Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 1/15 tsamba 21
  • Chidziwitso pa Nyuzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chidziwitso pa Nyuzi
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Lingaliro Loipa”
  • “Mpata mu Chisinthiko”
  • Kuipsidwa kwa Okalamba
  • Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mafunso Ophunzirira Brosha ya Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Kodi Ndimphatso ya Moyo Kapena Mpsopsono wa Imfa?
    Galamukani!—1990
  • Kulemekeza Moyo ndi Mwazi Mwaumulungu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 1/15 tsamba 21

Chidziwitso pa Nyuzi

“Lingaliro Loipa”

Kudera nkhawa kowonjezereka ponena za mwazi woipa kukukakamiza ogwira ntchito za using’anga kuyang’ananso kachiwiri pa kulangizidwa kwa kupatsidwa mwazi. Henry B. Soloway, M. D. ,mlembi wa pepala ya Pathologist, anasonyeza kuti kuyambira pa kubadwa kwake kupatsidwa kwa mwazi kwakhala kokanthidwa ndi mavuto. “Poyambirira,” iye analongosola, “kupatsidwa kwa mwazi woonongeka mkati mwa kusokhanitsa ndi kusunga . . . kunapangitsa imfa zambiri kuchokera ku sepsis [kupatsidwa matenda] ndi shoko ya endotoxic [poizoni]. Kupatsiridwa kwa hepatitis B kudzera ku mwazi ndi zopangidwa kuchokera ku mwazi kunapangitsa imfa zochuluka mkati mwa Nkhondo Yadziko II.” Ndipo ngakhale ndi kupangidwa kwa miyezo yapamwamba yokonzedwa kutsimikizira mwazi woperekedwa “wabwino”, kupatsiridwa kwa matenda monga ngati AIDS kukupitirizabe.

Kudera nkhawa kwatsopano kwapitirira opulumuka anthawi zakale odwala kansa pambuyo pa opareshoni mkati mwa imene mwazi unaperekedwa. Soloway anati: “Pali choipa chowonekera ponena za kupulumuka pamene . . . mwazi upatsidwa kwa odwala omwe akupita ku opareshoni kaamba ka kansa ya mu mapapo, bere, ndi matumbo a akulu.” Nziti, tsopano, zomwe ziri zolowa m’malo? Soloway akuyankha: “Mboni za Yehova zaumirira . . . kuti kupatsidwa mwazi liri lingaliro loipa. Mwina mwake tsiku lina adzatsimikiziridwa kukhala ali olakwa. Koma pa nthawi ino chiri chotsimikizirika kuchirikiza lingaliro lawo, mosasamala kanthu za ku dandaula kotsutsa kuchokera kwaosunga mwazi.”

Kwenikweni, kuli kumvera kulamulo laumulungu komwe kwapangitsa Mboni za Yehova kukhala zaufulu ku zoturukapo zoipa za kulandira mwazi. Levitiko 17:14 imati: “Musamadya mwazi wa nyama iri yonse; pakuti moyo wa nyama yonse ndi mwazi wake.” Ndipo Akristu anauzidwa ‘kusala mwazi.’ (Machitidwe 15:28, 29) Mwachimvekere, Mulungu amawona katengedwe ka mwazi mu njira iri yonse monga “lingaliro loipa.”

“Mpata mu Chisinthiko”

“Mapiko atizirombo touluka sanasinthike kuchokera ku nsonga iri yonse kapena kuchokera ku china chiri chonse. Iwo anayamba kotheratu monga mphukira zazing’ono zomaturuka kuchokera ku msana.” Inatero nyuzipepala ya Swedish Svenska Dagbladet, kuchitira ripoti ponena za mafufuzidwe aposachedwa onena za ndi motani mmene tizirombo touluka tinapezera mapiko awo. “Malinga ndi nthanthi imodzi,” ripotilo limati, “zikanagwiritsira ntchito mapiko awo oyembekezeredwawo monga ngati msampha wogwirira tizilombo, kufikira tsiku lina tikanapeza kuti tikanatha kuuluka ndi kudzitenga ito tokha kupita m’mwamba kuchokera pansi kudzera mu mpweya kapena kutsika pansi kuchokera m’mitengo.”

Ripotilo linasonyezanso kuti ophunzira za moyo akukambitsirana lingaliro lakuti “mapiko oyembekezereka,“ pamene ali ochepa kwambiri kaamba ka kuulukira, akanatumikira monga zolandirira za kutentha kwa dzuwa kaamba ka kutenthetsa ndi kuchangamutsa thupi. Kodi nchiyani chimene chinapangitsa iwo kukula kuchokera ku msinkhu waung’ono kufika ku msinkhu waukulu? “Pano pali mpata mu chisinthiko womwe uli wovuta kulongosola,” likuvomereza ripotilo.

Baibulo, komabe, mwachimvekere limasonyeza mmene tizirombo touluka tinapezera mapiko awo. “Mulungu ndipo analenga . . . mbalame za mapiko yonse monga mwa mtundu wake,” anatero Genesis 1: 21. Pamene zaka za mafufuzidwe a sayansi zafikira kokha ku malingaliro anthanthi ndi “mpata . . . womwe uli wovuta kulongosola,” mbiri ya Baibulo imayenerana ndi malingaliro odziwika. Kulinganiza kwabwino koposa ndi ntchito ya mapiko a tizirombo, kumapereka chiyamikiro osati kwa chisinthiko chakhungu koma kwa Mlengi wanzeru.

Kuipsidwa kwa Okalamba

Anthu okalamba mochulukirachulukira akukhala nkhole za kuipsidwa ndi kunyalanyazidwa. Chiri chofala lerolino kumva za maripoti a anthu achikulire akuchitidwa zoipa, kuberedwa, kumenyedwa, ndi kuphedwa​—angakhale mu maiko mmene okalamba mwa mwambo amalemekezedwa kwambiri. M’dziko limodzi la Kum’mawa, “wogwira ntchito za mayanjano m’modzi akukamba za mayi wa chikulire atamangiriridwa pa goli ndi banja lake kwa zaka khumi ndi zinai ndi kuloledwa kusamba kamodzi pa milungu iwiri,” ikuchitira ripoti Asiaweek. Ikuwonjezera kuti mu dziko lina la Chiasia mayi wachikulire wa zaka 60 “anafa posachedwapa mu nyumba ya anthu okalamba. Mwana wake wamwamuna ndi mpongozi wake sanafike nkomwe pa kama yake ya imfa.” Mkhalidwewu siuli wowona mocheperako mu maiko a Kumadzulo. “Chifupifupi m’modzi mwa okalamba 25 a Chiamereka amanyalanyazidwa kapena kuipsidwa, kaya kunyumba kapena ku malo ophunzirirako,” inatero U. S. News &World Report. “Kunyalanyazidwa uli mkhalidwe wofala kwambiri wa kuchitidwa zoipa . . . ponse pawiri kuipsidwa kwa kuthupi ndi kuipsidwa kwakugonedwa kuli kochulukira.”

Nzika za Israyeli wakale limodzinso ndi ziwalo za mpingo wa Chikristu woyambirira zinachenjezedwa kusonyeza ulemu, kulingalira, ndi kulemekeza okalamba. (Eksodo 20:12; Levitiko 19:32; Aefeso 6:1 2; 1 Timoteo 5:1, 2) Komabe, mtumwi Paulo ananeneratu kuti masiku otsiriza tidzakhala mu “nthawi zowawitsa“ kumene anthu adzakhala kutali kwambiri kuchoka kuchitsogozo cha Mulungu. (2 Timoteo 3:1) Chimodzi cha zisonyezero zomwe Paulo anatchula chinali chakuti anthu adzakhala “osowa kotheratu . . . chikondi chaumunthu chachibadidwe.” (2 Timoteo 3:2, 3, The New Testament in Modern English, lolembedwa ndi J. B. Phillips) Ndani amene angakaikire chowonadi cha mawu ake?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena