Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb23 July tsamba 16
  • Ntchito Yapadera Yolengeza za Ufumu wa Mulungu mu September

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ntchito Yapadera Yolengeza za Ufumu wa Mulungu mu September
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Nkhani Yofanana
  • Tidzagwira Ntchito Yapadera mu November Yolengeza za Ufumu wa Mulungu
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Ntchito Yapadera Yoyambitsa Maphunziro a Baibulo mu September
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Mwayi Winanso Wotamanda Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Muzilalikira Uthenga Wabwino Wakuti Dziko Labwino Layandikira
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
mwb23 July tsamba 16
Yesu wakhala pampando wachifumu kumwamba ndipo akulamulira dziko lapansi la Paradaiso.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Ntchito Yapadera Yolengeza za Ufumu wa Mulungu mu September

M’mwezi wa September, tidzagwira ntchito yapadera yothandiza anthu kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene uthetse mavuto amene tikukumana nawo. (Mt 24:14) Kodi tidzagwira bwanji ntchitoyi? Tidzawerengere anthu ambiri lemba lililonse lomwe limanena za Ufumu wa Mulungu m’mweziwu. Ngati wina wasonyeza chidwi, mudzam’patse magazini yogawira ya Nsanja ya Olonda Na. 2 2020. Kenako tidzabwerere mwachangu kwa anthu amene asonyeza chidwi ndipo tidzayambe kuphunzira nawo Baibulo pogwiritsa ntchito kabuku ka Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Amene adzachite upainiya wothandiza m’mwezi wa September, adzasankha kuchita wa maola 15 kapena 30.

“Nsanja ya Olonda” Na. 2 2020, yamutu wakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?”

Posachedwapa, Ufumu wa Mulungu uphwanya maulamuliro onse amene amatsutsa Ufumuwu. (Da 2:44; 1Ak 15:24, 25) Tiyeni tidzayesetse kugwira nawo ntchito yapaderayi kuti tidzasonyeze kuti tili ku mbali ya Yehova komanso Ufumu wake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena