Ma 1990—Zaka Khumi Zosatsimikizirika
KUFIKA kwa ma 1990 kwadza ndi ziyembekezo zatsopano za mtendere wadziko. Koma kwadzanso ndi kusatsimikizirika kosayerekezereka limodzi ndi chisokonezo.
Mwachitsanzo, pali kusatsimikizirika kwakukulu pazimene zidzachitika m’mitundu imene ikusiya makonzedwe azachuma olinganizidwa amene alephera. Maiko ambiri ameneŵa akuloŵa m’chikapitolizimu chamalonda odzifunira. Koma mitundu yambiri yokhala kale yakapitolizimu iri ndi umphaŵi wofalikira ndi ulova, kukwera mitengo kwazinthu ndi ngongole. Ngakhale United States ali ndi ngongole yaikulu ya mkati mwa dzikolo—madola okwanira mabiliyoni atatu—ndipo alinso mtundu wokongoletsa ngongole yaikulu koposa m’malonda amitundu yonse.
Chotulukapo chimodzi cha masoka achuma adziko chikusimbidwa ndi nkhani yamkonzi yamagazini a New York Times, imene inati: “Muli amphaŵi ambiri osoŵa chochita m’dziko koposa ndi kaleronse.”
Kumbali ina chifukwa chakukula kwa kusatsimikizirika, ambiri abwerera m’dyera: mkhalidwe wa ine choyamba, umbombo wa zinthu zakuthupi, chikhumbo chakukhuphuka mwamsanga mosasamala kanthu za zotulukapo zake. Kuwanda kwa kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa kuli umboni wazimenezi. Christopher Lasch, purofesala wophunzitsa mbiri yakale pa Yunivesite ya Rochester, akunena motere: “Maziko a mwambo wathu wamakhalidwe abwino agwa.”
Katswiri wazachuma wotchuka padziko lonse Arjo Klamer akunena kuti: “Akatswiri a maluso, azachuma, amalonda ndi mabanja anataya chikhulupiriro m’zitsimikizo za okhulupirira zamakono. . . . Kugwiritsidwa mwala kunafikira kukhala vuto lokhudza anthu a mbali zonse za moyo ndi maphunziro.” Akumalongosola kuti “chisokonezeko chafunga,” iye anawonjezera kuti: “Kusweka maganizo. Kuthedwa nzeru. Chinyengo. Chipwirikiti. Aŵa ndiwo ena a mawu ozoloŵereka. Mawuwa amalongosola lukanelukane wocholoŵana wapambuyo pa okhulupirira chimakono m’mene anthu amakono asokereramo.”
Uli umboni wochititsa chisoni wakuti madongosolo a ndale zadziko, a zachuma, ndi amakhalidwe a anthu adziko lino alibe njira zokhalitsa zothetsera mavuto aakulu alerolino ndi a kusatsimikizirika. Koma mkhalidwe weniweni umenewu unanenedweratu m’maulosi a Baibulo onena zanthaŵi yathuyi. Tamverani zitsanzo zoŵerengeka: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zowaŵitsa.” “Padziko lapansi chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru . . . anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza kudziko lapansi.”—2 Timoteo 3:1; Luka 21:25, 26.
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Fotografía de Publicaciones Capriles, Caracas, Venezuela