18 Atatero, anasonkhanitsa anthu onse pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri. Anawasonkhanitsa n’cholinga chakuti awalembe m’kaundula+ kuti adziwe mibadwo yawo malinga ndi mabanja awo, ndiponso nyumba za makolo awo. Anawalemba mayina kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo,+ mmodzi ndi mmodzi.