ano amalimbikitsidwa bwanji ndi zimenezi? (nkhani yaikulu yakuti “Masomphenya Aulemerero Okhudza Maulosi Amatilimbikitsa!”)

3. Kodi tingakulitse bwanji kudzichepetsa ngati kumene mneneri Danieli anasonyeza, ndipo kodi kuchita zimenezi kudzatipindulitsa bwanji? (Dan. 9:2, 5; 10:11, 12; nkhani yakuti “Ulemerero wa Yehova Umavumbulidwa kwa Anthu Odzichepetsa”)

4. (a) Kodi ndi zinthu zitatu ziti zokhudza chiŵeruzo cha Mulungu zimene tingaphunzire mu ulosi wa Amosi? (Amosi 1:3, 11, 13; 9:2-4, 8, 14) (b) Kodi Mboni za Yehova masiku ano zingaphunzire chiyani pa chenjezo limene limapezeka pa lemba la Amosi 2:12? (nkhani yakuti “Ulosi wa Amosi—Uthenga Wofunika M’nthaŵi Yathu”)

5. (a) Kodi kumwa moŵa mopitirira muyezo, ngakhale ngati munthuyo sanaledzere, n’koopsa bwanji? (b) Kodi munthu angathetse bwanji vuto la kumwa moŵa mopitirira muyezo? (Marko 9:43; Aef. 5:18; nkhani yakuti “Peŵani Msampha wa Kumwa Moŵa Mopitirira Muyezo”)

6. Kodi munapindula bwanji ndi nkhani yakuti “‘Dziko Lokoma’ Linali Chithunzi cha Paradaiso”?

7. Kodi ‘tingaonetse ulemerero wa Yehova monga akalirole’ m’njira zitatu ziti? (2 Akor. 3:18; nkhani yakuti “Onetsani Ulemerero wa Yehova Monga Akalirole”)

8. Kodi n’chiyani chimapangitsa anthu kudana nafe popanda chifukwa, ndipo n’chiyani chingatithandize kukhalabe okhulupirika ngakhale pamene anthu akudana nafe motero? (Sal. 109:1-3; nkhani yakuti “Odedwa Popanda Chifukwa”)

9. Kodi maganizo onga a Kristu pa nkhani ya kukhala wamkulu ndi otani, ndipo kodi munthu angadziŵe bwanji kuti ayenera kukulitsa maganizo amenewo? (Mat. 20:20-26; nkhani yakuti “Khalani ndi Maganizo Onga a Kristu Pankhani ya Kukhala Wamkulu”)

10. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe amphamvu mwauzimu ngakhale pamene tili otopa? (nkhani yakuti “Otopa Koma Osalefuka”)

11. Kodi zina mwa njira zimene Satana amafalitsira mabodza ndi ziti, ndipo kodi tiyenera kuchita chiyani mogwirizana ndi zimene Malemba amanena tikakumana ndi zinthu zofuna kuwononga chikhulupiriro chathu? (Yoh. 10:5; nkhani yakuti “Chenjerani ndi ‘Mawu a Alendo’”)

12. Kodi makolo angatsatire bwanji chitsanzo cha Yesu chimene achifotokoza pa lemba la Marko 10:14, 16? (nkhani yakuti “Ana Athu Ndi Choloŵa Chamtengo Wapatali”)

13. Kodi achinyamata akulemekeza bwanji Yehova? (1 Tim. 4:12; nkhani yakuti “Mmene Achinyamata Akulemekezera Yehova”)

14. Kodi ndi mbali ziti za seŵero lakuti “Kulalikira Molimba Mtima Ngakhale Pali Otsutsa” zimene zili zosaiŵalika kwa inu?

15. Kodi tingatsanzire bwanji chitsanzo cha (a)Petro ndi Yohane? (Mac. 4:10) (b) Stefano? (Mac. 7:2, 52, 53) (c) mpingo wachikristu wa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino? (Mac. 9:31; seŵero ndiponso nkhani yakuti “Lengezani Uthenga Wabwino ‘Mosaleka’”)

16. (a) Kodi tinatsimikiza kuti tidzam’patsa Mulungu ulemerero m’njira ziti? (b) Kodi tingayembekezere chiyani ngati tigwiritsa ntchito zimene tinaphunzira pa misonkhano yachigawo ya “Patsani Mulungu Ulemerero”? (Yoh. 15:9, 10, 16; nkhani yakuti “‘Pitirizani Kubala Zipatso Zambiri’ Kuti Yehova Alemekezeke”)

Kusinkhasinkha malangizo auzimu abwino kwambiri amene tinamva pa msonkhanowo kudzatilimbikitsa kugwiritsira ntchito zinthu zimene tinaphunzira. (Afil. 4:8, 9) Zimenezi zidzatithandiza kukhala otsimikiza ‘kuchita zonse ku ulemerero wa Mulungu.’—1 Akor. 10:31.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena