Khalani ndi Cholinga Chopeza Phunziro la Baibulo
1 “Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.” (Yoh. 4:35) Mawu amenewa, omwe analankhulidwa ndi Yesu Khristu amafotokoza bwino mmene ntchito ya Akhristu ilili masiku ano.
2 Anthu amene amafunadi kuphunzira za Yehova akupezekabe. Umboni wa zimenezi ndi anthu ambiri amene amabatizidwa chaka chilichonse. Ngati mukufunadi kukhala ndi phunziro la Baibulo, kodi muyenera kuchita chiyani?
3 Khalani ndi Cholinga: Choyamba, khalani ndi cholinga choyambitsa ndi kumachititsa phunziro la Baibulo mokhazikika. Mukakhala muutumiki wakumunda, musaiwale cholinga chimenechi. Popeza kuti ntchito ya Akhristufe ndi kuphunzitsa komanso kulalikira, tonsefe tiyenera kuyesetsa kuti tizichititsa phunziro la Baibulo.—Mat. 24:14; 28:19, 20.
4 Zinthu Zina Zofunika Kukumbukira: Pemphero lochokera pansi pamtima ndi lofunika kwambiri kwa olengeza Ufumu. Nthawi zina timapeza anthu amene apemphera kuti athandizidwe mwauzimu. Ndi dalitso lalikulu kuti Yehova atigwiritsire ntchito kupeza ndi kuphunzitsa anthu oterewo.—Hag. 2:7; Mac. 10:1, 2.
5 Mlongo wina anapemphera kuti apeze phunziro la Baibulo, kenako kuntchito kwake iye anaika poonekera timapepala ta mutu wakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? Mayi wina ataona timapepalato anatolapo kamodzi n’kukawerenga mpaka kumaliza, kenako anayamba kulemba pa danga lili pa tsamba lomaliza. Pamenepo mlongoyo analankhula ndi mayiyo moti anayamba kuphunzira naye Baibulo.
6 Ofalitsa anzanu amene ali ndi luso loyambitsa ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo angakuthandizeni kukwaniritsa cholinga chanu chopeza phunziro la Baibulo. Funafunani mwakhama munthu wofuna kuphunzira Baibulo, ndipo gwiritsani ntchito thandizo lililonse limene mungapeze kuti mukwaniritse cholinga chanu. Mwina nanunso posachedwapa mudzasangalala kukhala ndi phunziro la Baibulo.