Mungabweze Mbale Wanu
“Pita, num’langize panokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wam’bweza mbale wako.”—MATEYU 18:15.
1, 2. Kodi Yesu anapereka malangizo othandiza otani okhudza kuthetsa milandu?
ATATSALA ndi nthaŵi yautumiki wake yosakwanira chaka chimodzi, Yesu anali ndi maphunziro ofunika kwambiri kwa ophunzira ake. Mutha kuŵaŵerenga m’Mateyu chaputala 18. Phunziro limodzi linali la kufunika kwa kukhala odzichepetsa, monga ana. Kenako anagogomezera mfundo yakuti tizipeŵa kukhumudwitsa “kamodzi ka tiana iti” ndi kuti tiziyesa kubweza “aang’ono” amene akusokera kuti asatayike. Kenako Yesu anawonjezapo malangizo abwino, othandiza kuthetsa mavuto a pakati pa Akristu.
2 Mungakumbukire mawu ake akuti: “Ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, num’langize panokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wam’bweza mbale wako. Koma ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena aŵiri, kuti atsimikizidwe mawu onse pakamwa pa mboni ziŵiri kapena zitatu. Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.” (Mateyu 18:15-17) Kodi malangizo ameneŵa tiyenera kuwagwiritsa ntchito pankhani zotani, ndipo kodi tiyenera kukhala ndi malingaliro otani pochita zimenezo?
3. Kodi nthaŵi zambiri tiyenera kuchita chiyani pamene ena atilakwira?
3 Nkhani yoyambayo inagogomezera kuti popeza tonsefe ndife opanda ungwiro ndipo timalakwalakwa, tiyenera kuyesetsa kukhala okhululuka. Ziyenera kukhala motero makamaka pamene wina wakhumudwa ndi zimene Mkristu mnzake wanena kapena kuchita. (1 Petro 4:8) Nthaŵi zambiri zimakhala bwino kwambiri kungopitirira cholakwacho—kukhululuka ndi kuchiiŵala. Tingaone kuchita zimenezi monga kuchirikiza mtendere wa mpingo wachikristu. (Salmo 133:1; Miyambo 19:11) Komabe, pangakhale nthaŵi zina pamene mungaone kuti muyenera kukambirana nkhaniyo ndi mbale kapena mlongo wanu amene anakukhumudwitsani. Zikatero, mawu a Yesu amene ali pamwambawo amapereka chitsogozo.
4. Kodi m’lingaliro lalikulu tingagwiritse ntchito motani Mateyu 18:15 pazolakwa za ena?
4 Yesu analangiza kuti ‘um’langize panokha iwe ndi iye.’ Imeneyo ndi nzeru. Pamawu ameneŵa, mabaibulo ena achijeremani amati, muuze mlandu wake “pomwe pali maso anayi,” kutanthauza anu ndi ake. Pamene mukambirana vuto mtseri, nthaŵi zambiri silivuta kulithetsa. Mbale amene anachita kapena kunena kanthu kena kokhumudwitsa kapena kankhanza angavomereze mosavuta kulakwa kwake kwa inuyo pamene muli aŵiriŵiri. Patakhala anthu ena omvetsera, chibadwa cha anthu opanda ungwiro chingam’pangitse kuukana mlanduwo kapena kuyesa kupereka chodzikhululukira pazimene anachita. Koma pamene mukambirana nkhaniyo “pomwe pali maso anayi,” mungapeze kuti kunali kumvana molakwa ndipo osati uchimo kapena kulakwa dala. Nonse aŵiri mutaona kuti kunali kumvana molakwa, mungakambirane, popanda kulola nkhani yaing’ono kukula ndi kuwononga unansi wanu. Chotero, pulinsipulo la pa Mateyu 18:15 tingaligwiritse ntchito ngakhale pankhani zazing’ono pamoyo watsiku ndi tsiku.
Kodi Anatanthauzanji?
5, 6. Malinga ndi nkhani yake, kodi Mateyu 18:15 anali kunena za machimo otani, ndipo n’chiyani chikusonyeza zimenezo?
5 Malangizo a Yesu amakhudza makamaka nkhani zazikulu. Yesu anati: “Ngati mbale wako akuchimwira iwe.” M’lingaliro lalikulu, ‘tchimo’ lingakhale kulakwa kapena kuphophonya kwina kulikonse. (Yobu 2:10; Miyambo 21:4; Yakobo 4:17) Komabe, nkhani yake ikusonyeza kuti Yesu anali kutanthauza tchimo lalikulu. Linali lalikulu lomwe likanapangitsa wolakwayo kuonedwa “monga wakunja ndi wamsonkho.” Kodi mawu amenewo amatanthauzanji?
6 Ophunzira a Yesu omwe anali kumvetsera mawu amenewo anali kudziŵa kuti ayuda anzawo sanali kuyenderana ndi Akunja. (Yohane 4:9; 18:28; Machitidwe 10:28) Ndipo anali kupeŵa amsonkho, anthu amene anali Ayuda koma amene anasanduka kukhala ochitira anzawo zoipa. Choncho nkhani ya pa Mateyu 18:15-17 inkanena za machimo aakulu, osati kusiyana maganizo kapena kukhumudwitsana kumene mutha kungokhululukira ndi kukuiŵala.—Mateyu 18:21, 22.a
7, 8. (a) Kodi ndi machimo a mtundu wotani amene ayenera kusamalidwa ndi akulu? (b) Ndi machimo otani amene Akristu aŵiri angathe kukambirana, mogwirizana ndi Mateyu 18:15-17?
7 M’Chilamulo, machimo ena ankafuna zambiri zoposa kukhululukidwa ndi wochimwiridwayo. Mwano, mpatuko, kulambira mafano, ndi machimo okhudza kugonana monga dama, chigololo, ndi kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha anayenera kuululidwa kwa akulu (kapena ansembe) ameneno anali kusamalira milandu yake. Ndi mmenenso zilili mumpingo wachikristu. (Levitiko 5:1; 20:10-13; Numeri 5:30; 35:12; Deuteronomo 17:9; 19:16-19; Miyambo 29:24) Komano onani kuti mtundu wa machimo amene Yesu anali kunena pano anali oti anthu aŵiri okhudzidwawo angakambirane mlandu wake. Mwachitsanzo: Chifukwa cha kukwiya kapena nsanje, wina aneneza mnzake. Mkristu alonjeza kuchita ntchito ndi milimo yamtundu wakutiwakuti ndi kumaliza ntchitoyo patsiku loikidwa. Wina avomereza kuti adzabweza ndalama m’kupita kwa nthaŵi yakutiyakuti kapena patsiku lina loikidwa. Munthu alonjeza kuti wom’lemba ntchito akam’phunzitsa ntchito, sadzapikisana naye (ngakhale atakayamba ntchito kwina) kapena kuyesa kutenga makasitomala a wom’lemba ntchitoyo panthaŵi imene agwirizana kapena kumalo akutiakuti.b Ngati mbale sanasunge mawu ake ndipo sakulapa pazolakwa zimenezi, imeneyo ingakhaledi nkhani yaikulu. (Chivumbulutso 21:8) Koma anthu aŵiri okhudzidwawo angakambirane milandu imeneyi.
8 Komano tsono mungachite chiyani kuti muthetse nkhaniyo? Mawu a Yesuwo nthaŵi zambiri amaonedwa kukhala ndi mbali zitatu. Tiyeni tikambirane imodziimodzi. M’malo moona mawuwo ngati malamulo okhwima, yesetsani kuzindikira mfundo yake, ndipo musaiŵale cholinga chanu chachikondi.
Yesetsani Kubweza Mbale Wanu
9. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani pochita zimene Mateyu 18:15 amanena?
9 Yesu anayamba ndi mawu akuti: “Ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, num’langize panokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wam’bweza mbale wako.” Ndithudi simungachite zimenezi ngati mulibe umboni uliwonse. Muyenera kukhala ndi umboni kapena mfundo zomveka zimene mungalongosole pothandiza mbale wanu kuona kuti analakwa ndipo ayenera kuwongolera. Ndi bwino kuchita zimenezo msanga, osalola nkhaniyo kukula kapena kulola khalidwe lakelo kukhala chizoloŵezi. Ndipotu musaiŵale kuti kuganizira cholakwacho nthaŵi zonse kungakuwonongeni. Popeza kuti makambiranowo ayenera kukhala pakati pa inu ndi iyeyo basi, peŵani kuuza ena nkhaniyo musanakambirane pofuna kuti akuikireni kumbuyo kapena pofuna kudzisonyeza kuti ndinu munthu wabwino. (Miyambo 12:25; 17:9) Chifukwa chiyani? Chifukwa cha cholinga chanu.
10. N’chiyani chidzatithandiza kubweza mbale wathu?
10 Cholinga chanu chiyenera kukhala kubweza mbale wanu, osati kum’langa, kum’lalatira, kapena kum’vulaza maganizo. Ngatidi analakwa, unansi wake ndi Yehova uli pangozi. Inuyo mukufunadi kukhalabe naye monga mbale wanu wachikristu. Chiyembekezo chakuti nkhaniyo mudzaithetsa bwino chimakula ngati pokambirana naye m’tseri mukhalabe woleza mtima, mupeŵa mawu aukali kapena mawu omveka ngati mukumuimba mlandu. Pamakambirano achikondi a pamaso m’pamaso ameneŵa, kumbukirani kuti nonse aŵiri ndinu anthu opanda ungwiro, auchimo. (Aroma 3:23, 24) Pozindikira kuti simunam’chite miseche ndipo ataona kuti mukufuna kum’thandiza moona mtima, nkhaniyo ingathetsedwe mwamsanga. Njira imeneyi yokoma mtima ndiponso yolongosoka idzasonyeza nzeru makamaka zikapezeka kuti nonse aŵiri munali olakwa m’njira inayake kapena kuti kumvana molakwa n’kumene kwenikweni kunayambitsa vutolo.—Miyambo 25:9, 10; 26:20; Yakobo 3:5, 6.
11. Ngakhale kuti wochimwayo sakutimvera, kodi tingachitenji?
11 Ngati mwam’pangitsa kuona kuti analakwa ndi kuti ndi nkhani yaikulu, angakhudzike mtima kuti alape. Komatu, kunyada kungakhale chopinga. (Miyambo 16:18; 17:19) Chotero ngakhale kuti sanavomere cholakwacho ndi kulapa, mungayambe mwadikira musanapite nawo kwina mlanduwo. Yesu sananene kuti ‘pita kamodzi kokha, num’langize.’ Popeza ndi tchimo limene mungakambirane, lingalirani zokakambirananso naye mumzimu wa Agalatiya 6:1 komanso “pomwe pali maso anayi.” Mutha kulithetsa vutolo. (Yerekezani ndi Yuda 22, 23.) Komano, bwanji ngati muli wotsimikiza kuti anachitadi tchimo ndipo kuti sakufuna kumva?
Kupeza Chithandizo Chokhwima
12, 13. (a) Yesu analongosola mbali yachiŵiri iti yothetsera milandu? (b) Kodi pali malangizo oyenerera otani pochita mbali imeneyi?
12 Kodi inuyo mungakonde kuti ena angokulekererani mwamsanga mutapanga cholakwa chachikulu? Kutalitali. Ndiye chifukwa chake Yesu anasonyeza kuti mutachita mbali yoyamba, simuyenera kuleka kuyesa kubweza mbale wanu, kuti akhalebe wogwirizana nanu ndi ena polambira Mulungu m’njira yovomerezeka. Yesu anafotokoza mbali yachiŵiri: “Ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena aŵiri, kuti atsimikizidwe mawu onse pakamwa pa mboni ziŵiri kapena zitatu.”
13 Iye ananena kuti mutenge “wina mmodzi kapena aŵiri.” Sananene kuti mutachita mbali yoyamba, muli ndi ufulu wokambirana nkhani imeneyo ndi ena ambiri, kuonana ndi woyang’anira woyendayenda, kapena kulembera abale ena za vuto limenelo. Kaya mukhale wotsimikiza mtima chotani za cholakwacho, mulibe umboni wonse wofunikira. Simuyenera kufalitsa nkhani zoipa zimene zidzakupangitsani kukhala kazitape. (Miyambo 16:28; 18:8) Koma Yesu anati muyenera kutenga munthu winanso mmodzi kapena enanso aŵiri. Chifukwa chiyani? Nanga amenewo angakhale anthu otani?
14. Kodi tingatenge anthu ati pokakamba naye kachiŵiri?
14 Mukuyesa kubweza mbale wanu mwa kum’tsimikizira kuti wachita tchimo ndipo mwa kum’limbikitsa kulapa kuti akhale pamtendere ndi inu ndiponso ndi Mulungu. Kuti muchite zimenezo, zingakhale bwino kwambiri ngati “mmodzi kapena aŵiri” amenewo ali mboni za cholakwacho. Mwina analipo pamene iye anachimwa, kapena mwina ali ndi mfundo zenizeni zokhudza chimene chinachitikacho (kapena chimene sichinachitidwe) m’nkhani yabizinesi. Ngati mboni zoterozo palibe, awo amene mukutenga angakhale anthu odziŵa nkhani zimenezo ndipo angathe kudziŵa ngati zimene zinachitika zinalidi zolakwika. Komanso, ngati zingafunikire pambuyo pake, angakhale mboni ya zimene zinanenedwa, kutsimikizira mfundo zoperekedwazo ndi kuyesayesa komwe kunapangidwa. (Numeri 35:30; Deuteronomo 17:6) Chotero si anthu oti sanena chilichonse, kapena oweruza; koma amakhalapo kuti athandize kubweza mbale wanu ndi wawo.
15. N’chifukwa chiyani akulu achikristu angakhale othandiza pamene tikuchita mbali yachiŵiri?
15 Musaganize kuti awo amene mudzatenga afunikira kukhala akulu a mumpingo. Komabe, amuna okhwima amene ali akulu angathandizire chifukwa cha ziyeneretso zawo zauzimu. Akulu amenewo ali “monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.” (Yesaya 32:1, 2) Amadziŵa kukambirana ndi abale ndi alongo ndi kuwawongolera. Ndipo wolakwayo ali ndi chifukwa chabwino chosonyezera chidaliro mwa “mphatso za amuna” zimenezi.c (Aefeso 4:8, 11, 12, NW) Kukamba nkhani imeneyi pamaso pa anthu okhwima oterowo ndi kupemphera nawo kungasinthe mkhalidwe wonse ndi kuthetsa nkhani yomwe inkaoneka ngati yosatheka.—Yerekezani ndi Yakobo 5:14, 15.
Kuyesetsa Komaliza Kuti Mum’bweze
16. Kodi mbali yachitatu imene Yesu analongosola ndi iti?
16 Ngati mbali yachiŵiri yoti muthetse nkhaniyo ilephera, mosakayikira oyang’anira mumpingo amakhudzidwa pambali yachitatu. “Ngati iye samvera [mmodzi kapena aŵiriwo], uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.” Kodi zimenezi zimaloŵetsapo chiyani?
17, 18. (a) Kodi ndi chitsanzo chiti chimene chikutithandiza kumvetsa tanthauzo la ‘kuuza mpingo’? (b) Kodi mbali imeneyi timaichita motani lerolino?
17 Mawuwo sitikuwaona monga malangizo akuti mlandu wa tchimolo kapena cholakwacho udzikambidwa pamsonkhano wanthaŵi zonse kapena wapadera wa mpingo wonse. Titha kudziŵa njira yoyenera m’Mawu a Mulungu. Taonani zimene zinkachitika mu Israyeli wakale ngati panali kusamvera makolo, kuwononga zinthu, ndi kuledzera: ‘Munthu akakhala naye mwana wamwamuna wopulukira, ndi wopikisana naye, wosamvera mawu a atate wake, kapena mawu a mayi wake, wosawamvera angakhale anam’langa; azim’gwira atate wake ndi mayi wake, ndi kutulukira naye kwa akulu a mudzi wake, ndi kuchipata cha malo ake; ndipo anene kwa akulu a mudzi wake, Mwana wathu wamwamuna uyu n’ngwopulukira ndi wopikisana nafe, wosamvera mawu athu, ndiye womwazamwaza, ndi woledzera. Pamenepo amuna onse a mudzi wake am’ponye miyala.’—Deuteronomo 21:18-21.
18 Machimo a munthuyo sanali kufotokozedwa kwa mtundu wonse ndi kuweruzidwa ndi mtundu wonsewo kapena ndi fuko lake lonse. M’malo mwake, “akulu” oikidwawo anali kusamalira mlanduwo monga oimira mpingo. (Yerekezani ndi Deuteronomo 19:16, 17 amene amanena za mlandu wosamalidwa ndi ‘ansembe ndi oweruza okhalako m’masiku amenewo.’) Mofananamo lerolino, ngati muyenera kuchita mbali yachitatu, akulu, amene amaimira mpingo, ndi amene amasamalira nkhaniyo. Cholinga chawonso n’chimodzimodzi, kubweza mbale wachikristu ngati n’kotheka. Amachita zimenezi mwa kupeŵa kuweruziratu usanakambidwe mlanduwo kapena kukhala atsankhu.
19. Kodi akulu amene asankhidwa kusamalira nkhani imeneyo adzayesetsa kuchita chiyani?
19 Iwo adzayesetsa kupenda mfundo zake ndi kumvetsera mboni zofunika kuti aone ngati munthuyo anachimwadi (kapena adakachimwabe). Iwo amafuna kuteteza mpingo ku zinthu zoipitsa ndi kuti mumpingomo musaloŵe mzimu wa dziko. (1 Akorinto 2:12; 5:7) Mogwirizana ndi ziyeneretso zawo za m’Malemba, iwo adzayesetsa “kuchenjeza m’chiphunzitso cholamitsa, ndi kutsutsa otsutsana [nawo].” (Tito 1:9) Padzakhala chiyembekezo chakuti wolakwayo sadzachita monga Aisrayeli amene mneneri wa Yehova analemba za iwo kuti: “Ndinaitana, inu simunayankhe; pamene ndinanena, simunamve; koma munachita choipa m’maso mwanga, ndi kusankha chimene Ine sindinakondwera nacho.”—Yesaya 65:12.
20. Kodi Yesu anati n’chiyani chiyenera kuchitika ngati wochimwa safuna kumvera ndi kulapa?
20 Koma nthaŵi zina ndi zina, wolakwa amasonyezabe mzimu umenewo. Zikatero, malangizo a Yesu ndi omveka: “Akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.” Ambuye sanalimbikitse kukhala opanda chifundo kapena okonda kukhumudwitsa ena. Koma malangizo a mtumwi Paulo onena za kuchotsa ochimwa osalapa mumpingo ndi omveka bwino lomwe. (1 Akorinto 5:11-13) Ngakhale zimenezi m’kupita kwa nthaŵi zingakhale ndi chotsatirapo cha kubweza wochimwayo.
21. Kodi pamakhalabe mwayi wotani kwa amene wachotsedwa mumpingo?
21 Tingaone kutheka kwa zimenezo m’fanizo la Yesu la mwana woloŵerera. Malinga ndi fanizolo, atakhala kunja kwa chiyanjo cha nyumba ya atate wake kwa nthaŵi yaitali ndithu, wochimwayo “anakumbukira mumtima.” (Luka 15:11-18) Paulo anauza Timoteo kuti ochimwa ena panthaŵi inayake adzalapa ndipo “nzeru zawo zidzabwereramo, ndipo adzapulumuka mumsampha wa Satana.” (2 Timoteo 2:24-26, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Tingakhaledi ndi chiyembekezo chakuti alionse amene achimwa mosalapa ndipo achotsedwa mumpingo adzaona kutayikidwa kwawo—ponse paŵiri kwa chiyanjo cha Mulungu ndi mayanjano ndiponso maunansi osangalatsa ndi Akristu anzawo—ndipo adzakumbukira mumtima.
22. Kodi mbale wathu tingam’bwezebe motani?
22 Yesu sanali kuona anthu a mitundu ina ndi amsonkho ngati osatheka kuwomboledwa. Mmodzi wa amsonkhowo, Mateyu Levi, analapa, ‘n’kutsatira Yesu,’ ndiponso anasankhidwa kukhala mtumwi. (Marko 2:15; Luka 15:1) Ndiye chifukwa chake ngati wochimwa lerolino ‘samveranso Mpingo’ ndipo achotsedwa mumpingowo, tingadikire kuti tione ngati iye, m’kupita kwa nthaŵi, adzalapa ndi kuwongola njira ya mapazi ake. Atatero n’kukhalanso mbali ya mpingo, tidzasangalala kuti tabweza mbale wathu m’khola la kulambira koona.
[Mawu a M’munsi]
a Buku lotchedwa Cyclopedia lolembedwa ndi McClintock ndi Strong limati: “Amsonkho otchulidwa m’Chipangano Chatsopano ankaonedwa monga akapirikoni ndi am’patuko, odetsedwa chifukwa cha kuyanjana kwawo nthaŵi zonse ndi anthu akunja, pokhala ziŵiya za opondereza. Anali kuwaika m’gulu limodzi ndi ochimwa . . . Posankhulidwa chotero ndiponso kupeŵedwa ndi anthu a moyo wabwino, mabwenzi awo okha kapena anzawo anali kupezeka pakati pa awo amene anali anthu okanidwa ofanana ndi iwo.”
b Milandu ina ya chinyengo, bodza, kapena ukathyali m’nkhani zabizinesi kapena zandalama ingaphatikizidwe pa machimo amene Yesu anatanthauza. Chosonyeza zimenezo n’chakuti atapereka malangizo olembedwa pa Mateyu 18:15-17, Yesu anapereka fanizo la akapolo (antchito) amene anakongola ndalama nalephera kuzibweza.
c Katswiri wina wodziŵa Baibulo anati: “Nthaŵi zina zimachitika kuti wolakwa amamvetsera kwambiri aŵiri kapena atatu enawo (makamaka ngati ndi anthu olemekezeka) kusiyana ndi munthu mmodzi, makamaka ngati munthuyo ndi amene wasiyana naye maganizo.”
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndi mtundu uti wa tchimo umene Mateyu 18:15-17 akutanthauza kwenikweni?
◻ Kodi tiyenera kukumbukira chiyani ngati tikufuna kuchita mbali yoyamba?
◻ Kodi ndani angathandize ngati tikufuna kuchita mbali yachiŵiri?
◻ Kodi ndani akukhudzidwa pochita mbali yachitatu, ndipo mbale wathu tingam’bwezebe motani?
[Chithunzi patsamba 18]
Ayuda ankapeŵa amsonkho. Mateyu anatembenuka kuchoka panjira yake ndi kutsatira Yesu
[Chithunzi patsamba 20]
Nthaŵi zambiri tingathetse vuto “pomwe pali maso anayi”