Nyimbo Zimene Zimatsitsimula
1 Nyimbo ndiponso kuimba ndi zinthu zofunika kwambiri pa kulambira koona. Mu Israyeli wakale, Asafu ndi abale ake anaimba kuti: “Yamikani Yehova . . . Muimbireni, muimbireni zom’lemekeza; fotokozerani zodabwiza zake zonse.” (1 Mbiri 16:8, 9) Masiku ano timaimbira nyimbo Yehova pamisonkhano yathu ya mpingo imene timachita mlungu uliwonse. (Aef. 5:19) Umenewutu ndi mwayi waukulu wotamanda dzina lake!—Sal. 69:30.
2 Kumvetsera nyimbo za Ufumu za malimba za Kingdom Melodies, kungatithandize kukhala ndi maganizo auzimu. Mlongo wina anafotokoza kuti: “Nyimbozo zikamaimba, ndimakumbukira mawu ake m’maganizo mwanga. Imeneyi ndi njira yabwino kwambiri yoganizira za Yehova kwinaku ndikusangalala ndi nyimbo.”—Afil. 4:8.
3 Nthaŵi Zimene Mungamvere Nyimbo: Kumvetsera nyimbo za Kingdom Melodies kunyumba kumachititsa kuti pakhale mtima waubwenzi ndiponso woganizira zinthu zauzimu zimene zimathandiza kuti pabanjapo pakhale mtendere. Banja lina linalemba kuti: “Timamvetsera [nyimbozi] mobwerezabwereza kunyumba kwathu ndiponso m’galimoto ndipo sititopa nazo chifukwa anazikonza bwino kwambiri. Nthaŵi zambiri nyimbo za Kingdom Melodies zathandiza kuti tikhale ndi maganizo abwino pokonzekera misonkhano yachikristu kapena popita ku misonkhano yaikulu.” Mlongo wina ananena kuti: “Nyimbozi zimandisangalatsa kwambiri kuzimvetsera ndikamagwira ntchito zapakhomo, ndipo ndani angaganize kuti ndingamasangalale kwambiri popinda zovala ndi zinthu zina? Ndimamvetsera nyimbozi ndikakhumudwa. Nyimbozi zimachititsa kuti munthu ukhale wosangalala. . . . Nyimbo iliyonse imayambitsa chimwemwe.” Kodi pali nthaŵi zimene nyimbo zotsitsimula zimenezi zingakuthandizeni?
4 Nyimbo zambiri za masiku ano zimasonyeza mzimu wa dziko. Makolo angathandize ana awo kuti azikonda nyimbo zabwino pogwiritsa ntchito bwino nyimbo za Kingdom Melodies. Ophunzira Baibulo ambiri ndi anthu achidwi angasangalalenso kudziŵa za nyimbo zauzimu zabwino kwambiri zimenezi, zomwe zimalemekeza Yehova ndi kutsitsimula moyo.—Sal. 47:1, 2, 6, 7.