Kulambira Yehova Pamodzi Monga Banja
1 M’nthawi za m’Baibulo, anthu pabanja ankachitira pamodzi zinthu zambiri. Ankachitira limodzi ntchito zapakhomo koma chofunika kwambiri chinali chakuti ankalambira Yehova monga banja. (Lev. 10:12-14; Deut. 31:12) Masiku ano, m’madera ambiri, ndi zinthu zochepa zomwe anthu pabanja amachitira limodzi. Koma Akhristu amaona kuti kuchita zinthu pamodzi monga banja n’kofunika, makamaka pankhani yolambira. Yehova yemwe anayambitsa banja amasangalala kwambiri akamaona mabanja akum’lambira pamodzi mogwirizana.
2 Lalikirani Pamodzi: Banja limakhala logwirizana kwambiri likamagwirira pamodzi ntchito yolalikira uthenga wabwino. Motero, kuwonjezera pa kugwira ntchito yolalikira ndi anthu ena mumpingo, mkulu afunikiranso kumayenda mokhazikika ndi mkazi wake ndiponso ana ake. (1 Tim. 3:4, 5) Ngakhale kuti oyang’anira oyendayenda amakhala otanganidwa kwambiri, iwo amapatula nthawi yoyenda ndi akazi awo muutumiki.
3 Makolo amene amalalikira limodzi ndi ana awo amatha kuwathandiza kuti akhale aluso polengeza uthenga wabwino. Kuwonjezera pa kuona chimwemwe chimene makolo awo amakhala nacho muutumiki, ana adzaonanso mmene makolowo amakondera Yehova ndiponso anthu ena. (Deut. 6:5-7) Ngakhale anawo atakula zimenezi n’zofunikabe. Mwamuna wina ndi mkazi wake omwe ali ndi ana amuna atatu azaka za pakati pa 15 ndi 21 amayendabe limodzi ndi anawo muutumiki nthawi ndi nthawi. Bamboyo anati: “Nthawi zonse timawaphunzitsa kenakake. Ndipo timaonetsetsa kuti asangalale ndi kulimbikitsidwa.”
4 Konzekerani Pamodzi: Mabanja aona kuti n’kopindulitsa kukonzekera pamodzi utumiki wa kumunda. Nthawi zambiri ana amasangalala pamene m’banja muyeserera utumiki mukumasinthanasinthana kulalikira kapena kukhala mwininyumba. Mabanja ena amagwiritsa ntchito mphindi zomalizira za phunziro lawo labanja kuti achite zimenezi.
5 Chimwemwe chathu chimawonjezereka tikamagwira ntchito zofunika ndiponso zosangalatsa pamodzi ndi anthu amene timawakonda. Anthu m’banja amasangalala kwambiri akamachitira pamodzi utumiki wolalikira nyumba ndi nyumba, kupanga maulendo obwereza ndiponso kuchititsa maphunziro a Baibulo. Motero, mukamalambira Yehova pamodzi ndi banja lanu, munganene mosangalala kuti: ‘Ine, ndi a m’nyumba yanga, tizitumikira Yehova.’—Yos. 24:15.