MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Tidzagwira Ntchito Yapadera mu November Yolengeza za Ufumu wa Mulungu
Yesu analengeza “uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” (Lu 4:43) Iye anaphunzitsanso anthu kuti azipemphera kuti Ufumuwo ubwere. (Mt 6:9, 10) M’mwezi wa November tizidzayesetsa kulengeza kwambiri za Ufumu wa Mulungu. (Mt 24:14) Mukonze zinthu n’cholinga choti mudzathe kugwira nawo mwakhama ntchito imeneyi. Onse amene adzachite upainiya wothandiza adzatha kusankha kupereka maola 30 kapena 50 pa mwezi umenewu.
Tizidzayesetsa kuwerengera anthu ambiri m’gawo lathu lemba lokhudza Ufumu wa Mulungu. Mukamadzasankha lemba loti muwerenge, muzidzaganizira za chipembedzo cha anthuwo. Munthu akadzasonyeza chidwi, mudzamugawire Nsanja ya Olonda Na. 2 2020. Kenako musadzachedwe kupitanso kwa munthuyo n’cholinga choti mudzayambe kuphunzira naye Baibulo pogwiritsa ntchito chimodzi mwa Zinthu Zophunzitsira. Nthawi yoti Ufumu wa Mulungu uwononge maboma onse otsutsa Ufumuwo yayandikira kwambiri. (Da 2:44; 1Ak 15:24, 25) Choncho tiyeni tidzayesetse kugwira nawo mwakhama ntchito yapaderayi kuti tisonyeze kuti ndife okhulupirika kwa Yehova komanso Ufumu wake.
Ufumu wa Mulungu Udzabweretsa madalitso ambiri padzikoli!