Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/09 tsamba 2
  • Kodi Tingakonzekere Bwanji Msonkhano wa Utumiki?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tingakonzekere Bwanji Msonkhano wa Utumiki?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Malangizo Okhudza Abale Amene Amakamba Nkhani pa Msonkhano wa Utumiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Msonkhano Wautumiki Umatikonzekeretsa Kuchita Ntchito Iliyonse Yabwino
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Mfundo Zopatsa Chidziŵitso, Zofotokozedwa Momveka Bwino
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Muli Olandiridwa
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 5/09 tsamba 2

Kodi Tingakonzekere Bwanji Msonkhano wa Utumiki?

1. Kodi cholinga cha Msonkhano wa Utumiki n’chiyani, ndipo tingatani kuti tipindule kwambiri ndi msonkhano umenewu?

1 Msonkhano wa Utumiki umakonzedwa n’cholinga choti utithandize kukhala ogwira mtima mu utumiki. Nkhani za pamsonkhanowu zimakhala zokhudza kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu, kupanga ophunzira, ndiponso kulengeza chiweruzo cha Mulungu chimene chayandikira. (Mat. 28:20; Maliko 13:10; 2 Pet. 3:7) Timapindula kwambiri ndi msonkhano wofunika umenewu tikakonzekera bwino ndiponso tikamatenga nawo mbali.

2. Kodi tingakonzekere bwanji kumvetsera nkhani?

2 Nkhani: Nthawi zambiri, malangizo opita kwa wokamba nkhani amasonyeza kumene mfundo za nkhaniyo zikuchokera. Werengani nkhaniyo, kuphatikizapo malemba osagwidwa mawu ndipo ganizirani mmene mungagwiritsire ntchito mfundozo mu utumiki wa kumunda.

3. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikonzekere nkhani ya mafunso ndi mayankho?

3 Nkhani ya Mafunso ndi Mayankho: Nkhani imeneyi imachitika mofanana ndi phunziro la Nsanja ya Olonda. Imakhala ndi mawu oyamba komanso omaliza achidule. Dulani mzere kunsi kwa mfundo zazikulu m’ndime iliyonse ndipo konzekerani kupereka ndemanga zachidule zotsindika mfundo zimene mukukambirana.

4. Kodi tingakonzekere bwanji nkhani yokambirana ndi omvera?

4 Nkhani Yokambirana ndi Omvera: Mbali imeneyi imakambidwa ngati nkhani, koma wokamba nthawi zina amapempha omvera kupereka ndemanga. Ngati mungadule mzere kunsi kwa mfundo zazikulu ndiponso kuwerenga malemba osagwidwa mawu, mungathe kuyankhapo pamene akufunsa mafunso. M’bale amene akukamba nkhani imeneyi adzayesetsa kufunsa omvera pa mfundo zazikulu za nkhaniyo.

5. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizipindula kwambiri ndi zitsanzo?

5 Zitsanzo: M’nkhani zina mungakhale zitsanzo zosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito mfundo za m’nkhaniyo m’gawo lathu. Zitsanzo zimenezi zingachitidwe ndi akulu, ofalitsa aluso kapena apainiya. Pokonzekera mbali imeneyi, ndi bwino kuganizira mmene chitsanzocho chingachitikire. Onetsetsani kuti mwatenga mabuku kapena magazini amene akagwiritse ntchito pa chitsanzocho. Pamene akuchita chitsanzo chosonyezedwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu, muziganizira mmene mungafotokozere mfundozo kwa anthu osiyanasiyana mu utumiki. Mungapindulenso kwambiri ngati mungamayeseze zitsanzo zimenezi pamene mukuchita Kulambira kwa Pabanja.

6. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera Msonkhano wa Utumiki?

6 Msonkhano wa Utumiki umakhala wosangalatsa ngati takonzekera ndi kusinkhasinkha mfundo za mu nkhaniyo. Kutsatira malangizo amenewa kudzathandiza kuti tizilimbikitsana. (Aroma 1:11, 12) Tikamapeza nthawi yokonzekera Msonkhano wa Utumiki, tidzakhala okonzeka kukwaniritsa ntchito imene tapatsidwa.—2 Tim. 3:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena